Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 19

Khalani Pafupi ndi Yehova

Khalani Pafupi ndi Yehova

1, 2. Kodi citetezo ceni-ceni tingacipeze kuti masiku ano?

YELEKEZANI kuti muyenda pamseu, ndipo kuli cimphepo camphamvu. Kumwamba kwayamba kucita mdima cifukwa ca mitambo, mphezi zayamba kung’anima, ndipo mabingu ayamba kugunda. Posapita nthawi, cimvula puu! Muthamanga kuti mupeze malo obisalapo. Aha, mtima wakhala pansi! Mwapeza malo ouma ndipo ochingika bwino.

2 Citsanzo ici cionetsa mmene zinthu zilili masiku ano. Zinthu pa dziko lapansi zingoipilako-ipilalako. Mwina mumaganizapo kuti: ‘Kodi citetezo ceni-ceni ningacipeze kuti?’ Wa Masalimo analemba kuti: “Ndidzauza Yehova kuti: ‘Inu ndinu pothawilapo panga ndi malo anga acitetezo, Mulungu wanga amene ndimamukhulupilila.’” (Salimo 91:2) Zoona, Yehova angatiwombole ku mavuto athu onse, ndipo watilonjeza zinthu zabwino kwambili mtsogolo.

3. Tingacite ciani kuti Yehova akhale pothaŵilapo pathu?

3 Kodi Yehova angatiteteze bwanji? Angatithandize mocitila ndi vuto iliyonse. Ndipo ali ndi mphamvu kupambana adani athu onse. Ngakhale kuti adani aticitile coipa ciliconse, tikhulupilile ndi mtima wonse kuti Yehova adzakoza zonse mtsogolo. Baibulo imatilimbikitsa kuti: “Pitilizani kucita zinthu zimene zingacititse Mulungu kukukondani.” (Yuda 21) Conco, kuti Yehova azitithandiza pa nthawi ya mavuto, tiyenela kukhala naye pafupi. Nanga tingacite bwanji zimenezi?

MUZIYAMIKILA CIKONDI CA MULUNGU

4, 5. Kodi Yehova wationetsa bwanji cikondi cake?

4 Kuti tikhale pafupi ndi Yehova, tiyenela kudziŵa mmene iye amatikondela. Ganizilani cabe pa zonse zimene Yehova waticitila. Anatipatsa dziko lapansi lokongola, ndi kuikapo maluŵa, mitengo, ndi zinyama. Anatipatsanso zakudya zokoma, ndi madzi akumwa abwino. Kupitila m’Baibulo, Yehova watidziŵitsanso za dzina lake ndi makhalidwe ake abwino kupitila m’Baibulo. Copambana zonse, anationetsanso cikondi cake mwa kutumiza Yesu, Mwana wake wokondedwa, kudzapeleka moyo wake kaamba ka ife. (Yohane 3:16) Ndipo cifukwa ca nsembe imeneyi, tili ndi ciyembekezo ca umoyo wabwino mtsogolo.

5 Yehova anakhazikitsanso Ufumu wa Mesiya, umene ni boma lakumwamba limene lidzacotsa mavuto onse posacedwa. Ufumu umenewu udzasandutsa dziko lonse kukhala paradaiso. Munthu aliyense mmenemo adzakhala pamtendele ndi wacimwemwe kosatha. (Salimo 37:29) Njila ina imene Yehova wationetsela kuti amatikonda, ni yakuti watiphunzitsa mokhalila ndi umoyo wabwino. Amatilimbikitsanso kuti tizikamba naye m’pemphelo, cifukwa amamvela mapemphelo athu. Mosakaikila, Yehova wationetsa kuti amakonda munthu aliyense.

6. Kodi mufunika kucitapo ciani pa cikondi ca Yehova?

6 Kodi muyenela kucitapo ciani pa cikondi cimene Yehova waonetsa kwa inu? Muyenela kucita zinthu zoonetsa kuyamikila pa zonse zimene wakucitilani. Comvetsa cisoni n’cakuti anthu ambili masiku ano sayamikila. Ndi mmene zinthu zinalili ngakhale pa nthawi ya Yesu. Tsiku lina, Yesu anacilitsa anthu odwala khate okwana 10. Koma mmodzi cabe ni amene anamuyamikila. (Luka 17:12-17) Na ife tifuna kukhala monga munthu uja amene anayamikila Yesu. Tifuna kukhala oyamikila Yehova nthawi zonse.

7. Kodi cikondi cathu kwa Yehova ciyenela kukhala cikulu bwanji?

7 Nafenso tiyenela kumuonetsa Yehova kuti timam’konda. Yesu anauza ophunzila ake kuti ayenela kukonda Yehova ndi mtima wawo wonse, moyo wawo wonse, ndi maganizo awo onse. (Ŵelengani Mateyu 22:37.) Kodi zimenezi zitanthauza ciani?

8, 9. Tingamuonetse bwanji Yehova kuti timam’konda?

8 Kungokamba cabe kuti timakonda Yehova si kokwanila. Ngati timam’kondadi Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, ndi maganizo athu onse, tidzaonetsa zimenezi mwa zocita zathu. (Mateyu 7:16-20) Baibulo imaphunzitsa mosapita m’mbali kuti, ngati timam’konda Mulungu tidzasunga malamulo ake. Kodi n’cinthu covuta kusunga malamulo a Mulungu? Iyai, “malamulo a [Yehova] ndi osalemetsa.”—Ŵelengani 1 Yohane 5:3.

9 Tikamamvela Yehova, timakhala ndi moyo wokondweletsa ndi wopindulitsa. (Yesaya 48:17, 18) Koma n’ciani cingatithandize kuti tisunge ubwenzi wathu ndi Yehova? Tiyeni tione.

PITILIZANI KULIMBITSA UBWENZI WANU NDI YEHOVA

10. N’cifukwa ciani mufunika kupitiliza kuphunzila za Yehova?

10 Kodi munakhala bwanji bwenzi la Yehova? Kuphunzila Baibulo n’kumene kwakuthandizani. Mwacionekele munayamba mwa kuphunzila Baibulo. Pamene munayamba kudziŵa zambili za Yehova, ubwenzi wanu nawo unapitiliza kukula. Ubwenzi umenewu uli ngati moto umene simufuna kuti uzime. Monga mmene moto umafunila kusonkhela nkhuni kuti usazime, inunso mufunika kupitiliza kuphunzila za Yehova kuti ubwenzi wanu ndi iye ukhale wolimba.—Miyambo 2:1-5.

Mofanana ndi moto, cikondi canu pa Yehova cimafunika nkhuni kuti cisazime

11. Kodi pali ubwino wanji ngati mupitiliza kuphunzila Baibulo?

11 Pamene mupitiliza kuphunzila Baibulo, mudzadziŵa zinthu zimene zidzakhudza mtima wanu. Onani mmene ophunzila a Yesu aŵili anakhudzikila mtima pamene Yesu anali kuwafotokozela maulosi a m’Baibulo. Iwo anati: “Kodi si paja mitima yathu inali kunthunthumila pamene anali kulankhula nafe mumseu, ndi kutifotokozela Malemba momveka bwino?”—Luka 24:32.

12, 13. (a) N’ciani cingacitikile cikondi cathu pa Mulungu? (b) Tingacite ciani kuti cikondi cathu pa Yehova cisazime?

12 Monga mmene mitima ya ophunzila a Yesu inakhudzikila pamene anamvetsetsa Malemba, n’kutheka kuti inunso munakondwela kwambili pamene munayamba kumvetsetsa mfundo za m’Baibulo. Zimenezi zinakuthandizani kudziŵa Yehova ndi kum’konda. Mwacionekele, simungafune kuti cikondi cimeneci cizime.—Mateyu 24:12.

13 Mukakhala bwenzi la Mulungu, mufunika kucita khama kulimbitsa ubwenzi wanu. Muyenela kupitiliza kuphunzila za iye ndi za Yesu, ndiponso kuganizila zimene mumaphunzila, ndi mmene mungazigwilitsile nchito mu umoyo wanu. (Yohane 17:3) Pamene muŵelenga ndi kuphunzila Baibulo, muyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi zimenezi ziniphunzitsa ciani za Yehova Mulungu? N’cifukwa ciani niyenela kum’konda ndi mtima wanga wonse, ndi moyo wanga wonse?’—1 Timoteyo 4:15.

14. Kodi pemphelo limathandiza bwanji kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova?

14 Mukakhala ndi bwenzi la pamtima, mumakambitsana naye nthawi zonse, ndipo zimenezi zimalimbikitsa ubwenzi wanu. Mofananamo, ngati tikambitsana ndi Yehova m’pemphelo nthawi zonse, ubwenzi wathu ndi iye udzalimba kwambili. (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:17.) Pemphelo ni mphatso ya mtengo wapatali imene Atate wathu wa kumwamba anatipatsa. Tiyenela kukamba naye nthawi zonse kucokela pansi pa mtima. (Salimo 62:8) Sitiyenela kupeleka mapemphelo oloŵeza pamtima, koma kupemphela mocokela pansi pa mtima. Ndithudi, ngati tipitiliza kuphunzila Baibulo ndi kupemphela ndi mtima wonse, ubwenzi wathu ndi Yehova udzalimba kwambili.

MUZIUZAKO ENA ZA YEHOVA

15, 16. Kodi nchito yolalikila mumaiona bwanji?

15 Kuti ubwenzi wanu ndi Yehova upitilize, mufunika kumauzako ena za cikhulupililo canu. Ndipo ni mwayi wapadela umenewo. (Luka 1:74) Ndiponso, ni udindo umene Yesu anapatsa Akhiristu onse oona. Aliyense wa ife ayenela kulalikila uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu. Kodi inu munayamba kale kucita zimenezi?—Mateyu 24:14; 28:19, 20.

16 Mtumwi Paulo anaona kuti nchito yolalikila ni ya mtengo wapatali. Ndiye cifukwa cake anaicha “cuma.” (2 Akorinto 4:7) Kuuzako ena za Yehova ndi cifunilo cake ndiye nchito yofunika kwambili imene mungacite. Ni njila imodzi imene mungatumikile Yehova, ndipo iye amayamikila kwambili zimene mumacita. (Aheberi 6:10) Nchito imeneyi ingapindulitse inu pamodzi ndi anthu amene mumauzako za Ufumuwo. Zili conco cifukwa nchitoyi imathandiza inu ndi anthu enawo kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova, ndipo nonse mudzapeza moyo wosatha. (Ŵelengani 1 Akorinto 15:58.) Kukamba zoona, palibe nchito ina imene ingakupatseni cimwemwe yopambana imeneyi.

17. N’cifukwa ciani nchito yolalikila ifunika kucitika mwamsanga?

17 Nchito yolalikila iyenela kucitidwa mwamsanga. Tiyenela ‘kulalikila mau,’ ndipo tizicita zimenezi “modzipeleka.” (2 Timoteyo 4:2) Anthu afunika kumvela za Ufumu wa Mulungu. Baibulo imati: “Tsiku lalikulu la Yehova lili pafupi. Lili pafupi ndipo likubwela mofulumila kwambili.” Mapeto “sadzachedwa.” (Zefaniya 1:14; Habakuku 2:3) Zoona, posacedwa Yehova adzawononga dziko loipa ili la Satana. Koma zikalibe kucitika, anthu afunika kucenjezedwa kuti asankhe okha kutumikila Yehova kapena iyai.

18. N’cifukwa ciani tifunika kulambila Yehova pamodzi ndi Akhiristu anzathu?

18 Yehova amafuna kuti tizim’lambila pamodzi ndi Akhiristu oona anzathu. Baibulo imati: “Tiyeni tiganizilane kuti tilimbikitsane pa cikondi ndi nchito zabwino. Tisaleke kusonkhana pamodzi, monga mmene ena a cizolowezi cosafika pa misonkhano akucitila. Koma tiyeni tilimbikitsane, ndipo tiwonjezele kucita zimenezi, makamaka pamene mukuona kuti tsikulo likuyandikila.” (Aheberi 10:24, 25) Tifunika kucita zonse zimene tingakwanitse kuti tizipezeka ku misonkhano yonse. Misonkhano imatipatsa mpata wolimbikitsana wina ndi mnzake.

19. N’ciani cingatithandize kukonda Akhiristu anzathu?

19 Mukamapezeka ku misonkhano, mudzapeza mabwenzi abwino amene adzakulimbikitsani kulambila Yehova. Mudzakumana ndi abale ndi alongo osiyana-siyana amene nawonso amacita khama kuti alambile Mulungu. Mofanana ndi inu, nawonso ni opanda ungwilo, ndipo amalakwitsa zinthu nthawi zina. Conco ngati tsiku lina angakulakwileni, muyenela kuwakhululukila. (Ŵelengani Akolose 3:13.) Muziyang’ana kwambili pa zabwino mwa Akhiristu anzanu. Kucita zimenezi kudzakuthandizani kuwakonda ndi kulimbitsa ubwenzi wanu ndi Yehova.

MOYO WENI-WENI

20, 21. Kodi ‘moyo weni-weni’ n’ciani?

20 Yehova amafuna kuti mabwenzi ake onse akhale ndi umoyo wabwino kwambili. Baibulo imatiphunzitsa kuti mtsogolo umoyo wathu udzakhala wosiyana kwambili ndi umene tili nawo lelolino.

Yehova amafuna kuti inunso mukapeze ‘moyo weni-weni.’ Kodi mudzacitapo kanthu?

21 M’dziko latsopano, tidzakhala ndi moyo osati cabe kwa zaka 70 kapena 80, koma kwamuyaya. Tidzakondwela ndi “moyo wosatha” m’paradaiso, apo tili ndi thanzi langwilo, mtendele, ndi cimwemwe. Ndiye umene Baibulo imakamba kuti ‘moyo weni-weni.’ Inde, umene Yehova watilonjeza. Koma kuti tikaulandile, tifunika kulimbikila osaleka kuti ‘tigwile mwamphamvu’ moyo umenewu.—1 Timoteyo 6:12, 19.

22. (a) Tingacite ciani kuti ‘tigwile mwamphamvu moyo weni-weni’? (b) N’cifukwa ciani moyo wosatha sitingaugule ndi ciliconse?

22 Nanga tingacite ciani kuti ‘tigwile mwamphamvu moyo weni-weni’? Tifunika ‘kucita zabwino’ ndi kukhala “olemela pa nchito zabwino.” (1 Timoteyo 6:18) Izi zitanthauza kuti tifunika kucita zimene timaphunzila m’Baibulo. Ngakhale n’conco, moyo weni-weni sitingaupeze mwa mphamvu zathu cabe. Ndiponso, moyo wosatha sitingaugule ndi nchito zathu. Ni mphatso yaulele imene Yehova adzapatsa atumiki ake okhulupilika. Ndipo ni njila imodzi yoonetsela cisomo cake. (Aroma 5:15) Ndithudi, Atate wathu wakumwamba ni wofunitsitsa kupatsa atumiki ake okhulupilika mphatso imeneyi ya moyo wosatha.

23. N’cifukwa ciani mufunika kupanga zosankha zanzelu pa nthawi ino?

23 Dzifunseni kuti: ‘Kodi ine nimalambila Mulungu m’njila imene iye amavomeleza?’ Ngati muona kuti mufunika kusintha, musacedwe. Tikadalila Yehova ndi kumumvela mwakhama, adzakhala pothaŵila pathu. Iye adzateteza atumiki ake okhulupilika m’masiku ano otsiliza a dziko loipa la Satana. Ndiyeno potsilizila pake, Yehova adzatipatsa moyo wosatha m’paradaiso, mwa lonjezo lake. Inde, moyo weni-weni mukhoza kuupeza ngati mupanga zosankha zanzelu pa nthawi ino.