Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBALI 8

cokani-m’cipembedzo-conama-loŵani-m’cipembedzo-coona

cokani-m’cipembedzo-conama-loŵani-m’cipembedzo-coona

1. Kodi anthu masiku ano afunika kusankha ciani pankhani ya kulambila?

YESU anakamba kuti: “Amene sali kumbali yanga ndi wotsutsana ndi ine.” (Mateyu 12:30) Ngati sitili kumbali ya Yehova ndiye kuti tili kumbali ya Satana. Anthu ambili amaganiza kuti amalambila Mulungu m’njila imene iye amavomeleza, koma Baibo imakamba kuti Satana “akusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Chivumbulutso 12:9) Anthu mamiliyoni amakhulupilila kuti amalambila Mulungu, koma io maka-maka amatumikila Satana Mdyelekezi. Anthu masiku ano afunika kusankhapo cimodzi: Kaya kutumikila Yehova, “Mulungu wa coonadi,” kapena Satana, “tate wake wa bodza.”—Salimo 31:5; Yohane 8:44.

Masukani ku Cipembedzo Conama

2. Kodi njila ina imene Satana amaseŵenzetsa kuti aletse anthu kulambila Yehova ni iti?

2 Kusankha kutumikila Yehova ni cinthu canzelu, ndipo Mulungu amakondwela nako. Koma Satana sakondwela ndi anthu amene amatumikila Mulungu; ndipo amawabweletsela mavuto. Njila ina imene amavutitsila atumiki a Mulungu ni yakuti amasonkhezela anthu ena, ngakhale anzao ndi apabanja, kuti aziwaseka kapena kuwatsutsa. Yesu anacenjeza kuti: “Kunena zoona, adani a munthu adzakhala a m’banja lake leni-leni.”—Mateyu 10:36.

3. Ngati apabanja panu kapena anzanu amatsutsa kulambila kwanu Mulungu, kodi mudzacita bwanji?

3 Ngati zimenezi zakucitikilani, kodi mudzacita bwanji? Anthu ambili amadziŵa kuti kulambila kwao ni kwabodza, koma safuna kuleka. Amaganiza kuti akaleka ndiye kuti samalemekeza makolo. Kodi muganiza kuti ni canzelu kucita zimenezi? Ngati mwadziŵa kuti ena pabanja panu amagwilitsila nchito mankhwala osokoneza ubongo, kodi simudzawauzako kuti mankhwala ameneo ni oipa? Kodi inu mungayambe kugwilitsila nchito mankhwala ameneo?

4. Kodi Yoswa anawauza ciani Aisiraeli pankhani ya kulambila?

4 Yoswa analimbikitsa Aisiraeli kuleka zizoloŵezi ndi miyambo ya makolo ao ya cipembedzo conama. Iye anakamba kuti: “Tsopano opani Yehova ndi kumutumikila mosalakwitsa ndiponso mokhulupilika. Cotsani milungu imene makolo anu [anali kutumikila] kutsidya lina la Mtsinje ndi ku Iguputo, ndipo tumikilani Yehova.” (Yoswa 24:14) Yoswa anali wokhulupilika kwa Mulungu, ndipo Yehova anamudalitsa. Ngati tili okhulupilika kwa Yehova, ifenso adzatidalitsa.—2 Samueli 22:26.

Onongani Zinthu Zonse za Kulambila Konama

5. N’cifukwa ciani tiyenela kuononga zinthu zonse zamatsenga?

5 Ngati tifuna kumasuka ku cipembedzo conama, tiyenelanso kuononga zinthu zonse zamatsenga zimene tingakhale nazo, monga zithumwa, mphete (maling’i) ndi zibangili zamatsenga, ndi zina zaconco. Tifunika kucita zimenezi kuti tionetse kuti tikudalila Yehova ndi mtima wathu wonse.

6. Kodi Akristu oyambilila anacita bwanji ndi mabuku ao amatsenga?

6 Ganizilani zimene Akristu ena oyambilila anacita pamene anasankha kukhala m’cipembedzo coona. Baibo imakamba kuti: “Ambili ndithu amene anali kucita zamatsenga anasonkhanitsa mabuku ao pamodzi ndi kuwatentha pamaso pa onse.”—Machitidwe 19:19.

7. Kodi tiyenela kucita ciani ngati viŵanda vitivuta?

7 Ena amene amayamba kutumikila Yehova ndipo kale anali kucita ufiti kapena zamatsenga, nthawi zina viŵanda vingawavute. Ngati zimenezi zakucitikilani, pemphelani kwa Yehova mokweza mau ndi kuchula dzina lake. Iye adzakuthandizani.—Miyambo 18:10; Yakobo 4:7.

8. Kodi Akristu amaona bwanji mafano, zifanizilo kapena zithunzi-thunzi zimene zimagwilitsidwa nchito pakulambila konama?

8 Anthu amene afuna kutumikila Yehova ayenela kuleka kugwilitsila nchito mafano, zifanizilo, kapena zithunzi-thunzi za cipembedzo conama. Akristu oona amayenda “mwa cikhulupililo, osati mwa zooneka ndi maso.” (2 Akorinto 5:7) Amamvela lamulo la Mulungu limene limaletsa kugwilitsila nchito mafano pa kulambila.—Ekisodo 20:4, 5.

Gwilizanani ndi Anthu a Yehova

9. Kodi Baibo imakamba kuti tiyenela kucita ciani kuti tikhale anzelu?

9 Baibo imakamba kuti: “Munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu.” (Miyambo 13:20) Ngati tifuna kukhala anzelu, tiyenela kuyenda, kapena kuti kugwilizana, ndi Mboni za Yehova. Anthu amenewa ndi amene akuyenda panjila yopita kumoyo.—Mateyu 7:14.

10. Kodi Mboni za Yehova zingakuthandizeni bwanji kutumikila Mulungu?

10 Mboni zimaganizila anthu anzao. Nchito yao ndi kuthandiza anthu oona mtima kuti amvetsetse coonadi ca m’Baibo cimene cidzawatsogolela kumoyo wamuyaya. Zingakuthandizeni kumvetsetsa Baibo mwa kuphunzila ndi inu mahala. Zidzayankha mafunso anu ndipo zidzakuonetsani mmene mungagwilitsile nchito cidziŵitso ca m’Baibo pa umoyo wanu.—Yohane 17:3.

11. Kodi misonkhano ya Cikristu ingakuthandizeni bwanji?

11 Pamisonkhano yao, imene imacitikila ku Nyumba ya Ufumu, mungaphunzile zambili za Yehova ndi njila zake. Mwa kupezeka pamisonkhano, cikhumbo canu cofuna kukhala m’cipembedzo coona cidzalimba. Ndiponso mudzaphunzitsidwa mmene mungathandizile anthu ena kudziŵa coonadi ca m’Baibo.—Aheberi 10:24, 25.

12. Kodi pemphelo lingakuthandizeni bwanji kutumikila Mulungu?

12 Pamene mupitiliza kuphunzila zambili za cifunilo ca Yehova ndi colinga cake, mosalephela mudzamvetsetsa njila zake zacikondi ndipo mudzayamba kuzikonda. Mudzakulitsanso mtima wofuna kucita zinthu zimene iye amakondwela nazo ndi kupewa zimene samakondwela nazo. Kumbukilani kuti mungapemphele kwa Yehova kuti akuthandizeni kucita cabwino ndi kupewa coipa.—1 Akorinto 6:9, 10; Afilipi 4:6.

Kodi mungalambile bwanji m’njila ya coonadi?

13. Kodi muyenela kucita ciani kuti mukondweletse mtima wa Yehova?

13 Pamene mupitiliza kukula kuuzimu, mosakaikila inu mudzazindikila kuti mufunika kudzipeleka ndi kubatizika kuti mukhale wa Mboni za Yehova. Mukagwilizana ndi anthu a Yehova, mudzakondweletsa mtima wake. (Miyambo 27:11) Mudzakhala pakati pa anthu acimwemwe amene Mulungu amakamba za io kuti: “Ndidzakhala pakati pao ndi kuyenda pakati pao. Ndidzakhala Mulungu wao, ndipo io adzakhala anthu anga.”—2 Akorinto 6:16.