Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MUTU 1

Cikondi ca Mulungu N’camuyaya

Cikondi ca Mulungu N’camuyaya

“Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.” —1 YOHANE 5:3.

1, 2. N’cifukwa ciani mumam’konda Yehova Mulungu?

KODI mumam’konda Mulungu? Mwina mumam’konda kwambili, ndipo munadzipatulila kwa iye. Mumamuona kuti ni Bwenzi lanu lapamtima. Koma dziŵani kuti imwe musanam’konde Yehova, iye ndiye anayamba kukukondani. M’Baibo timaŵelenga kuti: “Timasonyeza cikondi, cifukwa iye ndi amene anayamba kutikonda.”—1 Yohane 4:19.

2 Ganizilani zonse zimene Yehova waticitila potionetsa cikondi cake. Anatipatsa dziko lapansi labwino, na zinthu zonse kuti tizikondwela na moyo. (Mateyu 5:43-48; Chivumbulutso 4:11) Iye amafuna kuti tikhale naye pa ubale wabwino, ndipo watithandiza kuphunzila za iye. Pamene tiŵelenga Baibo, timakhala tikumvetsela kwa Yehova. Ndipo pamene tipemphela, iye amakhala akumvetsela kwa ise. (Salimo 65:2) Amatitsogolela komanso kutilimbikitsa na mphamvu ya mzimu wake woyela. (Luka 11:13) Anacita kutumiza Mwana wake wapamtima padziko lapansi, kuti adzatiombole ku ucimo na imfa.—Ŵelengani Yohane 3:16; Aroma 5:8.

3. Tifunika kucita ciani kuti tisunge ubale wathu na Yehova?

3 Ganizilani mnzanu wapamtima, amene sanakusiyeni popita m’mavuto osiyana-siyana. Pamafunika khama kuti musunge ubwenzi wolimba wotelo. N’cimodzi-modzi na Yehova. Iye ni Bwenzi lathu la pamtima lopambana onse. Ubwenzi wathu na iye ungakhale kwamuyaya. Baibo imati: “Khalanibe m’cikondi ca Mulungu.” (Yuda 21, NWT-E) Nanga tingacite bwanji zimenezi? Baibo imayankha kuti: “Kukonda Mulungu kumatanthauza kusunga malamulo ake, ndipo malamulo akewo ndi osalemetsa.”—1 Yohane 5:3.

TANTHAUZO LA “KUKONDA MULUNGU”

4, 5. (a) Kodi “kukonda Mulungu” kumatanthauza ciani? (b) Nanga imwe munayamba bwanji kum’konda Yehova?

4 Kodi Baibo imatanthauza ciani ikati “kukonda Mulungu”? Mawu aya atanthauza mmene timamvela mumtima mwathu tikaganizila za Mulungu. Kodi mukumbukila pamene munayambila kum’konda Yehova?

Mukadzipatulila kwa Yehova na kubatizika, mumaonetsa kuti mumam’konda, ndipo mufuna kumumvelela nthawi zonse

5 Kumbukilani mmene munamvelela pamene munaphunzila kuti Yehova afuna kuti imwe mukakhale kwamuyaya m’dziko latsopano. Munaphunzila kuti adzacita zimenezi kupitila mu mphatso yamtengo wapatali imene Yehova anatipatsa, imene ni Mwana wake amene anatumiza pa dziko lapansi. (Mateyu 20:28; Yohane 8:29; Aroma 5:12, 18) Mutadziŵa kuti Yehova amakukondani kwambili, munakhudzika mtima, cakuti na imwe munayamba kum’konda.—Ŵelengani 1 Yohane 4:9, 10.

6. Kodi kukonda munthu kumaphatikizapo ciani? Nanga kukonda Mulungu kunakupangitsani kucita ciani?

6 Koma cikondi cimene munamvela cokonda Mulungu panali poyambila cabe. Mwacitsanzo, kukonda munthu kumaphatikizapo zambili, osati kukamba cabe kuti “Nimakukonda.” Cikondi ca zoona cimatipangitsa kucita zinthu zokondweletsa mnzathu. N’cimodzi-modzi kwa Yehova. Cifukwa comukonda, munayamba kucita zinthu zomukondweletsa. Pamene cikondi canu cinakula, munadzipatulila kwa Mulungu na kubatizika. Pocita zimenezi, munalonjeza kuti mudzatumikila Yehova kwamuyaya. (Ŵelengani Aroma 14:7, 8.) Kodi mungalikwanilitse bwanji lonjezo limenelo?

TIYENELA “KUSUNGA MALAMULO AKE”

7. Ngati Yehova timam’konda zoona, tidzacita ciani? Nanga malamulo ake ena amati ciani?

7 Cifukwa timam’konda Yehova, timamumvelela. Timacita zimenezo mwa ‘kusunga malamulo ake’ opezeka m’Baibo. Mawu ake, Baibo, amatiuza za umoyo umene Yehova afuna kuti tikhale nawo. Mwacitsanzo, iye amatiuza kuti kukolewa, kuba, kunama, kugonana na munthu amene sitinakwatilane naye, olo kulambila aliyense kapena ciliconse m’malo mwa iye, ni kulakwa.—1 Akorinto 5:11; 6:18; 10:14; Aefeso 4:28; Akolose 3:9.

8, 9. Ngati palibe lamulo lacindunji locokela m’Baibo, tingadziŵe bwanji zimene Yehova amafuna kuti ticite? Fotokozani citsanzo.

8 Koma kuti tikondweletse Yehova, tifunika kucita zambili, osati kumvela malamulo ake cabe. Iye sanatipatse malamulo onse pa cocitika ciliconse. Conco, nthawi zina pangakhale palibe lamulo lacindunji m’Baibo lotiuza kucita kapena kutiletsa cinacake. Kodi tingapange bwanji zosankha mwanzelu? (Aefeso 5:17) M’Baibo muli mfundo za makhalidwe abwino zotithandiza kudziŵa mmene Yehova amaonela zinthu. Pamene tiŵelenga Baibo, timafika podziŵa cikhalidwe ca Yehova. Timayamba kudziŵa mmene amaonela zinthu, zimene amakonda, na zimene amazonda.—Ŵelengani Salimo 97:10; Miyambo 6:16-19; onani Mfundo ya Kumapeto 1.

9 Mwacitsanzo, tingadziŵe bwanji zinthu zabwino kutamba pa TV kapena kuyang’ana pa Intaneti? Yehova sanacite kutomola kuti tizitamba zakuti-zakuti. Koma mfundo zimene anatipatsa zimatithandiza kusankha mwanzelu. Zosangalatsa zoculuka masiku ano zimaonetsanso kwambili zaciwawa, komanso zaciwelewele. Baibo imatiuza kuti Yehova “amadana kwambili ndi aliyense wokonda ciwawa,” na kuti iye “adzaweluza adama.” (Salimo 11:5; Aheberi 13:4) Kodi mfundo zimenezi zingatithandize bwanji kupanga zosankha mwanzelu? Tikadziŵa kuti cakuti-cakuti Yehova amadana naco, kapena amaciona kuti ni coipa, tiyenela kucipewa.

10, 11. Kodi tiyenela kumvelela Yehova cifukwa ciani?

10 N’cifukwa ciani tifunika kumumvelela Yehova? Sikuti timafuna kupewa cilango cabe, kapena mavuto amene angabwele pambuyo pake iyai. (Agalatiya 6:7) Koma, cifukwa cakuti timam’konda. Ana anzelu amafuna kukondweletsa atate awo. Na ise n’cimodzi-modzi. Timafuna kukondweletsa Atate wathu wakumwamba. Timamvela bwino ngako, tikadziŵa kuti Yehova tam’kondweletsa.—Salimo 5:12; Miyambo 12:2; onani Mfundo ya Kumapeto 2.

11 Komanso, timamvela Yehova osati cabe pa zinthu zosavuta, kapena cifukwa palibe mwina mocitila, iyayi. Ndipo siticita kusankhapo malamulo kapena mfundo zimene tingatsatile. (Deuteronomo 12:32) M’malo mwake, timamumvelela pa zonse, mogwilizana na mawu a wamasalimo amene anati: ‘Nimakondwela na malamulo anu amene nimawakonda.’ (Salimo 119:47; Aroma 6:17) Timafuna kukhala monga Nowa, amene anaonetsa cikondi cake kwa Yehova, mwa kucita zonse zimene Yehova anam’lamula. Baibo imakamba kuti Nowa “anacitadi momwemo.” (Genesis 6:22) Kodi na imwe simungakonde kuti Yehova akakambe zimenezi kwa imwe?

12. Tingamukondweletse bwanji Yehova?

12 Kodi Yehova amamvela bwanji ngati timumvelela? Amakondwela kwambili. (Miyambo 11:20; 27:11) Ganizani cabe, kukondweletsa Mlengi wa cilengedwe conse! Koma iye satiumiliza kucita zimenezo. Inde, cifukwa anatipatsa ufulu wosankha zocita. Izi zitanthauza kuti tili na ufulu wosankha kucita zabwino kapena zoipa. Yehova amafuna kuti cikondi cathu pa iye citipangitse kusankha kucita zinthu zabwino, kuti tikhale na umoyo wabwino.—Deuteronomo 30:15, 16, 19, 20; onani Mfundo ya Kumapeto 3.

‘MALAMULO AKE SI OLEMETSA’

13, 14. Timadziŵa bwanji kuti malamulo a Mulungu si yovuta kuyakonkha? Fotokozani citsanzo.

13 Bwanji ngati timaona kuti malamulo a Yehova ni yovuta kuyakonkha, na kuti angatilande ufulu? Baibo imakamba momveka bwino kuti: ‘Malamulo ake si olemetsa.’ (1 Yohane 5:3) Baibo yakuti New English Translation inamasulila vesi imeneyi kuti: “Malamulo ake sali monga cikatundu colema.” Inde, malamulo a Yehova si ‘olemetsa,’ sitingakangiwe kuyakonkha. Mulungu sangatiuze kucita zimene sitingakwanitse.

14 Mwacitsanzo, tikambe kuti mukuthandiza mnzanu kukukila ku nyumba ina. Iye walonga katundu yonse m’mabokosi. Mabokosi ena ni opepuka, koma ena ni olema kwambili, cakuti afunika kunyamuzana. Kodi mnzanuyo angakuuzeni kunyamula mwekha bokosi yolema yofunika kunyamula anthu aŵili? Sangacite zimenezo. Cifukwa? Safuna kuti mudzipweteke. Molingana na mnzanu ameneyo, Yehova sangatiuze kucita zimene sitingakwanitse. (Deuteronomo 30:11-14) Yehova amatidziŵa bwino. ‘Amadziŵa bwino mmene anatiumbila, amakumbukila kuti ndise fumbi.’—Salimo 103:14.

15. N’cifukwa ciani malamulo a Yehova ni otipindulitsa nthawi zonse?

15 Mose anauza mtundu wa Isiraeli kuti malamulo a Yehova anali opindulitsa kwa iwo nthawi zonse, na kuti kuwatsatila kudzawathandiza ‘kukhala na moyo.’ (Deuteronomo 5:28-33; 6:24) Cimodzi-modzi masiku ano. Ciliconse cimene Yehova amatiuza kucita n’cotipindulitsa. (Ŵelengani Yesaya 48:17.) Atate wathu Yehova, nthawi zonse amafuna kuti zinthu zitiyendele bwino. (Aroma 11:33) Baibo imatiuza kuti: “Mulungu ndiye cikondi.” (1 Yohane 4:8) Inde, ciliconse cimene Yehova wakamba olo kucita, cimacokela m’cikondi.

16. Tingakwanitse bwanji kumvela Mulungu olo kuti ndise opanda ungwilo, ndipo timakhala m’dziko loipa?

16 Ngakhale n’conco, kumvelela Mulungu kumavuta nthawi zina. Tikukhala m’dziko loipa limene wolamulila wake ni Mdyelekezi. Iye amatunthizila anthu kucita vinthu voipa. (1 Yohane 5:19) Tifunikilanso kulimbana na maganizo athu komanso mtima wopanda ungwilo, zimene zimatipangitsa kucimwila Mulungu. (Aroma 7:21-25) Koma cikondi cathu kwa Yehova cimatithandiza kucita zinthu zabwino. Amayamikila pamene tiyesetsa kumumvelela, ndipo amatithandiza mwa kutipatsa mphamvu ya mzimu wake woyela. (1 Samueli 15:22, 23; Machitidwe 5:32) Mzimu woyela umatithandiza kukhala na makhalidwe amene amatilimbikitsa kumvela Mulungu.—Agalatiya 5:22, 23.

17, 18. (a) Tidzaphunzila ciani m’buku ino? (b) Nanga tidzakambilana ciani m’nkhani yokonkhapo?

17 M’buku ino, tidzaphunzila mmene tingakhalile na umoyo wokondweletsa Yehova. Tidzaphunzilanso mmene tingagwilitsile nchito malamulo, na mfundo zake mu umoyo wathu. Kumbukilani kuti Yehova satikakamiza kuti tizimumvela. Koma tikasankha kumumvelela, tidzakhala na umoyo wabwino pali pano, komanso kutsogolo. Copambana zonse, ngati tikhala omvela, tidzaonetsa Mulungu kuti timam’konda kwambili.—Onani Mfundo ya Kumapeto 4.

18 Pofuna kutithandiza kudziŵa cabwino na coipa, Yehova anatipatsa cikumbumtima. Ngati cikumbumtima cathu ticiphunzitsa bwino, cingatithandize “kusunga malamulo ake.” Conco, kodi cikumbumtima ciani? Nanga tingaciphunzitse bwanji? Tiyeni tione.