Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBALI 3

Ndani Amene Ali ku Malo a Mizimu?

Ndani Amene Ali ku Malo a Mizimu?

1. Kodi cipembedzo ca makolo cimafanana bwanji ndi phili?

ZIKHULUPILILO za cipembedzo ca makolo mu Africa zili ngati phili. Pamwamba pake peni-peni pali Mulungu, amene ali ndi mphamvu zonse zauzimu. M’mbali mwa phili muli milungu ing’ono-ing’ono, kapena kuti mizimu, imene ndi atumiki a Mulungu. Milungu imeneyi ili pamodzi ndi mizimu ya makolo, imene imakumbukila apabanja amene ali padziko lapansi ndipo imawathandiza. Munsi mwa phili muli mphamvu za kuuzimu zocepelako izi: matsenga, kuombedza, ndi ufiti.

2. Kodi mwambi wina wa mu Africa umaonetsa bwanji kuti zikhulupililo za makolo zili ndi mphamvu m’zipembedzo?

2 Zikhulupililo za makolo zili ndi mphamvu kwambili m’zipembedzo zina za mu Africa. Mwambi wina wa mu Africa umati: “Kukhala m’Cipembedzo (Cikristu kapena Cisilamu) sikumatiletsa kulambila milungu ya makolo.”

3. Kodi ni kuti kumene tingaphunzile zeni-zeni za amene ali kumalo a mizimu?

3 Kodi zikhulupililo za makolo za mu Africa ni zoona? Baibo imatiuza zeni-zeni za amene ali kumalo a mizimu.

Yehova, Mulungu Woona

4. Kodi zipembedzo zazikulu mu Africa zimagwilizana pankhani iti?

4 M’zipembedzo zonse zitatu zazikulu mu Africa amakhulupilila kuti Mulungu aliko ndi kuti ni wam’mwamba-mwamba. Baibo imafotokoza kuti iye ndi “Mulungu wa milungu ndi Mbuye wa ambuye. Iye ndi Mulungu wamkulu, wamphamvu ndi woopsa.” (Deuteronomo 10:17) Asilamu nao amakhulupilila mwa Mulungu mmodzi wam’mwamba-mwamba. Ponena za cipembedzo ca makolo mu Africa, Pulofesa Geoffrey Parrinder anakamba kuti: “Anthu ambili mu Africa amakhulupilila mwa Mulungu wam’mwamba-mwamba, tate wa milungu ndi anthu, mlengi wa cilengedwe conse.”

5. Kodi maina ena amene anthu amachulila Mulungu ni ati?

5 Koma, ngakhale kuti cikhulupililo mwa Mulungu n’cofala, anthu ambili sam’dziŵa bwino-bwino Mulungu. Kuti tidziŵe munthu winawake, coyamba timafunika kudziŵa dzina lake. Pankhani yakuti dzina la Mulungu ndani, pali cisokonezo m’zipembedzo. M’machechi acikristu, ambili amakamba kuti iye ni Mulungu, dzina laudindo limene limatanthauza “Wamphamvu.” Asilamu amati ndi Allah. M’zipembedzo za makolo, amagwilitsila nchito maina osiyana-siyana a Wam’mwamba-mwamba malinga ndi citundu cao. M’buku lake lakuti Concepts of God in Africa, John S. Mbiti analemba maina wamba ndi maina audindo a Mulungu acifilika oposa 500. Mwacitsanzo, m’Ciyoruba (ku Nigeria), Mulungu ni Olodumare; Akikuyu (ku Kenya) amanena kuti ni Ngai; ndipo Azulu (ku South Africa) amati ni Unkulunkulu.

6, 7. Kodi dzina la Mulungu ndani, nanga tidziŵa bwanji?

6 Nanga Mulungu mwiniwake amakamba kuti bwanji pa dzina lake? Pamene Mulungu anauza Mose kuti akatulutse Aisiraeli mu Iguputo, Mose anafunsa kuti: “[Ndikafika] kwa ana a Isiraeli ndi kuwauza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ io n’kundifunsa kuti, ‘Dzina lake ndani?’ Ndikawayankha kuti ciani?”—Ekisodo 3:13.

7 Mulungu anayankha kuti: “Zimene ukauze ana a Isiraeli ndi izi, ‘Yehova Mulungu wa makolo anu . . . wandituma kwa inu.’ Limeneli ndilo dzina langa mpaka kale-kale, ndipo ndico condikumbukilila ku mibadwo-mibadwo.” (Ekisodo 3:15) Dzina la Mulungu limeneli limapezeka nthawi zopitilila 7,000 m’Baibo yonse, ngakhale kuti otembenuza Baibo ena alicotsa ndi kuikamo maina audindo monga “Mulungu” kapena “Ambuye.”

8. Kodi Yehova ndi wabwanji, nanga tiyenela kucita ciani kuti iye atiyanje?

8 Kodi Yehova ndi wabwanji maka-maka? Iye ni mzimu, ni wamphamvuyonse, ni waulemelelo. Ndi wam’mwamba-mwamba, wosayelekezeka, ndipo kulibe wolingana naye. (Deuteronomo 6:4; Yesaya 44:6) Yehova anauza Mose kuti: “Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wofuna kuti anthu azidzipeleka kwa ine ndekha.” M’mau ena, ngati tifuna kuti Yehova atiyanje, tiyenela kulambila iye yekha cabe. Iye safuna kuti tizilambila cina ciliconse kapena munthu wina aliyense.—Ekisodo 20:3-5.

Yesu Kristu, Mfumu ya Ufumu wa Mulungu

9. N’cifukwa ciani tikukamba kuti Yesu si wolingana ndi Yehova?

9 Masiku ano pali msokonezo waukulu ponena za Yesu. Ambili m’Machechi Acikristu amakhulupilila kuti Yesu ali mbali ya Utatu “Woyela.” Koma Baibo siphunzitsa kuti Mulungu ni anthu atatu mwa munthu mmodzi. Ndipo siphunzitsa kuti Yesu ni wolingana ndi Yehova. Yesu mwiniwake anakamba kuti: “Atate ndi wamkulu kuposa ine.”—Yohane 14:28.

10. Kodi Yesu anali kuti asanabwele padziko lapansi?

10 Baibo imaphunzitsa kuti Yesu asanakhale munthu padziko lapansi, anali colengedwa camphamvu cauzimu kumwamba. Yehova analenga angelo kumwamba ngati mmene analengela Adamu ndi Hava padziko lapansi. Yesu anali mngelo woyamba kulengedwa ndi Yehova.—Yohane 17:5; Akolose 1:15.

11. Kodi zinacitika bwanji kuti Yesu abadwe munthu?

11 Pafupi-fupi zaka 2,000 zapitazo, Yehova anasamutsila moyo wa colengedwa cauzimu cimeneci m’mimba mwa namwali Mariya. Mngelo Gabirieli anauza Mariya kuti: “Udzakhala ndi pakati ndipo udzabeleka mwana wamwamuna. Udzam’patsa dzina lakuti Yesu. Iye adzalamulila monga mfumu . . . , moti ufumu wake sudzatha konse.”—Luka 1:31, 33. *

12. Kodi cifukwa coyamba cimene Yesu anabwelela padziko lapansi n’ciani?

12 Motelo Yesu anabadwa, kukula, ndi kuphunzitsa anthu za cifunilo ca Yehova ndi colinga cake. Iye anauza bwanamkubwa wa Roma kuti: “Cimene ndinabadwila, ndiponso cimene ndinabwelela m’dziko, ndico kudzacitila umboni coonadi.” (Yohane 18:37) Mwa kuyang’ana zimene Yesu anaphunzitsa, tingadziŵe zoona ponena za cifunilo ca Mulungu ndi colinga cake. Tingadziŵe zimene tiyenela kucita kuti Mulungu atiyanje.

13. Kodi cifukwa caciŵili cimene Yesu anabwelela padziko lapansi n’ciani?

13 Cifukwa caciŵili cimene Yesu anabwelela m’dziko cinali cakuti apeleke moyo wake waumunthu dipo kamba ka anthu onse. (Mateyu 20:28) Anacita zimenezi kuti timasuke ku uchimo umene tinalandila kwa kholo lathu Adamu. Cifukwa ca zimenezi, n’zotheka kwa ife kukhala ndi moyo wamuyaya. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asaonongeke, koma akhale ndi moyo wamuyaya.”—Yohane 3:16.

14. (a) Kodi cimene cinacitika kwa Yesu pambuyo pa imfa yake n’ciani? (b) Kodi Yesu ali ndi udindo wabwanji kumwamba?

14 Pambuyo pa imfa yake, Yesu anaukitsidwa kupita kumwamba, kumene anakakhalanso ndi moyo monga colengedwa cauzimu camphamvu. (Machitidwe 2:32, 33) M’kupita kwa nthawi, Yehova anamupatsa “ulamulilo, ulemelelo, ndi ufumu kuti anthu a mitundu yosiyana-siyana, olankhula zinenelo zosiyana-siyana azimutumikila.” (Danieli 7:13, 14) Yesu waikidwa kukhala Mfumu yamphamvu; iye ni Mfumu ya boma la Yehova la kumwamba. Kwatsala pang’ono kuti iye aonetse mphamvu yake padziko lonse lapansi.

Angelo, Atumiki a Mulungu

15. Kodi angelo analengedwa liti, nanga anawalengela kuti?

15 Yehova ndi Yesu si amene cabe amakhala kumalo a mizimu. Yehova analenga zolengedwa zina zauzimu, angelo. Mmodzi wa io ni Gabirieli, amene analankhula ndi Mariya. Angelo sanayambile kukhala ndi moyo padziko lapansi ngati anthu. Iwo anacita kulengedwa kumwamba, kale kwambili anthu asanalengedwe padziko lapansi. (Yobu 38:4-7) Angelo aliko mamiliyoni ambili-mbili.—Danieli 7:10.

Angelo okhulupilika amakana kulambilidwa

16. N’cifukwa ciani ife anthu sitiyenela kulambila angelo?

16 Angelo okhulupilika safuna kuti ife tiziwalambila. Kaŵili konse pamene mtumwi Yohane anayesa kulambila angelo, io anamudzudzula, kuti: “Samala! Usatelo ai! . . . Lambila Mulungu.”—Chivumbulutso 19:10; 22:8, 9.

17. Kodi ni umboni uti umene uonetsa kuti angelo amachinjiliza atumiki a Mulungu, nanga n’cifukwa ciani zimenezi zili zokhazika mtima pansi?

17 Angelo analeka kuonekela kwa anthu a Mulungu padziko lapansi, ngati mmene anacitila potulutsa atumwi a Yesu m’ndende. (Machitidwe 5:18, 19) Ngakhale zili conco, ngati timalambila Yehova motsatila Mau ake, Baibo, tidziŵe kuti magulu a angelo amphamvu ndi osaoneka a Mulungu, adzatichinjiliza. Baibo imakamba kuti: “Mngelo wa Yehova amamanga msasa mozungulila onse oopa Mulungu, ndipo amawapulumutsa.” (Salimo 34:7; 91:11) N’cifukwa ciani zimenezi ni zokhazika mtima pansi? Cifukwa cakuti kumalo a mizimu kulinso adani oopsa amene amafuna kutiononga.

Satana, Mdani wa Mulungu

18. (a) N’cifukwa ciani mngelo wina anapandukila Mulungu? (b) Kodi mngelo wopanduka ameneyu anapatsidwa maina ati?

18 Si angelo onse a Mulungu amene anakhala okhulupilika. Ena anamupandukila. Anadzipanga okha kukhala adani a Mulungu ndi adani a anthu padziko lapansi. Kodi zimenezi zinacitika bwanji? Angelo onse amene Yehova analenga anali olungama ndi abwino. Koma mmodzi wa ana auzimu angwilo amenewa anafuna kuti anthu akazimulambila ndipo anatsatila cikhumbo coipa cimeneci. Colengedwa cauzimu cimeneco cinapatsidwa dzina lakuti Satana, limene limatanthauza “Wotsutsa [Mulungu].” Ndipo dzina lake lina ndi Mdyelekezi, kutanthauza “Wamisece,” cifukwa cakuti amanamizila Yehova vabodza.

19. N’cifukwa ciani Satana anazunza Yobu, ndipo anamuzunza bwanji?

19 Satana amayesa kukakamiza anthu kuti agwilizane naye kupandukila Mulungu. Ganizilani zimene anacita kwa Yobu, mtumiki wokhulupilika wa Mulungu. Yobu anali munthu wolemela kwambili. Anali ndi nkhosa (mbelele) 7,000, ngamila 3,000, ng’ombe zikazi ndi zimuna 1,000, ndi abulu akazi 500. Analinso ndi ana 10 ndi anchito ambili-mbili. Satana anayambila kupha ziŵeto za Yobu ndi anchito ake. Ndiyeno anatuma “cimphepo” cimene cinagwetsa nyumba ndi kupha ana onse a Yobu. Pambuyo pake, Satana anazunza Yobu ndi “zilonda zopweteka, kuyambila kuphazi mpaka kumutu.”—Yobu 1:3-19; 2:7.

20. (a) Kodi Yobu analandila mphotho yabwanji cifukwa ca kukhulupilika kwake? (b) Ngakhale kuti Yobu anali wokhulupilika kwa Mulungu, kodi Satana acita ciani kwa anthu ena ambili?

20 Ngakhale kuti Yobu anakumana ndi ciyeso copweteka cimeneci, anakhala wokhulupilika kwa Mulungu. Conco Yehova anamucilitsa ndipo “anayamba kupatsa Yobu zonse zimene anali nazo, kuwilikiza kaŵili.” (Yobu 42:10) Satana analephela kuononga mtima wosagaŵanika wa Yobu, koma akwanitsa kucotsa anthu ena ambili kwa Mulungu. Baibo imakamba kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”—1 Yohane 5:19.

21. (a) Kodi Satana anaonetsa bwanji kuti amafuna kulambilidwa? (b) N’cifukwa ciani Yesu anakana kulambila Satana?

21 Satana amafuna kuti tikazimulambila. Zimenezi zinaoneka kwambili pamene iye anayesa Yesu zaka pafupi-fupi 2,000 zapitazo. Baibo imakamba kuti: “Mdyelekezi anamutenganso [Yesu] ndi kupita naye paphili lalitali kwambili, ndipo anamuonetsa maufumu onse a padziko ndi ulemelelo wao. Kenako anamuuza kuti: “Ndikupatsani zinthu zonsezi ngati mutangogwada pansi n’kundiwelamila kamodzi kokha.” Yesu anakana, kuti: “Coka Satana! Pakuti Malemba amati, ‘Yehova Mulungu wako ndi amene uyenela kumulambila, ndipo uyenela kutumikila iye yekha basi.’” (Mateyu 4:8-10) Yesu anali kudziŵa bwino lamulo la Yehova, ndipo sanacite zimene Satana anali kufuna.

Viŵanda, Mizimu Yoipa

22. Kodi viŵanda vinacita ciani kwa anthu?

22 Angelo ena anagwilizana ndi Satana kupandukila Mulungu. Angelo amenewa, amene ndiye viŵanda, ni adani a anthu padziko lapansi. Iwo ali ndi nkhanza ndipo ni oipa mtima. Kale, io anacititsa anthu ena kukhala osalankhula ndi osaona. (Mateyu 9:32, 33; 12:22) Anadwalitsa anthu ena kapena kuwafunthitsa. (Mateyu 17:15, 18; Maliko 5:2-5) Iwo anali kuzunza ngakhale ana.—Luka 9:42.

23. (a) Kodi mizimu yoipa imafuna ciani kwa anthu? (b) Kodi Satana ndi viŵanda vake aputsitsa anthu kuti azicita ciani?

23 Mofanana ndi Satana, mizimu yoipa imenei imafuna kulambilidwa. M’malo mwa kukana kulambilidwa ndi anthu—cifukwa codziŵa kuti Yehova yekha ni amene ayenela kulambilidwa—mizimu yoipa imakhumbila kwambili kulambilidwa, imacita kufuna-funa amene angailambile, ndipo imalimbikitsa anthu kuilambila. Mwa kugwilitsila nchito macenjela, mabodza, ndi kuopseza anthu, Satana ndi viŵanda vake amacititsa anthu kuwalambila. Koma si anthu ambili amene amadziŵa kuti akulambila Satana ndi viŵanda vake. Anthu ambili angadabwe ndi kucita mantha kudziŵa kuti cipembedzo cao cimalemekeza Satana. Koma Baibo imacenjeza kuti: “Zinthu zimene mitundu ina imapeleka nsembe imazipeleka kwa ziŵanda, osati kwa Mulungu.”—1 Akorinto 10:20.

24. Kodi njila ina ya macenjela imene Satana amagwilitsila nchito kuputsitsila anthu ndi iti?

24 Njila ina imene Satana ndi viŵanda vake amaputsitsila anthu kuti aziwalambila ni ya kufalitsa mabodza ponena za anthu amene anafa. Tiyeni tione zimene Baibo imaphunzitsa pankhani iyi.

^ ndime 11 Koran imakamba za kubadwa kwa Yesu kozizwitsa pa Surah 19 (Mariya). Imati: “Tinatumiza mzimu Wathu kwa [Mariya] wooneka ngati munthu wamkulu. Ndipo pamene iye anauona anati: ‘Wacifundoyo andichinjilize kwa inu! Ngati mumaopa Ambuye, mundisiye ndi kupitiliza ulendo wanu.’ Koma mzimu unayankha kuti: ‘Ndine mthenga wa Ambuye wako, ndipo ndabwela kukupatsa mwana woyela.’ Iye anayankha kuti: ‘Ndingabale bwanji mwana ine namwali wosadziŵa mwamuna?’ Poyankha mzimu unati: ‘Ndi cifunilo ca Ambuye. Izi si zovuta kwa Iye. Ambuye ati: “Mwana ameneyo adzakhala cizindikilo kwa anthu onse ndi dalitso locokela kwa Ife. Uthenga Wathu ndi umeneo.”’”