Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MUTU 7

Kodi Mumaona Moyo Mmene Mulungu Amauonela

Kodi Mumaona Moyo Mmene Mulungu Amauonela

“Pakuti inu ndinu kasupe wa moyo.” —SALIMO 36:9.

1, 2. Kodi Yehova anatipatsa mphatso iti yapadela?

YEHOVA anapatsa aliyense wa ife mphatso ya mtengo wapatali. Inde, moyo umene tili nawo. (Genesis 1:27) Ndipo amafuna kuti tikhale na moyo wabwino kwambili. Ndiye cifukwa cake anatipatsa mfundo zotithandiza kupanga zosankha zabwino. Mfundozo zimatithandizanso “kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.” (Aheberi 5:14) Ngati tigwilitsila nchito mfundo zimenezo, timalola Yehova kutiphunzitsa kuganiza bwino. Pamenepo timakhala na umoyo wabwino, na kuona kuti mfundozo n’zothandiza kwambili.

2 Nthawi zina umoyo umakhala wovuta. Pakhoza kucitika zinthu zimene palibe lamulo la m’Baibo lacindunji. Mwacitsanzo, tingafunikile opaleshoni ku cipatala, koma akuti tifunika kuikiwa magazi. Kodi tingapange bwanji cosankha cokondweletsa Yehova? Baibo ili na mfundo zotidziŵitsa mmene Yehova amaonela moyo na magazi. Tikamvetsetsa mfundo zimenezi, timapanga zosankha zanzelu. Timakhalanso na cikumbumtima coyela. (Miyambo 2:6-11) Lomba tiyeni tione zina mwa mfundo zimenezo.

KODI MULUNGU AMAUONA BWANJI MOYO NA MAGAZI?

3, 4. (a) Kodi Mulungu anaonetsa bwanji za mmene amaonela magazi? (b) Nanga magazi amaimilako ciani?

3 Baibo imatiphunzitsa kuti magazi ni cinthu copatulika, cifukwa amaimilako moyo. Ndipo moyo ni cinthu camtengo wapatali kwa Yehova. Pamene Kaini anapha m’bale wake, Yehova anamuuza kuti: “Magazi a m’bale wako akundililila mu nthaka.” (Genesis 4:10) Magazi a Abele anaimilako moyo wake. Conco, pamene Kaini anapha Abele, anacotsa moyo wake.

4 Pambuyo pa Cigumula ca m’nthawi ya Nowa, Mulungu analola anthu kuti azidya nyama. Ndipo anawalangiza kuti: “Koma musadye nyama pamodzi ndi magazi ake, amene ndiwo moyo wake.” (Genesis 9:4) Lamulo limeneli limagwila nchito kwa mbadwa zonse za Nowa, kuphatikizapo ise. Mwacionekele, kwa Yehova, magazi amaimilako moyo. Ni mmene ifenso tiyenela kuonela magazi.—Salimo 36:9.

5, 6. Kodi Cilamulo ca Mose cinaonetsa bwanji mmene Yehova amaonela moyo na magazi?

5 Mu Cilamulo cimene Yehova anapatsa Mose, Iye anati: “Munthu aliyense . . . akadya magazi alionse, ndidzam’kana ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake. Pakuti moyo wa nyama uli m’magazi.”—Levitiko 17:10, 11.

6 Cilamulo ca Mose cinati ngati munthu wapha nyama kuti adye, anafunika kuthila magazi ake m’nthaka. Izi zinatanthauza kuti moyo wabwezedwa kwa amene anaulenga, Yehova. (Deuteronomo 12:16; Ezekieli 18:4) Koma Yehova sanayembekezele kuti Aisiraeli pokhetsa nyama, adzakwanitsa kucotselatu kagazi kalikonse iyai. Malinga ngati anaikhetsa magazi ambili n’kutuluka, anayenela kudya nyamayo na cikumbumtima coyela. Polemekeza magazi a nyama, analemekezanso Wopatsa moyo, Yehova. Cilamulo cinafunanso kuti Aisiraeli azipeleka nsembe nyama kuti akhululukidwe macimo awo.—Onani Mfundo ya Kumapeto 19 na 20.

7. Kodi Davide analemekeza bwanji magazi?

7 Zimene Davide anacita pamene anali kumenyana na Afilisiti, zionetsa kuti magazi ni amtengo wapatali. Asilikali a Davide, poona kuti iye anamvela njota kwambili, anaika miyoyo yawo pa ciwopsezo, pokaloŵa m’cigawo ca adani kuti akamutapile madzi akumwa. Koma atabweletsa madziwo kwa Davide, iye anakana kumwa. M’malo mwake, “anawapeleka kwa Yehova mwa kuwathila pansi.” Ndipo anati: “Sindingacite zimenezo inu Yehova! Kodi ndimwe magazi a amuna amene anaika miyoyo yawo pangozi kuti akatunge madziwa?” Davide anadziŵa kuti kwa Yehova, moyo na magazi n’zamtengo wapatali kwambili.—2 Samueli 23:15-17.

8, 9. Kodi Akhristu masiku ano ayenela kuwaona bwanji magazi?

8 Podzafika m’nthawi ya Akhristu oyambilila, anthu a Mulungu anali ataleka kale kupeleka nsembe za nyama. Koma anafunikilabe kulemekeza magazi. Pa malamulo ocepa amene Yehova anafuna kuti Akhristu apitilize kusunga, panalinso la “kupewa . . . magazi.” Kunali kofunika molingana na kupewa zaciwelewele kapena kupembedza mafano.—Machitidwe 15:28, 29.

Ningafotokoze bwanji za cosankha canga pa tumbali tung’ono-tung’ono twa magazi (blood fractions)?

9 N’cimodzi-modzi masiku ano. Monga Akhristu, timadziŵa kuti Yehova ndiye Gwelo la Moyo, na kuti miyoyo yonse ni yake. Timadziŵanso kuti magazi ni cinthu copatulika, ndipo amaimilako moyo. Conco ngati tifunika cithandizo ca kucipatala, koma akuti padzafunika magazi, tionetsetse kuti taganizila mfundo za m’Baibo popanga cosankha.

MAGAZI PA CITHANDIZO CA KUCIPATALA

10, 11. (a) Kodi Mboni za Yehova zimaona bwanji nkhani yoikidwa magazi, kaya mbali zake 4 zikulu-zikulu kapena tung’ono-tung’ono? (b) Nanga ni pa nkhani ziti pamene Mkhristu afunika kupanga yekha cosankha?

10 Mboni za Yehova zimadziŵa kuti “kupewa . . . magazi” sikukhudza cabe kudya kapena kumwa magazi. Kumatanthauza kukana kungenetsa magazi m’thupi mwathu, kusapeleka magazi athu kwa ena, komanso kuikidwa magazi athu amene ayamba asungidwa kwina. Kumatanthauzanso kukana kuikidwa mbali zikulu-zikulu zinayi izi za magazi—ma red cells, white cells, platelets, na plasma.

11 Mbali 4 zikulu-zikulu zimenezi zingagaŵidwe m’tumbali tung’ono-tung’ono tumene amati ma blood fractions. Mwa cikumbumtima cake, Mkhristu aliyense afunika kusankha ngati angalole tumbali utu kapena ayi. N’cimodzi-modzinso na njila zina zothandizila wodwala zofuna kuseŵenzetsa magazi ake. Mkhristu aliyense afunika kusankha yekha njila imene magazi ake adzasamalidwila pa opaleshoni, popimidwa, kapena pamene akulandila cithandizo camankhwala.—Onani Mfundo ya Kumapeto 21.

12. (a) N’cifukwa ciani zosankha zathu pa nkhani ya cikumbumtima n’zofunikadi kwa Yehova? (b) Nanga tingapange bwanji zosankha zanzelu pa nkhani ya cithandizo ca kucipatala?

12 Kodi Yehova amasamaladi zosankha zimene tipanga pa nkhani ya cikumbumtima? Inde amasamala. Yehova amafuna kudziŵa maganizo athu na zolinga zathu. (Ŵelengani Miyambo 17:3; 24:12.) Conco, popanga cosankha pa nkhani ya cithandizo ca mankhwala, tiyenela kupempha citsogozo ca Yehova, na kufufuza cithandizo coyenelela. Tisafunse ena kuti, ‘Mukanakhala imwe mukanacita bwanji?’ Komanso, mwa makambidwe athu, tisapangitse ena kupanga cosankha cofuna ife. Mkhristu aliyense afunika “kunyamula katundu wake.”—Agalatiya 6:5; Aroma 14:12.

MALAMULO A YEHOVA AMAONETSA KUTI AMATIKONDA

13. Kodi malamulo a Yehova na mfundo zake pa nkhani ya magazi amatiphunzitsa ciani za iye?

13 Ciliconse cimene Yehova watiuza kucita cimatipindulila, ndipo cimaonetsa kuti amatikonda. (Salimo 19:7-11) Koma cacikulu cimene timakhalila omvela kwa iye si kufuna phindu ayi. Timamumvela cifukwa timam’konda. Timakana kuikidwa magazi maka-maka cifukwa cokonda Yehova. (Machitidwe 15:20) Koma palinso citetezo ku thanzi lathu. Ngakhale anthu ambili masiku ano amadziŵa mavuto obwela na kuikidwa magazi. Ndipo pali madokotala ambili amene amakhulupilila kuti opaleshoni yopanda magazi ndiyo yabwino ku thanzi la munthu. Mwacionekele, njila za Yehova ni zanzelu komanso zacikondi nthawi zonse.—Ŵelengani Yesaya 55:9; Yohane 14:21, 23.

14, 15. (a) Kodi Yehova anapatsa anthu ake malamulo ati pofuna kuwateteza? (b) Kodi tingaseŵenzetse bwanji mfundo za malamulo amenewa?

14 Malamulo a Mulungu akhala opindulitsa kwa anthu nthawi zonse. Yehova anapatsa Aisiraeli akale malamulo owateteza ku ngozi. Mwacitsanzo, lamulo lina linati munthu akamanga nyumba, amangenso kampanda mozungulila mtenje wake wafulati, kuteteza munthu aliyense kuti asagwele pansi. (Deuteronomo 22:8) Lamulo lina linali pa zinyama. Ngati wina anali na ng’ombe yaimuna, unali udindo wake kuisamalila kuti isavulaze kapena kupha munthu. (Ekisodo 21:28, 29) Ngati Mwiisiraeli sanasamale malamulo amenewa, ndipo n’kupezeka kuti munthu wina wafa, unali kukhala mlandu wake.

15 Mwa malamulo amenewa, tikhoza kuona kuti kwa Yehova, moyo ni cinthu ca mtengo wapatali kwambili. Kodi kudziŵa zimenezi kuyenela kutikhudza bwanji? Ifenso tiyenela kuonetsa kuti timalemekeza moyo mwa kusamalila nyumba zathu, mamotoka yathu, mmene tiyendetsela motoka, komanso zosangalatsa zimene timasankha. Koma anthu ena, maka-maka anthu acicepele, amataya mantha na kucita zinthu zimene zingawavulaze. Zimenezi zimakhumudwitsa Yehova. Amafuna kuti moyo tiziusamalila—wathu ngakhale wa anthu ena.—Mlaliki 11:9, 10.

16. Kodi kucotsa mimba Yehova amakuona bwanji?

16 Kwa Yehova, moyo wa munthu aliyense ni wofunika. Ngakhale moyo wa mwana ali m’mimba. Malinga na Cilamulo ca Mose, ngati munthu wina mwangozi wavulaza mzimayi wapakati, cakuti iye n’kumwalila, kapena mwana ali m’mimba, kwa Yehova munthuyo anali kukhala na mlandu wa kupha munthu. Ngakhale kuti inali ngozi, koma cifukwa panafa munthu, moyo wake unafunika kulipilidwa. (Ŵelengani Ekisodo 21:22, 23.) Kwa Mulungu, mwana ali m’mimba ni munthu wamoyo. Ndiye muganiza amamvela bwanji munthu akacotsa mimba? Nanga muganiza amamvela bwanji poona mamiliyoni a makanda amene amatayidwa caka ciliconse mwa kucotsa mimba?

17. Mkazi amene anatayapo mimba akalibe kudziŵa Yehova safunika kuvutika maganizo. Cifukwa ciani?

17 Koma bwanji ngati munthu anacotsa mimba akalibe kudziŵa mmene Yehova amaionela nkhaniyi? Afunika kudziŵa kuti Yehova angam’khululukile pamaziko a nsembe ya Yesu. (Luka 5:32; Aefeso 1:7) Ngati mzimayi anacimwa kumbuyoku cosadziŵa, safunika kuona kuti ali na mlandu ngati analapa ca zoona. “Yehova ndi wacifundo ndi wacisomo, . . . Monga mmene kum’mawa kwatalikilana ndi kumadzulo, momwemonso, watiikila kutali zolakwa zathu.—Salimo 103:8-14.

PEWANI MAGANIZO ACIDANI

18. N’cifukwa ciani tiyenela kuyesetsa kucotsa maganizo acidani?

18 Kulemekeza mphatso ya moyo kumayambila mu mtima mwathu—mmene timamvelela za anthu ena. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Aliyense amene amadana ndi m’bale wake ndi wopha munthu.” (1 Yohane 3:15) Ngati tiipidwa na munthu wina, m’kupita kwa nthawi tingayambe kumuzonda. Cidani cimapangitsa munthu kusalemekeza ena, kuwanamizila nkhani, ngakhale kuwafunila imfa. Koma Yehova amadziŵa mmene timamvelela na anthu ena. (Levitiko 19:16; Deuteronomo 19:18-21; Mateyu 5:22) Ngati tipeza kuti tili na maganizo acidani na munthu wina, tiyenela kuyesetsa kuti ticotse maganizo amenewo.—Yakobo 1:14, 15; 4:1-3.

19. Kodi tiyenela kucita ciani podziŵa kuti Yehova amadana naco ciwawa?

19 Palinso njila ina imene tingaonetsele kuti timalemekeza moyo. Pa Salimo 11:5, timauzidwa kuti Yehova “amadana kwambili ndi aliyense wokonda ciwawa.” Ngati tisankha zosangalatsa zaciwawa, tingaonetse kuti timakonda ciwawa. Sitifuna kudyetsa maganizo athu mawu aciwawa, malingalilo, kapena zithunzi zaciwawa. M’malo mwake, tifunika kudyetsa maganizo athu malingalilo oyela komanso amtendele.—Ŵelengani Afilipi 4:8, 9.

MUSAKHALE MBALI YA MABUNGWE AMENE SALEMEKEZA MOYO

20-22. (a) Kodi Yehova amaliona bwanji dziko la Satana? (b) Kodi anthu a Mulungu angaonetse bwanji kuti ‘sali mbali ya dziko’?

20 Dziko la Satana sililemekeza moyo, ndipo lili na mlandu kwa Yehova, inde mlandu wakupha anthu. Kwa zaka mahandiledi, olamulila andale aphetsa anthu mamiliyoni ambili, kuphatikizapo atumiki a Yehova oculuka. M’Baibo, maulamulilo amenewa, kapena kuti maboma, amawachula kuti ni vilombo voyofya komanso vaukali. (Danieli 8:3, 4, 20-22; Chivumbulutso 13:1, 2, 7, 8) Masiku ano, kugulitsa zida zankhondo ni malonda aakulu. Anthu amapeza ndalama zoculuka pogulitsa zida zankhondo zoopsa. N’zoonekelatu kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.

21 Koma Akhristu oona ‘sali mbali ya dziko.’ Tikabwela pa zandale kapena nkhondo, anthu a Yehova satengako mbali. Popeza iwo sapha munthu, sakhalanso ku mbali ya bungwe lililonse limene limaphetsa anthu. (Yohane 15:19; 17:16) Pamene Akhristu azunzidwa, sabwezela ciwawa. Yesu anatiphunzitsa kuti tizikonda ngakhale adani athu.—Mateyu 5:44; Aroma 12:17-21.

22 Cipembedzo naconso capaitsa anthu mamiliyoni ambili-mbili. Pokamba za Babulo Wamkulu, kapena kuti citaganya conse ca zipembedzo zonyenga, Baibo imati: “Mwa iye munapezeka magazi a aneneli, a oyela, ndi a onse amene anaphedwa padziko lapansi.” Kodi mwaona cifukwa cake Yehova akuticenjeza kuti: “Tulukani mwa iye anthu anga”? Amene amalambila Yehova sali mbali ya cipembedzo conama.—Chivumbulutso 17:6; 18:2, 4, 24.

23. Kodi ‘kutuluka’ m’Babulo Wamkulu kumafuna kucita ciani?

23 ‘Kutuluka’ mu Babulo Wamkulu kumatanthauza kucoka m’cipembedzo ciliconse conama. Mwacitsanzo, tingafunikile kulemba kalata yopempha kuti dzina lathu alicotse m’kaundula wa cipembedzo. Koma palinso zina. Tiyenelanso kuleka komanso kudana nazo zinthu zoipa zimene cipembedzo conyenga cimacita. Zipembedzo zonyenga zimalimbikitsa makhalidwe oipa, zandale, komanso dyela. (Ŵelengani Salimo 97:10; Chivumbulutso 18:7, 9, 11-17) Cifukwa ca zimenezi, miyoyo yambili-mbili yataika kwa zaka zambili.

24, 25. Kodi tikadziŵa Yehova, timakhala bwanji na mtendele komanso cikumbumtima wabwino?

24 Tikalibe kudziŵa Yehova, ambili a ife tinacitako zinthu zoipa za m’dziko la Satana. Koma lomba tinasintha. Tinalandila dipo, ndipo tinapatulila miyoyo yathu kwa Mulungu. Tili mu ‘nyengo zotsitsimula . . . zocokela kwa Yehova.’ Tili na mtendele na cikumbumtima cabwino, podziŵa kuti tikutumikila Yehova.—Machitidwe 3:19; Yesaya 1:18.

25 Ngakhale ngati tinali m’bungwe losalemekeza moyo, Yehova angatikhululukile pamaziko a dipo. Timayamikila kwambili moyo umene Yehova anatipatsa. Ndipo timaonetsa kuyamikila pothandiza anthu ena kuphunzila za Yehova, kucoka m’dziko la Satana, kuti akhale paubwenzi wabwino na Mulungu.—2 Akorinto 6:1, 2.

MUZIUZAKO ENA ZA UFUMU WA MULUNGU

26-28. (a) Kodi Yehova anapatsa Ezekieli nchito yanji yapadela? (b) Nanga masiku ano, Yehova amafuna kuti ticite ciani?

26 Ku Isiraeli wakale, Yehova anauza mneneli Ezekieli kuti acenjeze anthu kuti Yerusalemu adzawonongedwa, na kuti awaphunzitse zofunika kucita kuti akapulumuke. Sembe Ezekieli sanacenjeze anthu, Yehova akanam’patsa mlandu woŵataitsa miyoyo yawo. (Ezekieli 33:7-9) Koma Ezekieli anaonetsa kuti amalemekeza moyo pocita zonse zotheka kuti alengeze uthenga wofunikawo.

27 Ifenso Yehova anatipatsa nchito yocenjeza anthu zakuti dziko la Satana lidzawonongedwa posacedwa. Na kuti tiwathandize kudziŵa Yehova kuti akaloŵe m’dziko latsopano. (Yesaya 61:2; Mateyu 24:14) Tifunika kulimbikila kuŵadziŵitsa za uthenga umenewo. Ifenso tifuna kukamba mawu a Paulo akuti: “Ine ndine woyela pa mlandu wa magazi a anthu onse. Pakuti sindinakubisileni kanthu, koma ndinakuuzani cifunilo conse ca Mulungu.”—Machitidwe 20:26, 27.

28 Koma palinso mbali zina mu umoyo zimene tifunika kukhala oyela. M’mutu wokonkhapo tidzakambilana zimenezo.