GAO 4
Anamvetsela kwa Satana—Nanga Cinacitika n’Ciani?
Adamu ndi Hava sanamvele Mulungu, conco anafa. Genesis 3:6, 23
Hava anamvetsela ku njoka ndipo anadya cipatso. Pambuyo pake, anapatsako Adamu, ndipo naye anadya.
Cimene iwo anacita cinali coipa—ni chimo. Mulungu anawathamangitsa m’mudzi wawo wa Paladaiso.
Umoyo wawo ndi wa ana awo unakhala wovuta. Iwo anakalamba ndi kufa. Sanapite kumalo a mizimu; analeka kukhala ndi moyo.
Genesis 3:19
Dothi lilibe moyo; ndi mmene akufa alili.Timafa cifukwa tinacokela kwa Adamu ndi Hava. Akufa sangaone kapena kumva kapena kucita cina ciliconse.—Mlaliki 9:5, 10.
Yehova sanafune kuti anthu tizifa. Posacedwa adzaukitsa akufa. Ngati iwo adzamvetsela kwa iye, adzakhala ndi moyo wamuyaya.