Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MUTU 17

Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu

Khalanibe m’Cikondi ca Mulungu

“Dzilimbitseni pa maziko a cikhulupililo canu coyela kopambana . . . Khalanibe m’cikondi ca Mulungu.”—YUDA 20, 21, NW.

1, 2. Kodi tifunika kucita ciani kuti tikhalebe m’cikondi ca Mulungu?

IFE TONSE timafuna kukhala olimba, komanso athanzi labwino. N’cifukwa cake timayesa kudya zakudya zabwino, kucita maseŵela olimbitsa thupi, na kusamalila bwino thupi lathu. Olo kuti pafunika kulimbikila, timakondwela na zotulukapo zake. N’cifukwa cake sitileka. Koma tifunikanso kukhala olimba komanso athanzi m’njila inanso.

2 Tinacita bwino kwambili kuyamba kuphunzila za Yehova. Koma tifunika kupitiliza kulimbitsa ubale wathu na iye. Pamene Yuda analimbikitsa Akhristu anzake kuti, “Khalanibe m’cikondi ca Mulungu,” anafotokoza mmene angacitile zimenezo. Anawauza kuti: “Dzilimbitseni pa cikhulupililo canu coyela kopambana.” (Yuda 20, 21, NW) Conco, kodi tingalimbitse bwanji cikhulupililo cathu?

PITILIZANI KULIMBITSA CIKHULUPILILO CANU

3-5. (a) Kodi Satana amafuna kuti malamulo a Yehova muziyaona bwanji? (b) Koma imwe m’mayaona bwanji malamulo a Yehova na mfundo zake?

3 N’cinthu cofunika kwambili kwa imwe, kukhulupilila na mtima wonse, kuti malangizo a Yehova ndiye abwino koposa. Koma Satana, amafuna muziganiza kuti malamulo a Mulungu ni ovuta kutsatila, na kuti mudzapeza cimwemwe ngati mudzisankhila mwekha cabwino na coipa. Kungoyambila m’munda wa Edeni, Satana wakhala akulimbikitsa maganizo amenewa. (Genesis 3:1-6) Ndipo mpaka masiku ano, akulimbikilabe.

4 Kodi maganizo amene Satana akulimbikitsa ni abwino? Kodi n’zoona kuti malamulo a Yehova ni ovuta kwambili? Iyai. Tiyeni tipeleke citsanzo. Tikambe kuti munali kuyenda m’nkhalango yokongola. Ndiyeno muona waya yaitali yochinga mbali ina. Pokhumudwa, mukuti, ‘Anaikilanji waya yochinga iyi, yanivalila njila!’ Panthawi imeneyo, mukumva kubangula kwa mkango kuseli kwa waya imeneyo. Kodi mudzaganiza bwanji lomba za waya imeneyo? Mudzaiyamikila kwambili, cifukwa mukanakhala cakudya ca mkangowo! Mfundo za Yehova ndiye waya yochinga. Ndipo Mdyelekezi ndiye mkango. Mawu a Mulungu amaticenjeza kuti: “Khalanibe oganiza bwino, ndipo khalani maso. Mdani wanu Mdyelekezi akuyenda-yenda uku ndi uku ngati mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.”—1 Petulo 5:8.

5 Yehova amatifunila umoyo wabwino kwambili. Safuna kuti Satana azitinamiza iyai. Ndiye cifukwa cake anatipatsa malamulo na mfundo zake, kuti atiteteze komanso kuti tikhale acimwemwe. (Aefeso 6:11) Yakobo analemba kuti: “Woyang’anitsitsa m’lamulo langwilo limene limabweletsa ufulu, amene alimbikila kutelo . . . adzakhala wosangalala policita.”—Yakobo 1:25.

6. N’ciani cimatithandiza kuona kuti njila za Mulungu ndiye zabwino koposa?

6 Ngati titsatila malangizo a Yehova, timakhala na umoyo wabwino, ndipo ubwenzi wathu na iye umalimba. Mwacitsanzo, timapindula tikamvela langizo lake lakuti tizipemphela kwa iye kaŵili-kaŵili. (Mateyu 6:5-8; 1 Atesalonika 5:17) Timakhala acimwemwe tikatsatila malangizo ake, monga a kusonkhana pamodzi pom’lambila na kulimbikitsana, komanso kutengako mbali mokwanila m’nchito yolalikila na kuphunzitsa anthu. (Mateyu 28:19, 20; Agalatiya 6:2; Aheberi 10:24, 25) Poona mmene zinthu zimenezi zatithandizila kulimbitsa cikhulupililo cathu, timakhutila na mtima wonse kuti njila za Yehova ndiye zabwino koposa.

7, 8. Cingatithandize n’ciani kuti tisamadele nkhawa za mayeselo amene tingakumane nawo kutsogolo?

7 Mwina tingade nkhawa kuti kutsogolo tingakakumane na mayeselo ovuta kuyapilila. Ngati nthawi zina mumaganizo conco, kumbukilani mawu a Yehova akuti: “Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendeleni bwino, amene ndimakucititsani kuti muyende m’njila imene muyenela kuyendamo. Zingakhale bwino kwambili mutamvela malamulo anga! Mukatelo mtendele wanu udzakhala ngati mtsinje, ndipo cilungamo canu cidzakhala ngati mafunde a m’nyanja.”—Yesaya 48:17, 18.

8 Inde, tikamamvela Yehova, mtendele wathu udzakhala monga mtsinje umene madzi ake saphwila. Ndipo cilungamo cathu cidzakhala monga mafunde a panyanja, amene amagavila pagombe lake mosalekeza. Kaya tikumane na vuto yabwanji mu umoyo wathu, tingakhale okhulupilika kwa iye. Baibo imatilimbikitsa kuti: “Umutulile Yehova nkhawa zako, ndipo iye adzakucilikiza. Sadzalola kuti wolungama agwedezeke.”—Salimo 55:22.

‘TIYESETSE KUKHALA OKHWIMA MWAUZIMU’

9, 10. Kodi kukhala wokhwima kumatanthauza ciani?

9 Pamene mulimbitsa ubale wanu na Yehova, mufunikilanso ‘kuyesetsa kukhala wokhwima mwauzimu.’ (Aheberi 6:1) Kodi kukhala wokhwima kutanthauza ciani?

10 Kukhwima mwauzimu sikubwela na kukula cabe kuthupi iyai. Kumabwela mwa kupanga Yehova kukhala Bwenzi lathu la pamtima, na kuyesa kuona zinthu mmene iye amazionela. (Yohane 4:23) Paulo analemba kuti: “Otsatila zofuna za thupi amaika maganizo awo pa zinthu za thupi, koma otsatila zinthu za mzimu amaika maganizo awo pa zinthu za mzimu.” (Aroma 8:5) Munthu wokhwima mwauzimu saika patsogolo zosangalatsa kapena cuma. M’malo mwake, amalunjika maganizo ake pa kutumikila Yehova, ndipo amapanga zosankha zanzelu mu umoyo wake. (Miyambo 27:11; ŵelengani Yakobo 1:2, 3.) Salola kuti ena amunyengelele kucita zoipa ayi. Munthu wokhwima mwauzimu amadziŵa cimene cili cabwino, ndipo palibe angamulepheletse kucicita.

11, 12. (a) Kodi Paulo anati ciani za ‘mphamvu za kuzindikila’ za Mkhristu? (b) Kodi kukhala Mkhristu wokhwima mwauzimu kumalingana bwanji na ukatswili wothamanga?

11 Kukhwima kumafuna khama. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Koma cakudya cotafuna ndi ca anthu okhwima mwauzimu, amene pogwilitsa nchito mphamvu zawo za kuzindikila, aphunzitsa mphamvuzo kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.” (Aheberi 5:14) Mawu akuti ‘kuphunzitsa,’ angatikumbutse za kuphunzitsa wina kuthamanga kwa mpikisano.

12 Tikaona katswili wothamanga atalikumba liŵilo pa mpikisano, timadziŵa kuti anatailapo nthawi yambili, komanso khama kuti afike pa luso limenelo. Sanabadwe ali katswili kale iyai. Mwana akabadwa, sadziŵa angakhale moseŵenzetsela manja na miyendo yake. Koma m’kupita kwa nthawi, amayamba kudziŵa mogwilila zinthu, kudamphila, mpaka kuyamba kuyenda. Ndipo akaphunzitsidwa, amafika pokhala katswili weni-weni. N’cimodzi-modzi na kukhwima mwauzimu. Kumafuna nthawi na khama.

13. N’ciani cingatithandize kuganiza molingana na Yehova?

13 M’buku ino, takambilana mmene tingakhalile na maganizo a Yehova, na kuona zinthu mmene iye amazionela. Taona kuti tiyenela kulemekeza malamulo a Yehova na kuyakonda. Popanga zosankha, tiyenela kumadzifunsa kuti: ‘Ni malamulo kapena mfundo za m’Baibo ziti zimene zingathandize? Kodi ningazigwilitsile nchito bwanji? Nanga Yehova angafune kuti nicite bwanji?’—Ŵelengani Miyambo 3:5, 6; Yakobo 1:5.

14. Kodi tifunika kucita ciani kuti tilimbitse cikhulupililo cathu?

14 Sitiyenela kuleka kulimbitsa cikhulupililo cathu mwa Yehova. Monga mmene zakudya zopatsa thanzi zimathandizila matupi athu kukhala olimba, kuphunzila za Yehova kumatithandiza kulimbitsa cikhulupililo cathu. Tikayamba kuphunzila Baibo, timadziŵa mfundo zoyambilila zokhudza Yehova, na njila zake. Koma m’kupita kwa nthawi, tifunika kumvetsa zinthu zozama. Izi n’zimene Paulo anatanthauza pamene anati: “Cakudya cotafuna ndi ca anthu okhwima mwauzimu.” Ngati tiseŵenzetsa zimene timaphunzila, timakhala anzelu. Baibo imatiuza kuti: ‘Nzelu ni cinthu cofunika kwambili.’—Miyambo 4:5-7; 1 Petulo 2:2.

15. N’cifukwa ciani tifunika kukonda Yehova na mtima wonse, komanso abale na alongo athu?

15 Munthu angakhale wolimba, komanso wa thanzi labwino. Koma kuti akhalebe wotelo, safunika kuleka kudzisamalila. Mofananamo, munthu wokhwima mwauzimu amadziŵa kuti pamafunika khama kuti ubale wake na Yehova ukhalebe wolimba. Paulo akutikumbutsa kuti: “Pitilizani kudziyesa kuti muone ngati mukadali olimba m’cikhulupililo . . . mudziŵe kuti ndinu munthu wotani.” (2 Akorinto 13:5) Koma cofunikila si cikhulupililo colimba cabe. Tifunikanso kumawonjezela cikondi cathu pa Yehova, komanso kwa abale na alongo athu. Paulo anakamba kuti: “Ngati ndili ndi mphatso . . . yodziŵa zinthu zonse, komanso ngati ndili ndi cikhulupililo conse coti n’kusuntha naco mapili, koma ndilibe cikondi, sindili kanthu.”—1 Akorinto 13:1-3.

LUNJIKANI MAGANIZO PA CIYEMBEKEZO

16. Kodi Satana amafuna tizikhala na maganizo abwanji?

16 Satana amafuna tiziganiza kuti sitifikapo kweni-kweni pa mlingo wokondweletsa Yehova. Amafuna tizikhala na maganizo otilefula, na kuona kuti palibe njila yothetsela mavuto athu. Safunanso kuti tizidalila Akhristu anzathu, komanso kukhala acimwemwe. (Aefeso 2:2) Satana amadziŵa kuti maganizo olefula akhoza kutiwononga, na kusokoneza ubale wathu na Mulungu. Koma Yehova watipatsa cinacake cotithandiza kugwebana na maganizo otilefula. Inde, watipatsa ciyembekezo.

17. Kodi ciyembekezo n’cofunika motani?

17 Pa 1 Atesalonika 5:8, Baibo imati ciyembekezo cathu cili monga cisoti cacigoba cimene cimateteza msilikali kunkhondo. Inde, “ciyembekezo cacipulumutso.” Kukhala na ciyembekezo m’malonjezo a Yehova kumateteza maganizo athu, na kutithandiza kupewa malingalilo odzilefula.

18, 19. Kodi ciyembekezo cinam’limbikitsa bwanji Yesu?

18 Ciyembekezo ca Yesu cinam’limbitsa. Usiku wake wotsiliza pa dziko lapansi, zovuta zothetsa nzelu zinangondondozana, pacoka ici pabwela cina. Mnzake wokondedwa anam’gulitsa. Winanso anamukana kuti samudziŵa. Ena anamuthaŵa n’kumusiya yekha. Anthu a mtundu wake anamuukila, na kufuula kuti apacikidwe. Kodi n’ciani cinam’thandiza kupilila zinthu zoŵaŵa zonsezi? “Cifukwa ca cimwemwe cimene anamuikila patsogolo pake, anapilila mtengo wozunzikilapo. Iye sanasamale kuti zocititsa manyazi zimucitikila, ndipo tsopano wakhala pansi kudzanja lamanja la mpando wacifumu wa Mulungu.”—Aheberi 12:2.

19 Yesu anadziŵa kuti akakhala wokhulupilika, Atate wake adzatamandika, koma Satana adzaonekela kuti ni wabodza. Ciyembekezo cimeneci cinam’patsa cimwemwe cacikulu ngako. Anadziŵanso kuti posakhalitsa, adzabwelelanso kwa Atate wake kumwamba. Ciyembekezo cimeneci, ndiye cinam’thandiza kupilila. Mofanana na Yesu, ifenso tifunika kulunjika maganizo pa ciyembekezo cathu. Cidzatithandiza kupitila, zivute zitani.

20. N’ciani cingakuthandizeni kukhala na maganizo olimbikitsa?

20 Yehova amaona cikhulupililo canu, komanso kupilila kwanu. (Yesaya 30:18; ŵelengani Malaki 3:10.) Analonjeza kuti ‘adzakupatsani zokhumba za mtima wanu.’ (Salimo 37:4) Conco, lunjikani maganizo pa ciyembekezo canu. Satana amafuna kukutaitsani ciyembekezo canu, pokupangitsani kuona kuti malonjezo a Yehova sadzakwanilitsika. Koma musamvelele malingalilo olefula amenewo! Mukaona kuti ciyembekezo canu ciyamba kufooka, pemphani thandizo kwa Yehova. Kumbukilani mawu opezeka pa Afilipi 4:6, 7 akuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Mukatelo, mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.”

21, 22. (a) Kodi Yehova ali nalo colinga canji dziko lapansi? (b) Ndipo ndimwe wofunitsitsa kucita ciani?

21 Nthawi na nthawi, muzisinkha-sinkha pa tsogolo losangalatsa limene tili nalo. Posacedwa, munthu aliyense pa dziko lapansi adzakhala wolambila Yehova. (Chivumbulutso 7:9, 14) Tangoganizani mmene umoyo udzakhalila m’dziko latsopano! Ubwino wake sitingathe ngakhale kuyelekezela! Satana, ziŵanda zake, komanso zoipa zonse, idzakhala mbili yakale. Simudzadwala, ndipo simudzafa. M’malo mwake, tsiku lililonse muziuka wamphamvu na thanzi labwino, na kusangalala nawo moyo. Padzakhala kugwilila pamodzi nchito yosintha dziko kukhala paradaiso. Tonse tidzakhala na vakudya vabwino, na nyumba zabwino zokhalamo. Anthu ankhanza kapena aciwawa kudzakhala kulibe. Aliyense adzakhala wokoma mtima kwa aliyense. M’kupita kwa nthawi, munthu aliyense pa dziko lapansi adzakhala na “ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu.”—Aroma 8:21.

22 Yehova amafuna kuti mum’pange kukhala Bwenzi lanu lapamtima. Conco, citani zonse zotheka kuti muzimumvela, na kumuyandikila-yandikila tsiku lililonse. Inde, tiyeni tonse tikhalebe m’cikondi ca Mulungu, ku umuyaya wonse!—Yuda 21.