Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MUTU 14

Khalani Oona Mtima M’zinthu Zonse

Khalani Oona Mtima M’zinthu Zonse

“Tikufuna kucita zinthu zonse moona mtima.”—AHEBERI 13:18.

1, 2. Kodi Yehova amamvela bwanji akaona kuti timayesetsa kukhala oona mtima?

TIYELEKEZE kuti mwana akubwelela ku nyumba kucokela ku sukulu. Pa njila aona munthu wina wagwetsa cola ca ndalama zambili. Kodi adzacita bwanji? M’malo motenga n’kubisa, acibweza kwa mwini wake. Mayi ake pomvela zimene wacita, amunyadila kwambili.

2 Makolo ambili amakondwela ngati ana awo ni oona mtima. Atate wathu wakumwamba, Yehova, ni “Mulungu wa coonadi,” ndipo amakondwela kwambili pamene tikhala oona mtima. (Salimo 31:5) Timafuna kumukondweletsa, mwa “kucita zinthu zonse moona mtima.” (Aheberi 13:18) Tiyeni tsopano tikambilane mbali zinayi m’zimene kuona mtima kungakhale kovutilapo. Kenako tidzaonanso mapindu amene timapeza tikakhalabe oona mtima.

KUKHALA OONA MTIMA KWA IFE ENI

3-5. (a) Kodi tingadzinamize bwanji tekha? (b) N’ciani cingatithandize kukhala oona mtima kwa ife eni?

3 Kuti tikhale oona mtima kwa ena, coyamba tiyenela kukhala oona mtima kwa ife eni. Zimenezi nthawi zina zimakhala zovuta. M’nthawi ya Akhristu oyambilila, abale mu mpingo wa Laodikaya anadzinamiza okha poganiza kuti anali kukondweletsa Mulungu, pamene m’ceni-ceni sizinali conco. (Chivumbulutso 3:17) Ifenso tikhoza kudzinamiza tekha za mtundu wa munthu amene tili.

4 Wophunzila Yakobo anafotokoza kuti: “Ngati munthu akudziona ngati wopembedza, koma salamulila lilime lake, ndipo akupitiliza kunyenga mtima wake, kupembedza kwa munthu ameneyo n’kopanda pake.” (Yakobo 1:26) Kungakhale kudzinamiza tekha ngati tiganiza kuti, malinga ngati timacita zinthu zina zabwino, Mulungu sangasamale kweni-kweni ngati tikhala amwano, kulankhula motafula, kapena kukamba mabodza. Kodi tingapewe bwanji kumadzinamiza tekha?

5 Tikayang’ana pa galasi, timaona mmene timaonekela kunja. Koma tikaŵelenga Baibo, timaona munthu wathu wamkati. Baibo ingatithandize kudziŵa mbali zimene ticita bwino, komanso zofooka zathu. Timadziŵa zofunika kusintha m’maganizo, m’zocita, komanso m’malankhulidwe. (Ŵelengani Yakobo 1:23-25.) Koma ngati tiganiza kuti zonse zili bwino kwa ife, sitingapange kusintha kulikonse. Conco, tifunika kudziyang’ana m’Baibo moona mtima. (Maliro 3:40; Hagai 1:5) Pemphelo limatithandizanso kudziyang’ana moona mtima. Tingam’pemphe Yehova m’pemphelo kuti atisanthule, na kutithandiza kuona zofooka zathu kuti tiziwongolele. (Salimo 139:23, 24) Tisaiŵale kuti “munthu wocita zaciphamaso Yehova amanyansidwa naye, koma amakonda anthu owongoka mtima.”—Miyambo 3:32.

KUKHALA OONA MTIMA M’BANJA

6. N’cifukwa ciani mwamuna na mkazi wake afunika kukhalilana oona mtima?

6 Kukhala oona mtima n’kofunika maningi m’banja. Mwamuna na mkazi wake ngati amamasukilana, amadzimva otetezeka, ndipo amakhulupililana. Kusaona mtima m’banja kumacitika m’njila zosiyana-siyana. Mwacitsanzo, munthu wapabanja angayambe kuceza motayilila na munthu wina, kumatamba zamalisece mseli, kapena kukhala na cisumbali. Koma onani zimene wamasalimo anakamba: “Sindinakhale pansi pamodzi ndi anthu acinyengo. Ndipo sindinayanjane ndi anthu obisa umunthu wawo.” (Salimo 26:4) Ngakhale kukhala na maganizo olakwika okhumbila munthu wina, n’kucita cinyengo kwa mnzanu wa m’cikwati. Ndipo kumeneko n’kuika cikwati canu paciswe.

Mwamsanga, pewani ciliconse cimene cingafooketse cikwati canu

7, 8. Kodi Baibo ingatithandize bwanji kuphunzitsa ana kuona ubwino wokhala oona mtima?

7 Ana nawonso ayenela kuphunzitsidwa kuti kuona mtima n’cinthu cofunika kwambili. Makolo angaseŵenzetse Baibo kucita zimenezi. Mu Baibo muli zitsanzo zoipa zofunika kupewa, za anthu amene anali osaona mtima. Muli ca Akani, amene anakhala kawalala; Gehazi, amene anakamba bodza kuti apeze ndalama; komanso Yudasi, amene anali kuba ndalama, ndipo pambuyo pake anapeleka Yesu na ndalama 30 zasiliva.—Yoswa 6:17-19; 7:11-25; 2 Mafumu 5:14-16, 20-27; Mateyu 26:14, 15; Yohane 12:6.

8 Koma m’Baibo mulinso zitsanzo zabwino za anthu ambili amene anali oona mtima. Muli ca Yakobo, amene analimbikitsa ana ake kubweza ndalama zomwe anapeza m’matumba awo; Yefita na mwana wake wamkazi, amene anasunga lonjezo kwa Mulungu; komanso Yesu, amene anakhalabe woona mtima pa zocitika zovuta kwambili. (Genesis 43:12; Oweluza 11:30-40; Yohane 18:3-11) Zitsanzo zimenezi zingathandize ana kuona kufunika kokhala oona mtima.

9. Cimacitika n’ciani kwa ana ngati makolo awo ni oona mtima?

9 Makolo angaphunzilepo kanthu pa mfundo ya m’Baibo yakuti: “Kodi iwe wophunzitsa enawe, sudziphunzitsa wekha? Iwe amene umalalikila kuti ‘Usabe,’ umabanso kodi?” (Aroma 2:21) Pamene makolo acita zosiyana na zimene amaphunzitsa ana awo, ana amadziŵa. Ngati timauza ana athu kuti azikamba zoona, koma ife n’kumakamba mabodza, ana amasokonezeka. Akaona kuti makolo awo amanama, ngakhale pa zinthu zazing’ono, nawonso angayambe kucita cimodzi-modzi. (Ŵelengani Luka 16:10.) Koma akamaona kuti makolo awo amakamba zoona, akakula amakhala makolo odalilika kwa ana awo.—Miyambo 22:6; Aefeso 6:4.

KUKHALA OONA MTIMA MU MPINGO

10. Kodi tingakhale bwanji oona mtima poceza na Akhristu anzathu?

10 Tifunikanso kukhala oona mtima kwa abale na alongo athu mu mpingo. N’cosavuta makambilano abwino-bwino kusintha n’kukhala mijedo, ngakhale misece. Ngati tiuza wina zimene tinamva, koma tilibe nazo umboni weni-weni, tingayambe kufalitsa mabodza. Tiyenela ‘kulamulila milomo yathu.’ (Miyambo 10:19) Kukhala oona mtima sikutanthauza kuti tizikamba ciliconse cimene tiganiza, cimene tidziŵa, kapena cimene tamvela. Olo kuti zimene tifuna kukamba n’za zoona, mwina nkhaniyo siitikhudza, ndipo kungakhale kosafunika, kapena kupanda cikondi kuuzako ena. (1 Atesalonika 4:11) Anthu ena amadzikhululukila akacita mwano, akumati: “Koma nikamba zoona.” Pokhala anthu a Yehova, mawu athu azikhala acisomo, komanso okoma mtima.—Ŵelengani Akolose 4:6.

11, 12. (a) Kodi zinthu zimaipila-ipila bwanji ngati munthu wocimwa abisa chimo lake? (b) Tikadziŵa kuti mnzathu anacita colakwa cacikulu, tiyenela kupewa maganizo ati, ndipo n’cifukwa ciani? (c) Nanga tingakhale bwanji oona mtima ku gulu la Yehova?

11 Yehova anapatsa akulu udindo wothandiza mpingo. Koma kuti akulu atithandize, tifunika kukhala oona mtima kwa iwo. Cifukwa ciani? Tiyelekeze kuti imwe mwadwala, ndiyeno mwapita kwa dokotala. Kodi mungabise osafotokoza mmene mumvelela m’thupi? Mukacita zimenezo, kodi dokotala angakuthandizeni bwanji? Mofananamo, tikacita colakwa cacikulu, sitiyenela kubisa. M’malo mwake, tifunika kupita kwa akulu na kukawafotokozela moona mtima. (Salimo 12:2; Machitidwe 5:1-11) Tiyelekezenso motele: Bwanji ngati mwadziŵa kuti mnzanu anacita colakwa cacikulu? (Levitiko 5:1) Kodi mudzakamba kuti: “Popeza ni mnzanga wapamtima, nidzasunga cisinsi”? Kapena mudzakumbukila kuti akulu ndiwo ali na udindo womuthandiza kuti akonzenso ubale wake na Yehova?—Aheberi 13:17; Yakobo 5:14, 15.

12 Tiyenela kukhalanso oona mtima ku gulu la Yehova pamene tilemba malipoti a utumiki wa kumunda. Timakhalanso oona mtima pamene tifunsila upainiya, kapena utumiki wina uliwonse.—Ŵelengani Miyambo 6:16-19.

13. Pa nkhani ya bizinesi na nchito, kodi tingakhale bwanji oona mtima?

13 Abale na alongo afunika kulekanitsa nkhani za bizinesi na kulambila. Mwacitsanzo, sitiyenela kucita za bizinesi pa Nyumba ya Ufumu, kapena pamene tili mu ulaliki. Komanso, sitifuna kudyela masuku pamutu abale na alongo pocita bizinesi. Ngati munalemba nchito Mboni, apatseni malipilo awo pa nthawi yake, komanso pa mlingo umene munapangana. Apatseninso mapindu onse ofunikila malinga na malamulo a boma. Izi zingaphatikizepo insuwalansi ya zacipatala kapena masiku a chuti. (1 Timoteyo 5:18; Yakobo 5:1-4) Ndipo ngati museŵenzela Mboni inzanu, musayembekezele kuti azicita zinthu mokukondelani. (Aefeso 6:5-8) Muyenela kugwila nchito kwa maola amene munagwililzana, komanso kuigwila molimbika.—2 Atesalonika 3:10.

14. Kodi Akhristu afunika kucita ciani asanayambe kucitila pamodzi bizinesi?

14 Nanga bwanji ngati tagwilizana kucita bizinesi na m’bale kapena mlongo wathu? Kapena mwina takongozana ndalama? Ni bwino kutsatila mfundo yothandiza kwambili ya m’Baibo: Lembelanani zonse! Pamene mneneli Yeremiya anagula munda, analemba makope aŵili a cipangano cawo, ndipo mboni zinasainila kope imodzi. Makope onse aŵiliwo anasungidwa monga umboni. (Yeremiya 32:9-14; onaninso Genesis 23:16-20.) Ena angaone kuti kucita kulembelana cipangano, kungaonetse monga simudalila m’bale wanu. Koma m’ceni-ceni, kulembelana cipangano kumapewetsa kumvana molakwa, kugwilitsana mwala, na mikangano. Ngakhale pa nkhani ngati zimenezi, kumbukilani kuti mtendele wa mpingo ni wofunikila kuposa bizinesi.—1 Akorinto 6:1-8; onani Mfundo ya Kumapeto 30.

KUKHALA OONA MTIMA M’DZIKOLI

15. Kodi Yehova amamvela bwanji poona zacinyengo m’mabizinesi?

15 Tiyenela kukhala oona mtima kwa aliyense, kuphatikizapo amene si Mboni za Yehova. Kwa Yehova n’cinthu cofunika kwambili kwa ife. “Sikelo yacinyengo imam’nyansa Yehova, koma mwala woyezela, wolemela mokwanila, umam’sangalatsa.” (Miyambo 11:1; 20:10, 23) Ngakhale mu nthawi za m’Baibo, anthu anali kuseŵenzetsa masikelo pocita malonda. Koma amalonda ena anali kubela makasitoma awo, mwacitsanzo mwa kuchuna masikelo awo. Ngakhale masiku ano, cinyengo n’cofala kwambili m’zamalonda. Yehova anali kunyansidwa na cinyengo kalelo, masiku anonso n’cimodzi-modzi.

16, 17. Kodi n’kusaona mtima kofala kuti kumene tiyenela kupewa?

16 Tonsefe timakumana na zocitika pamene tingacite mosaona mtima—monga pofunsila nchito, polemba mafomu a boma, kapena pa mayeso ku sukulu. Anthu ambili amaona kuti si vuto kweni-kweni kunama, kuwonjezela, kapena kupotozako mayankho. Izi n’zosatidabwitsa. Baibo inakambilatu kuti m’masiku otsiliza, anthu adzakhala “odzikonda, okonda ndalama, . . . osakonda zabwino.”—2 Timoteyo 3:1-5.

17 Ndipo nthawi zina, zingaoneke kuti anthu acinyengo zinthu zimawayendela masiku ano. (Salimo 73:1-8) Cifukwa ca kuona mtima, Mkhristu angacotsedwe nchito, kuluza ndalama, ngakhale kucitilidwa nkhanza ku nchito. Koma m’pake kutailapo ciliconse pa kuona mtima. Cifukwa ciani?

MADALITSO A KUONA MTIMA

18. N’cifukwa ciani mbili yabwino ni yofunika?

18 Kudziŵika monga munthu woona mtima, wokhulupilika, ndiponso wodalilika, ni cinthu camtengo wapatali, komanso cosoŵa m’dziko lino. Aliyense wa ife ali nawo mpata wodzipangila mbili imeneyi. (Mika 7:2) N’zoona kuti anthu ena angakusekeni cifukwa cokhala woona mtima, ndipo angati ndimwe wopusa. Koma alipo ena amene adzayamikila kuona mtima kwanu, ndipo azikukhulupililani. Zungulile dziko lapansi, Mboni za Yehova n’zodziŵika kuti ni anthu oona mtima. Anthu ena amakonda kulemba nchito Mboni podziŵa kuti ni oona mtima. Ndipo ena akacotsedwa nchito cifukwa ca kuba, nthawi zambili Mboni amazisungabe pa nchito.

Timalemekeza Yehova mwa kugwila nchito molimbika

19. Ngati mukhala woona mtima, kodi ubwenzi wanu na Yehova udzakhala wotani?

19 Mukakhala woona mtima m’zinthu zonse, mudzakhala na cikumbumtima coyela, na mtendele wa maganizo. Timakhala monga Paulo, amene analemba kuti: “Tikhulupilila kuti tili ndi cikumbumtima coona.” (Aheberi 13:18) Coposa zonse, Atate wathu wakumwamba, Yehova, adzaona na kuyamikila khama lanu poyesetsa kukhala woona mtima m’zinthu zonse.—Ŵelengani Salimo 15:1, 2; Miyambo 22:1.