Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 17

Mwayi wa Pepemphelo

Mwayi wa Pepemphelo

“Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi” amafuna kumvela mapemphelo athu.—Salimo 115:15

1, 2. Pemphelo ni mphatso yapadela cifukwa ciani? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kudziŵa zimene Baibulo imaphunzitsa pa nkhani ya pemphelo?

DZIKO LA PANSI ni ling’ono kwambili tikaliyelekezela ndi cilengedwe conse. Yehova akayang’ana pa dziko lapansi, anthu a mitundu yonse amaoneka monga kadontho cabe ka madzi. (Salimo 115:15; Yesaya 40:15) Ngakhale kuti tili aang’ono conco potiyelekezela ndi cilengedwe conse, lemba la Salimo 145:18, 19 limati: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanila pa iye. Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’coonadi, ndipo anthu amene amamuopa adzawacitila zokhumba zawo, adzamva kufuula kwawo kopempha thandizo ndipo adzawapulumutsa.” Inde, umenewu ni mwayi wa mtengo wapatali umene tili nawo. Yehova, Mlengi wamphamvuzonse, amafuna kukhala nafe pafupi ndi kumvetsela mapemphelo athu. Kukamba zoona, pemphelo ni mwayi ukulu, ndiponso ni mphatso ya mtengo wapatali imene Yehova watipatsa.

2 Koma kuti Yehova amvele mapemphelo athu, tiyenela kukamba naye m’njila imene iye amavomeleza. Kuti tiidziŵe njila imeneyo, tiyeni tiphunzile zimene Baibulo imakamba pa nkhani ya pemphelo.

N’CIFUKWA CIANI TIYENELA KUMAKAMBITSANA NDI YEHOVA M’PEMPHELO?

3. N’cifukwa ciani muyenela kumakambitsana ndi Yehova m’pemphelo?

3 Yehova amafuna kuti inu muzikamba naye m’pemphelo. Timadziŵa bwanji zimenezi? Ŵelengani Afilipi 4: 6, 7. Limeneli ni pempho lacikondi kwambili. Ganizani cabe! Wolamulila wa cilengedwe conse amakuganizilani, ndipo amafuna kuti muzimuuza za kukhosi kwanu ndi mavuto anu.

4. Ngati nthawi zonse tipemphela kwa Yehova, cingacitike n’ciani pakati pa ife ndi iye?

4 Pemphelo limatithandiza kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Ngati mabwenzi amakonda kuuzana za kukhosi kwawo ndi nkhawa zawo, ubwenzi wawo umakhala wolimba kwambili. Izi n’zimene zimacitika ngati tikambitsana ndi Yehova m’pemphelo. Iye amatiuza za kukhosi kwake ndi maganizo ake kupitila m’Baibulo. Amatiuzanso zimene adzacita mtsogolo. Nafenso tiyenela kumakambitsana ndi Mulungu nthawi zonse m’pemphelo, kumuuza za kukhosi kwathu zonse. Ngati ticita zimenezi, ubwenzi wathu ndi Yehova udzalimba kwambili.—Yakobo 4:8.

TINGACITE CIANI KUTI MULUNGU AZIMVELA MAPEMPHELO ATHU?

5. Timadziŵa bwanji kuti Yehova samvela mapemphelo onse?

5 Kodi Yehova amamvela mapemphelo onse? Iyai. M’nthawi ya mneneli Yesaya, Yehova anauza ana a Isiraeli kuti: “Ngakhale mupeleke mapemphelo ambili, ine sindimvetsela. Manja anu adzaza magazi amene mwakhetsa.” (Yesaya 1:15) Conco ngati sitisamala, tingacite zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Yehova, ndipo angaleke kumvela mapemphelo athu.

6. N’cifukwa ciani cikhulupililo n’cofunika kwambili? Nanga mungaonetse bwanji kuti muli ndi cikhulupililo?

6 Ngati tifuna kuti Yehova azimvela mapemphelo athu, tifunika kukhala ndi cikhulupililo mwa iye. (Maliko 11:24) Mtumwi Paulo anati: “Popanda cikhulupililo n’zosatheka kukondweletsa Mulungu. Pakuti aliyense wofika kwa Mulungu ayenela kukhulupilila kuti iye alikodi, ndi kuti amapeleka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” (Aheberi 11:6) Koma cikhulupililo si kukamba pakamwa cabe. Tifunika kuonetsa cikhulupililo cathu mwa kumvela Yehova tsiku lililonse.—Ŵelengani Yakobo 2:26.

7. (a) N’cifukwa ciani tiyenela kukhala aulemu ndi odzicepetsa popemphela kwa Yehova? (b) Tingaonetse bwanji kuti timapemphela moona mtima?

7 Pokambitsana ndi Yehova m’pemphelo, tiyenela kukhala odzicepetsa ndi aulemu. Cifukwa ciani? Ngati angakupatseni mwayi wokamba ndi mfumu kapena pulezidenti, ganizilani cabe ulemu umene mungakambe nawo. Koma pano tikamba za Yehova, Mulungu Wamphamvuzonse. Kukamba zoona, tiyenela kukambitsana naye mwaulemu waukulu, ndi modzicepetsa kwambili. (Genesis 17:1; Salimo 138:6) Ngakhalenso popemphela kwa Yehova, tiyenela kumuuza zocokela pansi pa mtima wathu, osati kumangobweleza mau amodzi-modzi iyai.—Mateyu 6:7, 8.

8. Kodi tikapempha cinthu kwa Mulungu m’pemphelo, tiyenelanso kucita ciani?

8 Komanso, tikapempha cinthu kwa Mulungu m’pemphelo, tifunikila kucita zinthu mogwilizana ndi zimene tapemphelela. Mwacitsanzo, tikapemphela kwa Yehova kuti atipatse cakudya, kapena zofunika zina mu umoyo, sitingakhale manja lende ndi kuyembekeza kuti Yehova adzatipatsa zonse. Tifunika kulimbikila kugwila nchito iliyonse imene ingatithandize. (Mateyu 6:11; 2 Atesalonika 3:10) Kapena tikapemphela kwa Yehova kuti atithandize kuleka kucita zoipa, tiyenela kupewa zinthu, malo, kapena anthu amene angatipangitse kucimwa. (Akolose 3:5) Tsopano, tiyeni tikambilane mafunso ena amene anthu amakonda kufunsa ponena za pemphelo.

MAFUNSO AMENE ANTHU AFUNSA PONENA ZA PEMPHELO

9. Tiyenela kupemphela kwa ndani? Nanga lemba la Yohane 14:6 limatiphunzitsa ciani za pemphelo?

9 Kodi tiyenela kupemphela kwa ndani? Yesu anaphunzitsa otsatila ake kupemphela kwa “Atate wathu wakumwamba.” (Mateyu 6:9) Iye anakambanso kuti: “Ine ndine njila, coonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzela mwa ine.” (Yohane 14:6) Conco, tiyenela kupemphela cabe kwa Yehova kupitila mwa Yesu. Kodi kupemphela kupitila mwa Yesu kumatanthauza ciani? Kuti Yehova amvele mapemphelo athu, tiyenela kulemekeza udindo umene Yehova anapatsa Yesu. Monga mmene tinaphunzilila, Yesu anabwela pa dziko lapansi kudzatipulumutsa ku ucimo ndi imfa. (Yohane 3:16; Aroma 5:12) Yehova anasankhanso Yesu kukhala Mkulu wa Ansembe ndi Woweluza.—Yohane 5:22; Aheberi 6:20.

Mungapemphele nthawi iliyonse

10. Kodi pali kakhalidwe kamodzi cabe kovomelezeka popemphela? Fotokozani.

10 Kodi popemphela tiyenela kukhala bwanji: kugwada, kukhala pansi, kapena kuimilila? Yehova sanapeleke lamulo lakuti popemphela tizikhala mwakuti-mwakuti. Baibulo imationetsa kuti tingakambe ndi Yehova m’njila iliyonse yoyenelela. (1 Mbiri 17:16; Nehemiya 8:6; Danieli 6:10; Maliko 11:25) Cacikulu kwa Yehova si mmene takhalila popemphela, koma kukamba naye mwaulemu ndi moona mtima. Tingapemphele momveka mau kapena ca mu mtima, pa malo alionse, pa nthawi ina iliyonse, usana kapena usiku. Pamene tipemphela kwa Yehova, tiyenela kukhala ndi cikhulupililo cakuti atimvela, ngakhale kuti ena sangatimvele.—Nehemiya 2:1-6.

11. Ni zinthu zina ziti zimene tingamuuze Yehova m’pemphelo?

11 Kodi tingapemphelele zinthu zabwanji? Tingapemphelele ciliconse cogwilizana ndi cifunilo ca Yehova. Baibulo imakamba kuti: “Ciliconse cimene tingamupemphe mogwilizana ndi cifunilo cake, amatimvela.” (1 Yohane 5:14) Kodi tingapemphelele ngakhale zinthu zaumwini? Inde. Kupemphela kwa Yehova kuyenela kukhala monga kukambitsana ndi mnzathu wa pamtima. Tingamuuze Yehova zilizonse za kukhosi kwathu. (Salimo 62:8) Tingapemphe Mulungu kuti atipatse mphamvu yake ya mzimu woyela kuti utithandize kucita zoyenela. (Luka 11:13) Tingapemphenso Yehova kuti atipatse nzelu pofuna kupanga zosankha zabwino, ndi kuti atipatse mphamvu zakuti tipilile mavuto. (Yakobo 1:5) Tiyenelanso kupempha Yehova kuti atikhululukile macimo athu. (Aefeso 1:3, 7) Tiyenelanso kupemphelela anthu ena, monga abululu ŵathu, ndiponso abale ndi alongo athu.—Machitidwe 12:5; Akolose 4:12.

12. Ni nkhani ziti zofunika kuika patsogolo m’pemphelo?

12 N’ciani cimene tiyenela kuika patsogolo m’mapemphelo athu? Yehova ndi cifunilo cake. Tiyenela kumuyamikila ndi mtima wonse pa zonse zimene amaticitila. (1 Mbiri 29:10-13) Tidziŵa zimenezi cifukwa pamene Yesu anali pa dziko lapansi, anaphunzitsa ophunzila ake mopemphelela. (Ŵelengani Mateyu 6:9-13.) Anawauza kuti coyamba ayenela kupemphela kuti dzina la Mulungu liyeletsedwe, kutanthauza kuti lionedwe kukhala loyela kapena lopatulika. Ndiyeno Yesu anaonetsa kuti tiyenela kupemphelelanso Ufumu wa Mulungu kuti ubwele. Ndiponso kuti cifunilo ca Yehova cicitike pa dziko lonse lapansi. Pambuyo pakuti Yesu wachula zinthu zofunika kwambili zimenezi m’pemphelo, m’pamene anachulanso zinthu zaumwini zimene tingapemphelele. Ngati titsogoza Yehova ndi cifunilo cake m’mapemphelo athu, timaonetsa kuti ndiye nkhani zofunika kwambili m’pemphelo.

13. Kodi mapemphelo athu ayenela kukhala atali bwanji?

13 Kodi mapemphelo athu ayenela kukhala atali bwanji? Baibulo siinaike mlingo uliwonse. Mapemphelo athu angakhale atali kapena afupi, malinga ndi mmene zinthu zilili. Mwacitsanzo, pemphelo la cakudya lingakhale lifupi cabe. Koma pamene tafuna kuyamikila Yehova pa zinthu zina kapena kumuuza nkhawa zathu, pemphelo lingakhale litali ndithu. (1 Samueli 1:12, 15) Sitifunika kupeleka mapemphelo atali cabe kuti ena atione, monga mmene anthu ena anali kucitila m’nthawi ya Yesu. (Luka 20:46, 47) Yehova sakondwela nawo mapemphelo a conco. Cakulu kwa Yehova n’cakuti tipemphele kucokela pansi pa mtima.

14. Kodi tiyenela kupemphela kangati? Nanga zimenezi zitiphunzitsa ciani za Yehova?

14 Kodi tiyenela kupemphela kangati? Yehova amafuna kuti tizikamba naye nthawi zonse. Baibulo imatilimbikitsa kuti “pemphelani kosalekeza,” “limbikilani kupemphela,” ndi kuti “muzipemphela mosalekeza.” (Mateyu 26:41; Aroma 12:12; 1 Atesalonika 5:17) Yehova ni wokonzeka nthawi zonse kumvela mapemphelo athu. Tsiku lililonse, tingamuyamikile Mulungu pa cikondi cake ndi mtima wake wopatsa. Komanso, tingam’pemphe kuti atitsogolele njila, kutilimbikitsa, ndi kutitonthoza mtima. Ngati timayamikila zoona mwayi wa pemphelo, tizikamba ndi Yehova pa mpata uliwonse umene tapeza.

15. N’cifukwa ciani tiyenela kukamba ‘ameni’ pambuyo pa pemphelo?

15 N’cifukwa ciani tiyenela kukamba ‘ameni’ pambuyo pa pemphelo? Liu lakuti ‘ameni’ limatanthauza kuti ‘zoona’ kapena kuti ‘inde.’ Tikati ‘ameni’ timaonetsa kuti takamba zocokeladi pansi pa mtima. (Salimo 41:13) Baibulo imatiphunzitsanso kuti tiyenela kukamba ‘ameni’ pambuyo pa pemphelo la pagulu, kaya momveka mau kapena ca mu mtima. Tikakamba conco timaonetsa kuti tavomeleza zimene zakambidwa m’pemphelo.—1 Mbiri 16:36; 1 Akorinto 14:16.

MMENE MULUNGU AMAYANKHILA MAPEMPHELO ATHU

16. Kodi n’zoona kuti Yehova amayankha mapemphelo athu? Fotokozani.

16 Kodi n’zoona kuti Yehova amayankha mapemphelo athu? Inde amayankha. Baibulo imamucha “Wakumva pemphelo.” (Salimo 65:2) Yehova amamva ndi kuyankha mapemphelo a anthu mamiliyoni ambili amene amapemphela moona mtima. Ndipo amayankha m’njila zosiyana-siyana.

17. Kodi Yehova aseŵenzetsa bwanji angelo ndi atumiki ake kuyankha mapemphelo athu?

17 Yehova amagwilitsila nchito angelo ndi atumiki ake pa dziko lapansi poyankha mapemphelo athu. (Aheberi 1:13, 14) Alipo anthu amene anapemphela kwa Mulungu kuti awathandize kuimvetsetsa Baibulo. Posapita nthawi anangoona wa Mboni za Yehova wafika pakhomo pawo. Baibulo imaonetsa kuti angelo amathandiza pa nchito yolengeza “uthenga wabwino” pa dziko lonse lapansi. (Ŵelengani Chivumbulutso 14:6.) Ngakhale ife amene, ambili tapemphelapo kwa Yehova cifukwa ca vuto linalake, kapena kupempha thandizo pa nkhani inayake. Pambuyo pake, tinangoona thandizo labwela kucokela kwa m’bale kapena mlongo mu mpingo.—Miyambo 12:25; Yakobo 2:16.

Yehova angayankhe mapemphelo athu kupitila mwa Akhiristu anzathu amene angatithandize

18. Kodi Yehova amaseŵenzetsa bwanji mzimu wake woyela ndi Baibulo kuyankha mapemphelo athu?

18 Yehova amagwilitsilanso nchito mzimu wake woyela kuyankha mapemphelo athu. Tikapemphela kuti atithandize kupilila vuto linalake, iye angaseŵenzetse mzimu wake woyela kutitsogolela ndi kutilimbikitsa. (2 Akorinto 4:7) Komanso, Yehova amagwilitsilanso nchito Baibulo kuyankha mapemphelo athu ndi kutithandiza kupanga zosankha zanzelu. Pamene tiŵelenga Baibulo, tingapeze malemba amene angatithandize. Pa misonkhano, Yehova angapangitse wina kuti apeleke ndemanga imene ingatithandize. Angapangitsenso mkulu kutilimbikitsa kuuzimu ndi mfundo ya m’Baibulo.—Agalatiya 6:1.

19. N’cifukwa ciani nthawi zina tingaone monga Yehova sayankha mapemphelo athu?

19 Koma mwina munafunsapo kuti: ‘N’cifukwa ciani Yehova sayankha mapemphelo anga? Kumbukilani kuti iye ndiye amadziŵa bwino nthawi yoyenelela yoyankha mapemphelo athu. Amadziŵanso njila yabwino yowayankhila. Iye amadziŵa zosoŵa zathu. Koma nafenso tiyenela kupitiliza kupemphela, pofuna kumuonetsa Mulungu kuti tifunitsitsa cimene tipempha, ndi kuti tili ndi cikhulupililo conse mwa iye. (Luka 11:5-10) Nthawi zina Yehova amayankha mapemphelo athu m’njila imene sitiyembekezela. Mwacitsanzo, tingapemphele kuti Mulungu aticotsele vuto linalake. Koma m’malo mocotsa vutolo, iye angatipatse mphamvu zotithandiza kupilila.—Ŵelengani Afilipi 4:13.

20. N’cifukwa ciani tiyenela kupemphela kwa Yehova kaŵili-kaŵili?

20 Ha, ukulilenji mwayi wokambitsana ndi Yehova m’pemphelo! Ndipo tisakaikile ngakhale pang’ono kuti adzamvela mapemphelo athu. (Salimo 145:18) Ngati tipemphela kwa Yehova moona mtima kaŵili-kaŵili, ubwenzi wathu ndi iye uzingolimbilako-limbilako.