Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBALI 2

Kodi Tingadziŵe Bwanji Zoona za Mulungu?

Kodi Tingadziŵe Bwanji Zoona za Mulungu?

1, 2. Kodi n’citsanzo citi cimene cionetsa kuti pafunika kukhala njila imodzi yodziŵila zoona pankhani za cipembedzo?

KODI Mulungu tingam’dziŵe bwanji? Kodi tifunika kucita kuyang’ana m’ziphunzitso zambili-mbili za zipembedzo zonse? Sitingakwanitse zimenezi. Ngakhale ngati tingakwanitse, kodi tingadziŵe bwanji ciphunzitso coona?

2 Kukamba zoona, popeza kuti zimene anthu amakhulupilila za Mulungu zimasiyana kwambili, tifunika kupeza njila yodziŵila zeni-zeni imene anthu onse angavomeleze. Mwacitsanzo, tinene kuti anthu kumaliketi akukangana pa kutalika kwa nsalu. Wogulitsa akamba kuti nsalu ni mamita atatu, koma wogula akana kuti sinakwane mamita atatu. Kodi io angaleke bwanji kukangana? Afunika kupima nsalu imeneyo ndi tepu.

3. N’cifukwa ciani Baibo inalembedwa?

3 Kodi pali tepu yopimila, kapena kuti njila imodzi, yodziŵila zeni-zeni pankhani za cipembedzo? Inde ilipo, ndipo ni Baibo. Mulungu anakonza kuti Baibo ilembedwe kuti anthu kulikonse adziŵe zoona za iye. Makope okwana mabiliyoni apulintiwa. Baibo yatembenuzidwa, yonse kapena mbali yake, m’zitundu zopitilila 2,100. Pafupi-fupi munthu aliyense angaŵelenge zoona za Mulungu m’citundu cake.

4. Kodi Baibo imakamba za ciani?

4 Baibo ni mphatso yamtengo wapatali yocokela kwa Mulungu. Imafotokoza zinthu zimene sitingadziŵe popanda io. Imatiuza za amene amakhala kumalo a mizimu. Imatidziŵitsa maganizo a Mulungu, umunthu wake, ndi colinga cake. Imasimba za zocita zake ndi anthu pazaka masauzande. Imakamba zinthu zimene zidzacitika mtsogolo. Ndipo imaonetsa mmene tingapezele njila ya kumoyo wamuyaya.

Cimene Muyenela Kukhulupilila Baibo

5. Kodi n’citsanzo citi cimene cionetsa kuti Baibo imagwilizana ndi sayansi?

5 Pali zifukwa zambili zimene tiyenela kukhulupilila kuti Baibo ndi Mau a Mulungu. Cifukwa cina n’cakuti Baibo imagwilizana ndi sayansi. Kale anthu padziko lonse lapansi anali kuganiza kuti dziko lapansi linakhazikika pa cinacake. Mwacitsanzo, kumadzulo kwa Africa anthu anali kukhulupilila kuti njoka yopombana pamwamba pa dziko lapansi nthawi 3,500 ndi pansi pake nthawi 3,500, ndi imene inali kugwila dziko lapansi. Koma wolemba Baibo zaka zoposa 3,500 zapitazo analemba zogwilizana ndi sayansi kuti Mulungu “anakoloŵeka dziko lapansi m’malele.”—Yobu 26:7.

6. Kodi umboni wamphamvu koposa wakuti Baibo inacokela kwa Mulungu ni uti?

6 Umboni wamphamvu koposa wakuti Baibo inacokela kwa Mulungu ndi mbili yake yodalilika yokambilatu zinthu za kutsogolo. Mulungu amasiyana ndi aneneli aumunthu cifukwa iye amadziŵa za kutsogolo; zonse zimene iye amakamba zimacitika.

7. Kodi maulosi ena a m’Baibo amene anakwanilitsika m’nthawi zakale ni ati?

7 Maulosi ambili-mbili a m’Baibo anakwanilitsika m’nthawi zakale. Mwacitsanzo, kukali zaka 700, Baibo inanena mosalakwitsa kuti Yesu adzabadwila m’tauni ya Betelehemu, ndipo ndi zimene zinacitika. (Mika 5:2; Mateyu 2:3-9) Kuonjezela pa maulosi ena ambili onena za Yesu, Baibo inakambilatu kuti iye adzabadwa kwa namwali ndipo adzapelekedwa ndi ndalama 30 za siliva. Izi ni zimene zinacitika. Kukamba zoona, kulibe munthu amene akanakambilatu zimenezi!—Yesaya 7:14; Zekariya 11:12, 13; Mateyu 1:22, 23; 27:3-5.

8. Kodi maulosi ena a m’Baibo amene akukwanilitsika masiku ano ni ati, nanga akuonetsa ciani?

8 Maulosi ambili a m’Baibo akukwanilitsika m’nthawi yathu. Ena a io ndi awa:

  • “Mtundu udzaukilana ndi mtundu wina, ndipo ufumu udzaukilana ndi ufumu wina. Kudzacitika zivomezi zamphamvu, ndipo kudzakhala milili ndi njala m’malo osiyana-siyana.”—Luka 21:10, 11.

  • Kudzakhala “kuonjezeka kwa kusamvela malamulo.”—Mateyu 24:12.

  • “Masiku otsiliza . . . anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, . . . osamvela makolo, . . . osadziletsa, oopsa, osakonda zabwino, . . . odzitukumula ndiponso onyada, okonda zosangalatsa, m’malo mokonda Mulungu.”—2 Timoteyo 3:1-5.

Kodi simuvomeleza kuti zinthu izi ni zimene zicitika masiku ano? Maulosi a m’Baibo amakamba zoona ndipo amakwanilitsika ndendende. Zimenezi zionetsa kuti Baibo ni buku lapadela. Ndi Mau a Mulungu.—2 Timoteyo 3:16.

Kodi Baibo Inasinthidwa?

9, 10. N’ciani cionetsa kuti Mulungu sanalole anthu kusintha Baibo?

9 Tinene kuti inu muli ndi fakitale ndipo mwaika malamulo pabodi kuti anchito anu akazitsatila. Ngati mdani wanu wasintha zimene munalemba, kodi mungacite ciani? Kodi simungakonze zimene iye anasintha? N’cimodzi-modzi ndi Mulungu. Iye samalola anthu kusintha coonadi ca m’Mau ake, Baibo.

10 Anthu amene ayesa kusintha ziphunzitso za m’Mau a Mulungu alephela. Tikayelekeza Baibo imene tili nayo lelo ndi makope akale a Baibo, zimafanana. Zimenezi zionetsa kuti Baibo sinasinthidwe ngakhale kuti papita zaka zambili-mbili.