Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

GAO 10

Kodi Anthu Amene Amamvetsela kwa Mulungu Adzapeza Madalitso Abwanji?

Kodi Anthu Amene Amamvetsela kwa Mulungu Adzapeza Madalitso Abwanji?

Ambili amene anafa adzauka ndi kukhala ndi moyo padziko lapansi. Machitidwe 24:15

Taonani madalitso amene mudzalandila mtsogolo ngati mumvetsela kwa Yehova. Mudzakhala ndi thanzi labwino; sikudzakhala munthu wodwala kapena wofooka. Sikudzakhala anthu oipa ndipo mudzakhulupilila munthu aliyense.

Sikudzakhala zoŵaŵa, cisoni kapena kulila. Sikudzakhala kukalamba ndi kufa.

Anthu amene mudzakhala nao adzakhala anzanu ndi acibanja. Umoyo m’Paladaiso udzakhala wokondweletsa.

Sikudzakhala mantha. Anthu adzakhala okondwela kwambili.

Ufumu wa Mulungu udzatsiliza mavuto onse. Chivumbulutso 21:3, 4