Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MUTU 15

Muzikondwela Nayo Nchito Yanu

Muzikondwela Nayo Nchito Yanu

‘Munthu aliyense . . . asangalale cifukwa cogwila nchito mwakhama.’—MLALIKI 3:13.

1-3. (a) Kodi anthu ambili amamvela bwanji akaganiza za nchito yawo? (b) Tidzakambilana mafunso ati m’mutu uno?

ZUNGULILE dziko lapansi, anthu amagwila nchito molimbika kuti adzisamalile, na kusamalila mabanja awo. Ambili sakonda nchito yawo, cakuti ena amaipidwa tsiku lililonse akamapita ku nchito. Ngati inunso m’mamva conco, kodi mungacite ciani kuti muzikondwela nayo nchito yanu?

2 Yehova amatiuza kuti: “Munthu aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, cifukwa coti wagwila nchito mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yocokela kwa Mulungu.” (Mlaliki 3:13) Yehova anatilenga na mtima wofuna kugwila nchito. Amafuna kuti tizikondwela na zimene ticita.—Ŵelengani Mlaliki 2:24; 5:18.

3 Conco, n’ciani cingatithandize kukondwela na nchito yathu? Ni nchito ziti zimene Akhristu ayenela kupewa? Ndipo tingalinganize bwanji bwino nchito yathu na kulambila Yehova? Nanga ni nchito iti yoposa zonse imene tifunika kugwila?

OGWILA NCHITO AŴILI OPAMBANA ONSE

4, 5. Kodi kugwila nchito amakuona bwanji Yehova?

4 Yehova amakonda kugwila nchito. Genesis 1:1 imati: “Pa ciyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Atatsiliza kupanga dziko lapansi na zonse zimene zilipo, anaona kuti zonse “zinali zabwino kwambili.” (Genesis 1:31) Mlengi wathu anakhutila na zimene anapanga.—1 Timoteyo 1:11.

5 Yehova saleka kugwila nchito. Yesu anakamba kuti: “Atate wanga akugwilabe nchito mpaka pano.” (Yohane 5:17) Olo kuti sitidziŵa zabwino zonse zimene Yehova wakhala akucita, zina timazidziŵako. Iye wakhala kusankha aja okalamulila kumwamba pamodzi na Mwana wake, Yesu Khristu. (2 Akorinto 5:17) Yehova alinso pa nchito yotsogolela na kusamalila anthu. Cifukwa ca nchito yolalikila, anthu mamiliyoni afika pom’dziŵa Yehova, ndipo ali na ciyembekezo cokalandila moyo wosatha m’paradaiso, pano pa dziko lapansi.—Yohane 6:44; Aroma 6:23.

6, 7. Kodi Yesu ni wanchito wa mtundu wanji?

6 Motengela Atate wake, Yesu nayenso amakonda kugwila nchito. Asanabwele pa dziko lapansi, Yesu anali “mmisili wa Mulungu,” potengako mbali m’kulenga zinthu zonse kumwamba na padziko lapansi. (Miyambo 8:22-31; Akolose 1:15-17) Ali pa dziko lapansi, Yesu anagwilabe nchito mwakhama. Monga mnyamata, anaphunzila nchito n’kukhala katswili pa zaukalipentala. Mwacionekele, anadziŵa kukhoma makapulosi, kupanga zitseko, matebulo, na mipando. Yesu anaiphunzila bwino nchito yake moti anadziŵika kuti “mmisili wamatabwa.”—Maliko 6:3.

7 Ngakhale n’telo, nchito yofunika kwambili kwa Yesu pa dziko lapansi inali kulalikila uthenga wabwino, na kuphunzitsa anthu za Yehova. Anali na zaka zitatu na hafu kuti atsilize utumiki wake. Ndipo anali kugwila nchito molimbika kucokela m’mamaŵa mpaka usiku. (Luka 21:37, 38; Yohane 3:2) Anali kuyenda mitunda ya makilomita ambili m’misewu yafumbi, akumalalikila uthenga wabwino kwa anthu ambili.—Luka 8:1.

8, 9. N’cifukwa ciani Yesu anali kupeza cimwemwe m’nchito yake?

8 Kwa Yesu, kugwila nchito ya Mulungu kunali monga cakudya cake. Nchito imeneyi inam’patsa nyonga na mphamvu. Ndipo masiku ena, Yesu anali kugwila nchito cakuti sanali kupeza ngakhale mpata wakuti adye. (Yohane 4:31-38) Anaseŵenzetsa mpata uliwonse kuti athandize ena kuphunzila za Atate wake. Ndiye cifukwa cake anakamba mawu aya kwa Yehova: “Ndakulemekezani padziko lapansi, popeza ndatsiliza kugwila nchito imene munandipatsa.”—Yohane 17:4.

9 Mwacionekele, Yehova na Yesu amalimbika pa nchito, ndipo amakondwela nayo na kukhutila nayo kwambili. Nafenso tifuna kutengelako kwa Mulungu, komanso ‘kutsatila [kwambili] m’mapazi a Yesu.’ (Aefeso 5:1; 1 Petulo 2:21) Ndiye cifukwa cake timakhala olimbika pa ciliconse cimene ticita.

KODI NCHITO YATHU TIYENELA KUIONA BWANJI?

10, 11. N’ciani cingathandize kukhala na maganizo olimbikitsa ponena za nchito yanu?

10 Monga anthu a Yehova, timagwila nchito molimbika kuti tizisamalile ife eni, komanso mabanja athu. Timafuna kukondwela nayo nchito yathu. Koma nthawi zina cingakhale covuta. Conco, kodi tingacite bwanji ngati nchito yathu sitikondwela nayo?

Kukhala na maganizo olimbikitsa kungathandize munthu kukondwela na nchito iliyonse

11 Muzikhala na maganizo olimbikitsa. Mwina sitingathe kusintha nchito, kapena kuculuka kwa nchito, koma tingasinthe maganizo athu. Kudziŵa zimene Yehova amafuna kwa ife kungathandize. Mwacitsanzo: Yehova amayembekezela mutu wa banja kupezela banja lake zofunikila. Paja Baibo imakambilatu kuti amene alephela kusamalila banja lake, ni “woipa kuposa munthu wosakhulupilila.” (1 Timoteyo 5:8) Ngati ndimwe mutu wa banja, muyenela kulimbikila kupezela banja lanu zofunikila. Kaya nchito yanu mumaikonda kapena ayi, dziŵani kuti posamalila banja lanu, mumakondweletsanso Yehova.

12. Kodi kugwila nchito molimbika komanso moona mtima, kumatipindulitsa bwanji?

12 Muzigwila nchito molimbika komanso moona mtima. Mukatelo, mudzayamba kukondwela nayo nchito yanu. (Miyambo 12:24; 22:29) Zili conco cifukwa bwana wanu adzakudalilani. Mabwana amafuna anchito oona mtima, cifukwa sakuba ndalama, katundu, kapena nthawi. (Aefeso 4:28) Ndipo coposa zonse, Yehova amaona kulimbika kwanu pa nchito, na kuona mtima kwanu. Conco, mumakhala na “cikumbumtima coona” podziŵa kuti mumakondweletsa Mulungu amene mumakonda.—Aheberi 13:18; Akolose 3:22-24.

13. Pali ubwino winanso uti ngati tigwila nchito yathu moona mtima?

13 Dziŵani kuti khalidwe lanu ku nchito lingabweletse citamando kwa Yehova. Ici n’cifukwa cinanso cokhalila okondwela na nchito yathu. (Tito 2:9, 10) Ndipo wanchito mnzanu angafune kuphunzila Baibo poona citsanzo canu cabwino.—Ŵelengani Miyambo 27:11; 1 Petulo 2:12.

KODI NIYENELA KUSANKHA NCHITO YANJI?

14-16. Kodi tifunika kuganizila ciani posankha nchito?

14 Baibo siinacite kundandalika nchito zimene Mkhristu angasankhe kapena kukana. Koma ili na mfundo zotithandiza kusankha nchito mwanzelu. (Miyambo 2:6) Pogwilitsila nchito mfundo za m’Baibo zimenezo, tingadzifunse mafunso otsatilawa.

Funani nchito yosawombana na miyezo ya Yehova

15 Kodi nchitoyi idzafuna kuti nizicita zinthu zimene Yehova amadana nazo? Tinaphunzila zinthu zimene Yehova amazonda, monga kuba na kunama. (Ekisodo 20:4; Machitidwe 15:29; Aefeso 4:28; Chivumbulutso 21:8) Conco, tisamale kuti tipewe nchito iliyonse yosemphana na miyezo ya Yehova.—Ŵelengani 1 Yohane 5:3.

16 Kodi nchitoyi imalimbikitsa zimene Yehova amaletsa? Mwacitsanzo, bwanji ngati mwapeza nchito yomanga chechi? Kumanga mwa iko kokha kulibe vuto. Koma imwe mudziŵa kuti Mulungu amadana na ziphunzitso zonama zimene zimaphunzitsidwa m’machechi. Conco, ngakhale kuti simungaphunzitseko ziphunzitso zimenezo, kodi kwa Yehova, mungakhale mulibe mlandu wocilikiza ziphunzitso zonyenga?—Chivumbulutso 18:4.

17. N’ciani cingatithandize kupanga zosankha zokondweletsa Mulungu?

17 Pogwilitsila nchito mfundo zaumulungu, tingakhale mtundu wa anthu ofotokozedwa pa Aheberi 5:14, “amene pogwilitsa nchito mphamvu zawo za kuzindikila, aphunzitsa mphamvuzo kusiyanitsa coyenela ndi cosayenela.” Ni bwino kudzifunsa kuti: ‘Nikangena nchito imeneyi, kodi ningakhumudwitse ena? Kodi idzafuna kuti nisiye mnzanga wa m’cikwati, komanso ana anga, kuti nikaseŵenzele kutali kwambili, ngakhale ku dziko lina? Kodi zimenezi zingawakhudze bwanji?’

TSIMIKIZILANI ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBILI

18. N’cifukwa ciani nthawi zina kungakhale kovuta kuika patsogolo kulambila kwathu?

18 Nthawi zina, cimakhala covuta kuika patsogolo kulambila Yehova ‘m’masiku otsiliza’ ano, ovuta kucita nawo. (2 Timoteyo 3:1) Kupeza nchito na kuisunga cingakhale cinthu covuta kwambili. Inde, tifunika kusamalila mabanja athu, komabe timadziŵa kuti tifunika kuika patsogolo kulambila kwathu. Tisalole zinthu zakuthupi kukhala zofunika maningi mu umoyo wathu. (1 Timoteyo 6:9, 10) Kodi tingatsimikizile bwanji zinthu zofunika kwambili, koma n’kusamalila bwino mabanja athu?—Afilipi 1:10.

19. Kodi kudalila Yehova kumatithandiza bwanji kulinganiza bwino zinthu pa nkhani ya nchito?

19 Dalilani Yehova na mtima wonse. (Ŵelengani Miyambo 3:5, 6.) Mulungu amadziŵa bwino zosoŵa zathu, ndipo amasamala kwambili za ife. (Salimo 37:25; 1 Petulo 5:7) Mawu ake amatiuza kuti: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutila ndi zimene muli nazo pa nthawiyo. Pakuti Mulungu anati: ‘Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.’” (Aheberi 13:5) Yehova sakondwela ngati nthawi zonse timada nkhawa na mmene tingasamalile mabanja athu. Mobweleza-bweleza, iye waonetsa kuti amatha kusamalila zosoŵa za anthu ake. (Mateyu 6:25-32) Kaya nchito yathu ikhale yotangwanitsa bwanji, tifunikabe kuŵelenga Mawu a Mulungu, kulalikila uthenga wabwino, komanso kupezeka ku misonkhano.—Mateyu 24:14; Aheberi 10:24, 25.

20. Kodi tingakhale bwanji na umoyo wosalila zambili?

20 Maso anu azilunjika pa cinthu cimodzi. (Ŵelengani Mateyu 6:22, 23.) Izi zitanthauza kukhala na umoyo wosalila zambili, kuti mulunjike maganizo pa kutumikila Yehova. Kungakhale kupanda nzelu ngati tilola ndalama, umoyo wofeŵa, kapena zipangizo zamakono, kukhala zofunika kuposa ubwenzi wathu na Mulungu. Conco, n’ciani cingatithandize kuika patsogolo zinthu zofunika? Tifunika kuyesetsa kupewa nkhongole. Ngati muli kale m’nkhongole, pezani njila yozicepetsela, kapena kuzibweza zonse. Ndipo ngati sitisamala, zinthu zakuthupi zingamatidyele nthawi na kutilemetsa kwambili, cakuti n’kulephela kupeza nthawi yopemphela, kuŵelenga, kapena kulalikila. M’malo molola zinthu zakuthupi kucolowanitsa umoyo wathu, kapena kuti kuutsamwitsa, tiyenela kukhala wokhutila na zinthu zofunikila kweni-kweni, monga ‘cakudya na zovala.’ (1 Timoteyo 6:8) Ndipo nthawi zonse, tiyenela kumaona mmene moyo wathu ukuyendela, pofuna kutumikila Yehova mokwanila.

21. N’cifukwa ciani tiyenela kuona cimene timaika patsogolo mu umoyo wathu?

21 Ikani patsogolo zinthu zofunikila. Tiyeni tigwilitsile nchito mwanzelu nthawi yathu, nyonga, na zinthu zakuthupi. Ngati sitisamala, zinthu zosafunikila koposa, monga maphunzilo na ndalama, zingatidyele nthawi yofunika kwambili. Yesu anati: “Pitilizani kufuna-funa Ufumu coyamba.” (Mateyu 6:33) Zosankha zathu, zinthu zimene timakonda, umoyo wathu wa tsiku na tsiku, komanso zolinga zathu, zonse zimaonetsa cimene timaika patsogolo mu mtima mwathu.

NCHITO YOPAMBANA ZONSE KWA IFE

22, 23. (a) Kodi kwa ife Akhristu, nchito yopambana zonse ni iti? (b) N’ciani cingatithandize kukondwela na nchito yathu?

22 Nchito yofunika koposa kwa ise, ni kutumikila Yehova, na kulalikila uthenga wabwino kwa ena. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Molingana na Yesu, timafuna kucita zonse zotheka m’nchito imeneyi. Ena akukila kumadela kumene alaliki ni ocepa. Ena akuphunzila citundu ca kwina kuti azitha kulalikila anthu a citundu cimeneco. Funsilani kwa anthu amene acita zimenezi, kuti akufotokozeleni mmene anakwanitsila. Adzakuuzani mmene apezela cimwemwe cowilikiza, komanso mapindu ambili.—Ŵelengani Miyambo 10:22.

Kutumikila Yehova ndiyo nchito yofunika koposa kwa ise

23 Masiku ano, ambili a ife timawononga maawazi ambili-mbili ku nchito, ndipo nthawi zina ku nchito zingapo, cabe kuti tipeze zofunikila zazikulu za banja lathu. Yehova amadziŵa zimenezi, ndipo amayamikila zonse zimene timacita posamalila mabanja athu. Conco, tiyeni tipitilize kutengela citsanzo ca Yehova na Yesu, pa nkhani ya kugwila nchito molimbika, zilibe kanthu kuti nchito yathu ni yabwanji. Ndipo tisaiŵale kuti nchito yopambana zonse, ni kutumikila Yehova, na kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Ndiyo ingatipatse cimwemwe ceni-ceni.