NKHANI 6
Munthu Akafa Amayenda Kuti?
1-3. Kodi anthu amakhala ndi mafunso anji pa nkhani ya imfa? Nanga zipembedzo zina zimapeleka mayankho anji?
BAIBULO imatiuza kuti tsiku lina “imfa sidzakhalaponso.” (Chivumbulutso 21:4) M’Nkhani 5, tinaphunzila kuti dipo linapelekedwa kuti anthu akhale ndi moyo wosatha. Koma anthu akali kufa. (Mlaliki 9:5) Conco funso n’lakuti, Kodi munthu akafa amayenda kuti?
2 Yankho pa funso limeneli limakhala lofunika kwambili, maka-maka pamene wacibanja wamwalila, kapena mnzathu amene timakonda. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi iye ali kuti maka-maka? Kodi ationa pali pano? Kodi angatithandize? Kodi tidzaonananso?’
3 Zipembedzo zimapeleka mayankho osiyana-siyana pa mafunso amenewa. Zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti ngati ndiwe munthu wabwino udzayenda kumwamba. Koma ngati ndiwe woipa udzayenda kumoto ku helo. Zina zimati munthu akafa mzimu wake umacoka kukakhala ndi mizimu ya acibanja amene anamwalila kale. Ndipo zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti munthu akafa, mzimu wake umakaweluzidwa. Ndiye pambuyo pake, umakabadwanso kukhala munthu wina kapena nyama.
4. Ni mfundo iti imene zipembedzo zambili zimaphunzitsa pa nkhani ya imfa?
4 Apa taona kuti zipembedzo zimaphunzitsa zinthu zosiyana-siyana. Ngakhale ni conco, zambili zimagwilizana pa mfundo imodzi. Zimaphunzitsa kuti munthu akafa, cimene cimafa ndi thupi cabe, mzimu wake umacoka m’thupi kukakhala ndi moyo kwina. Kodi zimenezi n’zoona?
KODI MUNTHU AKAFA AMAYENDA KUTI?
5, 6. N’ciani cimacitika munthu akafa?
5 Yehova amadziŵa zimene zimacitika munthu akafa. Ndipo amatiuza kuti munthu akamwalila, pamenepo moyo wake umatha. Pali imfa palibe moyo. Conco, munthu akafa sakhalanso ndi moyo kwinakwake. * Munthu akafa, saona, samvela, ndipo saganiza.
6 Mfumu Solomo analemba kuti: “Akufa sadziŵa ciliconse.” N’zoona, akufa sangakonde munthu kapena kuzonda munthu. Solomo anapitiliza kukamba kuti, “kulibe kugwila nchito, kuganiza zocita, kudziŵa zinthu, kapena nzelu, ku Manda.” (Ŵelengani Mlaliki 9:5, 6, 10.) Pa Salimo 146:4, Baibulo imatiuza kuti munthu akafa, “zonse zimene anali kuganiza” zimatha.
ZIMENE YESU ANAKAMBA PA NKHANI YA IMFA
7. Kodi Yesu anakamba ciani za imfa?
7 Lazaro anali mnzake wa Yesu wa pamtima. Pamene Lazaro anamwalila, Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Bwenzi lathu Lazaro ali m’tulo.” Apa Yesu sanali kutanthauza kuti Lazaro anali kupumula cabe iyai. Kupitiliza, Yesu anati: “Lazaro wamwalila.” (Yohane 11:11-14) Yesu anayelekezela imfa ndi tulo. Sanakambe kuti Lazaro anali kumwamba iyai, kapena kuti mzimu wake unali kwa mizimu ya abululu ŵake amene anamwalila ayi. Sanakambenso kuti Lazaro anali kupsa m’moto ku helo, kapena kuti anabadwanso kwina monga munthu kapena nyama iyai. Zinangokhala monga kuti Lazaro anali cabe m’tulo tofa nato. Malemba ena amayelekezela imfa ndi tulo tofa nato. Baibulo imakamba kuti pamene Sitefano anaphedwa, “anagona tulo ta imfa.” (Machitidwe 7:60) Mtumwi Paulo naye analemba kuti Akhiristu ena “anagona mu imfa.”—1 Akorinto 15:6.
8. Tidziŵa bwanji kuti Mulungu sanalenge anthu kuti azifa?
8 Pamene Mulungu analenga Adamu ndi Hava, kodi anakonzelatu kuti m’kupita kwa nthawi adzafa? Kutali-tali! Yehova anawalenga kuti akhale ndi moyo wamuyaya ali ndi thanzi labwino. Polenga munthu, Yehova anaika mu mtima mwake cikhumbo cofuna kukhala ndi moyo wosatha. (Mlaliki 3:11) Makolo sakondwela kuona ana awo akukalamba ndi kufa. Naye Yehova n’cimodzi-modzi. Sakondwela kutiona tikukalamba ndi kufa. Apa ndiye pamabwelela funso lakuti, Nanga n’cifukwa ciani timafa?
N’CIFUKWA CIANI TIMAFA?
9. N’cifukwa ciani lamulo limene Yehova anapatsa Adamu ndi Hava linali losavuta kutsatila?
9 M’munda wa Edeni, Yehova anauza Adamu ndi Hava kuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu uzidya ndithu. Koma usadye zipatso za mtengo wodziŵitsa cabwino ndi coipa. Cifukwa tsiku limene udzadya, udzafa ndithu.” (Genesis 2:9, 16, 17) Lamulo limeneli linali losavuta kutsatila. Cina n’cakuti, Yehova anali ndi mphamvu zouza Adamu ndi Hava kuti ici n’cabwino ici n’coipa. Sembe anamvela Yehova, sembe anaonetsa kuti anali kulemekeza ulamulilo wake ndi kuyamikila zonse zimene Mulungu anawapatsa.
10, 11. (a) Kodi Satana ananamiza bwanji Adamu ndi Hava? (b) N’cifukwa ciani Adamu ndi Hava analibe codzikhululukila pa zimene anacita?
10 N’zacisoni kuti Adamu ndi Hava anasankha kupandukila Yehova. Satana anafunsa Hava kuti: “Eti n’zoona kuti Mulungu anati musadye zipatso za mtengo uliwonse wa m’mundamu?” Hava poyankha anati: “Zipatso za mitengo yonse ya m’mundamu anatiuza kuti tizidya. Koma zipatso za mtengo umene uli pakati pa munda, Mulungu anati, ‘Musadye zipatso zake ayi, musaukhudze kuti mungafe.’”—Genesis 3:1-3.
11 Ndiyeno Satana anati: ‘Kufa simudzafa ayi. Mulungu adziŵa kuti tsiku limene mudzadya cipatso ca mtengo umenewu, maso anu adzatseguka ndithu, ndipo mudzafanana ndi Mulungu. Mudzadziŵa zabwino ndi zoipa.’ (Genesis 3:4-6) Apa Satana anafuna kuti Hava aganize kuti ali ndi ufulu wogamula pa yekha cabwino ndi coipa. Satana ananamiza Hava kuti palibe cimene cidzacitika akakana kumvela Mulungu. Hava anakhulupilila zimenezo, ndipo anadya cipatso coletsedwa, ndi kupatsako mwamuna wake. Adamu ndi Hava anali kudziŵa kuti Yehova anawaletsa kudya cipatso cimeneco. Mwa kudya cipatso cimeneco, iwo anasankha kuphwanya lamulo la Mulungu, losapita m’mbali ndiponso losavuta. Anaonetsanso kuti sanali kulemekeza Atate wawo wakumwamba ndi wacikondi. Analibe codzikhululukila ciliconse pa zimene anacita.
12. N’cifukwa ciani n’zokhumudwitsa kuti Adamu ndi Hava anapandukila Yehova?
12 N’zokhumudwitsa kwambili kuona mmene makolo athu oyambilila anacitila mwano kwa Mlengi wawo. Ngakhale inu mungamvele bwanji? Tiyelekeze kuti munalimbikila kulela bwino ana anu aŵili, mwamuna ndi mkazi. Koma pambuyo pake ana aja akupandukilani ndi kuyamba kucita zonse zimene munali kuwaletsa? Simungakhumudwe?
13. Kodi Yehova anatanthauza ciani pamene anauza Adamu kuti udzabwelela “kufumbi”?
13 Pamene Adamu ndi Hava anacimwa, anataya mwayi wokhala ndi moyo wosatha. Yehova anauza Adamu kuti: “Popeza ndiwe fumbi, kufumbiko udzabwelela.” (Ŵelengani Genesis 3:19.) Ici citanthauza kuti Adamu kudzakhala kulibe, ngati mmene zinalili poyamba Mulungu asanamuumbe ndi dothi. (Genesis 2:7) Conco, pamene Adamu anacimwa, anafa ndipo sanalinso ndi moyo kwina kulikonse.
14. N’cifukwa ciani timafa?
14 Adamu ndi Hava akanamvela Mulungu, sembe akalipo mpaka Aroma 5:12) Koma zimenezi sizinali colinga ca Mulungu pamene analenga anthu. Iye sanali kufuna kuti anthu azifa. Ndiye cifukwa cake Baibulo imakamba kuti imfa ni “mdani.”—1 Akorinto 15:26.
lelo. Koma cifukwa cosamvela Mulungu anacimwa, ndipo m’kupita kwa nthawi anafa. Ucimo uli ngati matenda oopsa amene makolo athu oyambilila anatiyambukiza. Ife tonse timabadwa ocimwa, n’cifukwa cake timafa. (COONADI CIMATIMASULA
15. Kodi coonadi cimamasula bwanji munthu pa nkhani ya imfa?
15 Munthu akaphunzila coonadi pa nkhani ya imfa, coonadico cimam’masula ku ziphunzitso zonama. Baibulo imatiphunzitsa kuti akufa samvela kuŵaŵa kapena cisoni. Sitingakambe nawo, ndipo nawonso sangakambe ndi ife. Sitingawathandize, iwonso sangatithandize. Ndipo sitiyenela kuwaopa cifukwa akufa sangaticite coipa ciliconse. Koma zipembedzo zambili zimaphunzitsa kuti akufa ali ndi moyo kwina kwake, ndi kuti tingawathandize tikapeleka ndalama kwa azibusa. Koma tikadziŵa coonadi pa nkhani ya imfa, sitidzakhulupilila mabodza amenewo.
16. Kodi zipembedzo zambili zimaphunzitsa ciani ponena za akufa?
16 Satana amagwilitsila nchito zipembedzo kunamiza anthu kuti akufa ali ndi moyo kwinakwake. Mwacitsanzo, zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti munthu akafa, mzimu wake umapitiliza kukhala ndi moyo kwinakwake. Kodi n’zimene mumaphunzila ku cipembedzo kwanu? Kapena mumaphunzila zoona zimene Baibulo imakamba pa nkhani ya imfa? Satana amaseŵenzetsa mabodza kuti apatutse anthu kwa Yehova.
17. N’cifukwa ciani kuphunzitsa kuti Mulungu amawocha anthu ku helo n’kumunyoza kwambili?
17 Zimene zipembedzo zambili zimaphunzitsa n’zodabwitsa kwambili. Mwacitsanzo, zipembedzo zina amaochedwa kwamuyaya m’moto ku helo. Bodza limeneli limanyoza Yehova kwambili. N’zosatheka kuti Mulungu angazunze anthu mwa njila imeneyo. (Ŵelengani 1 Yohane 4:8.) Inu mungamvele bwanji ngati muona kholo litenga manja a mwana wake n’kuika pa moto kuti limulange? Kunena zoona, mudzakamba kuti munthu ameneyo ni kapondo. Ndipo simungafune ngakhale kukhala naye pafupi. N’zimene Satana amafuna, kuti tiziona Yehova kukhala wankhanza kwambili.
zimaphunzitsa kuti anthu oipa18. N’cifukwa ciani sitiyenela kuopa anthu amene anafa?
18 Zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti anthu akafa amakhala mizimu. Amati ngati tiilemekeza mizimuyo ikhoza kutithandiza kwambili. Ngati sitiilemekeza, amati ikhoza kuticita zinthu zoipa. Anthu ambili amakhulupilila bodza limeneli. Cifukwa ca mantha, iwo amalambila mizimuyo m’malo molambila Yehova. Koma musaiŵale kuti akufa sangamvele ciliconse, kapena kucita ciliconse. Conco sitiyenela kuwaopa. Yehova ndiye Mlengi wathu. Iye ni Mulungu woona, ndipo tiyenela kulambila iye yekha cabe.—Chivumbulutso 4:11.
19. Kodi kudziŵa coonadi ponena za akufa kumathandiza bwanji?
19 Tikadziŵa coonadi ponena za akufa, timamasuka ku mabodza a zipembedzo. Ndipo coonadi cimatithandiza kumvetsetsa malonjezo a Yehova ponena za umoyo wathu ndi tsogolo lathu.
20. Kodi tidzadziŵa ciani m’nkhani yotsatila?
20 Kalekale kwambili, Yobu mtumiki wa Mulungu anafunsa kuti: “Munthu akafa, kodi angakhalenso ndi moyo?” (Yobu 14:14) Kodi zingacitike zoona kuti munthu amene anafa akhalenso ndi moyo? Mulungu amayankha funso limeneli m’Baibulo, ndipo yankho lake n’lokondweletsa kwambili. Tidzaona yankho limenelo m’nkhani yotsatila.
^ ndime 5 Anthu ena amakhulupilila kuti munthu akafa, mzimu wake umapitiliza kukhala ndi moyo. Kuti mumvele zambili, onani Zakumapeto 17 ndi 18.