Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MUTU 3

Sankhani Mabwenzi Okonda Mulungu

Sankhani Mabwenzi Okonda Mulungu

“Munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu.”—MIYAMBO 13:20.

1-3. (a) Kodi tiphunzilapo ciani pa Miyambo 13:20? (b) N’cifukwa ciani tiyenela kusankha mabwenzi mwanzelu?

KODI munaonapo mmene mwana wakhanda amayang’anila makolo ake? Asanayambe na kukamba, amasunga zimene amaona na kumvela. Ndipo pamene akula, amayamba kutengela makolo ake. N’cifukwa cake ngakhale anthu akulu-akulu amayamba kuganiza, na kucita zinthu motengela anthu amene amaceza nawo kwambili.

2 Miyambo 13:20, imakamba kuti: “Munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu.” Mau akuti ‘kuyenda na munthu’ amatanthauzanso kusankha munthu womaceza naye kwambili. Kumeneku si kungoceza naye cabe munthuyo. Katswili wina wa Baibo anakamba kuti kuyenda na munthu kumatanthauzanso kumukonda komanso kumvana naye. Ise anthu timakonda kutengela zocita na maganizo a anthu amene timaceza nawo kwambili, maka-maka amene timakonda.

3 Mabwenzi athu akhoza kutithandiza kukhala na makhalidwe abwino, komanso akhoza kutiwononga. Miyambo 13:20 ipitiliza kuti: “Wocita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” Mu Ciheberi, “kucita zinthu” na munthu wina kumatanthauzanso “kuyenda ndi” munthuyo, kapena kuti kukhala naye paubwenzi. (Miyambo 22:24; Oweruza 14:20) Mabwenzi okonda Mulungu, adzatilimbikitsa kukhala okhulupilika kwa iye. Koma kuti tidziŵe kusankha mabwenzi mwanzelu, tiyeni tikambilane mtundu wa mabwenzi amene Yehova amasankha.

KODI MABWENZI A MULUNGU NDANI?

4. N’cifukwa ciani ni mwayi waukulu kukhala bwenzi la Mulungu? N’ciani cinapangitsa Yehova kuchula Abulahamu kuti “bwenzi langa”?

4 Yehova, Mfumu ya Cilengedwe Conse, amafuna kuti ise tikhale mabwenzi ake. Umenewu ni mwayi wosaneneka. Koma Yehova amasankha mabwenzi ake mosamala kwambili. Amasankha aja amene amamukonda, amenenso amamukhulupilila. Citsanzo ni Abulahamu. Iye anali wokonzeka kucita ciliconse cimene Mulungu angamuuze. Mobweleza-bweleza, Abulahamu anaonetsa kuti anali wokhulupilika komanso womvela. Anali wokonzeka ngakhale kupeleka nsembe mwana wake Isaki. Inde, iye anali na cikhulupililo cakuti “Mulungu ali ndi mphamvu zomuukitsa kwa akufa.” (Aheberi 11:17-19; Genesis 22:1, 2, 9-13) Abulahamu anali wokhulupilika ndiponso womvela, cakuti Yehova anamuchula “bwenzi langa.”—Yesaya 41:8; Yakobo 2:21-23.

5. Kodi Yehova amawaona bwanji anthu okhulupilika kwa iye?

5 Mabwenzi a Yehova amakhulupilika kwa iye kuposa kwa wina aliyense. Nayenso Yehova amaona mabwenzi ake kukhala a mtengo wapatali. (Ŵelengani 2 Samueli 22:26.) Iwo amakhulupilika kwa iye na kumumvela cifukwa com’konda. Baibo imakamba kuti Mulungu “amakonda anthu owongoka mtima,” amene amamumvela. (Miyambo 3:32) Yehova amaitanila mabwenzi ake kuti akhale alendo apadela mu “cihema” cake. Akuwapempha kuti azimulambila na kupemphela kwa iye nthawi iliyonse.—Salimo 15:1-5.

6. Tingaonetse bwanji kuti timamukonda Yesu?

6 Yesu anakamba kuti: “Ngati munthu amandikonda, adzasunga malamulo anga. Atate wanga adzamukonda.” (Yohane 14:23) Conco, kuti tikhale bwenzi la Yehova, tifunikila kukonda Yesu na kucita zimene amatiphunzitsa. Mwacitsanzo, timalabadila malangizo a Yesu akuti tilalikile uthenga wabwino na kupanga ophunzila. (Mateyu 28:19, 20; Yohane 14:15, 21) Cifukwa cakuti timamukonda Yesu, ‘timatsatila mapazi ake mosamala kwambili.’ (1 Petulo 2:21) Yehova amakondwela ngako akaona kuti timatengela citsanzo ca Mwana wake m’zokamba zathu, na zocita zathu zonse.

7. N’cifukwa ciani tiyenela kuonetsetsa kuti tasankha mabwenzi amene alinso mabwenzi a Yehova?

7 Mabwenzi a Yehova amakhala okhulupilika, omvela, komanso okonda Mwana wake. Kodi na ise timasankha mabwenzi aconco? Ngati mabwenzi anu amatengela citsanzo ca Yesu, ndipo amakonda kugwila nchito yophunzitsa ena za Ufumu wa Mulungu, ndiye kuti angakuthandizeni kukhala munthu wabwino, komanso wokhulupilika kwa Yehova.

KUTENGELA PHUNZILO PA ZITSANZO ZA M’BAIBO

8. N’ciani cimakukondweletsani pa ubwenzi wa Rute na Naomi?

8 M’Baibo, timaŵelenga za anthu osiyana-siyana amene anali paubwenzi wolimba, monga pakati pa Rute na mpongozi wake Naomi. Azimayi amenewa anacokela ku maiko osiyana, ndiponso anali amakulidwe osiyana kwambili. Komanso, Naomi anali wamkulu kwambili pa Rute. Ngakhale n’conco, iwo anakhala mabwenzi a pamtima, cifukwa onse aŵili anali okonda Yehova. Pamene Naomi anafuna kucoka ku dziko la Moabu kuti abwelele kwawo ku Isiraeli, ‘Rute anamuumililabe.” Iye anauza Naomi kuti: “Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.” (Rute 1:14, 16) Rute anali wabwino mtima kwambili kwa Naomi. Pamene anafika ku Isiraeli, Rute analimbika kugwila nchito kuti athandize bwenzi lake. Nayenso Naomi anali kum’konda kwambili Rute, ndipo anam’patsa uphungu wabwino kwambili. Rute anamvela. Cotulukapo cake, onse aŵili analandila madalitso oculuka.—Rute 3:6.

9. N’ciani cimakucititsani cidwi pa ubwenzi wa Davide na Yonatani?

9 Citsanzo cina ni ca Davide na Yonatani. Iwo anali mabwenzi a ponda apa m’pondepo, komanso okhulupilika kwa Yehova. Yonatani anali wamkulu pa Davide na zaka pafupi-fupi 30, komanso ndiye anali pamzele wokaloŵa ufumu mu Isiraeli. (1 Samueli 17:33; 31:2; 2 Samueli 5:4) Koma pamene iye anamvela kuti Yehova wasankha Davide kudzakhala mfumu, sanacite nsanje kapena kufuna kupikisana naye iyai. M’malo mwake, Yonatani anacita ciliconse cofunikila pokhalila kumbuyo Davide. Mwacitsanzo, pamene Davide anali paciopsezo, Yonatani anam’thandiza mwa kum’limbikitsa “kudalila Mulungu.” Ndipo anaika moyo wake paciswe cifukwa ca Davide. (1 Samueli 23:16, 17) Davide nayenso anali bwenzi lokhulupilika. Iye analonjeza kuti adzasamalila banja la Yonatani, ndipo anasunga lonjezo limenelo ngakhale Yonatani atamwalila.—1 Samueli 18:1; 20:15-17, 30-34; 2 Samueli 9:1-7.

10. Muphunzilapo ciani pa ubwenzi wa anyamata atatu aciheberi?

10 Sadirake, Mesake, na Abedinego, anali anyamata aciheberi, ndipo anali mabwenzi. Pamene anali acicepele, anacotsedwa ku mabanja awo n’kupelekedwa ku dziko lakutali. Kumeneko, anali kulimbikitsana wina na mnzake kuti akhalebe okhulupilika kwa Yehova. Pamene anakula, cikhulupililo cawo cinayesedwa pamene Mfumu Nebukadinezara anawalamula kuti alambile cifano cagolide. Koma Sadirake, Mesake, na Abedinego anakana kwa mtu wagalu kulambila cifano cimeneco, ndipo anauza mfumuyo kuti: “Ife sititumikila milungu yanu, ndipo sitilambila fano limene mwaimika.” Ngakhale pa ciyeso coyofya ngati cimeneci, mabwenzi atatu amenewa sanagwedezeke pa cikhulupililo cawo kwa Mulungu.—Danieli 1:1-17; 3:12, 16-28.

11. Kodi Paulo na Timoteyo anakhala bwanji mabwenzi abwino?

11 Pamene mtumwi Paulo anakumana na mnyamata Timoteyo, anaona kuti Timoteyo anali kukonda kwambili Yehova na mpingo wake. Conco, Paulo anaphunzitsa Timoteyo mmene angathandizile abale na alongo ku malo osiyana-siyana. (Machitidwe 16:1-8; 17:10-14) Timoteyo anagwila nchito molimbika, cakuti Paulo anati za iye: “Watumikila monga kapolo pamodzi ndi ine kupititsa patsogolo uthenga wabwino.” Paulo anadziŵa kuti Timoteyo ‘angawasamaliledi moona mtima’ abale na alongo. Pamene Paulo na Timoteyo analimbikila capamodzi kutumikila Yehova, anakhala mabwenzi apamtima.—Afilipi 2:20-22; 1 Akorinto 4:17.

MMENE TINGASANKHILE MABWENZI

12, 13. (a) N’cifukwa ciani tifunika kusamala posankha mabwenzi ngakhale mu mpingo? (b) Kodi mtumwi Paulo anapelekelanji cenjezo ili pa 1 Akorinto 15:33?

12 Mu mpingo, tingaphunzile zambili kwa abale na alongo, komanso tingathandizane wina na mnzake kuti tikhalebe okhulupilika. (Ŵelengani Aroma 1:11, 12.) Ngakhale n’conco, tifunikabe kusamala posankha mabwenzi apamtima olo mu mpingo. Pali abale na alongo abwino kwambili ocokela m’mitundu yosiyana-siyana, komanso amakulidwe osiyana-siyana. Ena ni acatsopano, pamene ena atumikila Yehova kwa zaka zambili. Pamatenga nthawi kuti munthu akulitse ubwenzi wake na Yehova, monga mmene pamatengela nthawi kuti cipatso cikhwime na kupsa. Conco, tifunikila kulezelana mtima, kukondana wina na mnzake, na kusankha mabwenzi mwanzelu.—Aroma 14:1; 15:1; Aheberi 5:12–6:3.

13 Nthawi zina pangabuke vuto lalikulu mu mpingo, ndipo tingafunikile kukhala wosamala kwambili. Mwina m’bale kapena mlongo amacita zinthu zimene Baibo imaletsa. Olo kapena munthu wina ali na mzimu wokonda kuŵilingula umene ungawononge mpingo. Zimenezi zikacitika, tisadabwe kwambili, cifukwa ngakhale m’nthawi ya atumwi, nthawi zina panali kubuka mavuto mu mpingo. Ndiye cifukwa cake Paulo anacenjeza Akhristu a m’masiku amenewo kuti: “Musasoceletsedwe. Kugwilizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:12, 33) Paulo anacenjezanso Timoteyo kuti asamale posankha mabwenzi oceza nawo. Na ise masiku ano tifunika kusamala.—Ŵelengani 2 Timoteyo 2:20-22.

14. Cingacitike n’ciani ku ubale wathu na Yehova cifukwa ca mabwenzi amene timasankha?

14 Tifunika kuuteteza ubale wathu na Yehova. Ndiye cinthu copambana kwa ise. Mwa ici, sitifuna kukhala paubwenzi na munthu aliyense amene angawononge cikhulupililo cathu, na ubale wathu kwa Mulungu. Monga mmene thonje siingakhalilebe yoyela tikaiviika m’madzi adothi, ifenso sitingakhale na makhalidwe abwino ngati timaceza na anthu a makhalidwe oipa. Inde, tiyeni tisankhe mosamala mabwenzi oceza nawo.—1 Akorinto 5:6; 2 Atesalonika 3:6, 7, 14.

Mungapeze mabwenzi abwino okonda Yehova

15. Cofunika n’ciani kuti mupeze mabwenzi abwino mu mpingo?

15 Mu mpingo, mudzapeza anthu amene amakondadi Yehova. Iwo angakhale mabwenzi anu abwino ngako. (Salimo 133:1) Musasankhe cabe mabwenzi a msinkhu wanu, kapena ocokela ku mabanja amene mumalingana nawo m’njila zakuti-zakuti. Kumbukilani kuti Yonatani anali wamkulu kwambili pa Davide, ndipo Rute anali wamng’ono kwambili kwa Naomi. Tiyeni tilabadile langizo la m’Baibo lakuti: “Futukulani mtima wanu.” (2 Akorinto 6:13; ŵelengani 1 Petulo 2:17.) Conco, ngati mutengela citsanzo ca Yehova, anthu ambili adzafuna kukhala mabwenzi anu.

PAKAKHALA MAVUTO

16, 17. Ngati munthu wina watikhumudwitsa mu mpingo, tiyenela kupewa kucita ciani?

16 M’banja iliyonse anthu amakhala osiyana-siyana zibadwa, maganizo, na kacitidwe ka zinthu. Olo mu mpingo n’cimodzi-modzi. Kusiyana-siyana kumeneku kumapangitsa umoyo kukhala wokondweletsa, ndipo tingaphunzile zambili kwa wina na mnzake. Koma nthawi zina, cifukwa ca kusiyana-siyana kumeneku, tingayambe kuona abale na alongo athu molakwika na kuyamba kuipidwa nawo. Ndiponso nthawi zina tingafike pocita kukhumudwa nawo, ngakhale kukwiya kumene.—Miyambo 12:18.

17 Koma kodi tiyenela kulola mavuto amenewa kutilefula, kapena kuleka kuyanjana na mpingo? Iyai. Olo kuti munthu wina atikhumudwitse bwanji, sitifunika kuleka kuyanjana na mpingo. Si Yehova amene watikhumudwitsa. Iye anatipatsa moyo na zonse zofunikila. Ise tifunikila kumukonda na kukhala okhulupilika kwa iye. (Chivumbulutso 4:11) Mpingo ni mphatso yocokela kwa Yehova, ndipo umatithandiza kukhalabe olimba m’cikhulupililo. (Aheberi 13:17) Kodi ise tingaikane mphatso yake imeneyi cifukwa cakuti munthu wina watikhumudwitsa? Kutalitali!—Ŵelengani Salimo 119:165.

18. (a) N’ciani cingatithandize kuti tizimvana nawo abale na alongo athu? (b) N’cifukwa ciani tiyenela kumakhululukila ena?

18 Tiyenela kuwakonda abale na alongo athu, na kumvelana nawo. Yehova sayembekezela munthu aliyense kucita zinthu mwangwilo, ifenso sitiyenela kutelo. (Miyambo 17:9; 1 Petulo 4:8) Tonse timalakwitsa, koma cikondi n’cimene cidzatithandiza “kukhululukilana ndi mtima wonse.” (Akolose 3:13) Cifukwa ca cikondi, tidzapewa kukulitsa nkhani zing’ono-zing’ono kukhala civuto cacikulu. N’zoona kuti munthu akatikhumudwitsa, cimakhala covuta kungoiŵalako. N’capafupi kukwiya na kusungila mnzathu cakukhosi. Koma vuto n’lakuti amavutika ndise amene, posoŵa cimwemwe cifukwa ca mkwiyo umene ukutukusila mu mtima mwathu. Koma ngati tim’khululukila amene watilakwila, timasunga mtendele m’maganizo mwathu, mgwilizano mu mpingo, ndipo coposa zonse, ubwenzi wabwino na Yehova.—Mateyu 6:14, 15; Luka 17:3, 4; Aroma 14:19.

MUNTHU WINA AKACOTSEDWA MU MPINGO

19. Ni liti pamene tiyenela kuleka kuyanjana na munthu mu mpingo?

19 Ngati anthu amakondana m’banja, aliyense amacita zinthu zokondweletsa anzake. Koma tiyeni tiyelekeze kuti wina m’banja wayamba kusamvela. Aliyense wayesa-yesa kum’thandiza, koma iye safuna zimenezo. Potsilizila pake, iye angadzicokele yekha panyumba, kapena atate ake olo wina womusunga, angamucotse panyumba. N’cimodzi-modzi na mu mpingo. Munthu angayambe kucita zinthu zokhumudwitsa Yehova na kusokoneza mpingo. Iye angakane cithandizo ciliconse, na kuonetselatu mwa zocita zake kuti safunanso kukhala mu mpingo. Pothela pake, angadzicokele yekha mu mpingo, kapena angacotsedwe. Izi zikacitika, Baibo siipita m’mbali. Imakambilatu kuti “muleke kuyanjana” naye. (Ŵelengani 1 Akorinto 5:11-13; 2 Yohane 9-11) Ici cingakhale covuta ngati munthu ameneyo ni mnzathu kapena m’bululu wathu. Koma apa m’pamene cikhulupililo cathu kwa Yehova cifunika kukhala colimba kuposa cikondi cathu kwa wina aliyense.—Onani Mfundo ya Kumapeto 8.

20, 21. (a) N’cifukwa ninji makonzedwe ocotsa munthu mu mpingo ni acikondi? (b) N’cifukwa ciani tiyenela kusamala posankha mabwenzi?

20 Makonzedwe a kucotsa munthu mu mpingo amaonetsa cikondi ca Yehova. Mpingo umatetezedwa kwa anthu osalemekeza malamulo a Yehova. (1 Akorinto 5:7; Aheberi 12:15, 16) Ngati ticilikiza makonzedwe amenewa, na ise timaonetsa mmene timakondela dzina la Yehova loyela, malamulo ake apamwamba, na Yehova amene. (1 Petulo 1:15, 16) Ndiponso, makonzedwe ocotsa munthu amaonetsanso cikondi kwa uyo amene wacotsedwa. Cilango camphamvu cimeneci cingam’thandize kuzindikila kuti cimene anacita n’colakwa, ndipo afunika kusintha. Ambili amene anacotsedwa kumbuyoku anabwelela kwa Yehova, ndipo mpingo unawalandila na manja aŵili.—Aheberi 12:11.

21 Kaya mabwenzi athu ni abwino kapena ayi, makhalidwe awo adzatiyambukila. Conco, tiyenela kusankha mabwenzi mosamala. Ngati timakonda anthu amene Yehova amawakonda, tidzakhala na mabwenzi otithandiza kukhalabe okhulupilika kwa iye mpaka muyaya.