Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Zakumapeto

Zakumapeto

 1 MFUNDO

Malamulo a Mulungu ni ozikidwa pa mfundo zake. Mfundo zimenezo ni maziko a coonadi opezeka m’Baibo. Zimatithandiza kudziŵa maganizo a Mulungu na mmene amaonela zinthu. Mfundozo zimatithandiza kupanga zosankha zanzelu, komanso kucita zinthu zoyenela. Zimatithandiza maka-maka pa nkhani zimene Baibo siikambapo mwacindunji.

Mutu 1, ndime 8

 2 KUMVELA

Kumvela Yehova kutanthauza kukhala ofunitsitsa kucita zimene amatiuza. Yehova amafuna kuti tizimumvela cifukwa cakuti timamukonda. (1 Yohane 5:3) Ngati timakonda Mulungu na kum’khulupilila, timatsatila malangizo ake m’zocitika zilizonse. Timamumvela olo pamene zingakhale zovuta kwa ise. N’cinthu canzelu kumvela Yehova, cifukwa amatiphunzitsa mokhalila na umoyo wabwino. Komanso, watilonjeza madalitso ambili kutsogolo.—Yesaya 48:17.

Mutu 1, ndime 10

 3 UFULU WOSANKHA ZOCITA

Yehova anapatsa munthu aliyense ufulu wosankha zocita, kapena kupanga zosankha. Sanatipange monga makina amaloboti. (Deuteronomo 30:19; Yoswa 24:15) Timaseŵenzetsa ufulu wathu umenewo kupanga zosankha zabwino. Koma tikaleka kusamala, tingapange zosankha zoipa. Conco, mwa ufulu umenewu, tiyenela kusankha ife eni kukhala wokhulupilika kwa Yehova, na kuonetsa kuti timam’kondadi, kapena ayi.

Mutu 1, ndime 12

 4 MIYEZO YA MAKHALIDWE

Yehova ndiye amakhazikitsa miyezo, kapena kuti malangizo, pa makhalidwe kapena zocita. Miyezo imeneyo imapezeka m’Baibo, ndipo timaphunzilamo za mmene ingatithandizile kukhala na umoyo wabwino. (Miyambo 6:16-19; 1 Akorinto 6:9-11) Malangizo amenewo amatithandiza kudziŵa zimene Mulungu amaziona kuti n’zabwino kapena zoipa. Amatiphunzitsanso za kukondana, kukomelana mtima, komanso kupanga zosankha zanzelu. Olo kuti makhalidwe m’dziko akuloŵela-loŵela pansi, miyezo ya Yehova pa makhalidwe siisintha. (Deuteronomo 32:4-6; Malaki 3:6) Kutsatila miyezo imeneyo kumatiteteza kuti tisavulale kuthupi kapena m’maganizo.

Mutu 1, ndime 17

 5 CIKUMBUMTIMA

Cikumbumtima ni mtima umene umatiuza kuti ici n’cabwino, ici n’coipa. Yehova anapatsa aliyense wa ife cikumbumtima. (Aroma 2:14, 15) Koma kuti cikumbumtima cathu cizigwila bwino nchito, tiyenela kuciphunzitsa miyezo ya Yehova. Tikatelo, cidzatithandiza kupanga zosankha zokondweletsa Mulungu. (1 Petulo 3:16) Cikumbumtima cathu cingaticenjeze pamene tifuna kupanga cosankha copanda nzelu. Ndiponso, cingativutitse kwambili tikacita colakwa. Cikumbumtima cathu cingaleke kugwila bwino nchito. Koma mwa thandizo la Yehova, tikhoza kucilimbitsanso. Cikumbumtima cimatipatsa mtendele wa maganizo, ndipo cimatisungila ulemu wathu.

Mutu 2, ndime 3

 6 KUWOPA MULUNGU

Kuwopa Mulungu, kumatanthauza kum’lemekeza kwambili na kum’konda, cakuti sitingacite ciliconse com’khumudwitsa. Kuopa Mulungu kumatithandiza kucita zinthu zabwino, na kupewa kucita zoipa. (Salimo 111:10) Kumatipangitsa kumvetsela mwachelu ku ciliconse cimene Yehova atiuza. Kumatithandizanso kusunga mapangano athu kwa iye, cifukwa cakuti timam’lemekeza kwambili. Kuopa Mulungu kumakhudza mmene timaganizila, mmene timacitila na anthu ena, komanso zosankha zimene timapanga tsiku na tsiku.

Mutu 2, ndime 9

 7 KULAPA

Kulapa kuphatikizapo kumva cisoni cacikulu mu mtima pa colakwa cimene tacita. Amene amatumikila Mulungu, amamva cisoni kwambili akazindikila kuti acita cinthu cophwanya malamulo ake. Tikacita colakwa, tiyenela kucondelela Yehova kuti atikhululukile pa maziko a nsembe ya Yesu. (Mateyu 26:28; 1 Yohane 2:1, 2) Tikalapa moona mtima na kuleka kucita colakwaco, tisakaikile kuti Yehova adzatikhululukila. Pamenepo sitifunika kudziimbanso mlandu pa zimene zinacitika kumbuyo. (Salimo 103:10-14; 1 Yohane 1:9; 3:19-22) Tifunika kutengelapo phunzilo pa zolakwa zathu, kucotsa maganizo olakwika alionse, ndiponso kukhala na umoyo wotsatila miyezo ya Yehova.

Mutu 2, ndime 18

 8 KUCOTSA MUNTHU MU MPINGO

Munthu akacita chimo lalikulu koma salapa, saloledwa kukhalabe mu mpingo. Iye amacotsedwa mu mpingo. Akacotsedwa, sitimacita naye ciliconse, ndipo timalekelatu kukamba naye. (1 Akorinto 5:11; 2 Yohane 9-11) Makonzedwe a kucotsa munthu mu mpingo, amathandiza kuti dzina la Yehova komanso mpingo, zikhalebe zoyela. (1 Akorinto 5:6) Kucotsedwa mu mpingo, ni cilangonso cimene cingathandize wocimwayo kulapa kuti abwelele kwa Yehova.—Luka 15:17.

Mutu 3, ndime 19

 9 CITSOGOZO, CILANGIZO, NA UPHUNGU

Yehova amatikonda, ndipo amafuna kutithandiza. Ndiye cifukwa cake amatipatsa citsogozo, cilangizo, na uphungu. Amacita zimenezi kupitila m’Baibo, komanso anthu okonda Mulungu. Monga anthu opanda ungwilo, timafunikila kwambili thandizo lake. (Yeremiya 17:9) Tikamamvetsela mwaulemu kwa aja amene Yehova amawaseŵenzetsa kutitsogolela, timaonetsa kuti timam’lemekeza, ndipo timafunitsitsa kumumvela.—Aheberi 13:7.

Mutu 4, ndime 2

 10 KUNYADA NA KUDZICEPETSA

Popeza ndife opanda ungwilo, n’capafupi kukhala odzikonda komanso onyada. Koma Yehova amafuna kuti tizikhala odzicepetsa. Kambili, timayamba kuphunzila kudzicepetsa tikadziyelekezela na Yehova n’kuona kuti ndife ocepa kwambili. (Yobu 38:1-4) Njila ina yofunika ya kudzicepetsa, ndiyo kuganizila kwambili za kucitila ena zabwino, m’malo mongoganizila zofuna zathu. Kunyada kumapangitsa munthu kuona kuti ni wofunika kuposa ena. Munthu wodzicepetsa amadziyang’ana moona mtima, na kuona mbali zimene amacita bwino, komanso zofooka zake. Saopa kuvomeleza zolakwa zake, kupepesa, na kulandila maganizo a ena kapena uphungu. Munthu wodzicepetsa amadalila Yehova, ndipo amatsatila malangizo ake.—1 Petulo 5:5.

Mutu 4, ndime 4

 11 ULAMULILO

Ulamulilo ni mphamvu zimene munthu amakhala nazo kuti azipeleka malamulo na kupanga zosankha. Yehova ndiye ali na ulamulilo woposa aliyense, kumwamba ngakhale padziko lapansi. Popeza ndiye analenga zinthu zonse, palibe wina amam’posa mphamvu m’cilengedwe conse. Ndipo amagwilitsila nchito mphamvu zake kupindulitsa ife. Koma Yehova amapatsa anthu ena udindo wakuti azitiyang’anila. Mwacitsanzo, makolo, akulu mu mpingo, komanso maboma. Conco, Yehova afuna kuti tiziwamvela. (Aroma 13:1-5; 1 Timoteyo 5:17) Koma pamene malamulo a munthu awombana na malamulo a Mulungu, timamvela Mulungu osati munthu. (Machitidwe 5:29) Ngati tigonjela ulamulilo wa aja amene Yehova akuwaseŵenzetsa, timaonetsa Yehova kuti timalemekeza zosankha zake.

Mutu 4, ndime 7

 12 AKULU

Yehova amaseŵenzetsa akulu, amene ni amuna acidziŵitso, kuti asamalile mpingo. (Deuteronomo 1:13; Machitidwe 20:28) Amuna amenewa amatithandiza kulimbitsa ubale wathu na Yehova, ndiponso kuti tizim’lambila mwamtendele, komanso mwadongosolo. (1 Akorinto 14:33, 40) Kuti akulu asankhidwe na mzimu woyela, afunika coyamba akwanilitse ziyenelezo zopezeka m’Baibo. (1 Timoteyo 3:1-7; Tito 1:5-9; 1 Petulo 5:2, 3) Cifukwa timakhulupilila gulu la Mulungu na kulicilikiza, timakhala omvela kwa akulu.—Salimo 138:6; Aheberi 13:17.

Mutu 4, ndime 8

 13 MUTU WA BANJA

Yehova anapatsa makolo udindo wosamalila ana awo komanso banja lonse. Komabe, Baibo imafotokoza kuti tate ndiye mutu wa banja. Ngati m’banja mulibe tate, mayi ndiye amakhala mutu wa banja. Udindo wa mutu wa banja umaphatikizapo kupezela banja zakudya, zovala, komanso malo okhala. N’cinthu cofunikanso kwambili kuti mutu wa banja udzitsogolela banja lake pa kulambila Yehova. Mwacitsanzo, afunika kuonetsetsa kuti onse akupezeka ku misonkhano ya mpingo, mu utumiki wakumunda, na kuphunzila Baibo pamodzi. Mutu wa banja afunikanso kutsogolela popanga zosankha. Amayesetsa kutengela citsanzo ca Yesu pokhala wokoma mtima komanso woganizila ena, osati wankhanza kapena waukali. Akamacita izi, m’banja mumakhala mtendele, ndipo onse amadzimva kukhala otetezeka, komanso ubale wawo na Yehova umalimba.

Mutu 4, ndime 12

 14 BUNGWE LOLAMULILA

Bungwe Lolamulila ni kagulu ka abale omwe ali na ciyembekezo copita kumwamba. Mulungu amawagwilitsila nchito kuyang’anila nchito ya anthu ake. M’zaka za zana loyamba, Yehova anagwilitsila nchito bungwe lolamulila kuyang’anila mpingo wa Akhristu, komanso nchito yolalikila. (Machitidwe 15:2) Masiku anonso, pali kagulu ka abale amene akutumikila monga Bungwe Lolamulila. Bungweli ndilo limayang’anila, kutsogolela, na kuteteza anthu a Mulungu. Pamene abalewa apanga zosankha, amadalila Mawu a Mulungu na mzimu wake woyela. Kagulu ka amuna odzozedwa amenewa, Yesu anakachula kuti “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.”—Mateyu 24:45-47.

Mutu 4, ndime 15

 15 COPHIMBA KUMUTU

Nthawi zina, mlongo angapemphedwe kucita mbali mu mpingo imene imasamalilidwa na m’bale. Pocita mbali imeneyo, mlongoyo amalemekeza makonzedwe a Yehova mwa kuvala cakumutu. Koma zimenezi zimangofunikila m’zocitika zina cabe. Mwacitsanzo, mlongo angafunikile kuvala cophimba kumutu ngati akucititsa phunzilo la Baibo ali pamodzi na mwamuna wake, kapena m’bale wina wobatizika.—1 Akorinto 11:11-15.

Mutu 4, ndime 17

 16 SITITENGAKO MBALI M’NDALE ZA DZIKO

Pokhala anthu osakhalila mbali, timakana kutengako mbali m’nkhani za ndale. (Yohane 17:16) Anthu a Yehova amacilikiza Ufumu wake. Posatengako mbali m’ndale za dzikoli, timatengela citsanzo ca Yesu.

N’zoona kuti Yehova amatilamula kuti ‘tizimvela maboma ndiponso olamulila.’ (Tito 3:1, 2; Aroma 13:1-7) Koma malamulo a Mulungu amaletsa kupha munthu. Conco, cikumbumtima ca Mkhristu sicingamulole kupita ku nkhondo. Ngati boma lipeleka mwayi wosankhapo kugwila nchito yotumikila anthu m’malo mokaphunzila zankhondo, Mkhristu aliyense afunika kuona ngati cikumbumtima cake cimulola kukagwila nchito imeneyo.

Ife timalambila Yehova yekha, cifukwa ndiye Mlengi wathu. Olo kuti timalemekeza zizindikilo za maiko, siticitila saliyuti mbendela (kuipatsa ulemu wapadela), kapena kuimbako nyimbo ya fuko. (Yesaya 43:11; Danieli 3:1-30; 1 Akorinto 10:14) Komanso, mtumiki wa Yehova aliyense amasankha yekha kusavotako pamasankho a ndale. Timacita izi cifukwa tinasankha kale ufumu wa Mulungu.—Mateyu 22:21; Yohane 15:19; 18:36.

Mutu 5, ndime 2

 17 MZIMU WA DZIKO

Dziko limalimbikitsa maganizo a Satana. Maganizo amenewo ni ofala kwa anthu ambili amene sakonda Yehova, kapena kutengela maganizo ake, komanso amene amanyalanyaza miyezo ya Mulungu. (1 Yohane 5:19) Maganizo amenewo pamodzi na macitidwe ake, ndiwo mzimu wa dziko. (Aefeso 2:2) Anthu a Yehova amaonetsetsa kuti sakugonja ku mzimu umenewu. (Aefeso 6:10-18) M’malo mwake, ife timakonda njila za Yehova, ndipo timacita khama kuti tisaleke kutengela maganizo ake.

Mutu 5, ndime 7

 18 MPATUKO

Mpatuko umatanthauza kutsutsa coonadi ca m’Baibo. Ampatuko amapandukila Yehova pamodzi na Yesu, wolongedwa kukhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Ndipo amanyengelela ena kuti agwilizane nawo. (Aroma 1:25) Iwo amayesa kubyala mbewu za cikaiko m’maganizo mwa anthu olambila Yehova. Mu mpingo wacikhristu woyambilila, anthu ena anapanduka n’kukhala ampatuko. Zikali kucitika ngakhale masiku ano. (2 Atesalonika 2:3) Koma anthu okhulupilika kwa Yehova sayanjana nawo ampatuko. Sitifuna kukhala na cidwi, kapena kunyengeleledwa ndi ena kuti tiŵelengeko nkhani zampatuko, kapena kuzimvetselako. Ife timakhala okhulupilika kwa Yehova, ndipo timalambila iye yekha basi.

Mutu 5, ndime 9

 19 KUPHIMBA MACIMO

Malinga na Cilamulo ca Mose, mtundu wa Isiraeli unapempha Yehova kuti awakhululukile macimo awo. Iwo anabweletsa ku kacisi nsembe zophimba macimo za mbewu, mafuta, na nyama. Izi zinali kukumbutsa Aisiraeli kuti Yehova anali wofunitsitsa kukhululuka macimo awo monga mtundu, komanso aliyense payekha-payekha. Koma pambuyo pake, pamene Yesu anapeleka moyo wake kaamba ka macimo athu, nsembe zophimba macimo zimenezo sizinafunikilenso. Yesu anapeleka nsembe yangwilo “kamodzi kokha.”—Aheberi 10:1, 4, 10.

Mutu 7, ndime 6

 20 KUSACITILA NKHANZA ZINYAMA

Malinga na Cilamulo ca Mose, anthu analoledwa kudya nyama. Analamulidwanso kupeleka nsembe za nyama. (Levitiko 1:5, 6) Ngakhale n’conco, Yehova sanali kulola anthu ake kucitila nkhanza zinyama. (Miyambo 12:10) Ndipo Cilamulo cimeneco cinali na malamulo oteteza zinyama ku nkhanza. Aisiraeli analamulidwa kusunga bwino ziŵeto zawo.—Deuteronomo 22:6, 7.

Mutu 7, ndime 6

 21 TUMBALI TUNG’ONO-TUNG’ONO TWA M’MAGAZI NA MITUNDU YA OPALESHONI

Tumbali tung’ono-tung’ono twa m’magazi. M’magazi muli mbali zinayi zikulu-zikulu—maselo ofiila, maselo oyela, maselo ochedwa platelets, komanso madzi ochedwa plasma. Mbali zinayi zikulu-zikulu zimenezi, zingagaŵidwe m’tumbali tung’ono-tung’ono twa m’magazi. *

Akhristu amakana kuikidwa magazi, kapena iliyonse ya mbali zake zikulu-zikulu zinayi zija. Koma kodi ayenela kuvomela kuikidwa tumbali tung’ono-tung’ono twa m’magazi? Baibo siipeleka malangizo acindunji pa mbali imeneyi. Conco, Mkhristu aliyense afunika kupanga cosankha malinga na cikumbumtima cake cophunzitsidwa Baibo.

Akhristu ena amakana ngakhale tumbali tung’ono-tung’ono tumeneto. Mfundo yawo ingakhale yakuti malinga na Cilamulo ca Mulungu, Aisiraeli anauzidwa kuti magazi alionse ocotsedwa m’nyama, anafunikila ‘kuwathila pansi.’—Deuteronomo 12:22-24.

Koma ena amasankha mosiyana. Cikumbumtima cawo cingawalole kulandila tumbali tung’ono-tung’ono twa m’magazi. Iwo angaone kuti tumbali tumenetu situimilakonso moyo wa munthu.

Popanga cosankha pa nkhani yokhudza tumbali tung’ono-tung’ono twa m’magazi, dzifunseni kuti:

  • Kodi nikudziŵa kuti kukana tumbali tung’ono-tung’ono twa m’magazi kumatanthauza kuti nakananso zithandizo zina za mankhwala olimbana na matenda, kapena othandiza magazi kuundana kuti munthu aleke kutaya magazi?

  • Ningamufotokozele bwanji dokotala cifukwa cake nasankha kukana kapena kuvomela tumbali tung’ono-tung’ono twa m’magazi?

Mitundu ya opaleshoni. Pokhala Akhristu, sitipeleka magazi kapena kuwasungitsa kwa mawiki angapo, kuti adzatiikenso pambuyo pa opaleshoni. Komabe, pali njila zina zothandizila wodwala zofuna kuseŵenzetsa magazi ake. Mkhristu aliyense afunika kusankha yekha njila imene magazi ake adzasamalidwila pa opaleshoni, popimidwa, kapena pamene akulandila cithandizo camankhwala. Panthawi ngati zimenezi, magazi angawacotse m’thupi la wodwalayo, na kuwasunga pambali kwa kanthawi.—Kuti mudziŵe zambili, onani Nsanja ya Olonda ya October 15, 2000, mapeji 30-31.

Mwacitsanzo, pali mtundu wina wa opaleshoni wochedwa hemodilution. Asanayambe opaleshoni imeneyi, amacotsa magazi m’thupi la wodwala na kuikamo madzi amankhwala ochedwa volume expander. Ndiyeno mkati mwa opaleshoniyo, kapena akangotsiliza, magazi aja amawabwezanso m’thupi la munthuyo.

Opaleshoni ina imachedwa cell salvage. Pa opaleshoni imeneyi, magazi a wodwala amene amatuluka amawasunga, kuwayeletsa, kenako n’kuwabweza m’thupi la wodwalayo opaleshoni ili mkati, kapena mwamsanga pambuyo pake.

Dokotala aliyense angacite maopaleshoni amenewa mosiyanako. Mkhristu aliyense akalibe kuvomela opaleshoni iliyonse, kapena kupimiwa, afunika kufunsa bwino zimene dokotala adzacita kweni-kweni na magazi ake.

Popanga cosankha cokhudza maopaleshoni amene adzafuna kuti museŵenzetse magazi anu, dzifunseni kuti:

  • Ngati ena a magazi acotsedwa m’thupi langa na kusungidwa kwina ngakhale kwa kanthawi kocepa, kodi cikumbumtima canga cingandilole kuona kuti magaziwo akali mbali ya thupi langa, komanso kuti sayenela ‘kuthilidwa pansi’?—Deuteronomo 12:23, 24.

  • Kodi pa opaleshoni cikumbumtima canga cophunzitsidwa Baibo cinganivute ngati angatenge magazi anga na kuwakonza-konza, kenako n’kuwabwezeletsanso m’thupi langa?

  • Kodi nikudziŵa kuti kukana njila zonse za cithandizo ca mankhwala zogwilitsila nchito magazi anga, kumatanthauza kuti nikukananso njila zopelekela cithandizo monga kucotsa magazi kuti apime matenda, kugwilitsila nchito makina osefa magazi, kapena makina othandizila mtima na mapapo?

Tisanapange cosankha cokhudza tumbali tung’ono-tung’ono twa m’magazi, komanso cithandizo ca mankhwala cofuna kugwilitsila nchito magazi athu, tiyenela kupempha citsogozo kwa Yehova, na kucita kafuku-fuku wokwanila. (Yakobo 1:5, 6) Tikatelo, tifunika kupanga cosankha mwa kuseŵenzetsa cikumbumtima cathu cophunzitsidwa Baibo. Tisafunse ena kuti, ‘Mukanakhala imwe mukanacita bwanji?’ Komanso, mwa makambidwe athu, tisapangitse ena kupanga cosankha cofuna ife.—Aroma 14:12; Agalatiya 6:5.

Mutu 7, ndime 11

 22 KUKHALA OYELA M’MAKHALIDWE

Kukhala oyela m’makhalidwe kumatanthauza kuti khalidwe lathu na zocita zathu zizikhala zoyela kwa Mulungu. Kumaphatikizapo zimene timaganiza, zokamba, komanso zocita zathu. Yehova amatilamula kuti tipewe mtundu uliwonse wa zaciwelewele. (Miyambo 1:10; 3:1) Tifunika kukhala na mtima wofuna kutsatila malangizo oyela a Yehova, ngakhale tisanakumane na mayeselo okhudza zakugonana. Tiyenela kupemphela nthawi zonse. Inde, kupempha thandizo la Mulungu kuti tisungebe maganizo athu kukhala oyela, komanso kukanilatu mayeselo pa zaciwelewele.—1 Akorinto 6:9, 10, 18; Aefeso 5:5.

Mutu 8, ndime 11

 23 KUSAMVELA KWACIPONGWE NDI CODETSA

Kusamvela kwacipongwe, ni khalidwe lolankhula kapena kucita zinthu monyozela kwambili miyezo ya Mulungu, moonetsanso mzimu wopanda manyazi. Munthu woteloyo amaonetsa kuti salemekeza malamulo a Mulungu. Ngati munthu waonetsa khalidwe la kusamvela kwacipongwe, nkhaniyo ifunika kusamalilidwa na komiti yaciweluzo. Codetsa cimaphatikizapo zolakwa zosiyana-siyana. Malinga na kuopsa kwa cocitikaco, nkhani zina zokhudza codetsa zingafune kusamalilidwa na komiti yaciweluzo mu mpingo.—Agalatiya 5:19-21; Aefeso 4:19; kuti mumve zambili, ŵelengani “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” mu Nsanja ya Olonda ya July 15, 2006.

Mutu 9, ndime 7; Mutu 12, ndime 10

 KUDZIPUKUSA UMALISECE

Yehova anakonza nkhani ya kugonana kuti mwamuna na mkazi wake adzionetsana cikondi. Ndiye cifukwa cake kudzipukusa umalisece, kapena kucita zosayenela na umalisece wake n’kulakwa. Mcitidwe umenewu ungawononge ubale wa munthu na Yehova. Ungayambitse zilakolako zolakwika, ndipo munthuyo angayambe kuona nkhani yakugonana mwa njila ina. (Akolose 3:5) Ngati wina ali na cizolowezi cimeneci, ndipo akuvutika kuti aleke, sayenela kutaya mtima. (Salimo 86:5; 1 Yohane 3:20) Ngati na imwe muli na vuto limeneli, muzipemphela kwa Yehova moona mtima. M’pempheni kuti akuthandizeni. Komanso, muzipewa zinthu monga zamalisece, zimene zingakupatseni maganizo oipa. Kambani na makolo anu acikhristu, kapena bwenzi lofikapo limene limalemekeza malamulo a Yehova. (Miyambo 1:8, 9; 1 Atesalonika 5:14; Tito 2:3-5) Dziŵani kuti Yehova amaona na kuyamikila kuyesetsa kwanu kuti mukhale woyela m’makhalidwe.—Salimo 51:17; Yesaya 1:18.

Mutu 9, ndime 9

 25 KUKWATILA CIPALI

Cipali ni pamene munthu wakwatila akazi aŵili kapena kuposapo. Yehova anakonza kuti cikwati cizikhala pakati pa mwamuna mmodzi na mkazi mmodzi. Mu Isiraeli wakale, Mulungu analola mwamuna kukhala na akazi aŵili kapena kuposapo. Koma sindico cinali colinga cake poyamba. Masiku ano, Yehova salola anthu ake kukwatila cipali. Mwamuna afunika kukhala na mkazi mmodzi cabe. Nayenso mkazi ayenela kukhala na mwamuna mmodzi basi.—Mateyu 19:9; 1 Timoteyo 3:2.

Mutu 10, ndime 12

 26 CISUDZULO NA KUPATUKANA

Colinga ca Yehova n’cakuti mwamuna na mkazi wake asalekane kwa moyo wawo wonse. (Genesis 2:24; Malaki 2:15, 16; Mateyu 19:3-6; 1 Akorinto 7:39) Amalola cisudzulo cabe pamene wina wa m’cikwati wacita cigololo. Zimenezi zikacitika, Yehova amapatsa wa m’cikwati wosalakwayo ufulu wosankha kusudzulana kapena ayi.—Mateyu 19:9.

Nthawi zina, Akhristu angasankhe kupatukana ngakhale kuti sipanacitike cigololo. (1 Akorinto 7:11) Zifukwa zina zimene Mkhristu angasankhile kupatukana ni izi.

  • Kulephela mwadala kusamalila banja: Ngati mwamuna akana kupezela banja zinthu zofunikila, cakuti banja lake likusoŵa ndalama kapena cakudya.—1 Timoteyo 5:8.

  • Ciwawa: Ciwawa cofika pamlingo woika thanzi kapena moyo wa mnzake paciwopsezo.—Agalatiya 5:19-21.

  • Kuika paciopsezo ubale wa munthu na Yehova: Ngati mwamuna kapena mkazi alepheletsa mnzake kutumikila Yehova.—Machitidwe 5:29.

Mutu 11, ndime 19

 27 KUYAMIKILANA KOMANSO KULIMBIKITSANA

Tonse timafuna kuyamikilidwa na kulimbikitsidwa. (Miyambo 12:25; 16:24) Tingalimbikitsane komanso kutonthozana wina na mnzake mwa mawu acifundo ndi acikondi. Mawu otelo angathandize abale na alongo athu kupilila, na kupitiliza kutumikila Yehova, ngakhale pamene akumana na mavuto aakulu. (Miyambo 12:18; Afilipi 2:1-4) Ngati wina ni wolefulidwa, tiyenela kumvetsela mwaulemu pamene akutidandaulila. Tiyeni tiyese kuganizila mmene cikumvekela. Kucita izi, kudzatithandiza kudziŵa momuthandizila. (Yakobo 1:19) Muzikhala na mtima wofuna kuwadziŵa bwino abale na alongo, pofuna kudziŵa zosoŵa zawo. Mukatelo, mudzawalimbikitsa kutembenukila ku Gwelo la citonthozo na cilimbikitso conse, kumene angapeze citsitsimulo ceni-ceni.—2 Akorinto 1:3, 4; 1 Atesalonika 5:11.

Mutu 12, ndime 16

 28 KUMANGITSA CIKWATI

Baibo siinaike malamulo acindunji omangitsila cikwati. Zikhalidwe komanso malamulo a boma ni osiyana m’maiko osiyana-siyana. (Genesis 24:67; Mateyu 1:24; 25:10; Luka 14:8) Cinthu cofunika kwambili pomangitsa cikwati, ni malumbilo amene akwatiwo amacita pamaso pa Yehova. Omanga cikwati ambili amapempha abanja na mabwenzi awo kuti akakhalepo pocita malumbilo awo, komanso kuti mkulu akawakambile nkhani yacikwati yozikidwa pa Baibo. Ngati ofuna kukwatilanawo afuna kukakhala na phwando lacikwati pambuyo pake, cili kwa iwo kusankha mtundu wa phwando limene afuna. (Luka 14:28; Yohane 2:1-11) Koma afunika kuonetsetsa kuti zilizonse zimene akonza pa weding’i yawo, zikakhale zolemekeza Yehova. (Genesis 2:18-24; Mateyu 19:5, 6) Mfundo za m’Baibo zingawathandize kupanga zosankha zabwino. (1 Yohane 2:16, 17) Ngati asankha kuti ku weding’i yawo kudzakhala moŵa, ayenela kuonetsetsa kuti kudzakhala uyang’anilo wabwino. (Miyambo 20:1; Aefeso 5:18) Komanso ngati kudzakhala nyimbo kapena zosangalatsa zilizonse, aonetsetse kuti zikakhale zolemekeza Yehova. Okaloŵa m’banjawo afunika kuika patsogolo ubale wawo na Mulungu, komanso wa pakati pa iwo aŵili, m’malo mongoganizila za weding’i cabe.—Miyambo 18:22; kuti mudziŵe zambili, ŵelengani Nsanja ya Olonda ya October 15, 2006, mapeji 18-31.

Mutu 13, ndime 18

 29 KUPANGA ZOSANKHA ZANZELU

Tiyenela kupanga zosankha zanzelu zozikidwa pa mfundo za m’Mawu a Mulungu. Mwacitsanzo, Mkhristu angapemphedwe na mnzake wa m’cikwati, amene si Mboni ya Yehova, kuti akapezekepo pa cakudya ca kubanja kwawo ca paholide. Ngati ni mmene zilili kwa imwe, kodi mungacite ciani? Ngati cikumbumtima canu cikulolani kupita, muyenela kufotokozela mnzanu wa m’cikwati kuti ngati phwandolo lidzaloŵetsamo miyambo ya dziko, simudzatengako mbali. Komanso, muyenela kuganizila ngati ena angakhumudwe akamvela kuti munapita ku maceza amenewo.—1 Akorinto 8:9; 10:23, 24.

Mwinanso abwana anu kunchito angakupatseni malipilo aciwongola dzanja (bonasi), pa nthawi ya holide. Kodi muyenela kukana kuilandila? Osati kweni-kweni. Ziyenela kudalila na mmene bwana wanu akuionela bonasi imeneyo. Kodi akuiona kuti ni yokondwelela holide, kapena colinga cake ni kuyamikila magwilidwe anu anchito? Kuganizila mfundo imeneyi kungakuthandizeni kuona ngati mungailandile kapena ayi.

Kapenanso, munthu wina angakupatseni mphatso pa nthawi ya holide. Angakuuzeni kuti: “Nidziŵa kuti simukondwelela holide imeneyi. Ni mphatso cabe.” Mwina munthuyo wangokukomelani mtima. Komanso mwina akuyesa cikhulupililo canu, kapena angofuna kuti mutengeko mbali m’cikondwelelo cimeneco? Mukaganizila mfundo zimenezi, mungasankhe bwino kulandila kapena kusalandila mphatso imeneyo. M’zosankha zathu zonse, tifunika kukhala na cikumbumtima coyela, komanso okhulupilika kwa Yehova.—Machitidwe 23:1.

Mutu 13, ndime 22

 30 NKHANI ZA BIZINESI NA MALAMULO

Nthawi zambili, pakakhala kusiyana maganizo, koma mukambilana mwamsanga komanso mwamtendele, nkhani siimakula kwambili. (Mateyu 5:23-26) Kwa Akhristufe, udindo wathu woyambilila n’kulemekeza Yehova, na kusungitsa mgwilizano mu mpingo.—Yohane 13:34, 35; 1 Akorinto 13:4, 5.

Ngati Akhristu asiyana maganizo pa nkhani ya bizinesi, ayenela kukambilana m’malo motengelana kukhoti. Pa 1 Akorinto 6:1-8, pali uphungu wa mtumwi Paulo pa nkhani yotengelana kumakhoti. Kutengela m’bale wathu kukhoti sikupeleka cithunzi cabwino ca Yehova na mpingo. Pa Mateyu 18:15-17, pali masitepu atatu amene Akhristu angacite bwino kutsatila kuti pasakhale kunenezana milandu ya misece kapena cinyengo: (1) Coyamba afunika kuyesetsa kuthetsa nkhaniyo pa uŵili wawo. (2) Ngati sitepu iyi yalephela, apemphe munthu mmodzi kapena aŵili okhwima bwino a mu mpingo kuti athandize. (3) Ngati kwakhala kofunikila, angapeleke nkhaniyo kwa akulu mu mpingo kuti aisamalile. Zikafika pamenepa, akulu adzagwilitsila nchito mfundo za m’Baibo kuti athandize onse okhudzidwa kuthetsa nkhaniyo mwamtendele. Ngati ena sagwilizanika pa kutsatila miyezo ya Baibo, akulu sangacitile mwina koma kuisamalila mwaciweluzo.

Koma zilipo zocitika zina pamene kupita kukhoti kungakhale kofunikila malinga na malamulo. Zingakhale nkhani zokhudza cisudzulo, udindo wosunga ana, ndalama zopeleka kwa wosudzulidwa, nkhani za wilu, ndi zina zotelo. Ngati Mkhristu atsatila ndondomeko za malamulo zimenezi pofuna kuthetsa nkhani mwamtendele, sakunyozela uphungu wa Paulo.

Komanso ngati pacitika milandu yoopsa, monga kugona munthu mwacikakamizo, kugona mwana, ciwawa, umbava, kapena kupha munthu, Mkhristu amene wamang’ala nkhaniyo kupolisi sananyozele uphungu wa Paulo.

Mutu 14, ndime 14

 31 MACENJELA A SATANA

Kucokela m’munda wa Edeni, Satana wakhala akunamiza anthu. (Genesis 3:1-6; Chivumbulutso 12:9) Amadziŵa kuti ngati angapotoze maganizo athu, akhoza kutipangitsa kucita colakwa. (2 Akorinto 4:4; Yakobo 1:14, 15) Pofuna kulimbikitsa maganizo ake kuti aoneke abwino kwa ife, amaseŵenzetsa nkhani zandale, cipembedzo, gawo la zamalonda, zosangalatsa, maphunzilo, na zinthu zina zambili.—Yohane 14:30; 1 Yohane 5:19.

Satana amadziŵa kuti nthawi yamuthela kale yosoceletsa anthu. Conco, akucita zonse zotheka kuti asoceletse ambili nthawi isanatheletu. Amafuna kusoceletsa maka-maka atumiki a Yehova. (Chivumbulutso 12:12) Ngati sitisamala, pang’ono-m’pang’ono Mdyelekezi akhoza kupotoza maganizo athu. (1 Akorinto 10:12) Mwacitsanzo, Yehova amafuna kuti vikwati vizikhalitsa. (Mateyu 19:5, 6, 9) Koma anthu ambili masiku ano amaona cikwati monga cipangano wamba cimene akhoza kucithetsa nthawi iliyonse. Mafilimu ambili na mapulogilamu a pa TV amalimbikitsa maganizo amenewa. Mwa ici, tiyeni tionetsetse kuti sitikutengela kaonedwe ka dziko ka cikwati.

Njila ina imene Satana amayesa kutipusitsila ni mwa kulimbikitsa mzimu wodzidalila. (2 Timoteyo 3:4) Ngati sitisamala, tingayambe kutaya ulemu kwa amuna amene Yehova anaika paudindo. Mwacitsanzo, m’bale angayambe kukana citsogozo ca akulu mu mpingo. (Aheberi 12:5) Kapena mlongo angayambe kupeputsa makonzedwe aumutu m’banja.—1 Akorinto 11:3.

Tisam’patse mpata Mdyelekezi kuti asokoneze maganizo athu. M’malo mwake, titengele maganizo a Yehova, na ‘kuika maganizo athu pa zinthu zakumwamba.’—Akolose 3:2; 2 Akorinto 2:11.

Mutu 16, ndime 9

 32 CITHANDIZO CA MANKHWALA

Tonse timafuna kukhala na thanzi labwino, komanso kupeza cithandizo cabwino tikadwala. (Yesaya 38:21; Maliko 5:25, 26; Luka 10:34) Masiku ano, pali macilitso osiyana-siyana, kuyambila kwa madokotala mpaka kwa anthu ena. Posankha mtundu wa cithandizo ca mankhwala, tifunika kutsatila mfundo za m’Baibo. Timakumbukila kuti Ufumu wa Mulungu cabe, ni umene udzaticilitsa kothelatu. Conco, sibwino kuika maganizo athu onse pa thanzi lathu kufika pamlingo wonyalanyaza kulambila kwathu Yehova.—Yesaya 33:24; 1 Timoteyo 4:16.

Tiyenela kupewa cithandizo ca mankhwala ciliconse cooneka kuti cimaloŵetsapo mphamvu ya ziŵanda. (Deuteronomo 18:10-12; Yesaya 1:13) Conco, tisanalandile cithandizo ciliconse, kapena mankhwala, tiyeni tifunsile mokwanila zonse zoloŵetsedwamo, komanso maganizo amene cimalimbikitsa. (Miyambo 14:15) Tisaiŵale kuti Satana angakonde kutipusitsa kuti tizilumikizana na ziŵanda. Ngakhale ngati pali cikaiko cabe cakuti cithandizoco cikukhudzana na ziŵanda, tiyeni ticipewe.—1 Petulo 5:8.

Mutu 16, ndime 18

^ ndime 98 Madokotala ena angaone mbali zinayi zikulu-zikulu za magazi kukhala tumbali tung’ono-tung’ono. Conco, mungafunike kufotokoza cosankha canu cokana kuikidwa magazi athunthu, kapena mbali zake zinayi zikulu-zikulu, zochedwa maselo ofiila, maselo oyela, maselo ochedwa platelets, komanso madzi ochedwa plasma.