Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mau Oyamba

Mau Oyamba

MULUNGU WAMPHAMVUYONSE ni Mfumu ya cilengedwe conse. Moyo wathu, walelo ndi wa mtsogolo, umadalila iye. Ali ndi mphamvu yopeleka mphoto ndi yopeleka cilango. Ali ndi mphamvu yopatsa moyo ndi yolanda moyo. Ngati iye atiyanja, zinthu zidzatiyendela bwino; akaleka kutiyanja, zinthu sizidzatiyendela bwino. Conco kulambila kwathu kuyenela kukhala kovomelezeka kwa iye.

Anthu amalambila m’njila zosiyana-siyana. Cipembedzo cili ngati njila. Ndiyeno kodi njila zonse za cipembedzo ni zovomelezeka kwa Mulungu? Iyai, si zonse. Yesu, mneneli wa Mulungu, anaonetsa kuti pali njila ziŵili cabe. Iye anati: “Mseu waukulu ndi wotakasuka ukupita kucionongeko, ndipo anthu ambili akuyenda mmenemo. Koma cipata coloŵela kumoyo n’copapatiza komanso mseu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi oŵelengeka.”—Mateyu 7:13, 14.

Pali zipembedzo mitundu iŵili cabe: cina ca kumoyo ndi cina ca kucionongeko. Colinga ca kabuku aka ni kukuthandizani kupeza njila ya kumoyo wamuyaya.