Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila

Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila

Kwa imwe okonda Yehova Mulungu na Mawu ake, Baibo:

Yesu anati: “Mudzadziŵa coonadi, ndipo coonadi cidzakumasulani.” (Yohane 8:32) Tangoganizani mmene munamvelela pamene munapeza coonadi ca m’Baibo! Cinali cinthu cokondweletsa ngako, kuona kuti m’dziko lino lodzala na mabodza, munthu n’kupeza coonadi.—2 Timoteyo 3:1.

Yehova Mulungu amafuna kuti tidziŵe coonadi. Ndipo cifukwa timakonda anthu, timafuna kuŵauzako za coonadi cimeneco. Koma kutumikila Mulungu kumaloŵetsamo zambili. Tiyenela kuyesetsa kukhala monga Akhristu, cifukwa timalemekeza kwambili mfundo za Yehova. Yesu anafotokoza njila yofunika kwambili yoonetsela kuti timakonda Mulungu. Iye anati: “Mukasunga malamulo anga, mudzakhalabe m’cikondi canga, monga mmene ine ndasungila malamulo a Atate ndi kukhalabe m’cikondi [cawo].”—Yohane 15:10.

Yesu amaŵakonda kwambili Atate wake, ndipo amacita ciliconse cimene amamuuza. Ngati tingatengele citsanzo ca Yesu mu umoyo wathu, Yehova adzatikonda kwambili, ndipo tidzapeza cimwemwe ceni-ceni. N’cifukwa cake Yesu anakamba kuti: “Ngati zimenezi mukuzidziŵa, ndinu odala mukamazicita.”—Yohane 13:17.

Tikhulupilila kuti buku ino, idzakuthandizani kudziŵa mokhalila na umoyo wogwilizana na coonadi ca m’Baibo, kuti mukhale bwenzi la Mulungu. Pemphelo lathu n’lakuti cikondi canu pa Mulungu cikule, ndipo mukhalebe “mu cikondi ca Mulungu . . . kuti mukapeze moyo wosatha.”—Yuda 21, NW.

Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova