Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MUTU 16

Mutsutseni Mdyelekezi

Mutsutseni Mdyelekezi

“Tsutsani Mdyelekezi, ndipo adzakuthaŵani.” —YAKOBO 4:7.

1, 2. Kodi tiyenela kuzindikila ciani za Satana na ziŵanda zake?

UMOYO m’dziko latsopano la Yehova udzakhala wosangalatsa ngako. Tidzakhala na umoyo umene Mulungu wakhala akutifunila. Koma pakali pano, tikukhala m’dziko loyendetsedwa na Satana na ziŵanda zake. (2 Akorinto 4:4) Olo kuti sitiwaona, iwo aliko ndipo ni amphamvu kwambili.

2 M’mutu uno, tidzakambilana za mmene tingakhalile pafupi na Yehova, kuti atiteteze kwa Satana. Yehova analonjeza kuti adzatithandiza. Koma tiyenela kuzindikila njila zimene Satana na ziŵanda zake amaseŵenzetsa kuti atipusitse na kutiukila.

“NGATI MKANGO WOBANGULA”

3. N’ciani cimene Mdyelekezi amafunitsitsa kucita kwa ife?

3 Satana amakamba kuti anthu amatumikila Yehova cabe cifukwa cofunako zinthu zabwino. Amati koma zinthu zikavuta, akhoza kuleka kum’tumikila. (Ŵelengani Yobu 2:4, 5.) Munthu aliyense akaoneka kuti afuna kuphunzila za Yehova, Satana na ziŵanda zake amayesetsa kum’leketsa. Akaona kuti munthu wadzipatulila kwa Yehova na kubatizika, amakwiya kwambili. Baibo imayelekezela Mdyelekezi na “mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Petulo 5:8) Colinga ca Satana ni kuwononga ubale wathu na Yehova basi.—Salimo 7:1, 2; 2 Timoteyo 3:12.

Satana amakwiya kwambili tikadzipatulila kwa Yehova

4, 5. (a) Kodi Satana sanaloledwe kukhala na ciani? (b) Kodi tingamutsutse bwanji Mdyelekezi?

4 Koma sitifunika kumuopa Satana na ziŵanda zake. Yehova sanawalole kukhala na mphamvu zoticita cina ciliconse cimene angafune. Ndipo Yehova analonjeza kuti “khamu lalikulu” la Akhristu oona, lidzapulumuka “cisautso cacikulu.” (Chivumbulutso 7:9, 14) Palibiletu cimene Mdyelekezi angacite kuti alepheletse zimenezo, cifukwa Yehova amateteza anthu ake.

5 Ngati tikhalabe pafupi na Yehova, Satana sangakwanitse kuwononga mgwilizano wathu na Mulungu. Mawu Mulungu amatitsimikizila kuti: “Yehova akhala nanu inuyo mukapitiliza kukhala naye.” (2 Mbiri 15:2; ŵelengani 1 Akorinto 10:13.) Amuna komanso akazi okhulupilika akale, monga Abele, Inoki, Nowa, Sara, na Mose, anam’tsutsa Mdyelekezi mwa kukhalabe pafupi na Yehova. (Aheberi 11:4-40) Ifenso tikhoza kucita cimodzi-modzi. Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti: “Tsutsani Mdyelekezi ndipo adzakuthaŵani.”—Yakobo 4:7.

TILI PA NKHONDO

6. Kodi Satana amatiukila bwanji?

6 Olo kuti Satana amadziŵa kuti Yehova anam’cepetsela mphamvu pa ife, iye amayesetsabe kucita ciliconse kuti awononge ubale wathu na Mulungu. Masiku ano, Mdyelekezi amatiukila m’njila zambili, ndipo amaseŵenzetsa macenjela amene wawagwilitsila nchito kwa zaka masauzande. Kodi ena mwa iwo ni ati?

7. N’cifukwa ciani Satana amaukila anthu a Yehova?

7 Mtumwi Yohane analemba kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Satana ndiye akuyendetsa dziko loipali, ndipo amafunanso kulamulila anthu a Yehova. (Mika 4:1; Yohane 15:19; Chivumbulutso 12:12, 17) Mdyelekezi podziŵa kuti nthawi yamuthela, amayesetsa kupanikiza aliyense wa ife kuti tipandukile Mulungu. Nthawi zina amatiukila mwacindunji. Koma nthawi zina, amayesa kutikopa mwamacenjela.

8. Kodi Mkhristu aliyense afunika kudziŵa ciani?

8 Malinga na Aefeso 6:12, tikulimbana na “makamu a mizimu yoipa, m’malo akumwamba.” Inde, Mkhristu aliyense payekha akulimbana, kapena kuti kugwebana, na Mdyelekezi na ziŵanda zake. Tiyenela kudziŵa kuti onse amene anadzipatulila kwa Yehova, ali pa nkhondo imeneyi. M’kalata yake kwa Aefeso, mtumwi Paulo analimbikitsa Akhristu katatu konse kuti asasunthike, koma akhale olimba.—Aefeso 6:11, 13, 14.

9. Kodi Satana na ziŵanda zake amayesetsa kucita ciani kwa ife?

9 Satana na ziŵanda zake amayesa kutinyenga m’njila zosiyana-siyana. Ngati Satana walephela kutipusitsa pa ciyeselo cimodzi, sindiye kuti basi sangaticenjelele pa ciyeselo cina. Nthawi zonse Mdyelekezi amakhala akufuna-funa zofooka zathu kuti asankhe bwino misampha yotichela nayo. Koma mwayi wathu ni wakuti, Baibo imatiphunzitsa bwino lomwe za misampha ya Mdyelekezi. (2 Akorinto 2:11; onani Mfundo ya Kumapeto 31.) Umodzi wa misampha imeneyo ni zaziŵanda.

KHALANI KUTALI NA ZIŴANDA

10. (a) Kodi zaziŵanda zimaloŵetsamo ciani? (b) Nanga Yehova amaziona bwanji?

10 Zaziŵanda zimaphatikizapo zocitika zopangitsa munthu kuyamba kukambilana na ziŵanda, monga kulosela zakutsogolo, zaufiti, kuwombeza, kapena kuyesa kukambilana na anthu akufa. Baibo imatiuza kuti zaziŵanda ‘zimamunyansa’ Mulungu, ndiponso kuti sitingadziloŵetse mu zaziŵanda, panthawi imodzi-modzi n’kumalambila Yehova. (Deuteronomo 18:10-12; Chivumbulutso 21:8) Akhristu ayenela kupewelatu ciliconse cokhudzana na ziŵanda.—Aroma 12:9.

11. Kodi cingacitike n’ciani ngati timacita cidwi na zamizimu?

11 Satana amadziŵa kuti ngati timacita cidwi na zamizimu, m’posavuta kuti atikopele ku zaziŵanda. Ciliconse cokhudza zaziŵanda cingawononge ubale wathu na Yehova.

SATANA AMAYESA KUTIPUSITSA

12. Kodi Satana amayesa bwanji kusokoneza maganizo athu?

12 Satana amasokoneza maganizo a anthu. Coyamba amabyala mbewu za cikaikilo. Pang’ono-m’pang’ono, anthu amayamba kuganiza kuti “cabwino n’coipa ndipo coipa n’cabwino.” (Yesaya 5:20) Mdyelekezi amalimbikitsa maganizo akuti uphungu wa m’Baibo sugwila nchito, ndipo tingakhale acimwemwe ngati tinyalanyaza miyezo ya Mulungu.

13. Kodi Satana wayesa motani kuyambitsa zikaikilo?

13 Kufalitsa zikaikilo ndiyo njila imodzi imene Satana amapusitsa nayo anthu ambili. Wakhala akuseŵenzetsa njila imeneyi kuyambila kale-kale. M’munda wa Edeni, Satana anayambitsa cikaikilo pamene anafunsa Hava kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?” (Genesis 3:1) M’nthawinso ya Yobu, Satana anafunsa Yehova pamaso pa angelo kuti: “Kodi mukuganiza kuti Yobu amangoopa Mulungu pacabe?” (Yobu 1:9) Yesu atabatizika, Satana anamuyesa pomuuza kuti: “Ngati ndinudi mwana wa Mulungu, uzani miyala iyi kuti isanduke mitanda ya mkate.”—Mateyu 4:3.

14. Kodi Satana angapangitse bwanji anthu kukaikila ngati zaziŵanda zilidi zoopsa?

14 Ngakhale masiku ano, Mdyelekezi akupitiliza kubyala mbewu za cikaikilo m’mitima ya anthu. Amapangitsa anthu kukaikila ngati zaziŵanda zilidi zoipa, pozipangitsa kuoneka monga zopanda vuto. Ngakhale Akhristu ena saona kuopsa kwake. (2 Akorinto 11:3) Conco, tingacite ciani kuti tidziteteze? Tingatsimikize bwanji kuti Satana sakutipusitsa na macenjela ake? Tiyeni tione njila ziŵili zimene angatipusitse nazo: zosangalatsa na cithandizo ca mankhwala.

SATANA AMAYESA KUTILOŴELA KU ZIKUMBO ZATHU ZACIBADWA

15. Kodi tingadziloŵetse bwanji m’zaziŵanda kupitila m’zosangalatsa?

15 Mwacibadwa, ife anthu timakhala na cikhumbo cofuna kusangalala. Koma masiku ano, mafilimu ambili, mavidiyo, mapulogilamu a pa TV, maseŵela apakompyuta, komanso mawebusaiti a pa Intaneti, amaonetsa zaziŵanda, zamatsenga, komanso mphamvu ya zamizimu. Anthu ambili amaona kuti zinthu zimenezi n’zosangalatsa cabe, ndipo sazindikila kuopsa kolola ziŵanda mu umoyo wawo. Munthu angadziloŵetsenso mu zaziŵanda mwa kukhulupilila nyenyezi (ma horoscope), kupenda mizele ya padzanja, makhadi amatsenga, komanso magilasi ooneka monga bola. Mdyelekezi amabisa kuopsa kwa zinthu zimenezi, na kuzipangitsa kuoneka monga ni zosangalatsa komanso zocititsa cidwi. Ndipo munthu angaziona monga kupenyelela zaziŵanda kapena zamizimu kulibe vuto, malinga ngati iye sangaciteko zinthu zimenezo. Koma n’cifukwa ciani kaganizidwe kameneka n’kangozi?—1 Akorinto 10:12.

16. N’cifukwa ciani tifunika kupewa zosangalatsa zophatikizamo zamizimu?

16 Satana na ziŵanda zake sakwanitsa kudziŵa zili m’maganizo mwathu. Koma amatha kudziŵa zimene timalaka-laka poona zosankha zathu zokhudza ife na banja lathu, komanso zosangalatsa. Ngati tisankha mafilimu, nyimbo, kapena mabuku okhudza zamizimu, matsenga, anthu ogwidwa na ziŵanda, mfiti, vipuku, kapena nkhani zina zofananako, pamenepo Satana na ziŵanda zake amadziŵa kuti timacita nazo cidwi. M’pamene amatikopa kuti tiloŵeletu m’zaziŵanda.—Ŵelengani Agalatiya 6:7.

17. Kodi Satana angapezelepo bwanji mpata pamene tifuna cithandizo ca mankhwala?

17 Satana angapezeleponso mpata pamene tifuna cithandizo ca mankhwala. Masiku ano, anthu ambili amadwala matenda ovutitsa. Munthu angakhale atayesa zithandizo zosiyana-siyana koma osacila. (Maliko 5:25, 26) Pothedwa nzelu, angafune kungoyesa zilizonse. Koma kwa ife Akhristu, tiyenela kusamala kuti tisasankhe macilitso ophatikizamo “mphamvu zamatsenga.”—Yesaya 1:13.

Mukadwala, dalilani Yehova na mtima wonse

18. Kodi Mkhristu ayenela kupewa macilitso otani?

18 Mu Isiraeli wakale, anthu ena anali kuseŵenzetsa “mphamvu zamatsenga.” Ndipo Yehova anati kwa iwo: “Mukatambasula manja anu, ndimakubisilani maso anga. Ngakhale mupeleke mapemphelo ambili, ine sindimvetsela.” (Yesaya 1:15) Tangoganizani! Yehova sanali kufuna ngakhale kumvetselako cabe mapemphelo awo! Mwa ici, sitingafune kucita ciliconse cosokoneza ubale wathu na Yehova, kuopela kuti angaleke kutithandiza, maka-maka pamene tikudwala. (Salimo 41:3) Conco, ngati tikufuna cithandizo ciliconse pa matenda, titsimikizile kuti sicikuloŵetsamo zaziŵanda, kapena mphamvu zamatsenga, m’njila iliyonse. (Mateyu 6:13) Ngati pali kuthekela kwakuti cimakhudzako ku zimenezo, ticikane cithandizo cimeneco!—Onani Mfundo ya Kumapeto 32.

NKHANI ZOKHUDZA ZIŴANDA

19. N’ciani cikupangitsa anthu ambili kumuyopa Mdyelekezi?

19 Anthu ena amaganiza kuti Mdyelekezi na ziŵanda kulibe, n’zongoganizila cabe. Koma ena amadziŵa kuti zilikodi cifukwa ca zimene zinawacitikilapo. Ambili amacita mantha na mizimu yoipa, ndipo ali mu ukapolo wa miyambo. Ena amapangitsa anthu ambili kuopa ziŵanda, powauza zoopsa zimene akuti ziŵanda zinacita kwa anthu ena. Kambili, anthu amacita cidwi na nkhani zimenezi, cakuti nawonso amazifalitsa kwa ena. Ndiye cifukwa cake anthu amamuyopa Mdyelekezi.

20. Kodi tingam’thandizile bwanji Satana kufalitsa mabodza ake?

20 Ganizilani izi: Satana amafuna kuti anthu azimuyopa. (2 Atesalonika 2:9, 10) Iye ni wabodza, ndipo amadziŵa mopusitsila anthu amene amakopeka na zamizimu. Amawapangitsa kukhulupilila zinthu zimene si zazoona. Anthu amenewo angafotokoze zinthu zimene m’maganizo mwawo, amakhulupilila kuti anaziona kapena kuzimva. Ndipo anthu ena posimbilakonso ena nkhani zimenezo, mabodza ake amangokulila-kulila. Sitifuna kuti ifenso tizithandizila Satana kufalitsa nkhani zimenezo, zimene zimaika anthu mu ukapolo wa mantha.—Yohane 8:44; 2 Timoteyo 2:16.

21. M’malo momasimbila ena nkhani zokhudza ziŵanda, kodi tingakambilaneko nkhani zanji?

21 Ngati wa Mboni za Yehova anavutitsidwapo na ziŵanda, sayenela kusimbilako ena monga nkhani ya maceza cabe ayi. Sitifunika kuopseza anthu a Yehova na zimene Mdyelekezi na ziŵanda zake angacite. M’malo mwake, tifunika kusumika maganizo athu pa Yesu, komanso mphamvu zimene Yehova anam’patsa. (Aheberi 12:2) Yesu sanali kuceza na ophunzila ake za nkhani zokhudza ziŵanda ayi. Iye anasumika maganizo ake pa uthenga wa Ufumu, na “zinthu zazikulu za Mulungu.”—Machitidwe 2:11; Luka 8:1; Aroma 1:11, 12.

22. Kodi mufunika kukhala wotsimikiza mu mtima mwanu kucita ciani?

22 Tisaiŵale kuti colinga ca Satana ni kuwononga ubale wathu na Yehova. Amacita ciliconse cotheka kuti akwanilitse colinga cake. Koma ife timawadziŵa macenjela a Mdyelekezi, ndipo ndife okonzeka kutsutsa mtundu uliwonse wa zaziŵanda. Ndipo ‘sitidzam’patsa mpata Mdyelekezi’ kuti atifooketse. (Ŵelengani Aefeso 4:27.) Inde, tikamutsutsa Mdyelekezi, tidzapewa misampha yake, na kukhala m’citetezo ca Yehova.—Aefeso 6:11.