Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MUTU 9

“Thaŵani Dama”

“Thaŵani Dama”

“Cititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, cilakolako ca kugonana, cikhumbo coipa, ndi kusilila kwa nsanje, kumene ndiko kulambila mafano.”—AKOLOSE 3:5.

1, 2. Kodi Balamu anacita ciani pofuna kupweteketsa anthu a Yehova?

MUNTHU woŵedza nsomba amapita pamalo amene adziŵa kuti angagwilepo mtundu wa nsomba zimene afuna. Amasankha nyambo yoika ku mbedza yake na kuponya pamadzi. Ndiyeno amakhala phee kuyembekezela. Ndipo nsomba ikadyela amati nthambo ija khwe! kuti mbedza ikoŵe m’kamwa mwa nsomba, kenako amaidonsa.

2 Anthu nawonso amagwilika cimodzi-modzi. Mwacitsanzo, Aisiraeli anali atayandikila kale Dziko Lolonjezedwa pamene anamanga msasa m’Cigwa ca Mowabu. Mfumu ya Mowabu inalonjeza Balamu ndalama zambili ngati angatembelele Aisiraeli. Potsilizila pake, Balamu anapeza njila yopangitsa Aisiraeli kudzibweletsela okha tembelelo. Iye anasankha nyambo yake mocenjela kwambili. Anatumiza atsikana acimowabu mu msasa wa Aisiraeli kuti akawakope.—Numeri 22:1-7; 31:15, 16; Chivumbulutso 2:14.

3. Kodi Aisiraeli anagwilika bwanji pa msampha wa Balamu?

3 Kodi nyambo ya Balamu inaseŵenza? Inde. Amuna aciisiraeli ambili-mbili anacita “ciwelewele ndi akazi a ku Mowabu.” Amunawo anayambanso kulambila milungu yonyenga, kuphatikizapo mulungu wonyansa wa zakugonana, Baala wa ku Peori. Cifukwa ca izi, Aisiraeli 24,000 anaphedwa pakhomo peni-peni pa Dziko Lolonjezedwa.—Numeri 25:1-9.

4. N’cifukwa ciani Aisiraeli masauzande onsewo anagwela m’zaciwelewele?

4 N’cifukwa ciani Aisiraeli ambili anagwela mu msampha wa Balamu? Cifukwa anali kungoganizila zofuna zawo zadyela, na kuiŵala zonse zimene Yehova anawacitila. Pa zifukwa zambili, Aisiraeli anafunika kukhala okhulupilika kwa Mulungu. Anali atawamasula mu ukapolo ku Iguputo, anawapatsa cakudya m’cipululu, mpaka kuwafikitsa motetezeka ku malile a Dziko Lolonjezedwa. (Aheberi 3:12) Koma n’zacisoni kuti iwo ananyengedwabe na zaciwelewele. M’pake kuti mtumwi Paulo anacenjeza kuti: “Tisamacite dama, mmene ena mwa iwo anacitila dama, n’kufa.”—1 Akorinto 10:8.

5, 6. Titengapo phunzilo lanji pa zimene zinacitika m’Cigwa ca Mowabu?

5 Dziko latsopano lili pafupi kwambili. Monga Aisiraeli aja, ifenso tili pakhomo pa Dziko Lolonjezedwa, titelo kukamba kwake. (1 Akorinto 10:11) Masiku ano, anthu m’dziko amakondetsetsa zakugonana kuposa ngakhale Amowabu aja. Kukonda zakugonana kumeneku kungakhudzenso anthu a Yehova. Ndipo pa misampha yonse ya Mdyelekezi, ciwelewele ndiye namba wani.—Numeri 25:6, 14; 2 Akorinto 2:11; Yuda 4.

6 Dzifunseni kuti, ‘Kodi ningasankhe citi, kusangalala na cinthu comveka bwino koma cakanthawi cabe, kapena umoyo wa cimwemwe camuyaya m’dziko latsopano?’ Kodi si kwanzelu kumvela lamulo la Yehova lakuti: “Thaŵani dama”?—1 Akorinto 6:18.

KODI DAMA, KAPENA CIWELEWELE, N’CIANI?

7, 8. Kodi dama kapena kuti ciwelewele n’ciani? Ndipo n’cifukwa ciani ili nkhani yoopsa?

7 Anthu ambili masiku ano saŵelengela malamulo a Mulungu pa nkhani za kugonana. M’Baibo, mawu akuti “dama” kapena ciwelewele, amatanthauza kugonana kwa anthu amene si okwatilana mwalamulo. Dama limaphatikizaponso mathanyula (kugonana kwa anthu olingana ziwalo), komanso kugonana na nyama. Zaciwelewele zimaphatikizaponso kugonana m’kamwa, kugonana kumbuyo, kapena kusisitana ziwalo zogonanila. Olo kuti kungakhale kocititsa manyazi kukambilana nkhaniyi, kuimvetsetsa bwino n’kofunikila kuti tipewe zimene Mulungu amadana nazo.—Onani Mfundo ya Kumapeto 23.

8 Baibo imamveketsa bwino kuti ngati munthu acita ciwelewele koma osalapa, afunika kucotsedwa mu mpingo. (1 Akorinto 6:9; Chivumbulutso 22:15) Komanso, munthu wocita zaciwelewele amadzitayila ulemu, ndipo anthu amaleka kum’khulupilila. Ciwelewele nthawi zonse cimaitana mavuto. Zotulukapo zimakhala cikumbumtima cokuvutitsa, kutenga mimba, mavuto m’banja, matenda, ngakhale imfa imene. (Ŵelengani Agalatiya 6:7, 8.) Kuganizila modekha zotsatilapo za ciwelewele, munthu wanzelu sangafune kucita ciwelewele. Vuto n’lakuti munthu amangoganizila za kukhutilitsa cilakolako cake. Ndipo kambili sitepu yoyamba imakhala kutamba zamalisece.

SITEPU YOYAMBA—ZAMALISECE

9. N’cifukwa ciani zamalisece n’zoopsa?

9 Colinga ca zamalisece ni kuutsa cilakolako ca kugonana. Masiku ano, zamalisece zili paliponse—m’magazini, m’mabuku, m’nyimbo, m’mapulogilamu a pa TV, ngakhalenso pa Intaneti. Anthu ambili amaona kuti zamalisece zilibe vuto. Koma kukamba zoona, n’zoopsa kwambili. Zingapangitse munthu kukondetsetsa kwambili kugonana, na kuyamba kulaka-laka njila zacilendo za kugonana. Munthu akayamba kutamba zamalisece, zotsatilapo zake zimakhala kuyamba cizolowezi codzipukusa malisece, mavuto m’banja, ngakhale cisudzulo.—Aroma 1:24-27; Aefeso 4:19; onani Mfundo ya Kumapeto 24.

Tiyenela kukhala osamala poseŵenzetsa Intaneti

10. Kodi mfundo ya pa Yakobo 1:14, 15 ingatithandize bwanji kupewa zaciwelewele?

10 Tifunika kudziŵa bwino mmene zaciwelewele zingatikopele. Onani cenjezo iyi yopezeka pa Yakobo 1:14, 15, yakuti: “Munthu aliyense amayesedwa mwa kukopedwa ndi kukodwa m’cilakolako cake. Ndiye cilakolako cikatenga pakati, cimabala chimo. Nalonso chimo likakwanilitsidwa, limabweletsa imfa.” Conco, malingalilo olakwika akabwela m’maganizo mwanu, acotseni nthawi imeneyo. Ngati mwaona zithunzi zoutsa cilakolako, cotsankoni maso! Zimyani kompyuta, kapena sinthani chanelo! Musalole zilakolako zoipa kuloŵa mu mtima mwanu. Cifukwa zingakhale zamphamvu cakuti mungalephele kuzilamulila.—Ŵelengani Mateyu 5:29, 30.

11. Kodi Yehova angatithandize bwanji ngati takhala na maganizo olakwika?

11 Yehova amatidziŵa bwino kwambili kuposa mmene timadzidziŵila ife eni. Conco, amakumvetsa bwino kupanda ungwilo kwathu. Koma amadziŵanso kuti tikhoza kuzigonjetsa zilakolako zoipa. N’cifukwa cake akutiuza kuti: “Conco cititsani ziwalo za thupi lanu padziko lapansi kukhala zakufa ku dama, zinthu zodetsa, cilakolako ca kugonana, cikhumbo coipa, ndi kusilila kwa nsanje, kumene ndiko kulambila mafano.” (Akolose 3:5) Ngakhale kuti zingakhale zovutilapo, Yehova amaleza nafe mtima, ndipo amatithandiza. (Salimo 68:19) M’bale wina wacicepele anagwela m’cizolowezi cotamba zamalisece na kudzipukusa malisece. Anzake ku sukulu ndiwo anali kumuuza kuti kucita zimenezi ndiye kukula. Koma iye anati: “Zinawononga cikumbumtima canga, cakuti n’nayamba zaciwelewele.” Iye anazindikila kuti afunika kulamulila cilakolako cake, ndipo mothandizidwa na Yehova, anathetsa cizolowezi coipa cimeneco. Ngati imwenso m’makhala na maganizo a zaciwelewele, pemphani kwa Yehova “mphamvu yoposa yacibadwa,” kuti maganizo anu azikhala oyela.—2 Akorinto 4:7; 1 Akorinto 9:27.

12. N’cifukwa ciani tifunika ‘kuuteteza mtima wathu’?

12 Solomo analemba kuti: “Uteteze mtima wako kuposa zonse zimene ziyenela kutetezedwa, pakuti mu mtimamo ndiye muli akasupe a moyo.” (Miyambo 4:23) “Mtima” ni munthu wathu wamkati, amene Yehova amayang’ana. Zimene timayang’ana zimatikhudza kwambili. Yobu wokhulupilikayo anati: “Ndacita pangano ndi maso anga. Conco ndingayang’anitsitse bwanji namwali?” (Yobu 31:1) Mofanana na Yobu, tifunika kudziletsa pa zimene timayang’ana na kuganiza. Komanso mofanana na wamasalimo, tizipempha kuti: “Cititsani maso anga kuti asaone zinthu zopanda pake.”—Salimo 119:37.

DINA ANASANKHA MABWENZI OLAKWIKA

13. Kodi Dina anasankha mabwenzi abwanji?

13 Mabwenzi athu akhoza kutithandiza kapena kutiwononga. Ngati musankha mabwenzi otsatila miyezo ya Mulungu, angakuthandizeni kucita cimodzi-modzi. (Miyambo 13:20; ŵelengani 1 Akorinto 15:33.) Zimene zinacitikila Dina zimaonetsa kufunika kosankha bwino mabwenzi. Iye anali mmodzi wa ana aakazi a Yakobo. Conco anakulila m’banja lolambila Yehova. Dina sanali wa makhalidwe oipa ayi. Koma anayamba kuceza na atsikana acikanani, amene sanali kulambila Yehova. Akanani anali na maganizo osiyana kwambili na anthu a Mulungu pa nkhani ya zakugonana, ndipo anali odziŵika na zaciwelewele. (Levitiko 18:6-25) Pamene Dina anali kuceza na atsikana anzake, anakumana na Sekemu mnyamata wacikanani, amene anatengeka na Dina. Mnyamatayu anali “wolemekezeka kwambili” m’banja mwawo. Koma iye sanali kukonda Yehova.—Genesis 34:18, 19.

14. N’ciani cinacitika kwa Dina?

14 Kwa Sekemu, zimene anacitazo zinali zoyenela komanso zacibadwa. Cifukwa cokhumbila Dina, “anamutenga n’kumugwilila.” (Ŵelengani Genesis 34:1-4.) Vuto limeneli linaputa mavuto ena amene anabweletsa tsoka pa Dina, na banja lawo lonse.—Genesis 34:7, 25-31; Agalatiya 6:7, 8.

15, 16. Kodi tingakhale bwanji anzelu?

15 Kuti tidziŵe ubwino wa miyezo ya Yehova, sitifunikila kucita kulakwa coyamba monga Dina. “Munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu, koma wocita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” (Miyambo 13:20) Mukakhala wanzelu, ‘zocita zanu zonse zidzakuyendelani bwino,’ ndipo mudzapewa zoŵaŵa na zopweteka.—Miyambo 2:6-9; Salimo 1:1-3.

16 Tingakhale anthu anzelu ngati tiŵelenga Mawu a Mulungu, kupemphela kwa iye pofuna kupanga zosankha, na kutsatila malangizo ocokela kwa kapolo wokhulupilika ndi wanzelu. (Mateyu 24:45; Yakobo 1:5) Mudziŵa bwino kuti tonsefe ndife ofooka komanso opanda ungwilo. (Yeremiya 17:9) Koma kodi mungacite bwanji ngati wina wakucenjezani kuti mungagwele m’chimo la ciwelewele? Kodi mungakhumudwe, kapena mungayamikile modzicepetsa?—2 Mafumu 22:18, 19.

17. Fotokozani citsanzo ca mmene uphungu wa Mkhristu mnzathu ungatithandizile.

17 Tiyelekeze conco. Ku nchito kwa mlongo, mwamuna wina wayamba kum’citila zinthu zom’komela mtima. Tsiku lina am’pempha kuti akaceze naye kwina. Mwamunayo satumikila Yehova, koma ni wacifundo, wokomanso mtima kwambili. Mlongo wina aŵaona ali pamodzi, ndipo pambuyo pake acenjeza mlongo mnzakeyo. Kodi mlongo woyambayu adzacita bwanji? Kodi adzafuna kudzilungamitsa, kapena adzayamikila cenjezo limenelo? Mlongoyu amakonda Yehova, ndipo amacita zoyenela. Koma ngati apitiliza kupita kokaceza na mwamuna uyu, kodi tingati ‘akuthaŵa dama,’ kapena ‘akudalila mtima wake’?—Miyambo 22:3; 28:26; Mateyu 6:13; 26:41.

TENGANI PHUNZILO KWA YOSEFE

18, 19. Fotokozani mmene Yosefe anathaŵila dama.

18 Ali mnyamata, Yosefe anali kapolo ku Iguputo. Tsiku na tsiku, mkazi wa mbuye wake anali kum’nyengelela kuti agone naye. Koma Yosefe anadziŵa kuti kucita zimenezo n’kulakwa. Yosefe anali kukonda Yehova kwambili, cakuti sanafune kum’khumudwitsa. Conco, anapitiliza kukana. Koma popeza anali kapolo, sakanatha kungocoka kwa mbuye wake. Tsiku lina pamene mkazi wa mbuye wake anayesa kum’kakamiza kuti agone naye, anathaŵila panja.—Ŵelengani Genesis 39:7-12.

19 Sembe kuti Yosefe anali kukonda kuganizila zaciwelewele, olo sembe mu mtima mwake anali kum’khumbila mzimayiyo, zikanacitika n’zina. Koma kwa Yosefe, panalibe cinthu cofunikila kuposa ubale wake na Yehova. N’cifukwa cake anauza mzimayiyo kuti: “Mbuye wanga . . . anaika ciliconse m’manja mwanga kupatulapo inuyo, cifukwa ndinu mkazi wake. Ndiye ndingacitilenji coipa cacikulu conci n’kucimwila Mulungu?”—Genesis 39:8, 9.

20. Tidziŵa bwanji kuti Yehova anali kukondwela naye Yosefe?

20 Olo kuti Yosefe anali kutali kwambili na kwawo, komanso acibale ake, nthawi zonse anali wokhulupilika kwa Mulungu. Ndipo Yehova anali kum’dalitsa. (Genesis 41:39-49) Kukhulupilika kwa Yosefe kunali kum’kondweletsa kwambili Yehova. (Miyambo 27:11) Nthawi zina kungakhale kovuta kupewa ciwelewele. Koma kumbukilani mawu aya: “Inu okonda Yehova danani naco coipa. Iye amateteza moyo wa anthu ake okhulupilika. Amawalanditsa m’manja mwa anthu oipa.”—Salimo 97:10.

21. Kodi m’bale wina wacicepele anatengela bwanji citsanzo ca Yosefe?

21 Tsiku na tsiku, anthu a Yehova amaonetsa kuti ‘amadana na coipa,’ na ‘kukonda cabwino.’ (Amosi 5:15) Kaya ndimwe a msinkhu wanji, mungakhale wokhulupilika kwa Yehova. M’bale wina wacicepele, cikhulupililo cake cinayesedwa ku sukulu. Mtsikana wina anamuuza kuti adzagona naye ngati angam’thandize masamu pa mayeso. Kodi m’baleyu anacita ciani? Anacita molingana na Yosefe. Iye anati: “Mosawaya-waya, n’namuuza kuti siningacite zimenezo. Pocita mokhulupilika, n’nadzisungilanso ulemu wanga.” Inde, ‘zosangalatsa zosakhalitsa’ zilizonse za ciwelewele, zimabweletsa mavuto na cisoni. (Aheberi 11:25) Koma kumvelela Yehova, nthawi zonse kumabweletsa cimwemwe cokhalitsa.—Miyambo 10:22.

LOLANI KUTI YEHOVA AKUTHANDIZENI

22, 23. Kodi Yehova angatithandize bwanji pamene tagwela m’chimo lalikulu?

22 Satana sadzaleka kutichela na msampha wa ciwelewele, ndipo zikhoza kukhaladi zovuta. Tonsefe maganizo olakwika amatibwelela nthawi zina. (Aroma 7:21-25) Koma Yehova amadziŵa zimenezi, ndipo amakumbukila kuti “ndife fumbi.” (Salimo 103:14) Koma bwanji ngati Mkhristu wacita chimo la ciwelewele? Kodi ndiye kuti basi watayikilatu? Iyai. Ngati munthuyo ni wolapa ca zoona, Yehova amam’khululukila. Mulungu ni “wokonzeka kukhululuka.”—Salimo 86:5; Yakobo 5:16; ŵelengani Miyambo 28:13.

23 Yehova anatipatsanso “mphatso za amuna”—inde, akulu amene amatisamalila mwacikondi. (Aefeso 4:8, 12; Yakobo 5:14, 15) Anatipatsa akulu kuti azitithandiza kukonzanso ubale wathu na Mulungu.—Miyambo 15:32.

GWILITSILANI NCHITO “NZELU”

24, 25. Kodi “nzelu” zingatithandize bwanji kupewa zaciwelewele?

24 Kuti tizipanga zosankha zabwino, tiyenela kumvetsetsa mmene malamulo a Yehova amatipindulitsila. Sitifuna kukhala monga mnyamata uja wa pa Miyambo 7:6-23. Pokhala “wopanda nzelu,” anagwidwa na nyambo ya ciwelewele. Kukhala wanzelu kumaposa kucenjela cabe. Tikakhala anzelu, timamvetsetsa maganizo a Mulungu, na kuyaseŵenzetsa mu umoyo wathu. Muzikumbukila mawu akuti: “Amene wapeza mtima wanzelu akukonda moyo wake. Wopitiliza kusonyeza kuzindikila amapeza zabwino.”—Miyambo 19:8.

25 Kodi mumakhulupilila na mtima wonse kuti miyezo ya Mulungu ni yolungama? Kodi mumakhulupililadi kuti ngati muitsatila mungakhaledi acimwemwe? (Salimo 19:7-10; Yesaya 48:17, 18) Ngati simuli wotsimikiza, ganizilani zabwino zonse zimene Yehova wakucitilani. “Talaŵani ndipo muone kuti Yehova ndi wabwino.” (Salimo 34:8) Mukatelo, mudzayamba kumukonda kwambili. Kondani zimene amakonda, na kuzonda zimene amazonda. Dzazani maganizo anu na malingalilo abwino—zinthu zilizonse zoona, zolungama, zoyela, zacikondi, ndiponso khalidwe labwino. (Afilipi 4:8, 9) Tingakhale monga Yosefe, amene anapindula na nzelu zocokela kwa Yehova.—Yesaya 64:8.

26. Kodi tidzakambilana ciani m’mitu yotsatila?

26 Kaya ndimwe mbeta kapena wokwatila, Yehova amafuna kuti mukhale na umoyo wacimwemwe. Mitu iŵili yokonkhapo, idzatiunikila mmene tingakhalile na cikwati copambana.