Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 11

N’Cifukwa Ciani pa Dziko Lapansi Pali Mavuto Ambili Conco?

N’Cifukwa Ciani pa Dziko Lapansi Pali Mavuto Ambili Conco?

1, 2. Kodi anthu ambili amafunsa ciani?

GANIZILANI zocitika izi: Cigumula camadzi ca Tsunami cawonongelatu mudzi wonse. Mwamuna wina aloŵa m’chalichi ndi kuwombela mfuti, kupha ndi kuvulaza anthu ambili. Mzimayi wafa ndi kansa, ndipo wasiya ana asanu.

2 Pakacitika masoka ngati amenewa, ambili amafunsa kuti, “N’cifukwa ciani zinthu zimenezi zimacitika?” Ambili amafunsa kuti n’cifukwa ciani pali kuzondana kwakukulu ndi mavuto ambili conco. Kodi ngakhale inu munafunsapo mafunso a conco?

3, 4. (a) Kodi Habakuku anafunsa mafunso anji? (b) Ndiyeno Yehova anamuyankha bwanji?

3 Tikaŵelenga Baibulo, timapeza kuti ngakhale anthu amene anali ndi cikhulupililo colimba mwa Mulungu anafunsa mafunso a conco. Mwacitsanzo, mneneli Habakuku anafunsa Yehova kuti: “N’cifukwa ciani mukundicititsa kuona zinthu zopweteka? N’cifukwa ciani mukupitiliza kuyang’ana khalidwe loipa? N’cifukwa ciani kufunkha ndi ciwawa zikucitika pamaso panga? Ndipo n’cifukwa ciani pali mikangano ndi kumenyana?”—Habakuku 1:3.

4 Pa Habakuku 2:2, 3, timapezapo mayankho a Mulungu kwa Habakuku. Ndipo anamulonjeza kuti adzacitapo kanthu. Yehova amakonda anthu kwambili. Baibulo imati: “Amakudelani nkhawa.” (1 Petulo 5:7) Ndipo iye safuna ngakhale pang’ono kuona anthu akuvutika. (Yesaya 55:8, 9) Lomba n’cifukwa ninji m’dziko muli mavuto ambili conco? Tiyeni tikambilane nkhani imeneyi.

N’CIFUKWA CIANI PALI MAVUTO AMBILI CONCO?

5. Kodi alaliki azipembedzo ambili amati ciani za mavuto? Nanga Baibulo imaphunzitsa ciani?

5 Azibusa, ansembe, ndi alaliki a m’zipembedzo, kaŵilikaŵili amaphunzitsa kuti kuvutika kwa anthu ni cifunilo ca Mulungu. Ena amakamba kuti ciliconse cimene cimacitika kwa munthu, ngakhale zinthu zoipa, Mulungu analembelatu, kapena anakonzelatu. Ndipo amati ife anthu sitingamvetsetse cifukwa cake. Palinso ena amene amakamba kuti anthu akafa, ngakhale ana ang’ono, ni cifunilo ca Mulungu kuti iwo akakhale naye kumwamba. Koma zimenezi si zoona. Yehova sacititsa zinthu zoipa olo pang’ono. Baibulo imati: “Mulungu woona sangacite zoipa m’pang’ono pomwe, ndipo Wamphamvuyonse sangacite zinthu zopanda cilungamo ngakhale pang’ono.”—Yobu 34:10.

6. N’cifukwa ciani anthu ambili amaimba Mulungu mlandu pa mavuto amene ali m’dziko?

6 Anthu ambili amaimba Mulungu mlandu pa mavuto ali m’dziko poganiza kuti Mulungu ndiye alamulila dziko lapansi. Koma monga tinaphunzilila m’Nkhani 3, Satana Mdyelekezi ndiye wolamulila weni-weni wa dziko.

7, 8. N’cifukwa ninji m’dziko muli mavuto ambili conco?

7 Baibulo imatiuza kuti: “Dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19) Woipayo amene alamulila dziko ni Satana. Iye ni wolusa ndiponso wankhanza. ‘Amasoceletsa dziko lonse lapansi.’ (Chivumbulutso 12:9) Anthu ambili amatengela zocita zake. Ici n’cimodzi mwa zifukwa zocititsa kuti dziko lidzale ndi mabodza, cizondi, ndi nkhanza.

8 Palinso zifukwa zina zopangitsa kuti m’dziko mukhale mavuto ambili. Pamene Adamu ndi Hava anacimwa, onse obadwa kwa iwo anatengela ucimo wawo. Mwa ici, anthu ambili amakhalila kuvutitsa anthu anzawo. Amangofuna kukhala apamwamba kuposa anthu ena. Ndiye cifukwa cake pamakhala kumenyana, nkhondo, ndi kupondelezana. (Mlaliki 4:1; 8:9) Nthawi zina anthu amakumana ndi mavuto cifukwa ca “tsoka ndi zinthu zosayembekezeleka.” (Mlaliki 9:11) Ndipo nthawi zina ngozi kapena zinthu zina zoipa zimagwela anthu cabe cifukwa copezeka pa malo olakwika, ndi pa nthawi yolakwika.

9. N’cifukwa ciani sitikaikila kuti Yehova ali ndi cifukwa comveka cimene walolela mavuto kupitiliza?

9 Yehova sabweletsa mavuto alionse. N’kulakwa kumuimba mlandu cifukwa ca nkhondo, ciwawa, ndi kupondelezana kumene kuli m’dziko. Ngakhale ngozi zacilengedwe monga zivomezi, mphepo zamkuntho, ndi kusefukila kwa madzi, si Mulungu amene amazicititsa iyai. Mwina mungafunse kuti: ‘Ngati Yehova ni wamphamvu zonse m’cilengedwe conse, bwanji saletsa zinthu zoipa kucitika?’ Koma popeza kuti Mulungu amatikonda ngako, ndipo amasamala za ife, ayenela kukhala ndi cifukwa comveka ndiponso cabwino, cimene walolela mavuto kupitiliza mpaka lelo.—1 Yohane 4:8.

CIMENE MULUNGU AMALOLELA MAVUTO KUPITILIZA

10. Mwa zimene Satana anacita, ananeneza Yehova ciani?

10 Mdyelekezi anasoceletsa Adamu ndi Hava m’munda wa Edeni. Satana ananeneza Mulungu kuti ni Wolamulila woipa. Iye anati Mulungu anali kubisila Adamu ndi Hava cinthu cina cabwino. Colinga cake cinali cakuti Adamu ndi Hava aone kuti iye angakhale wolamulila wabwino kupambana Yehova, ndi kuti iwo safunikila Mulungu.—Genesis 3:2-5; onani Zakumapeto 27.

11. Kodi ni funso lanji lofunikila yankho?

11 Adamu ndi Hava sanamvele Mulungu ndipo anam’pandukila. Iwo anaganiza kuti anali ndi ufulu wonse wodzigamulila cabwino ndi coipa. Kukamba zoona, apandu aja anali olakwa, ndipo Yehova ndiye amadziŵa cimene cili cabwino kwa ife. Kodi Yehova anafunikila kucita ciani kuti aonetse mfundo imeneyi?

12, 13. (a) N’cifukwa ciani Yehova sanawaphe apandu aja pa nthawi imeneyo? (b) Kodi Yehova analolelanji kuti Satana azilamulila dziko, ndi kuti maboma a anthu aziyendetsa zinthu okha?

12 Yehova sanaphe Adamu ndi Hava pa nthawi yomweyo. M’malo mwake, anawalola kubala ana. Ndiyeno Yehova analola ana a Adamu ndi Hava kuti akasankhe okha amene afuna kukhala wolamulila wawo. Cifuno ca Yehova cinali cakuti dziko lonse likadzale ndi anthu angwilo. Ndipo anatsimikiza mtima kuti kaya Mdyelekezi afune olo asafune, mpaka zimenezo zidzakwanilitsika basi.—Genesis 1:28; Yesaya 55:10, 11.

13 Satana anatsutsa ucifumu wa Yehova pamaso pa angelo mamiliyoni ambili-mbili. (Yobu 38:7; Danieli 7:10) Mwa ici, Yehova anapatsa Satana nthawi yoonetsa ngati zokamba zake zinali zoona. Nawonso anthu anawapatsa nthawi yokhazikitsa maboma awo pansi pa utsogoleli wa Satana. Inde, kuti aonetse ngati angayendetse bwino zinthu popanda utsogoleli wa Mulungu.

14. Kodi zapita zonsezi zatsimikizila ciani?

14 Kwa zaka zambili-mbili, anthu ayesa kudzilamulila okha, koma akangiwa. Satana lomba waonekela poyela kuti ni wabodza. Nawonso anthu, aonekelatu kuti popanda Mulungu sangaime paokha. Anakamba Yeremiya kuti: “Ine ndikudziŵa bwino, inu Yehova, kuti munthu wocokela kufumbi alibe ulamulilo woongolela njila ya moyo wake. Munthu amene akuyenda alibe ulamulilo woongolela mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.

N’CIFUKWA CIANI YEHOVA WAYEMBEKEZA KWA NTHAWI ITALI CONCO?

15, 16. (a) N’cifukwa ciani Yehova walola mavuto kupitiliza kwa nthawi itali conco? (b) Bwanji Yehova sanacotsepo mavuto amene Satana anayambitsa?

15 N’cifukwa ciani Yehova walola mavuto kupitiliza kwa nthawi itali conco? Bwanji sacitapo kanthu kuti zoipa zonse zileke? Patenga nthawi itali kuti ulamulilo wa Satana udziŵike kuti wakanga. Anthu ayesa maboma osiyana-siyana, koma onse alephela. Ngakhale kuti anthu apita patsogolo m’mbali zina, monga m’za sayansi ndi luso la zinthu zamakono, ku mbali ina zinthu ziipilako-ipilako, monga cisalungamo, umphawi, ciwawa, ndi nkhondo. Zacita kuonekelatu kuti ife anthu sitingadzilamulile popanda utsogoleli wa Mulungu.

16 Ngakhale kuti Yehova akhoza kucotsapo mavuto amene Satana anayambitsa, iye sanacite zimenezo. Kuti acotsepo mavuto pa dziko, ndiye kuti athandizila ulamulilo wa Satana. Koma Mulungu sali ku mbali ya Satana. Naonso anthu akanaganiza kuti adzakwanitsa kudzilamulila okha popanda utsogoleli wa Mulungu. Koma limenelo ni bodza, ndipo Yehova sangagwilizane ndi bodza. Paja Mulungu sanganame.—Aheberi 6:18.

17, 18. Kodi Yehova adzacitapo ciani pa mavuto onse amene Satana anayambitsa?

17 Kodi n’zoona kuti Yehova akhoza kucotsapo mavuto onse amene anabwela cifukwa ca kupanduka kwa Satana ndi anthu? Inde. Zinthu zonse n’zotheka ndi Mulungu. Yehova adziŵa bwino pamene adzatsilizila mabodza onse a Satana. Pambuyo pake, adzatsandutsa dziko kukhala paradaiso monga poyamba. Onse ali “m’manda acikumbutso” adzaukitsidwa. (Yohane 5:28, 29) Anthu sadzadwalanso kapena kumwalila. Yesu adzacotsa mavuto onse amene Satana anabweletsa. Yehova adzagwilitsila nchito Yesu kuti “awononge nchito za Mdyelekezi.” (1 Yohane 3:8) Tili oyamikila kuti pali pano Yehova waleza nafe mtima kuti tim’dziŵe bwino, ndi kuti tisankhe iye kukhala Wolamulila wathu. (Ŵelengani 2 Petulo 3:9, 10.) Ngakhale tikumane ndi mavuto abwanji, Mulungu amatithandiza kupilila.—Yohane 4:23; ŵelengani 1 Akorinto 10:13.

18 Yehova satikakamiza kuti tim’sankhe kukhala Wolamulila wathu. Iye anapatsa anthu ufulu wosankha. Ndipo ufulu umenewo ni mphatso ya mtengo wapatali. Lomba tiyeni tione ubwino wa mphatso imeneyi.

MUDZAUSEŴENZETSA BWANJI UFULU WANU WOSANKHA?

19. Ni mphatso ya mtengo wapatali iti imene Yehova anatipatsa? Ndipo n’cifukwa ninji tiyenela kuyamikila kwambili?

19 Ufulu wosankha umene Yehova anatipatsa ni wabwino kwambili. Umatisiyanitsa ndi nyama. Izo zimangocita zinthu mwacibadwa. Koma ife anthu timacita kusankha zimene tifuna kucita ndi umoyo wathu. Cili kwa ife kusankha kucita zinthu zokondweletsa Yehova kapena iyai. (Miyambo 30:24) Sitili monga makina amene amangocita zinthu zimene anawapangila cabe. Ife tili ndi ufulu wosankha makhalidwe amene tifuna, anzathu amene tifuna, ndi zimene tifuna kucita ndi moyo wathu. Koma Yehova amafuna kuti tikondwele nawo moyo wathu.

20, 21. Kuti ufulu wanu wosankha muuseŵenzetse mwanzelu pali pano, muyenela kusankha ciani copambana zonse?

20 Yehova afuna kuti tizim’konda. (Mateyu 22:37, 38) Iye ali monga tate amene amakondwela akamva mwana wake amuuza mocokela pansi pa mtima, osati mokakamizika, kuti, “Nikukondani atate.” Yehova anatipatsa ufulu wosankha kum’tumikila kapena kusam’tumikila. Satana, Adamu, ndi Hava, anakana Yehova. Nanga inu mudzauseŵenzetsa bwanji ufulu wanu wosankha?

21 Gwilitsilani nchito ufulu wanu kutumikila Yehova. Pali anthu mamiliyoni ambili amene asankha kukondweletsa Mulungu ndi kukana Satana. (Miyambo 27:11) N’ciani cimene muyenela kucita pali pano kuti mukapezeke m’dziko latsopano pamene Mulungu adzacotsapo zoipa zonse? Nkhani yotsatila idzayankha funso limeneli.