Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MUTU 13

Kodi Zikondwelelo Zonse Zimakondweletsa Mulungu?

Kodi Zikondwelelo Zonse Zimakondweletsa Mulungu?

“Nthawi zonse muzitsimikiza kuti covomelezeka kwa Ambuye n’citi.”—AEFESO 5:10.

1. Tiyenela kucita ciani kuti Yehova azikondwela na kulambila kwathu? Nanga n’cifukwa ciani?

YESU anakamba kuti: “Olambila oona adzalambila Atate motsogoleledwa ndi mzimu ndi coonadi, pakuti Atate amafuna otelowo azimulambila.” (Yohane 4:23; 6:44) Aliyense wa ife afunika ‘nthawi zonse azitsimikiza kuti covomelezeka kwa Ambuye n’citi.’ (Aefeso 5:10) Koma nthawi zina zimakhala zovuta. Satana amayesetsa kutisokoneza kuti ticite zinthu zokhumudwitsa Yehova.—Chivumbulutso 12:9.

2. Fotokozani zimene zinacitika pafupi na phili la Sinai.

2 Kodi Satana amayesa bwanji kutisoceletsa? Njila imodzi, amafuna kutisokoneza pa cabwino na coipa. Onani zimene zinacitikila mtundu wa Isiraeli pa msasa munsi mwa phili la Sinai. Mose atakwela m’philimo, anthu anali kuyembekezela kuti abweleko. Koma atalema kuyembekezela, anapempha Aroni kuti awapangile mulungu. Iye anawapangila fano lagolide la mwana wa ng’ombe. Atatelo, anthuwo anacita cikondwelelo. Anali kuvina mozungulila mwana wa ng’ombeyo na kumugwadila. Iwo anakhulupilila kuti pogwadila mwana wa ng’ombeyo, anali kulambila Yehova. Zinalibe kanthu kuti m’kuona kwawo cinali “cikondwelelo ca Yehova.” Kwa Yehova kunali kulambila mafano, ndipo ambili anaphedwa. (Ekisodo 32:1-6, 10, 28) Pali phunzilo lanji kwa ife? Tisalole aliyense kutipusitsa. ‘Tisakhudze codetsa ciliconse,’ kutanthauza kuti, tisatengeko mbali iliyonse m’cipembedzo conama. Yehova yekha ndiye ayenela kutiuza cabwino na coipa.—Yesaya 52:11; Ezekieli 44:23; Agalatiya 5:9.

3, 4. N’cifukwa ciani m’pofunika kudziŵa mmene zikondwelelo zofala zambili zinayambila?

3 Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anaphunzitsa atumwi ake kukhala zitsanzo pa kulambila koyela. Iye atamwalila, atumwiwo anapitiliza kuphunzitsa ophunzila atsopano mfundo za Yehova. Koma pamene atumwi anatha kumwalila, aphunzitsi onama anabweletsa mu mpingo maganizo opotoka, miyambo, na zikondwelelo zacikunja. Iwo anasintha maina a zikondwelelo zina zacikunja kuti zimveke zacikhristu. (2 Atesalonika 2:7, 10; 2 Yohane 6, 7) Zikondwelelo zambili zimenezi zikali zofala masiku ano. Ndipo zimalimbikitsabe zikhulupililo zonama, komanso zaziŵanda. *Chivumbulutso 18:2-4, 23.

4 Kuzungulila dziko lonse, zikondwelelo na maholide ni zinthu zofunika ngako m’miyoyo ya anthu. Koma pamene mupitiliza kuphunzila mmene Yehova amaonela zinthu, mudzaona kufunika kosintha maganizo anu pa zikondwelelo zina. Zingakhale zovuta, koma Yehova adzakuthandizani. Lomba tiyeni tione mmene zikondwelelo zina zofala zinayambila, kuti timvetsetse mmene Yehova amazionela.

KODI KHRISIMASI INAYAMBA BWANJI?

5. Pali umboni wabwanji woonetsa kuti Yesu sanabadwe pa December 25?

5 M’maiko ambili, anthu amakondwelela Khrisimasi pa December 25, poganiza kuti ndiye tsiku limene Yesu anabadwa. Koma Baibo siikamba kuti Yesu anabadwa tsiku liti, kapena mwezi wanji. Koma imangotipatsa cithunzi ca nyengo m’caka. Luka analemba kuti pamene Yesu anabadwa ku Betelehemu, “abusa . . . anali kugonela kubusa akuyang’anila nkhosa zawo.” (Luka 2:8-11) M’mwezi wa December, ku Betelehemu kumakhala kozizila, kwamvula, ndipo nthawi zina kumagwa cipale cozizila (m’Cizungu snow). Conco, m’nyengo imeneyi aciŵeta sakanatha kumagona kunja na ziŵeto zawo. Kodi izi zitiuza ciani? Kuti Yesu sanabadwe mu December, m’nyengo yozizila. Umboni wa m’Baibo, ngakhalenso wa m’zolemba za mbili yakale, umaonetsa kuti Yesu anabadwa pakati pa September na October.

6, 7. (a) Kodi miyambo yambili ya Khrisimasi inayamba bwanji? (b) Kodi cifukwa copatsila mphatso ciyenela kukhala ciani?

6 Nanga Khrisimasi inayamba bwanji? Inacokela ku zikondwelelo zacikunja, monga cikondwelelo ca Satenaliya, cokondwelela Sateni, mulungu wa zaulimi. Buku ina (The Encyclopedia Americana) imati: “Satenaliya inali cikondwelelo ca Aroma cimene cinali kucitika capakati pa December. N’kumene anthu anatengelako miyambo yambili yokondwelela Khrisimasi, monga kucita madyelelo, kupeleka mphatso, na kuyasha makendulo.” Komanso, cikondwelelo ca mulungu-dzuŵa wa ku Perisiya, dzina lake Mithra, cinali kucitikanso pa December 25.

7 Komabe, anthu ambili okondwelela Khrisimasi masiku ano, saganizilako zakuti inacokela ku miyambo yacikunja imeneyi. Iwo amangodziŵa zakuti Khrisimasi ni nthawi yosangalala pamodzi monga banja, kukondwela na zakudya zabwino, na kupatsana mphatso. N’zoona kuti timakonda mabanja athu na mabwenzi athu, ndipo Yehova amafuna kuti atumiki ake azipatsana zinthu. 2 Akorinto 9:7 imatiuza kuti, “Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.” Koma Yehova safuna kuti tizingopatsana zinthu pa zocitika zapadela cabe. Anthu ake amakondwela kupatsana mphatso, komanso kusangalala na maceza pamodzi na acibanja, komanso mabwenzi pa nthawi iliyonse m’caka. Ndipo amacita zimenezi mosayembekezela kuti nawonso apatsidwe cinacake. Amapatsa cifukwa amakonda ena.—Luka 14:12-14.

Kudziŵa ciyambi ca zikondwelelo kungatithandize kudziŵa zofunika kupewa

8. Kodi okhulupilila nyenyezi anapeleka mphatso kwa Yesu pamene anali khanda? Fotokozani.

8 Pofuna kupeleka maziko a mfundo yopatsana mphatso pa Khrisimasi, anthu ambili amakamba kuti amuna anzelu atatu anabweletsa mphatso kwa Yesu ali khanda m’khola la ziŵeto. N’zoona kuti amuna ena anabweletsa mphatso kwa Yesu. M’nthawi za m’Baibo, zinali zofala kupeleka mphatso kwa munthu wofunika kwambili. (1 Mafumu 10:1, 2, 10, 13) Koma kodi mudziŵa kuti Baibo imaonetsa kuti amuna amenewo anali okhulupilila nyenyezi, okhulupilila zamatsenga, ndipo sanali kulambila Yehova? Komanso, iwo sanapite kukaona Yesu pamene anali khanda m’khola la ziŵeto. Anapita kukamuona pambuyo pake, ali “mwana” wosinkhukilapo, ndipo akukhala m’nyumba.—Mateyu 2:1, 2, 11.

KODI BAIBO IMAKAMBA CIANI ZA MASIKU AKUBADWA?

9. Ni zikondwelelo za masiku akubadwa ati cabe zimene Baibo imakambako?

9 Mwana akabadwa, limakhala tsiku lokondweletsa kwambili. (Salimo 127:3) Koma kodi uwu ni umboni wakuti tiyenela kukondwelela masiku akubadwa? Ganizilani izi: Baibo imangochula zikondwelelo ziŵili za masiku akubadwa cabe. Cikondwelelo ca kubadwa kwa Farao, mfumu ya Iguputo, komanso ca kubadwa kwa Mfumu Herode Antipa. (Ŵelengani Genesis 40:20-22; Maliko 6:21-29.) Olamulila onse awa sanali atumiki a Yehova. Ndipo Baibo siikambako zakuti mtumiki wa Yehova aliyense anakondwelelako tsiku la kubadwa.

10. Kodi Akhristu oyambilila anali kuiona bwanji nkhani yokondwelela masiku akubadwa?

10 Buku ina (The World Book Encyclopedia) imati Akhristu oyambilila, “anali kuona kuti kukondwelela tsiku la kubadwa kwa munthu aliyense unali mwambo wacikunja.” Miyambo imeneyi inali kucokela ku zikhulupililo zonama. Mwacitsanzo, Agiriki akale anali kukhulupilila kuti munthu aliyense anali na mzimu womuteteza kucokela pa kubadwa kwake. Anali kuganiza kuti mzimu umenewo, unali wa mulungu amene tsiku lake la kubadwa ni lofanana na munthu ameneyo. Kuwonjezela pa zikhulupililo zimenezo, masiku akubadwa amakhudzananso na kukhulupilila nyenyezi.

11. Kodi Yehova amafuna kuti kupatsa kwathu tizikuonetsa liti?

11 Anthu ambili amaona kuti tsiku la kubadwa ni tsiku lapadela, lofunika kuyamikilidwa na kuonetsedwa cikondi. Koma cikondi kwa abululu athu na mabwenzi, tiyenela kucionetsa pa nthawi iliyonse m’caka, osati pa tsiku limodzi cabe. Yehova amafuna kuti tizikhala okoma mtima komanso opatsa nthawi zonse. (Ŵelengani Machitidwe 20:35.) Tsiku iliyonse, osati cabe pa tsiku la kubadwa, timayamikila Mulungu cifukwa ca mphatso yapadela ya moyo wathu.—Salimo 8:3, 4; 36:9.

Akhristu oona amapatsa ena mphatso cifukwa cowakonda

12. Kodi tsiku la kumwalila lingapambane bwanji tsiku la kubadwa?

12 Mlaliki 7:1 imati: “Mbili yabwino imaposa mafuta onunkhila, ndipo tsiku lomwalila limaposa tsiku lobadwa.” Kodi tsiku lomwalila lingapambane bwanji tsiku la kubadwa? Tikabadwa, palibe ciliconse cimene tacitako mu umoyo wathu, cabwino kapena coipa. Koma tikaseŵenzetsa moyo wathu kutumikila Yehova, na kucitila zabwino anthu ena, timapanga “mbili yabwino,” kapena dzina labwino. Ndipo Yehova adzatikumbukila ngakhale timwalile. (Yobu 14:14, 15) Anthu a Yehova sacita cikondwelelo ca tsiku lawo la kubadwa, kapena la Yesu. Ndipo cikondwelelo cokha cimene Yesu analamula kuti tizicita, ni Cikumbutso ca imfa yake—Luka 22:17-20; Aheberi 1:3, 4.

CIYAMBI CA ISITALA

13, 14. Kodi cikondwelelo ca Isitala cinabwela bwanji?

13 Anthu ambili pokondwelela Isitala, amakhulupilila kuti akukondwelela kuuka kwa Yesu ku imfa. Koma m’ceni-ceni, cikondwelelo ca Isitala cinali ca Isitire, mulungu wacikunja wa Angelezi Amakedzana, wa matandakuca na nyengo yophuka zomela. Buku ina (The Dictionary of Mythology) imafotokoza kuti mulungu ameneyu, analinso wa mphamvu zakubala. Miyambo ina ya Isitala ni yogwilizana na zimenezi. Mwacitsanzo, buku ina (Encyclopædia Britannica) imati mazila, “akhala cizindikilo cofala ca moyo watsopano na kuuka ku imfa.” Ndipo kwa nthawi yaitali, akalulu agwilitsilidwa nchito monga zizindikilo za mphamvu zakubala m’kulambila kwacikunja. Conco, n’zoonekelatu kuti Isitala siikhudzana na kuuka kwa Yesu.

14 Kodi zingamukondweletse Yehova kuona kuti anthu akusakaniza miyambo ya zipembedzo zonama na ciukililo ca Mwana wake? Kutali-tali! (2 Akorinto 6:17, 18) Ndipo Yehova sanatiuzepo kuti tizikondwelela kuuka kwa Yesu.

CIKONDWELELO CA NYUYE—CAKA CATSOPANO

15. Kodi Nyuye inayamba bwanji?

15 Pa December 31, anthu ambili sagona mpaka pakati pa usiku. Amafuna “kuona mmene caka cakale cidzapitila.” Akaloŵa m’caka catsopano, kumakhala madyelelo, kumwa, kupatsana mphatso, na kufunilana mafuno abwino. Kukondwelela caka catsopano kunayamba kale-kale. Zolemba zamakedzana zimaonetsa kuti Nyuye inali kucitika ku Babulo m’ma 2000 B.C.E. Malinga n’kunena kwa buku lina (The World Book Encyclopedia) “mu Roma wakale, tsiku loyamba la caka linali lokondwelela Junasi, mulungu wa mageti na zitseko, komanso wa ciyambi na mapeto. . . . Mu chechi ya Cikhristu, Nyuye inakhazikitsidwa mu A.D. 487.” M’maiko ambili, anthu pa tsikuli amacita maphwando, kumwa na kuvina. Komabe, Aroma 13:13 imatilangiza kuti: “Tiyeni tiyende moyenela monga usana, osati m’maphwando aphokoso ndi kumwa mwauchidakwa, osati m’ciwelewele ndi khalidwe lotayilila.”

MAWEDING’I OKONDWELETSA MULUNGU

16, 17. Tiyenela kuganizila ciani pokonzekela weding’i?

16 Tsiku la weding’i ni tsiku la cisangalalo. Ndipo zisangalalo za maaweding’i zimacitika mosiyana-siyana padziko lonse lapansi. Komanso, anthu samaganizilanso za kumene miyambo ya pa weding’i inacokela. Sadziŵa kuti miyambo ina inacokela ku zikhulupililo zacikunja. Koma Akhristu amene akukonzekela weding’i yawo afunika kuonetsetsa kuti idzalemekeza Yehova. Conco, kuti akapange zosankha zanzelu, afunika kudziŵa kumene miyambo ina ya pa weding’i inacokela.—Maliko 10:6-9.

17 Anthu ena amakhulupilila kuti miyambo ina ya pa weding’i imabweletsa mwayi kwa okwatilanawo. (Yesaya 65:11) Mwacitsanzo, ena amawaza kumutu kwa mkwati na mkwatibwi mpunga, kapena zinazake zonga mpunga. Amakhulupilila kuti zidzawapatsa ana, cimwemwe, na moyo wautali, komanso kuwateteza ku masoka. Akhristu afunika kupewa zilizonse zokhudzana na miyambo ya cipembedzo conyenga.—Ŵelengani 2 Akorinto 6:14-18.

18. Ni mfundo ziti zofunika kukumbukila pokonzekela weding’i?

18 Okonzekela cikwati amafuna kuti weding’i yawo ikakhale yosangalatsa komanso yolemekezeka, kuti onse opezekapo akakondwele. Aja oitanidwa ku weding’i safunika kukambapo mawu acipongwe, okhudzana na zakugonana, kapena ocititsa manyazi akwati komanso anthu ena. (Miyambo 26:18, 19; Luka 6:31; 10:27) Weding’i ya Akhristu siifunika kukhala ‘yodzionetsela na zimene munthu ali nazo.’ (1 Yohane 2:16) Ngati mukukonzekela weding’i, onetsetsani kuti ikakusiyeni na cikumbukilo cosangalatsa.—Onani Mfundo ya Kumapeto 28.

KUCITA TOSTI—KUKWEZA M’MWAMBA ZOMWELA

19, 20. Kodi kucita tosti kunacokela kuti?

19 Pamaweding’i ena, kapena pa zisangalalo zina, anthu amakonda kucita tosti, kapena kuti kugundanitsa zomwela zawo na kuzikweza m’mwamba. Amati wina akakamba mawu a mafuno abwino, ena amanyamula zomwela zawo m’mwamba. Kodi Mkhristu ayenela kuiona bwanji nkhani yocita tosti?

20 Buku ina (International Handbook on Alcohol and Culture) limakamba kuti kucita tosti, kuyenela kuti kunacokela ku mwambo wakale wacikunja “wopeleka magazi na vinyo kwa milungu.” Anali kucita zimenezi “pofunilana mafuno abwino, na pemphelo lacidule lakuti ‘moyo wautali’ kapena kuti ‘thanzi labwino!’” M’nthawi zamakedzana, anthu anali kukweza m’mwamba makapu awo popempha milungu yawo kuti iwadalitse. Koma si mmene Yehova amadalitsila anthu.—Yohane 14:6; 16:23.

“INU OKONDA YEHOVA DANANI NACO COIPA”

21. Ni zikondwelelo zina ziti zimene Akhristu ayenela kupewa?

21 Pofuna kuona ngati mungakapezeke ku cikondwelelo kapena ayi, ganizilani zimene zimalimbikitsidwa kumeneko. Mwacitsanzo, ku zikondwelelo zina kumakhala kuvina koutsa cilakolako ca kugonana, kumwa mwaucidakwa, ngakhale zaciwelewele. Zikondwelelo zimenezo zimalimbikitsanso mathanyula (amuna kapena akazi kugonana okha-okha), kapenanso kukweza dziko lanu. Ngati titengako mbali m’zikondwelelo zimenezi, kodi tingati timadana na zimene Yehova amanyasidwa nazo?—Salimo 1:1, 2; 97:10; 119:37.

22. N’ciani cingathandize Mkhristu kusankha kukapezeka ku cikondwelelo kapena ayi?

22 Akhristu ayenela kusamala kwambili kuti apewe zikondwelelo zilizonse zonyoza Mulungu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kaya mukudya kapena kumwa kapena mukucita cina ciliconse, citani zonse ku ulemelelo wa Mulungu.” (1 Akorinto 10:31; onani Mfundo ya Kumapeto 29.) Koma sikuti zikondwelelo zonse zimakhudzana na zaciwelewele, cipembedzo conama, kapena kusankhana mtundu ayi. Ngati cikondwelelo siciwombana na mfundo za m’Baibo, munthu angasankhe kukapezekako kapena ayi, ni nkhani yaumwini. Koma tiganizilenso mmene cosankha cathu cingakhudzile ena.

LEMEKEZANI YEHOVA MWA ZOKAMBA NA ZOCITA ZANU

23, 24. Kodi abululu athu amene si Mboni, tingawafotokozele bwanji cosankha cathu cokhudza zikondwelelo zina?

23 Mwacidziŵikile, munaleka kutengako mbali m’zikondwelelo zonyoza Yehova. Koma a banja lanu ena amene si Mboni za Yehova, angaone monga simuwakonda, kapena simufuna kuyanjana nawo. Angaone kuti pa maholide, ndiyo nthawi cabe imene banja lonse limakhala na maceza capamodzi. Ndiye mungacite bwanji? Zilipo njila zingapo zimene mungawaonetsele kuti mumawakondabe, na kuti ni ofunika kwa imwe. (Miyambo 11:25; Mlaliki 3:12, 13) Mungawaitanile kunyumba kwanu kuti mukaceze nawo nthawi zina.

24 Ngati abululu anu afuna kudziŵa cimene simupezekela pa maholide ena, mungafufuze m’zofalitsa, komanso pa jw.org, zifukwa zimene mungawafotokozele. Osakamba nawo mwa njila yoonetsa monga mungofuna kutsutsana nawo, kapena kuwaumiliza kuganiza mmene muganizila. Athandizeni kuona kuti munayang’ana mbali zambili, ndipo munapanga cosankha canu. Khalani wodekha, ndipo “nthawi zonse mawu anu azikhala acisomo, okoma ngati kuti mwawatila mcele.”—Akolose 4:6.

25, 26. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kukonda miyezo ya Yehova?

25 Aliyense wa ife, afunika kudziŵa bwino zifukwa zimene sititengelako mbali m’zikondwelelo zina zake. (Aheberi 5:14) Colinga cathu ni kukondweletsa Yehova. Ngati ndife makolo, tizipatula nthawi yothandiza ana athu kumvetsa mfundo za m’Baibo. Athandizeni kumvetsa kuti Yehova alikodi, ndipo angakhale bwenzi lawo. Mukatelo, nawonso adzafuna kuti azim’kondweletsa.—Yesaya 48:17, 18; 1 Petulo 3:15.

26 Yehova amakondwela poona kuti timayesetsa kucita zimene tingathe kuti tim’lambile m’njila yoyela, komanso moona mtima. (Yohane 4:23) Koma ambili amaganiza kuti padziko pali cinyengo kwambili, cakuti n’zosatheka munthu kukhala woona mtima m’ceni-ceni. Kodi n’zoona zimenezi? Tiyeni tikakambilane nkhaniyi m’mutu wotsatila.

^ ndime 3 Mungaŵelenge zambili pa zikondwelelo zina mu Watch Tower Publications Index, Buku Lofufuzila Nkhani la Mboni za Yehova, komanso pa jw.org.