Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MUTU 12

Muzikamba Mawu Olimbikitsa

Muzikamba Mawu Olimbikitsa

“Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu, koma alionse olimbikitsa.”—AEFESO 4:29.

1-3. (a) Kodi Yehova anatipatsanso mphatso yabwino iti? Nanga tingaiseŵenzetse bwanji molakwa? (b) Kodi tiyenela kuiseŵenzetsa bwanji?

TIYELEKEZE kuti tate wagulila mwana wake wacinyamata njinga. Iye ni wokondwa kupatsa mwana wakeyo mphatso yapadela imeneyo. Koma bwanji ngati mwanayo ayendetsa njinga yake mosasamala, cakuti agunda munthu, iyenso n’kudzicita? Kodi tate wake angamvele bwanji?

2 Yehova ndiye Wopeleka “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo.” (Yakobo 1:17) Mphatso ina yabwino imene anatipatsa ni luso la kukamba. Mwa mwawu, tikhoza kuonetsa maganizo athu na mmene timvelela. Timatha kukamba mawu othandiza anthu ena kumvela bwino. Koma mawu athu akhozanso kuvulaza ena, na kuwakhumudwitsa.

3 Mawu ali na mphamvu kwambili. Ndipo Yehova amatiphunzitsa kuseŵenzetsa bwino mphatso ya kukamba. Iye amatiuza kuti: “Mawu alionse owola asatuluke pakamwa panu, koma alionse olimbikitsa monga mmene kungafunikile, kuti asangalatse owamva.” (Aefeso 4:29) Tiyeni tione mmene tingagwilitsile nchito mphatso yocokela kwa Mulungu imeneyi, m’njila yom’kondweletsa komanso yolimbikitsa ena.

SAMALANI NA MAWU ANU

4, 5. Kodi tiphunzilanji m’Baibo za mphamvu ya mawu?

4 Mawu ali na mphamvu. Conco, tiyenela kusankha bwino zokamba, na mozikambila. Miyambo 15:4 imati: “Lilime lodekha lili ngati mtengo wa moyo, koma lilime lacinyengo limapweteketsa mtima.” Monga mmene mtengo wobiliŵila umatsitsimulila na kucilikiza moyo, mawu okoma amatsitsimula womvela. Koma mawu ankhadzulila amapweteka ena, cakuti amakwinyilila kwambili.—Miyambo 18:21.

Mawu odekha amatsitsimula

5 Miyambo 12:18 imati mawu amalasa monga lupanga. Inde, mawu ankhadzulila amapweteka mu mtima, ndipo amawononga maubale. Mwina mungakumbukile pamene wina anakukambilani mawu oipa amene anakuŵaŵani kwambili. Komabe, lemba la Miyambo lipitiliza kuti: “Koma lilime la anthu anzelu limacilitsa.” Mawu oganizidwa bwino amacilitsa mtima woŵaŵa, na kukonzanso maubale ogwedezeka cifukwa comvana molakwa. (Ŵelengani Miyambo 16:24.) Ngati tikumbukila kuti mawu athu akhoza kupweteka ena, tidzasamala zokamba.

6. N’cifukwa ciani zimakhala zovuta kulamulila lilime lathu?

6 Cifukwa cina cosamalila na mawu athu n’cakuti ndise opanda ungwilo. “Maganizo a anthu amakhala oipa,” ndipo mawu athu nthawi zambili amavumbula zili mu mtima mwathu. (Genesis 8:21; Luka 6:45) Koma nthawi zina zimakhala zovuta ndithu kulamulila lilime lathu. (Ŵelengani Yakobo 3:2-4.) Komabe, tifunika kupitiliza kuyesetsa kukonza mokambila na anthu.

7, 8. Kodi mawu athu angakhudze bwanji ubale wathu na Yehova?

7 Cinanso cokhalila osamala na mawu athu, n’cakuti Yehova adzatiŵelengela mlandu pa zokamba zathu, na mmene timazikambila. Yakobo 1:26 imati: “Ngati munthu akudziona ngati wopembedza, koma salamulila lilime lake, ndipo akupitiliza kunyenga mtima wake, kupembedza kwa munthu ameneyu n’kopanda pake.” Mawu akuti ‘kupanda pake,’ angatanthauzenso kupanda nchito. (1 Akorinto 15:17) Ngati sitisamala na mawu athu, tingawononge ngakhale ubale wathu na Yehova.—Yakobo 3:8-10.

8 Mwacionekele, tili na zifukwa zabwino zokhalila osamala na mawu athu, na mmene timawakambila. Koma kuti tidziŵe bwino makambidwe okondweletsa Yehova, tiyenela coyamba kudziŵa makambidwe ofunika kuyapewa.

MAWU OPASULA

9, 10. (a) Ni malankhulidwe ati amene afala m’dziko masiku ano? (b) Nanga n’cifukwa ciani tiyenela kuyapewa?

9 Kutukwana na manyozo n’zofala kwambili masiku ano. Anthu ena amaona kuti akatukwana m’pamene zokamba zake zimamveka. Akatswili anthabwala pofuna kuseketsa anthu, amadalila kwambili zotukwana na mawu onyoza. Koma mtumwi Paulo anakamba kuti: “Zonsezo muzitaye kutali ndi inu. Mutaye mkwiyo, kupsa mtima, kuipa, ndi mawu acipongwe, ndipo pakamwa panu pasatuluke nkhani zotukwana.” (Akolose 3:8) Paulo anakambanso kuti “nthabwala zotukwana,” “zisachulidwe n’komwe pakati” pa Akhristu.—Aefeso 5:3, 4.

10 Mawu otukwana amakhumudwitsa Yehova, komanso anthu ena omukonda. Ndipo ni onyansa. M’Baibo, zinthu zonyansa, kapena kuti “zodetsa,” zimaphatikizapo “nchito za thupi.” (Agalatiya 5:19-21) Inde, “zodetsa” zingaphatikizeponso macimo osiyana-siyana. Ndipo mcitidwe wodetsa uliwonse umaitananso unzake. Ngati munthu ali na cizolowezi cokonda kutukwana, ndipo safuna kuleka, sayenelela kukhala mu mpingo.—2 Akorinto 12:21; Aefeso 4:19; onani Mfundo ya Kumapeto 23.

11, 12. (a) Kodi makambilano athu angafike bwanji pokhala mijedo yovulaza? (b) N’cifukwa ciani tiyenela kupeŵa kucitila misece aliyense?

11 Tiyenela kupewanso mijedo yovulaza. N’cibadwa ife anthu kufuna kudziŵako za ena, na kuuzako ena nkhani zokhudza anzathu komanso abululu athu. Ngakhale Akhristu oyambilila, anali kufuna kudziŵa za abale na alongo awo, na mmene angawathandizile. (Aefeso 6:21, 22; Akolose 4:8, 9) Komabe, makambilano okhudza ena angasinthe mosavuta n’kukhala mijedo yovulaza. Ngati na ise tiuzako ena mijedo imene tamvela, tingafalitse mabodza, kapena kuulula zisinsi za ena. Ngati sitisamala, tingapezeke kuti tanamizila munthu wina, kapena kum’citila misece. Afarisi anacitila Yesu misece pom’namizila zinthu zimene sanacite. (Mateyu 9:32-34; 12:22-24) Misece imawononga mbili ya munthu, imabweletsa mikangano, kupsetsana mtima, na kuwononga maubwenzi.—Miyambo 26:20.

12 Yehova amafuna kuti mawu athu tizithandiza nawo anthu ena na kuwalimbikitsa, osati kusandutsila mabwenzi athu kuti akhale adani. Yehova amazonda anthu “opikisanitsa abale.” (Miyambo 6:16-19) Woneneza ena woyamba anali Satana Mdyelekezi, amene ananamizila Mulungu. (Chivumbulutso 12:9, 10) Masiku ano, anthu ambili amakonda kunamizilana. Koma izi n’zosayenela mu mpingo wacikhristu. (Agalatiya 5:19-21) Conco, tifunika kusamala na zokamba zathu. Komanso, tiziganiza tisanakambe. Musanauzeko munthu wina zimene munamvela, dzifunseni kuti: ‘Kodi cimene nifuna kukamba n’ca zoona? Kodi n’cabwino kukamba? Kodi n’cothandiza? Kodi ningakonde kuti mwini wake adziŵe zimene nikamba? Ningamvele bwanji ngati munthu wina angauze ena zimenezi, koma akukamba za ine?—Ŵelengani 1 Atesalonika 4:11.

13, 14. (a) Kodi mawu acipongwe angapangitse munthu kumvela bwanji? (b) Kodi kulalata n’ciani? N’cifukwa ciani Akhristu afunika kupewa khalidwe limeneli?

13 Nthawi zina, ife tonse timakamba zinthu zimene timamva kuipa pambuyo pake. Koma sitifuna kukhala na cizolowezi cokamba mawu osuliza anthu ena, onyozela, kapena otafula. Mawu acipongwe alibe malo m’miyoyo yathu. Paulo anakamba kuti: “Kuŵaŵidwa mtima konse kwa njilu, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu acipongwe zicotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse.” (Aefeso 4:31) Ma Baibo ena amamasulila “mawu acipongwe” kuti “mawu oipa,” “mawu opweteka,” komanso “mawu otukwana.” Mawu acipongwe amacotsela anthu ulemu wawo, ndipo amadzimva monga acabe-cabe. Maka-maka ana amakhumudwa mosavuta. Conco, tiyenela kusamala kuti tisawakhwetemule na mawu athu.—Akolose 3:21.

14 Baibo imaticenjeza za mtundu wa mawu acipongwe oipa kwambli—kulalata. Kulalata ni kupitiliza kutafulila munthu wina n’colinga cakuti akhumudwe. Zingakhale zacisoni kwambili ngati munthu atafulila mnzake wa m’cikwati, kapena ana ake. Ndipo ngati munthu saleka khalidwe lotafulila anthu ena, sayenelela kukhala mu mpingo. (1 Akorinto 5:11-13; 6:9, 10) Monga taphunzilila, ngati tikamba mawu otukwana, abodza, kapena acipongwe, timawononga ubale wathu na Yehova, komanso na anthu ena.

MAWU OLIMBIKITSA

15. Ni mawu otani amene amalimbikitsa maubale?

15 Kodi tingaseŵenzetse bwanji mphatso ya kukamba mmene Yehova amafunila? Olo kuti Baibo siicita kutichulila zoyenela na zosayenela kukamba, imatiuza kuti tiyenela kukamba “mawu alionse olimbikitsa.” (Aefeso 4:29) Mawu olimbikitsa ni mawu oyela, acisomo, komanso oona. Yehova amafuna kuti mawu athu tizilimbikitsa nawo anthu ena na kuwathandiza. Koma izi zingakhale zovuta nthawi zina. Kukamba zinthu zolimbikitsa kumafuna khama, kusiyana n’kukamba zinthu zosuliza kapena zolefula. (Tito 2:8) Tiyeni tikambilane njila zina zolimbikitsila ena na mawu athu.

16, 17. (a) N’cifukwa ciani tiyenela kuyamikila ena? (b) Ndani amene tingawayamikile?

16 Yehova na Yesu, onse amakonda kuyamikila ena. Tiyenela kutengela citsanzo cawo. (Mateyu 3:17; 25:19-23; Yohane 1:47) Kuti tipeleke ciyamikilo colimbikitsadi munthu, tiyenela kum’ganizila munthuyo na kuonetsa cidwi cathu pa iye. Miyambo 15:23 imati: “Mawu onenedwa pa nthawi yoyenela ndi abwino kwambili.” Munthu wina akatiyamikila mocokela pansi pa mtima pa cinthu cabwino cimene tacita, zimatilimbikitsa kwambili.—Ŵelengani Mateyu 7:12; onani Mfundo ya Kumapeto 27.

17 Ngati mukhala na cizolowezi coyang’ana pa zabwino mwa ena, sicivuta kuwayamikila moona mtima. Mwacitsanzo, mungaone kuti wina mu mpingo amakonzekela bwino nkhani zake, kapena amapeleka ndemanga zabwino pa misonkhano. Mwinanso pali wacicepele amene amaimila bwino coonadi ku sukulu, kapena wacikulile wokangalika mu ulaliki. Mawu owayamikila angawalimbikitse kwambili. N’cinthu cofunikanso kwambili mwamuna kumauza mkazi wake kuti amamukonda kwambili, komanso kumamuyamikila. (Miyambo 31:10, 28) Monga mmene zomela zimafunila kuwala na madzi, anthu amafuna kuwayamikila. Zimenezi n’zoona maka-maka kwa ana. Yesani kupeza mipata yowayamikila pa zimene amacita bwino. Tikawayamikila, amakhala olimba mtima ndiponso acidalilo. Amakhalanso ofunitsitsa kuwonjezela zabwino zimene amacita.

Tikhoza kulimbikitsa na kutonthoza ena mwa mawu athu na mmene tiwakambila

18, 19. N’cifukwa ciani tiyenela kulimbikitsa na kutonthoza ena? Nanga tingacite bwanji zimenezo?

18 Pamene tilimbikitsa ena na kuwatonthoza, timatengela citsanzo ca Yehova. Iye amasamala kwambili za “anthu opsinjika,” komanso “anthu onyozeka.” (Yesaya 57:15) Yehova amafuna kuti ‘tipitilize kulimbikitsana’ na ‘kutonthoza’ a mtima wacisoni. (1 Atesalonika 5:11, 14) Pamene tilimbikila kucita zimenezi, Yehova amaona ndipo amayamikila kwambili.

19 Mwina mungaone kuti munthu wina mu mpingo ni wolefulidwa, kapena wopsinjika maganizo. Kodi mungamuuze mawu anji omuthandiza? Ngakhale kuti simungathetse vuto lake, mungaonetse kuti mumamudela nkhawa. Mwacitsanzo, mungapatule nthawi yokamuona. Mungaŵelenge naye vesi yolimbikitsa m’Baibo, ngakhale kupemphela naye. (Salimo 34:18; Mateyu 10:29-31) Auzeni kuti abale na alongo mu mpingo amawakonda kwambili. (1 Akorinto 12:12-26; Yakobo 5:14, 15) Kambani moonetsa kuti zimene mukamba n’zoona, ndipo mumazikhulupilila.—Ŵelengani Miyambo 12:25.

20, 21. N’ciani cimathandiza anthu kulandila bwino uphungu?

20 Komanso, timalimbikitsa anthu ena powapatsa uphungu wabwino. Pokhala anthu opanda ungwilo, tonse timafunikila uphungu nthawi na nthawi. Miyambo 19:20 imati: “Mvela uphungu ndipo utsatile malangizo kuti udzakhale wanzelu m’tsogolo.” Si akulu cabe amene angapeleke uphungu kapena malangizo. Makolo afunikila kulangiza ana awo. (Aefeso 6:4) Alongo nawonso angapeleke uphungu wabwino kwa alongo anzawo. (Tito 2:3-5) Popeza timawakonda abale na alongo athu, sitifuna kuwapatsa uphungu m’njila yowamvetsa kuipa. Kodi cingatithandize n’ciani?

21 Mwina mungakumbukile pamene wina anakupatsani uphungu wabwino m’njila yosavuta kuulandila. N’cifukwa ciani uphunguwo unali wokufikani pa mtima? N’cifukwa coona kuti munthuyo anali kukufunilani zabwino. Kapenanso n’cifukwa cakuti anakamba na imwe mokoma mtima, komanso mwacikondi. (Akolose 4:6) Mwacionekele, uphunguwo unazikidwanso pa Baibo. (2 Timoteyo 3:16) Kaya tigwila mawu m’Baibo kapena ayi, pazikhala maziko a m’Malemba pa uphungu uliwonse umene tipeleka. Palibe ayenela kuumiliza maganizo ake pa ena, kapena kupotoza malemba kuti agwilizane na maganizo ake. Kukumbukila mmene ena anakupatsilani uphungu wabwino, kudzakuthandizani popatsa ena uphungu.

22. Kodi mufuna kuti mphatso yanu ya kukamba muziiseŵenzetsa bwanji?

22 Kukamba ni mphatso yocokela kwa Mulungu. Conco pokonda Mulungu wathu, mphatsoyi tifunika kuiseŵenzetsa moyenelela. Dziŵani kuti mawu ali na mphamvu yopasula, komanso yolimbikitsa. Mwa ici, tiyenela kumayesetsa kugwilitsila nchito mawu athu kulimbikitsa na kumangiliza ena.