Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kukhala Olekana Nalo Dziko

Kukhala Olekana Nalo Dziko

Kukhala Olekana Nalo Dziko

“Simuli mbali ya dzikoli.” —YOHANE 15:19.

1. Kodi Yesu anadela nkhawa za ciani usiku wotsiliza asanaphedwe?

USIKU wotsiliza Yesu asanaphedwe, anadziŵa kuti adzawasiya ophunzila ake. Ndipo anadela nkhawa za tsogolo lawo. Conco, anawauza kuti: “Simuli mbali ya dzikoli.” (Yohane 15:19) Komanso, tsiku lina powapemphelela kwa Atate wake, iye anakamba kuti: “Iwo sali mbali ya dziko, monganso ine sindili mbali ya dziko.” (Yohane 17:15, 16) Kodi Yesu anatanthauza ciani?

2. Kodi “dziko” limene Yesu anakambapo n’ciani?

2 Pano, mawu akuti “dziko” atanthauza anthu amene sadziŵa Mulungu ndipo alamuliliwa na Satana. (Yohane 14:30; Aefeso 2:2; Yakobo 4:4; 1 Yohane 5:19) Nanga tingapewe bwanji kukhala “mbali ya dziko”? M’nkhani ino, tidzakambilana njila zingapo izi: Mwa kukhala wokhulupilika ku Ufumu wa Mulungu, na kusaloŵelela m’nkhani za ndale; mwa kukana mzimu wa dziko; mwa kuvala mwaulemu na kudzikongoletsa moyenelela, na kusakondetsetsa ndalama; komanso, mwa kuvala na kunyamula zida zonse zankhondo zimene Mulungu amatipatsa.—Onani Mfundo ya Kumapeto 16.

KHALANI WOKHULUPILIKA KU UFUMU WA MULUNGU

3. Kodi Yesu anali kuziona bwanji ndale?

3 Pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anaona kuti anthu anali na mavuto ambili, cakuti umoyo wawo unali wovuta. Anali kuwadela nkhawa kwambili, ndipo anali wofunitsitsa kuwathandiza. Kodi iye anakhala mtsogoleli wandale? Iyai. Anadziŵa kuti cimene anthu anali kufunikila maka-maka unali Ufumu wa Mulungu, kapena kuti boma la Mulungu. Yesu ndiye anali kudzakhala Mfumu ya Ufumu umenewo. Ndiye cifukwa cake, nkhani yaikulu imene anali kulalikila inali ya Ufumuwo. (Danieli 7:13, 14; Luka 4:43; 17:20, 21) Yesu sanangene m’zandale za dziko, kapena kukhalila mbali cipani ciliconse. Pamene anali pamaso pa Bwanamkubwa waciroma, Pontiyo Pilato, Yesu anakamba kuti: “Ufumu wanga suli mbali ya dziko lino.” (Yohane 18:36) Ophunzila ake naonso sanangene m’ndale za dziko. Buku ina (On the Road to Civilization) inakamba kuti Akhristu oyambilila “sanali kungena nchito zokhudzana na ndale.” N’cimodzi-modzinso Akhristu masiku ano. Timacilikiza Ufumu wa Mulungu, ndipo sitiloŵelela m’ndale za dziko.—Mateyu 24:14.

Kodi mungafotokoze cifukwa cake mumacilikiza Ufumu wa Mulungu?

4. Kodi Akhristu oona amacilikiza bwanji Ufumu wa Mulungu?

4 Akazembe a dziko lililonse amaimila boma lawo m’dziko lacilendo. Conco, saloŵelela m’nkhani zandale za dzikolo. Ni mmene zililinso kwa odzozedwa, amene akuyembekezela kukalamulila pamodzi na Khristu kumwamba. Paulo analembela odzozedwa kuti: “Ndife akazembe m’malo mwa Khristu.” (2 Akorinto 5:20) Odzozedwa amaimila boma ya Mulungu. Iwo sadziloŵetsa m’nkhani za ndale kapena m’mikangano ya maiko. (Afilipi 3:20) M’malo mwake, athandiza mamiliyoni a anthu kuphunzila za boma la Mulungu. A “nkhosa zina,” amene ayembekezela kudzakhala na moyo wamuyaya m’dziko latsopano la Mulungu, amacilikiza Akhristu odzozedwa. Nawonso satengako mbali m’ndale za dziko. (Yohane 10:16; Mateyu 25:31-40) Inde, Mkhristu wazoona aliyense sangatengeko mbali m’ndale za dziko.—Ŵelengani Yesaya 2:2-4.

5. N’cifukwa cimodzi citi cimene Akhristu satengelako mbali m’nkhondo?

5 Akhristu oona amaona Akhristu anzawo onse kuti ni banja imodzi, ndipo amagwilizana olo kuti akhale a dziko liti kapena mtundu uti. (1 Akorinto 1:10) Kuti tiyende ku nkhondo, tikhoza kupezeka kuti timenyana ndi a m’banja lathu, okhulupilila anzathu, amene Yesu anatilamula kuti tiyenela kuwakonda. (Yohane 13:34, 35; 1 Yohane 3:10-12) Ndipo Yesu anauza ophunzila ake kukonda ngakhale adani awo.—Mateyu 5:44; 26:52.

6. Kodi atumiki odzipatulila a Yehova amawaona bwanji maboma?

6 Olo kuti sitingena m’ndale pokhala Akhristu, timayesetsa kukhala nzika zabwino m’dziko. Mwacitsanzo, timalemekeza boma mwa kumvela malamulo ake na kukhoma misonkho. Ngakhale n’conco, sitiiŵala kupeleka “zinthu za Mulungu . . . kwa Mulungu.” (Maliko 12:17; Aroma 13:1-7; 1 Akorinto 6:19, 20) “Zinthu za Mulungu” ziphatikizapo kum’konda, kumumvela, na kum’lambila. Ndise okonzeka ngakhale kutaya moyo wathu kuti timvele Yehova.—Luka 4:8; 10:27; ŵelengani Machitidwe 5:29; Aroma 14:8.

KANIZANI “MZIMU WA DZIKO”

7, 8. Kodi “mzimu wa dziko” n’ciani? Nanga umawakhudza bwanji anthu?

7 Kukhala olekana na dziko la Satana kutanthauza kusalola “mzimu wa dziko” kutilamulila. Kodi mzimu wa dziko ndiye ciani? Ni maganizo na makhalidwe amene Satana amalimbikitsa kwa anthu amene satumikila Yehova. Koma Akhristu amatsutsa maganizo amenewo. Monga anakambila Paulo, “sitinalandile mzimu wa dziko, koma mzimu wocokela kwa Mulungu.”—1 Akorinto 2:12; Aefeso 2:2, 3; onani Mfundo ya Kumapeto 17.

8 Mzimu wa dziko umalengetsa anthu kukhala odzikonda, onyada, komanso okonda kupandukila. Umawapangitsa kuganiza kuti safunikila kumvela Mulungu. Satana amafuna kuti anthu azingocita vilivonse vamene afuna, mosaganizila zotulukapo zake. Amafuna kuti anthu azikhulupilila kuti ‘cilakolako ca thupi, na cilakolako ca maso,’ ndiye zinthu zofunika kwambili mu umoyo wa munthu. (1 Yohane 2:16; 1 Timoteyo 6:9, 10) Maka-maka ise atumiki a Yehova, ni amene Mdyelekezi amaikilapo nzelu kwambili kuti atisoceletse. Amafuna kuti tiziganiza mmene iye amaganizila.—Yohane 8:44; Machitidwe 13:10; 1 Yohane 3:8.

9. Kodi mzimu wa dziko ungatiyambukile bwanji?

9 Mofanana na mpweya umene timapuma, mzimu wa dziko uli kulikonse kumene tingakhale. Ngati sitilimbikila kuupewa, udzatiyambukila. (Ŵelengani Miyambo 4:23.) Zimenezi zingayambe m’njila zooneka monga zilibe vuto, monga kutengela maganizo na macitidwe ena a anthu osalambila Yehova. (Miyambo 13:20; 1 Akorinto 15:33) Kapena tingayambe kutengeka na zinthu monga zamalisece, zampatuko, kapena maseŵela a mpikisano wa wafa-wafa.—Onani Mfundo ya Kumapeto 18.

10. Nanga tingaukanize bwanji mzimu wa dziko?

10 Nanga tingapewe bwanji kutengeka na mzimu wa dziko? Tiyenela kukhala pafupi na Yehova kuti azititsogolela mwa nzelu zake. Tifunika nthawi zonse kupemphelela mzimu wake na kukhala otangwanika kum’tumikila. Yehova ndiye wamphamvuzonse m’cilengedwe conse. Tili na cidalilo conse kuti adzatithandiza kutsutsa mzimu wa dziko.—1 Yohane 4:4.

MAVALIDWE ATHU AZILEMEKEZA MULUNGU

11. Kodi anthu ambili m’dziko amavala bwanji?

11 Njila ina imene timaonetsela kuti sitili mbali ya dziko ni mavalidwe athu, na mmene timadzikongoletsela. Anthu ambili m’dziko amavalila kuti ena awaone, kapena kuti awafune, kapenanso kuonetsa mzimu wopanduka, kapenanso kudzionetsela kuti ni andalama. Palinso anthu ena amene alibe nazo kanthu na maonekedwe awo, kaya sanavale bwino kapena aoneke adothi. Koma ise tifunika kupewa mavalidwe onsewa. Tifunika kuvala bwino na kudzisamalila bwino.

Kodi mavalidwe anga amalemekeza Yehova?

12, 13. Ni mfundo ziti zimene zingatithandize kusankha bwino mavalidwe athu?

12 Monga atumiki a Yehova, nthawi zonse tifunika kuvala bwino, mwaudongo, mwaulemu, komanso moyenelela cocitikaco. Timavala moyenela komanso mwaulemu, monga anthu amene “amalemekeza Mulungu.”—1 Timoteyo 2:9, 10; Yuda 21.

13 Mavalidwe athu angakhudze mmene anthu ena angaonele Yehova na anthu ake. Tifuna kucita zinthu zonse “ku ulemelelo wa Mulungu.” (1 Akorinto 10:31) Pokhala odzicepetsa, tifunika kuganizila mmene ena zingawakhudzile. Conco posankha zovala, kapena mmene tifuna kuvalila, tizikumbukila kuti zokonda zathu zimakhudza anthu ena.—1 Akorinto 4:9; 2 Akorinto 6:3, 4; 7:1.

14. Pokasonkhana kapena kulalikila, kodi tifunika kukumbukila ciani za mavalidwe?

14 Kodi timavala bwanji tikakhala ku misonkhano, kapena mu ulaliki? Kodi timavala kuti ena aziona ise? Kodi zovala zathu zimamvetsa manyazi ena? Kodi timakhala na maganizo akuti ‘amene camuŵa ni zake’? (Afilipi 4:5; 1 Petulo 5:6) N’zoona kuti mwacibadwa timafuna kuoneka bwino. Koma kukongola kweni-kweni kumabwela na makhalidwe acikhristu. Ni amene Yehova amayang’ana mwa ife. Amaonetsa ‘munthu wobisika wa mumtima . . . , amene ali wamtengo wapatali pamaso pa Mulungu.’—1 Petulo 3:3, 4.

15. N’cifukwa ciani Yehova sanacite kutisankhila zovala zoyenela na zosayenela?

15 Yehova sanatipatse mndandanda wa malamulo a zoyenela kuvala na zosayenela. Koma anatipatsa mfundo za m’Baibo zotithandiza kupanga zosankha zanzelu. (Aheberi 5:14) Amafuna kuti zosankha zathu, zazing’ono kapena zazikulu, zizitsamila pa cikondi cathu kwa iye na anthu anzathu. (Ŵelengani Maliko 12:30, 31.) Kulikonse pa dziko lapansi, anthu a Yehova amavala mosiyana-siyana malinga na zikhalidwe za kwawo, komanso makonda awo. Kusiyana-siyana kumeneku n’kokongola komanso n’kosangalatsa.

KAONEDWE KABWINO KA NDALAMA

16. Kodi mmene dziko limaonela ndalama zisiyana bwanji na zimene Yesu anaphunzitsa? Nanga tifunika kudzifunsa mafunso ati?

16 Satana amafuna kuti anthu aziona ndalama na zinthu zakuthupi kuti ndiye zingawapatse cimwemwe. Koma ise atumiki a Yehova timadziŵa kuti izi si zoona. Timakhulupilila mawu a Yesu akuti: “Ngakhale munthu atakhala ndi zoculuka cotani, moyo wake sucokela m’zinthu zimene ali nazo.” (Luka 12:15) Ndalama sizingatipatse cimwemwe ceni-ceni. Sizingatipatse mabwenzi eni-eni, mtendele weni-weni wa maganizo, kapena moyo wosatha. N’zoona kuti timafunikila zinthu zakuthupi, ndipo timafuna kukhala na moyo wokondweletsa. Koma Yesu anatiphunzitsa kuti cimwemwe ceni-ceni tingacipeze ngati tikhala pa ubwenzi na Mulungu, komanso ngati kulambila tikuika patsogolo mu umoyo wathu. (Mateyu 5:3; 6:22) Ndiye dzifunseni kuti: ‘Kodi inenso n’natengelako mmene dziko limaonela ndalama? Kodi nthawi zambili nimakonda kukamba pa zandalama?’—Luka 6:45; 21:34-36; 2 Yohane 6.

17. Ngati mukana kaonedwe ka dziko ka ndalama, kodi umoyo wanu ungakhale bwanji waphindu?

17 Ngati tilunjika maganizo athu pa kutumikila Yehova, na kukana kaonedwe ka dziko ka ndalama, moyo wathu udzakhala waphindu. (Mateyu 11:29, 30) Tidzakhala okhutila na zimene tili nazo. Tidzakhalanso na mtendele m’maganizo komanso mu mtima. (Mateyu 6:31, 32; Aroma 15:13) Ndipo tidzacepetsa nkhawa pa zinthu zakuthupi. (Ŵelengani 1 Timoteyo 6:9, 10.) Cinanso, tidzapeza cimwemwe cifukwa copatsa. (Machitidwe 20:35) Ndipo tizapeza mpata wabwino wocezako na anthu amene timakonda. Tikhoza kumagonanso tulo twabwino.—Mlaliki 5:12.

“ZIDA ZONSE ZANKHONDO”

18. Kodi colinga ca Satana n’ciani?

18 Colinga ca Satana ni kuwononga ubwenzi wathu na Yehova. Mwa ici, tifunika kulimbikila kuti tiuteteze. Nkhondo yathu ni yolimbana na “makamu a mizimu yoipa.” (Aefeso 6:12) Satana na viŵanda vake safuna kuti tizikhala acimwemwe, kapena kuti tikapeze moyo wosatha. (1 Petulo 5:8) Adani amphamvu amenewa ndiwo akulimbana nafe. Koma Yehova amatithandiza kuti tipambane.

19. Kodi Aefeso 6:14-18 imazifotokoza bwanji “zida za nkhondo” yauzimu?

19 M’nthawi zamakedzana, asilikali anali kunyamula na kuvala zida zowateteza pa nkhondo. Na ise n’cimodzi-modzi. Tifunika kunyamula na kuvala “zida zonse zankhondo” zimene Yehova amatipatsa. (Aefeso 6:13) Zida zimenezi zimatithandiza kuti tikhale otetezeka. Timaŵelenga za zida zimenezi pa Aefeso 6:14-18. Pamati: “Cotelo khalani olimba, mutamanga kwambili coonadi m’ciuno mwanu, mutavalanso codzitetezela pacifuŵa cacilungamo, mapazi anu mutawaveka nsapato zokonzekela uthenga wabwino wamtendele. Koposa zonse, nyamulani cishango cacikulu cacikhulupililo, cimene mudzathe kuzimitsila mivi yonse yoyaka moto ya woipayo. Komanso landilani cisoti colimba cacipulumutso, ndiponso lupanga la mzimu, lomwe ndilo mawu a Mulungu. Pamene mukutelo, muzipemphela pa cocitika ciliconse mu mzimu, mwa mtundu uliwonse wa pemphelo ndi pembedzelo.”

20. Tiyenela kucita ciani kuti “zida zankhondo” zitithandize?

20 Ngati msilikali angaiŵale kuvala cida cimodzi comuteteza, mbali imeneyo ya thupi lake ni imene mdani wake angamulase. Ngati tifuna kuti covala cathu ca kunkhondo cititeteze, sitifunika kuiŵala mbali yake iliyonse. Nthawi zonse tifunikila kuzivala zida zonse zankhondo, na kuonetsetsa kuti n’zolimba bwino. Nkhondo yathu idzapitilizabe mpaka dziko la Satana likawonongedwe, komanso mpaka iye pamodzi na viŵanda vake akacotsedwepo. (Chivumbulutso 12:17; 20:1-3) Conco, ngati tikulimbana na zilakolako zoipa, kapena zofooka zinazake, tisaleme!—1 Akorinto 9:27.

21. Kodi tingapambane bwanji pa nkhondo yathu?

21 Patekha, sitingalimbane naye Mdyelekezi. Koma mwa thandizo la Yehova, timakwanitsa kugwebana naye! Kuti tikhalebe okhulupilika, tifunikila kumapemphela kwa Yehova, kuŵelenga Mawu ake, ndiponso kuyanjana na abale komanso alongo athu. (Aheberi 10:24, 25) Kucita izi kudzatithandiza kukhalabe okhulupilika kwa Mulungu, komanso kukhala okonzeka kuteteza cikhulupililo cathu.

KHALANI WOKONZEKA KUTETEZA CIKHULUPILILO CANU

22, 23. (a) N’ciani cingatithandize kukhala okonzeka nthawi zonse kuteteza cikhulupililo cathu? (b) Tidzakambilana ciani m’mutu wokonkhapo?

22 Nthawi zonse tifunika kukhala okonzeka kuteteza cikhulupililo cathu. (Yohane 15:19) Pa nkhani zina, Mboni za Yehova zimakhala na maganizo osiyana kweni-kweni na anthu ambili. Dzifunseni kuti: ‘Kodi nimamvetsetsa cifukwa cake timasiyana na anthu ena? Kodi nimakhulupilila kuti zimene Baibo imakamba n’zoona? Kodi nimakhulupililanso kuti zimene kapolo wokhulupilika ndi wanzelu amakamba n’zoona? Kodi nimanyadila kukhala Mboni ya Yehova? (Salimo 34:2; Mateyu 10:32, 33) Kodi zimene nimakhulupilila ningazifotokoze bwino-bwino kwa anthu ena?’—Mateyu 24:45; Yohane 17:17; ŵelengani 1 Petulo 3:15.

23 M’zocitika zambili, timadziŵilatu zofunika kucita kuti tikhale olekana nalo dziko. Koma nthawi zina, sitingadziŵe bwino-bwino. Satana amayesa kutichela msampha m’njila zolekana-lekana. Msampha wina umene amatichela nawo ni zosangalatsa. Kodi tingasankhe bwanji mwanzelu zosangalatsa? Tidzakambilana m’mutu wokonkhapo.