Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBALI 4

Kodi Makolo Athu Anapita Kuti?

Kodi Makolo Athu Anapita Kuti?

1, 2. Kodi anthu ambili amakhulupilila ciani za anthu amene anafa?

ANTHU mamiliyoni mu Africa amakhulupilila kuti moyo sumathela pa imfa, ndipo munthu akafa amapita kumalo ena kumene amakhala ndi moyo. Ambili amaganiza kuti makolo ao amene anafa anacoka padziko pano kupita kudziko lina losaoneka, anacoka m’dziko la anthu kupita kudziko la mizimu.

2 Anthu amakhulupilila kuti makolo amenewa, kapena kuti mizimu ya makolo, imaonetsetsa kuti mabanja ao padziko lapansi ali otetezeka ndipo ali ndi moyo wabwino. Conco, anthu amakhulupilila kuti mizimu ya makolo ni mabwenzi amphamvu ndipo imathandiza kuti io akolole zambili, akhale athanzi, ndipo imawachinjiliza. Amakhulupilila kuti ngati samalemekeza mizimu ya makolo kapena akaikwiitsa, imabweletsa tsoka—matenda, kusauka, ndi ngozi.

3. Kodi anthu ena amalambila bwanji mizimu ya makolo ao?

3 Anthu amoyo amacita miyambo yosiyana-siyana pofuna kulemekeza mizimu ya makolo ndi kuchinjiliza ubale wao ndi mizimuyo. Zimenezi zimaoneka kwambili m’miyambo ya malilo, monga mwambo wa kucezela pamalilo. Kulambila makolo kumacitikanso m’njila zina. Mwacitsanzo, anthu ena akalibe kumwa moŵa, amathila wina pansi kupatsako mizimu ya makolo. Ndiponso, akaphika cakudya, amasiyako cina m’poto kuti mizimu ya makolo ikabwela, ipeze cakudya.

4. Kodi anthu ambili amakhulupilila ciani za mzimu?

4 Anthu ena amakhulupilila kuti munthu wamoyo ali ndi mzimu wosafa umene umapulumuka thupi likafa. Ngati munthu anali wabwino, ati mzimu wake umapita kumwamba, kapena kuti kupaladaiso, koma ngati anali woipa, ati mzimu wake umapita kuhelo. Nthawi zambili anthu amaphatikiza pamodzi mfundo imenei ndi zikhulupililo za makolo. Mwacitsanzo, pambali imene imakamba za malilo m’nyuzipepa, pamene amalengeza za mwambo wa malilo wa m’chechi, amakambanso kuti munthuyo “makolo amuitana” kapena “wapita ku mizimu.” Maziko a zikhulupililo zonse zimenezi ndi mfundo yakuti thupi likafa, mzimu umapulumuka. Kodi Baibo imakamba ciani pankhani imenei?

Kodi Mzimu n’Ciani?

5. Kodi m’Baibo mzimu ni ciani?

5 Tikaphunzila Baibo bwino-bwino, timapeza kuti mau oyambilila a Cihebeli ndi Cigiliki amene anatembenuzidwa kuti “mzimu,” amatanthauza zambili. Mau ameneo amakamba za cinthu cimene maso a anthu sangaone ndipo cimaonetsa umboni wakuti pali mphamvu imene ikugwila nchito. Mau amenewa angatanthauze (1) mphepo; (2) mphamvu ya moyo imene imagwila nchito mwa anthu ndi nyama; (3) mphamvu imene ili mumtima wophiphilitsa wa munthu ndipo imamusonkhezela kukamba ndi kucita zinthu m’njila inayake; (4) mizimu; ndi (5) mphamvu ya Mulungu yogwila nchito, kapena kuti mzimu woyela. Izi ndi zina zimene mau akuti “mzimu” m’Baibo amatanthauza.

6. Kodi mzimu umene uli mwa anthu n’ciani?

6 Conco pamene Baibo ikamba za mzimu umene uli mwa anthu, kambili imatanthauza mphamvu ya moyo yosaoneka imene imasonkhezela anthu kucita zinthu zimene zamoyo zimacita. Mzimu uli ngati mphamvu ya malaiti. Mphamvu ya malaiti imacititsa fani kuzungulila ndi kuyendetsa mpweya kapena wailesi kulila, koma payokha singayendetse mpweya kapena kutulutsa mau. N’cimodzi-modzi ndi mzimu wathu. Umaticititsa kuona, kumva, ndi kuganiza. Koma mzimu paokha sungacite zimenezi ngati palibe maso, matu, kapena ubongo.

7. Kodi cimacitika n’ciani ngati mzimu waleka kugwila nchito m’thupi?

7 Cotelo, munthu aliyense ali ndi mphamvu ya moyo, kapena kuti mzimu, umene umacilikiza moyo wake. Kuti mphamvu ya moyo imenei igwile nchito imadalila kupuma, koma sindiye kupuma iyai. M’malo mwake, ndi mphamvu imene imapezeka m’maselo ndipo imacititsa selo iliyonse m’thupi mwathu kukhala yamoyo. Ngati mphamvu ya moyo imenei yaleka kugwila nchito m’thupi, thupi limafa. N’cifukwa cake Baibo imakamba kuti: “Thupi lopanda mzimu limakhala lakufa.”—Yakobo 2:26.

8. Kodi n’ciani cimene cimacitikila maganizo a munthu pamene mphamvu ya moyo yaleka kugwila nchito m’thupi lake?

8 Baibo imakambanso kuti munthu akafa, si thupi cabe limene limafa. Pa Salimo 146:4, coyamba timaŵelenga kuti pamene “mzimu” wa munthu “umacoka”—kutanthauza kuti waleka kugwila nchito—munthu “amabwelela kunthaka,” kutanthauza kuti thupi limabwelela kudothi. Koma onani kuti lemba limeneli lipitiliza kuti: “Pa tsiku limenelo zonse zimene anali kuganiza zimathelatu.”

9. Kodi mzimu sumacita ciani?

9 Cotelo, Baibo sikamba kuti mzimu, kapena kuti mphamvu ya moyo, imacoka m’thupi pamene munthu wafa ndi kupitiliza kukhala ndi moyo kumalo a mizimu. Conco, munthu akafa mzimu sungacite ciliconse. Sungatidalitse, kutiopsa, kapena kuticitila zoipa zilizonse.

Mmene Akufa Alili

10. Kodi Baibo imakamba ciani za mmene anthu akufa alili?

10 Nanga kodi akufa angacite ciliconse? Popeza kuti Yehova ndiye analenga anthu, amadziŵa cimene cimacitika ngati tafa. Mau ake amaphunzitsa kuti akufa sali amoyo, samamva, samaona, samalankhula, kapena kuganiza ciliconse. Baibo imati:

  • “Akufa sadziŵa ciliconse.”—Mlaliki 9:5.

  • “Cikondi cao, cidani cao ndiponso nsanje yao zatha kale.”—Mlaliki 9:6.

  • “Kulibe kugwila nchito, kuganiza zocita, kudziŵa zinthu, kapena nzelu, ku Manda kumene ukupitako.”—Mlaliki 9:10.

11. Kodi pamene Adamu anacimwa Yehova anamuuza ciani?

11 Ganizilani zimene Baibo imakamba za Adamu, kholo lathu loyamba. Yehova anaumba Adamu “kucokela kufumbi lapansi.” (Genesis 2:7) Ngati Adamu anamvela lamulo la Yehova, akanakhala padziko lapansi ndi moyo wamuyaya ndiponso wokondweletsa. Koma Adamu sanamvele lamulo la Yehova, ndipo analandila cilango ca imfa. Kodi Adamu anapita kuti pamene anafa? Mulungu anamuuza kuti: “U[dza]bwelela kunthaka, pakuti n’kumene unatengedwa. Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwelela.”—Genesis 3:19.

12. Kodi cinacitika kwa Adamu n’ciani pamene anafa?

12 Kodi Adamu anali kuti Yehova asanamulenge ndi dothi lapansi? Iye sanali kwina kulikonse. Conco pamene Yehova anakamba kuti Adamu ‘adzabwelela kunthaka,’ anatanthauza kuti Adamu sadzakhalanso ndi moyo, ngati dothi. Adamu sanapite kukakhala ndi moyo kudziko la mizimu. ‘Sanasamuke’ kupita kumalo a mizimu ya makolo. Sanapite kumwamba kapena kuhelo. Anakhalanso wopanda moyo; analeka kukhalako.

13. Kodi cimene cimacitika kwa anthu ndi nyama pa imfa n’ciani?

13 Kodi izi n’zimene zimacitika kwa anthu onse? Inde. Baibo imakamba kuti: “[Anthu ndi nyama a]mapita kumalo amodzi. Zonse zinacokela kufumbi ndipo zonse zimabwelela kufumbi.”—Mlaliki 3:19, 20.

14. Kodi tiyembekeza kuti cidzacitika n’ciani kwa akufa?

14 Baibo imalonjeza kuti Mulungu adzaukitsa akufa kuti akakhale ndi moyo m’paladaiso padziko lapansi. (Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15) Koma zimenezi zidzacitika mtsogolo. Panthawi ino, io akugona tulo mu imfa. (Yohane 11:11-14) Sitiyenela kuwaopa kapena kuwalambila, cifukwa sangatithandize kapena kuticitila zoipa.

15, 16. Kodi Satana amayesa-yesa bwanji kucititsa anthu kukhulupilila kuti anthu akufa ali moyo?

15 Mfundo yakuti ife anthu sitimafa ni bodza la Satana Mdyelekezi. Pofuna kuti anthu akhulupilile zimenezi, iye ndi viŵanda vake amayesa-yesa kucititsa anthu kuganiza kuti matenda ndi mavuto ena amabwela cifukwa ca mizimu ya akufa. Ni zoona kuti viŵanda vimabweletsa mavuto ena. Ndiponso ni zoona kuti mavuto ena si viŵanda vimene vimacititsa. Koma si zoona kuti anthu akufa angatibweletsele mavuto.

16 Pali njila inanso imene viŵanda vimayesa-yesa kucititsa anthu kuganiza kuti zimene Baibo imakamba za akufa si zoona. Vimaputsitsa anthu kuti ayambe kuganiza kuti aonana ndi munthu wakufa kapena kukamba naye. Viŵanda vimacita zimenezi kupitila m’masomphenya, maloto, anthu olankhula ndi mizimu, kapena njila zina. Ngakhale zili conco, anthu ameneo sakamba ndi akufa iyai, koma amakamba ndi viŵanda vimene vimanamizila kukhala anthu amene anafa. Ndiye cifukwa cake Yehova amatsutsilatu anthu amene amalankhula ndi mizimu ndi amene amafunsila kwa akufa.—Deuteronomo 18:10-12; Zekariya 10:2.