Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBALI 6

Kodi Mulungu Amavomeleza Zipembedzo Zonse?

Kodi Mulungu Amavomeleza Zipembedzo Zonse?

1. Malinga ndi Mau a Mulungu, kodi mitundu iŵili yokha ya zipembedzo zimene zilipo ndi iti?

YESU anakamba kuti: “Loŵani pacipata copapatiza. Pakuti mseu waukulu ndi wotakasuka ukupita kucionongeko, ndipo anthu ambili akuyenda mmenemo. Koma cipata coloŵela kumoyo n’copapatiza komanso mseu wake ndi wopanikiza, ndipo amene akuupeza ndi oŵelengeka.” (Mateyu 7:13, 14) Apa Mau a Mulungu akuonetsa kuti pali zipembedzo mitundu iŵili: cina coona ndi cina conama; cina cabwino, cina coipa; cina cimapita kumoyo ndi cina cimapita kucionongeko.

2. Kodi Malemba amaonetsa bwanji kuti si zipembedzo zonse zimene Mulungu amakondwela nazo?

2 Anthu ena amaganiza kuti Mulungu amakondwela ndi zipembedzo zonse. Malemba otsatila amaonetsa kuti zimenezi si zoona:

  • “Ana a Isiraeli anayambanso kucita zoipa pamaso pa Yehova, ndipo anayamba kutumikila Abaala, zifanizilo za Asitoreti, milungu ya ku Siriya, milungu ya ku Sidoni, milungu ya ku Mowabu, milungu ya ana a Amoni ndi milungu ya Afilisiti. Motelo io anasiya Yehova ndipo sanam’tumikile. Pamenepo mkwiyo wa Yehova unayakila ana a Isiraeli.” (Oweruza 10:6, 7) Ngati tilambila mafano kapena milungu ina m’malo mwa kulambila Mulungu woona, Yehova sadzakondwela ndi ife.

  • “Anthu awa amandilemekeza ndi milomo yokha, koma mitima yao ili kutali ndi ine. Amandipembedza pacabe cifukwa amaphunzitsa malamulo a anthu ngati ziphunzitso za Mulungu.” (Maliko 7:6, 7) Ngati anthu amene amakamba kuti amalambila Mulungu amaphunzitsa za m’maganizo mwao osati za mu Baibo, kulambila kwao ni kwacabe. Mulungu savomeleza kulambila kumeneko.

  • “Mulungu ndiye Mzimu, ndipo onse omulambila ayenela kumulambila motsogoleledwa ndi mzimu ndi coonadi.” (Yohane 4:24) Kulambila kwathu kuyenela kugwilizana ndi coonadi ca Mau a Mulungu.

Zipatso za Cipembedzo Conama

3. Kodi njila imodzi yosiyanitsila cipembedzo coona ndi conama ni iti?

3 Kodi tingadziŵe bwanji kuti Mulungu amakondwela kapena samakondwela ndi cipembedzo? Yesu anati: “Mtengo ulionse wabwino umabala zipatso zabwino, koma mtengo ulionse wovunda umabala zipatso zopanda pake . . . Mudzawazindikila ndi zipatso zao.” Mu mau ena, ngati cipembedzo ndi cocokela kwa Mulungu, cimabala zipatso zabwino; koma ngati cipembedzo ndi cocokela kwa Satana cimabala zipatso zoipa.—Mateyu 7:15-20.

4. Kodi olambila Yehova amaonetsa khalidwe liti?

4 Cipembedzo coona cimabala anthu amene amakondana ndipo amakonda anthu ena. Izi zili conco cifukwa cakuti Yehova ni Mulungu wacikondi. Yesu anakamba kuti: “Mwakutelo, onse adzadziŵa kuti ndinu ophunzila anga, ngati mukukondana.” Kodi zipembedzo zimacita bwanji pamfundo imenei ya kulambila koona?—Yohane 13:35; Luka 10:27; 1 Yohane 4:8.

5. Kodi buku lina linakamba ciani za malonda a akapolo mu Africa?

5 Ganizani za malonda ogulitsa akapolo mu Africa. Buku lakuti The New Encyclopædia Britannica inakamba kuti: “Anthu a mu Africa pafupi-fupi 18,000,000 anagwidwa ukapolo ndi kugulitsidwa pamalonda a akapolo amene Asilamu anali kucita kudutsa m’cipululu ca Sahara kupita ku Indian Ocean kuyambila m’ma 650 mpaka 1905. M’zaka za m’ma 1400 Azungu anayamba kucita malonda a akapolo kumadzulo kwa Africa, ndipo pofika mu 1867 anthu pakati pa 7,000,000 ndi 10,000,000 anawagwila ukapolo ndi kuwatumiza kumaiko a ku America.”

6. Kodi cipembedzo cinacita ciani pa malonda a akapolo?

6 Kodi cipembedzo cinacitapo ciani panthawi yovuta imenei mu Africa pamene amuna, akazi, ndi ana anali kuwagwila ndi kuwatenga ukapolo kusiya midzi yao ndi mabanja ao, kumangidwa macheni, kudindidwa ndi nsimbi zakupsa, ndi kugulitsidwa ngati ng’ombe? Mu Daily Nation ya ku Nairobi ku Kenya, Bethwell Ogot analemba kuti: “Akristu ndi Asilamu amakhulupilila kuti anthu onse ayenela kugwilizana, koma io ndi amene anayambitsa malonda a akapolo amene analimbikitsa tsankho. . . . Tiyenela kuvomeleza kuti Asilamu ndi Akristu, komanso maiko a Azungu ndi a ku Middle East ali ndi mlandu, ndiponso kuti cifukwa ca cikumbumtima cao cakufa, analekelela nkhanza zimene anthu mu Africa anavutika nazo kwadzaoneni zaka zambili-mbili.”

Cipembedzo Pankhondo

7. Kodi atsogoleli a zipembedzo acita ciani pankhondo?

7 Cipembedzo conama caonetsa zipatso zake zovunda, kapena kuti zoola, m’njila zina. Mwacitsanzo, ngakhale kuti Baibo imakamba kuti “uzikonda mnzako,” atsogoleli a zipembedzo padziko lonse amacilikiza ndi kulimbikitsa nkhondo.—Mateyu 22:39.

Cipembedzo conama catengamo mbali m’nkhondo ndi m’malonda a akapolo

8. (a) Kodi atsogoleli a zipembedzo analimbikitsa bwanji kupha anthu pankhondo za mu Africa? (b) Kodi pasita wina anakamba ciani za atsogoleli a zipembedzo ku Nigeria panthawi ya nkhondo yaciweniweni?

8 Anthu ambili amadziŵa kuti mu 1994, aviligo ndi ansembe ena anathandiza kupha anthu ku Rwanda. Ndiponso zipembedzo zatengamo mbali kwambili m’nkhondo zina mu Africa. Mwacitsanzo, pankhondo yaciweniweni imene inapha anthu ambili-mbili ku Nigeria, zipembedzo kumbali zonse ziŵili zinalimbikitsa anthu kumenya nkhondo. Pamene nkhondo imenei inapitiliza, pasita wina anakamba kuti atsogoleli a machechi “anaiŵala” nchito imene Mulungu anawapatsa. Anakambanso kuti: “Ife amene timakamba kuti ndife abusa a Mulungu tasanduka abusa a Satana.”

9. Kodi Baibo imakamba ciani za atumiki a Satana?

9 Baibo imakamba cimodzi-modzi, kuti: “Satana amadzisandutsa mngelo wa kuwala. Conco n’zosadabwitsa ngati atumiki ake naonso amadzisandutsa atumiki a cilungamo.” (2 Akorinto 11:14, 15) Mofanana ndi anthu oipa amene amanamizila kukhala anthu abwino, Satana amaputsitsa anthu kugwilitsila nchito atumiki, kapena kuti abusa, amene amaoneka ngati olungama koma nchito zao ni zoipa ndipo zipatso zao ni zoola.

10. Kodi atsogoleli a zipembedzo amukana bwanji Mulungu?

10 Padziko lonse lapansi, atsogoleli a zipembedzo amalalikila za cikondi, mtendele, ndi ubwino, koma ali ndi cidani, amacita nkhondo, ndi zinthu zoipa. Baibo imawafotokoza bwino. Imakamba kuti: “Amanena poyela kuti amadziŵa Mulungu, koma amamukana ndi zocita zao.”—Tito 1:16.

Cokani mu “Babulo Wamkulu”

11. Kodi Baibo imacifotokoza bwanji cipembedzo conama?

11 Tikaŵelenga buku la m’Baibo la Chivumbulutso, timaona zimene Yehova amaganiza pacipembedzo conama. M’buku limeneli, cipembedzo conama cimafotokozedwa kuti ndi mkazi wophiphilitsa, “Babulo Wamkulu.” (Chivumbulutso 17:5) Onani mmene Mulungu akufotokozela mkazi ameneyu:

  • “Hule lalikulu . . . limene mafumu a dziko lapansi anacita nalo dama.” (Chivumbulutso 17:1, 2) M’malo mokhulupilika kwa Mulungu, cipembedzo conama cimaloŵa m’ndale, ndipo nthawi zambili cimauza maboma zocita.

  • “Mwa iye munapezeka magazi a aneneli, a oyela, ndi a onse amene anaphedwa padziko lapansi.” (Chivumbulutso 18:24) Cipembedzo conama cazunza ndi kupha atumiki okhulupilika a Mulungu ndipo cili ndi mlandu wa kupha anthu mamiliyoni pankhondo.

  • “Anadzipezela ulemelelo ndi kusangalala ndi cuma.” (Chivumbulutso 18:7) Cipembedzo conama cili ndi cuma cambili, cimene atsogoleli ake amagwilitsila nchito kukhala ndi umoyo wa mwana alilenji.

  • “Mitundu yonse ya anthu inasoceletsedwa ndi zocita zako zamizimu.” (Chivumbulutso 18:23) Cifukwa ca ciphunzitso cake conama cakuti mzimu sumafa, cipembedzo conama catsegulila mpata mtundu ulionse wa zamizimu ndi matsenga, ndipo cimalimbikitsa anthu kuopa akufa ndi kulambila mizimu ya makolo.

12. Kodi Baibo imapeleka cenjezo lakuti bwanji pacipembedzo conama?

12 Pocenjeza anthu mwamphamvu kuti acoke m’cipembedzo conama, Baibo imakamba kuti: “Tulukani mwa iye anthu anga, ngati simukufuna kugaŵana naye macimo ake, ndiponso ngati simukufuna kulandila nao ina ya milili yake.”—Chivumbulutso 18:4, 5.

13. Kodi cimene cidzacitikila cipembedzo conama ndi anthu amene alimo n’ciani?

13 Posacedwapa, Babulo Wamkulu, ufumu wa padziko lonse wa zipembedzo zonama, adzaonongedwelatu. Baibo imakamba kuti: “M’tsiku limodzi, milili yake idzafika. Milili yakeyo ndiyo imfa, kulila, ndi njala. Ndipo adzanyekelatu ndi moto cifukwa Yehova Mulungu, amene anamuweluza, ndi wamphamvu.” (Chivumbulutso 18:8) Kuti tisalandileko ina ya milili yake, tiyenela kusiilatu cipembedzo conama, ndi kupewelatu miyambo, zikondwelelo, ndi zikhulupililo zimene Mulungu sakondwela nazo. Tiyenela kucita zimenezi mwamsanga. Moyo wathu uli pangozi!—2 Akorinto 6:14-18.