Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

MBALI 9

True Religion Can Benefit You Forever!

True Religion Can Benefit You Forever!

1. Kodi cimene cidzacitika n’ciani ngati ‘tiyandikila Mulungu’?

YEHOVA amakonda anthu amene amamutumikila. Ngati mumalambila Yehova, adzakudalitsani panthawi ino ndi mtsogolo. Baibo imakamba kuti: “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.”—Yakobo 4:8.

2. Kodi tingamuyandikile bwanji Mulungu, ndipo zimenezi zimakhudza bwanji mapemphelo athu?

2 Kuti muyandikile Mulungu, muyenela kuphunzila Mau ake ndi kutsatila zimene amanena. Ngati mupemphela mogwilizana ndi cifunilo cake, Yehova adzamvela mapemphelo anu ndi kuwayankha. Mtumwi Yohane analemba kuti: ‘Timamudalila [Mulungu] kuti ciliconse cimene tingamupemphe mogwilizana ndi cifunilo cake, amatimvela. Komanso, popeza timadziŵa kuti amatimvela tikapempha ciliconse, timakhala ndi cikhulupililo kuti tilandila zinthu zimene tamupempha.’—1 Yohane 5:14, 15.

3-7. Kodi tingapeze bwanji nzelu yocokela kwa Mulungu, nanga ingatithandize bwanji?

3 Ndiponso, pamene muyandikila Mulungu, adzakupatsani nzelu zokuthandizani kulimbana ndi mavuto pa umoyo wanu wa tsiku ndi tsiku. Baibo imakamba kuti: “Ngati wina akusoŵa nzelu, azipempha kwa Mulungu.”—Yakobo 1:5.

4 Kodi nzelu yocokela kwa Mulungu ingakuthandizeni bwanji? Coyamba, ingakuthandizeni kudziŵa zinthu zimene Yehova sakondwela nazo. Mungadziŵenso cifukwa cake zinthu zimenezi zili zoipa ndiponso cimene muyenela kucita kuti muzipewe. Cidziŵitso cimeneci cingakucinjilizeni ku mavuto amene anthu ambili amakumana nao. Mwacitsanzo, kumvela uphungu wa Mulungu wakuti tizikhala oyela m’makhalidwe kumacinjiliza anthu a Mulungu ku zinthu monga mimba zapathengo, matenda akatengela, ndiponso mavuto a m’cikwati kapena kulekana.

5 Kodi nzelu yocokela kwa Mulungu ingakuthandizeninso bwanji? Ingakuthandizeni kukhala ndi umoyo wabwino kwambili. Ingakuthandizeninso kupanga zosankha zanzelu pankhani zofunika, monga kuseŵenzetsa bwino ndalama. Ndipo mudzakhala ndi zolinga zaphindu ndi kupewa zolinga zimene zilibe phindu.

6 Nzelu yocokela kwa Mulungu ingakuthandizeni kukhala bwino ndi anthu ena. Mudzakhala ndi umoyo wapabanja wokondweletsa. Mudzakhala mabwenzi a pamtima ndi anthu ena, ndipo anthu adzayamba kukupatsani ulemu, kuphatikizapo anthu amene satumikila Mulungu.

7 Ndiponso, nzelu yocokela kwa Mulungu idzakuthandizani kukhala ndi kaonedwe kabwino pa umoyo wanu. Idzakuthandizani kulimbana ndi mavuto osiyana-siyana. Ndiponso, simudzakhala ndi nkhawa yaikulu poganiza za kutsogolo. Zimenezi zidzakuthandizani kusavutika maganizo ndi kukhala athanzi.—Miyambo 14:30; Yesaya 48:17.

8. Kodi simudzaopa ciani ngati mutumikila Mulungu?

8 Ngati mutumikila Mulungu woona, mudzaleka kuopa zinthu zimene anthu amene satumikila Mulungu amaopa. Mwacitsanzo, cifukwa ca kudziŵa kuti akufa ali kumanda ndipo si amoyo, simudzawaopa. Cifukwa cakuti muli ndi cikhulupililo cakuti Mulungu adzaukitsa akufa, simudzaopa kufa. Ndipo cifukwa ca kudziŵa kuti Mulungu ni wamphamvuyonse, simudzaopa mfiti kapena matsenga.—Yohane 8:32.

Olungama Adzalandila Dziko Lapansi

9-11. Kodi ndani adzakhala m’Paladaiso, nanga ndani amene sadzakhalamo?

9 Ngati muyandikila Mulungu, simudzaopa za kutsogolo. Monga mmene taonela, Baibo inakambilatu za mavuto amene akucitika m’dziko masiku ano. Yehova amatiuza kuti zinthu zimenezi ni zakanthawi; posacedwa Ufumu wa Mulungu udzasandutsa dziko lapansi kukhala paladaiso.—Luka 21:10, 11, 31; 23:43.

10 Anthu okha amene amayandikila Yehova ndi kumutumikila, ndi amene adzakhala m’Paladaiso. Baibo imakamba kuti: “Patsala kanthawi kocepa, woipa sadzakhalakonso. Udzayang’ana pamene anali kukhala, ndipo sadzapezekapo. Koma anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendele woculuka.”—Salimo 37:10, 11.

11 Amene amacita nthota ndi kukana kumvela malamulo olungama a Mulungu adzafa. (2 Atesalonika 1:8, 9) Iwo sadzakhalakonso. Adzafa imfa yosatha pamodzi ndi Satana ndi viŵanda vake. (Chivumbulutso 20:10, 14) Koma amene amaphunzila za Yehova ndi kumutumikila adzasangalala ndi mtendele woculuka m’Paladaiso padziko lapansi.

Umoyo Wabwino Mtsogolo!

12. Kodi Baibo imakamba kuti umoyo kutsogolo udzakhala wabwanji?

12 Yehova wasungila anthu amene amamukonda zinthu zabwino kwambili! Onani mmene Mau ake amafotokozela umoyo umene udzakhala m’Paladaiso padziko lapansi:

  • Zakudya zambili-mbili: “Padziko lapansi padzakhala tiligu wambili [kutanthauza zakudya]. Pamwamba pa mapili padzakhala tiligu woculuka.”—Salimo 72:16.

  • Nyumba zabwino: “Iwo adzamanga nyumba n’kukhalamo.”—Yesaya 65:21.

  • Nchito yokondweletsa: “Anthu anga osankhidwa mwapadela adzapindula mokwanila ndi nchito ya manja ao. Sadzagwila nchito pacabe.”—Yesaya 65:22, 23.

  • Sikudzakhala kudwala: “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: “Ndikudwala.”—Yesaya 33:24.

  • Sikudzakhala kulemala: “Panthawi imeneyo, maso a anthu akhungu [osaona] adzatsegulidwa, ndipo makutu a anthu ogontha [osamva] adzayamba kumva. Panthawiyo, munthu wolumala [wolemala] adzakwela phili ngati mmene imacitila mbawala yamphongo. Lilime la munthu wosalankhula lidzafuula mokondwa.”—Yesaya 35:5, 6.

  • Sikudzakhala zoŵaŵa, kulila, imfa: “[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwao, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”—Chivumbulutso 21:4.

  • Sikudzakhala nkhondo: “[Mulungu] akuletsa nkhondo mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.”—Salimo 46:9.

  • Moyo wamuyaya: “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Salimo 37:29.

13. Kodi ndani cabe amene angasandutse dziko kukhala paladaiso, nanga n’cifukwa ciani mwayankha conco?

13 Anthu sangakwanitse kucita zinthu zimenezi, koma Yehova ali ndi mphamvu yocita zinthu zilizonse zimene akamba kuti adzacita. Palibe cimene cingamuletse kucita zimene afuna. Baibo imakamba kuti: “Zimene Mulungu wanena, sizilepheleka.”—Luka 1:37.

14. Kodi njila yopita kumoyo wamuyaya mungaipeze bwanji?

14 Yehova kupitila mwa Mboni zake, akupatsa anthu mwai wakuti ‘aloŵe pacipata copapatiza’ ndi kuyenda panjila yopita kumoyo wamuyaya. Inunso landilani ciitano cimeneci kuti mukhale osangalala. Loŵani m’cipembedzo coona kuti mukalandile madalitso a Yehova osatha!—Mateyu 7:13, 14.

[Mafunso Ophunzilila]