Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MUTU 6

Mmene Tingasankhile Zosangalatsa

Mmene Tingasankhile Zosangalatsa

“Citani zonse ku ulemelelo wa Mulungu.” —1 AKORINTO 10:31.

1, 2. N’cifukwa ciani tifunika kusamala posankha zosangalatsa?

YELEKEZANI kuti mufuna kuluma cipatso kuti mudye, koma muona kuti mbali ina ni yoola. Mungacite ciani? Kodi mungadye cabe? Kodi mungataye? Kapena mungajuŵeko mbali yoolayo kuti mudye yabwinoyo?

2 Zosangalatsa nazonso zili monga cipatso. Mbali zake zina n’zabwino. Koma zambili n’zaciwelewele, zaciwawa, kapena zamizimu. Conco posankha zosangalatsa, kodi mumati: “Cili kwa ine kusankha zilizonse zimene nifuna”? Kapena mumati: “Zosangalatsa zonse n’zoipa”? Olo kapena mumasamala kupewa zoipa na kusankha zabwino?

3. Kodi tiyenela kuganizila ciani posankha zosangalatsa?

3 Tonse timafuna kusangulukako kapena kusangalalako. Ndiye cifukwa cake tiyenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi zosangalatsa zimene ningasankhe zidzakhudza bwanji ubale wanga na Yehova?’

“CITANI ZONSE KU ULEMELELO WA MULUNGU”

4. Ni mfundo iti ya m’Baibo imene ingatithandize kusankha bwino zosangalatsa?

4 Tikadzipatulila kwa Yehova, timam’lonjeza kuti tidzaseŵenzetsa moyo wathu kum’tumikila. (Ŵelengani Mlaliki 5:4.) Timalonjeza kuti tidzacita “zonse ku ulemelelo wa Mulungu.” (1 Akorinto 10:31) Izi zitanthauza kuti timakhalabe odzipatulila kwa Mulungu olo pamene tikupumula kapena kusangalala. Osati cabe pamene tili ku misonkhano kapena mu ulaliki.

5. Kodi Yehova amalandila kulambila kwa bwanji?

5 Ciliconse cimene timacita mu umoyo cimakhudza kulambila kwathu Yehova. Paulo anaunika mfundoyi pamene anati: “Mupeleke matupi anu ngati nsembe yamoyo, yoyela ndi yovomelezeka kwa Mulungu.” (Aroma 12:1) Yesu anati: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, maganizo ako onse ndi mphamvu zako zonse.” (Maliko 12:30) Nthawi zonse, timafuna kupatsa Yehova zabwino koposa. Aisiraeli akale popeleka nsembe kwa Yehova, anafunikila kupeleka nyama za thanzi labwino. Mulungu sanali kulandila nyama yokhala na cilema. (Levitiko 22:18-20) Cimodzi-modzinso masiku ano. Yehova angakane kulambila kwathu. Motani?

6, 7. Kodi zosangalatsa zingakhudze bwanji kulambila kwathu Yehova?

6 Yehova amatiuza kuti: “Mukhale oyela, cifukwa ine ndine woyela.” (1 Petulo 1:14-16; 2 Petulo 3:11) Yehova amangolandila kulambila kumene ni koyela, kosadetsedwa. (Deuteronomo 15:21) Koma sikungakhale koyela ngati ticita zinthu zimene Yehova amanyansidwa nazo, monga zaciwelewele, ciwawa, olo zamizimu. (Aroma 6:12-14; 8:13) Komanso, Yehova amakhumudwa ngati tisangalala na zinthu zimenezi. Pa cifukwa cimeneci, kulambila kwathu kungakhale kodetsedwa komanso kosalandilika kwa Yehova. Ndipo zingawononge ubale wathu na iye.

7 Ndiye tingasankhe bwanji mwanzelu zosangalatsa? Ni mfundo ziti zimene zingatithandize kusiyanitsa zosangalatsa zabwino na zoipa?

MUZIDANA NAZO ZOIPA

8, 9. Ni zosangalatsa ziti zimene timapewa? Cifukwa?

8 Zosangalatsa zilipo zambili-mbili masiku ano. Zina n’zololeka kwa Akhristu, koma zambili n’zosaloleka. Conco, tiyeni tiyambe na kukambilana zosangalatsa zimene tiyenela kupewa.

9 Mafilimu ambili, mawebusaiti, zimene amatambitsa pa TV, magemu apavidiyo, na nyimbo, n’zaciwelewele, zaciwawa, kapena zamizimu. Zinthu zoipa zimenezi amazitambitsa m’njila yoonetsa kuti n’zabwino komanso zokondweletsa. Koma Akhristu sapusitsika. Amapewa zosangalatsa zilizonse zosemphana na miyezo ya Yehova. (Machitidwe 15:28, 29; 1 Akorinto 6:9, 10) Tikapewa zosangalatsa zimenezi, timaonetsa Yehova kuti zoipa timadana nazo.—Salimo 34:14; Aroma 12:9.

10. Koti cingatsatilepo n’ciani ngati timasankha zosangalatsa zoipa?

10 Koma alipo anthu ena amene amaona kuti zosangalatsa zaciwawa, zaciwelewele, kapena zamizimu, zilibe vuto. Amati: ‘Nanga vuto lili pati? N’tambako cabe, siningacite zimenezi.’ Ngati timaganizo conco, timadzipusitsa tekha. Baibo imati: “Mtima ndi wonyenga kwambili kuposa cina ciliconse ndipo ungathe kucita cina ciliconse coipa.” (Yeremiya 17:9) Ngati tilola zinthu zimene Yehova amadana nazo kutisangalatsa, kodi tingakambe kuti timadana nazo? Tikamazitamba, pang’ono m’pang’ono zimayamba kuoneka kuti n’zabwino cabe. M’kupita kwa nthawi, cikumbumtima cathu cimayamba kufooka, na kuleka kutiŵeleŵesha kapena kutinong’oneza, inde kuticenjeza tikafuna kucita coipa.—Salimo 119:70; 1 Timoteyo 4:1, 2.

11. Kodi Agalatiya 6:7 ingatithandize bwanji kusankha bwino zosangalatsa?

11 Mawu a Mulungu amatiuza kuti: “Ciliconse cimene munthu wafesa, adzakololanso comweco.” (Agalatiya 6:7) Ni mfundo yosakanika. Ngati tisankha zosangalatsa zolakwika, m’kupita kwa nthawi tidzapezeka kuti tikucita zimenezo. Alipo ena amene anatengeka na zosangalatsa zaciwelewele, amene potsilizila pake anagweladi m’ciwelewele. Koma Yehova amatithandiza kusankha mwanzelu zosangalatsa.

TSATILANI MFUNDO ZA M’BAIBO POPANGA ZOSANKHA

12. N’ciani cingatithandize kusankha mwanzelu pa nkhani ya zosangalatsa?

12 Zosangalatsa zina n’zoonekelatu kuti Yehova amadana nazo, ndipo tiyenela kuzipewa. Koma bwanji ngati si zocita kuonekelatu? Yehova sanacite kutipatsa mndandanda wa zoyenela kapena zosayenela kutamba, kumvetsela, kapena kuŵelenga. Amafuna kuti tiziseŵenzetsa cikumbumtima cathu cophunzitsidwa Baibo. (Ŵelengani Agalatiya 6:5.) Yehova amatipatsa mfundo, inde zotiunikila mmene amaonela zinthu. Mfundo zimenezi ndiye zimaphunzitsa cikumbumtima cathu. Zimatithandiza “kuzindikila cifunilo ca Yehova,” kuti tipange zosankha zom’kondweletsa.—Aefeso 5:17.

Mfundo za m’Baibo zimatithandiza kusankha bwino zosangalatsa

13. N’cifukwa ciani Akhristu amasankha zosangalatsa zosiyana-siyana? Koma cofunika kwa Akhristu onse n’ciani?

13 Koma zosangalatsa zimene Mkhristu wina angakonde, wina sangazikonde. Cifukwa? Makonda timasiyana. Komanso, zimene wina angaone kuti zili bwino, wina angazione kuti n’zosayenela. Koma cofunika kwa Akhristu onse posankha zinthu, ni kutsatila mfundo za m’Baibo. (Afilipi 1:9) Zidzatithandiza kusankha zosangalatsa zololeka kwa Mulungu.—Salimo 119:11, 129; 1 Petulo 2:16.

14. (a) Kodi cofunika kukumbukila n’ciani ponena za mmene timaseŵenzetsela nthawi? (b) Nanga Paulo anapeleka cilangizo cotani?

14 Cina cofunika kuganizila ni nthawi imene timatayila pa zosangalatsa. Zimaonetsa kuti zosangalatsa n’zofunika motani kwa ise. Monga Akhristu, cinthu cofunika koposa mu umoyo wathu ni kutumikila Yehova. (Ŵelengani Mateyu 6:33.) Koma mosadziŵa, tingalole zosangalatsa kumatilanda nthawi pang’ono-pang’ono. Paulo analangiza Akhristu kuti: “Samalani kwambili kuti mmene mukuyendela si monga anthu opanda nzelu, koma ngati anzelu. Muzigwilitsa nchito bwino nthawi yanu.” (Aefeso 5:15, 16) Inde, tifunika kumaika malile pa nthawi imene tiwonongela pa zosangalatsa. Nthawi zonse, tizionetsetsa kuti timaika patsogolo kutumikila Yehova mu umoyo wathu.—Afilipi 1:10.

15. Kodi tingadziteteze bwanji ku zosangalata zimene zingawononge ubale wathu na Yehova?

15 Mwacidziŵikile, tifunika kupewa zosangalatsa zoonekelatu kuti Yehova amadana nazo. Koma bwanji tikangozikaikila? Kodi nazonso tifunika kusamala nazo? Ganizilani izi. Ngati munali kuyenda pamwamba pa phili losongoka, kodi mungamafendele kumbali kosondoka? Iyai. Ngati moyo wanu mumaukonda, muzingoyendela capakati. N’cimodzi-modzi na zosangalatsa zimene timasankha. Mawu a Mulungu amaticenjeza kuti: “Cotsa phazi lako pa zoipa.” (Miyambo 4:25-27) Inde, tifunika kupewelatu zosangalatsa zodziŵikilatu kuti n’zoipa. Komanso, ngakhale zija zimene tiziganizila kuti zingawononge ubwenzi wathu na Yehova.

KUDZIŴA KAONEDWE KA YEHOVA

16. (a) Kodi zina mwa zinthu zimene Yehova amadana nazo n’ziti? (b) Nanga timaonetsa bwanji kuti timadana na zinthu zimene Yehova amadana nazo?

16 Wamasalimo analemba kuti: “Inu okonda Yehova danani naco coipa.” (Salimo 97:10) Baibo imatiuza mmene Yehova amaganizila na mmene amamvelela. Ni bwino kumadzifunsa kuti, ‘Kodi zimene nimaphunzila zinganithandize bwanji kuona zinthu mmene Yehova amazionela?’ Mwacitsanzo, timaphunzila kuti Yehova amadana na “lilime lonama, manja okhetsa magazi a anthu osalakwa, mtima wokonzela ena ziwembu, mapazi othamangila kukacita zoipa.” (Miyambo 6:16-19) Timaphunzilanso kuti tiyenela kupewa “dama, . . . kupembedza mafano, kucita zamizimu, . . . nsanje, kupsa mtima, . . . kaduka, kumwa mwaucidakwa, maphwando aphokoso, ndi zina zotelo.” (Agalatiya 5:19-21) Kodi mukuona mmene mfundo za m’Baibo zimenezi zingakuthandizileni kusankha bwino zosangalatsa? Timafuna kutsatila miyezo ya Yehova m’mbali zonse za moyo wathu, kaya tili na anthu ena olo tili kwa tekha. (2 Akorinto 3:18) Ndipo zimene timasankha pamene tili patekha n’zimene zimaonetsadi mtundu wa munthu amene tili.—Salimo 11:4; 16:8.

17. Tikalibe kusankha zosangalatsa, tifunika kudzifunsa mafunso ati?

17 Conco posankha zosangalatsa, dzifunseni kuti: ‘Kodi cosankha canga cidzakhudza bwanji ubale wanga na Yehova? Nanga cikumbumtima canga cidzamvela bwanji?’ Tiyeni tionenso mfundo zina zotithandiza posankha zosangalatsa.

18, 19. (a) Kodi Paulo anapeleka malangizo anji kwa Akhristu? (b) Ni mfundo ziti zimene zingatithandize kusankha bwino zosangalatsa?

18 Pamene tisankha zosangalatsa, tidziŵe kuti tikusankha zimene tifuna kudyetsa maganizo athu. Paulo analemba kuti: “Zinthu zilizonse zoona, zilizonse zofunika kwambili, zilizonse zolungama, zilizonse zoyela, zilizonse zacikondi, zilizonse zoyamikilika, khalidwe labwino lililonse, ndi ciliconse cotamandika, pitilizani kuganizila zimenezi.” (Afilipi 4:8) Pamene tidyetsa maganizo athu zinthu zabwino ngati zimenezi, tingakambe kuti: “Mawu a pakamwa panga ndi kusinkha-sinkha kwa mtima wanga, zikukondweletseni, inu Yehova.”—Salimo 19:14.

19 Ndiye dzifunseni kuti: ‘Kodi maganizo anga nimawadyetsa ciani? Pambuyo potamba filimu inayake, kodi imanisiya na maganizo abwino, otsitsimula? Kodi nimakhala na mtendele wa maganizo, na cikumbumtima coyela? (Aefeso 5:5; 1 Timoteyo 1:5, 19) Kodi nimamasuka kupemphela kwa Yehova? Kapena zimanivuta? Kodi cosangalatsaco canisiya nikuganizila za ciwawa kapena zaciwelewele? (Mateyu 12:33; Maliko 7:20-23) Kodi zosangalatsa zimene nimasankha sizikunipangitsa ‘kutengela nzelu za nthawi ino’?’ (Aroma 12:2) Kuyankha mafunso amenewa moona mtima, kungatithandize kuona zofunika kusintha, kuti ubale wathu na Yehova ukhalebe wolimba. Monga anacitila wamasalimo, tizipemphela kuti: “Cititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.” *Salimo 119:37.

ZOSANKHA ZATHU ZIMAKHUDZA ANTHU ENA

20, 21. N’cifukwa ciani tifunika kuganizila ena posankha zosangalatsa?

20 Nayi mfundo ina yofunika kuikumbukila: “Zinthu zonse ndi zololeka, koma si zonse zimene zili zolimbikitsa. Aliyense asamangodzifunila zopindulitsa iye yekha basi, koma zopindulitsanso wina.” (1 Akorinto 10:23, 24) Pokhala na ufulu wocita cinacake, sikuti basi tiyenela kucicita iyai. Tiyenela kuganiza mosamala za mmene cosankha cathu cingakhudzile abale na alongo athu.

21 Sikuti tonse tili na zikumbumtima zolingana iyai. Mwacitsanzo, cikumbumtima canu cingakuloleni kutamba pulogilamu inayake pa TV. Koma bwanji ukadziŵa kuti pulogilamu imeneyo ikuvutitsa cikumbumtima ca mlongo olo m’bale wanu? Mungacite bwanji? Ngakhale muli na ufulu woitamba, mungangoleka. Cifukwa? Eya, cifukwa simufuna ‘kucimwila abale anu,’ kapena ‘kucimwila Khristu.’ (1 Akorinto 8:12) Sitifuna kucita ciliconse cokhumudwitsa Mkhristu mnzathu.—Aroma 14:1; 15:1; 1 Akorinto 10:32.

22. Tingaonetse bwanji kuti timaganizila ena pa zosankha zimene Akhristu anzathu amapanga?

22 Koma bwanji ngati cikumbumtima canu sicikulolani kutamba, kuŵelenga, kapena kucita cinthu cina cimene wina alibe naco vuto? Cifukwa mumalemekeza na kukonda m’bale wanu, simungamuletse cifukwa ca cikumbumtima canu. Munthu woyendetsa motoka amadziŵa kuti ena amathamanga kuposa iye, ndipo ena amayendetsa pang’ono-pang’ono, koma onse ni madilaiva abwino. Mofananamo, imwe na m’bale wanuyo mumakonkha mfundo za m’Baibo. Mumangosiyanako cabe mtundu wa zosangalatsa zimene muona kuti n’zabwino.—Mlaliki 7:16; Afilipi 4:5.

23. N’ciani cingatithandize kusankha bwino zosangalatsa?

23 Conco, n’ciani cingatithandize kusankha bwino zosangalatsa? Ngati timvelela cikumbumtima cathu cophunzitsidwa bwino mfundo za m’Baibo, ndipo timadeladi nkhawa abale na alongo athu, tidzasankha mwanzelu. Ndipo tikatelo, tidzakondwela kuti tikucita “zonse ku ulemelelo wa Mulungu.”

^ ndime 19 Mfundo zina zothandiza kusankha bwino zosangalatsa tingazipeze pa Miyambo 3:31; 13:20; Aefeso 5:3, 4; komanso Akolose 3:5, 8, 20.