Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 1

Cisinsi Cimene Ndife Okondwela Kudziŵa

Cisinsi Cimene Ndife Okondwela Kudziŵa

Kodi munthu wina anakuuzako nkhani yacisinsi?— * Baibulo limakamba za cisinsi capadela kwambili ndipo cimachedwa “cisinsi copatulika.” Ndi copatulika cifukwa cinacokela kwa Mulungu. Ni cisinsi cifukwa cakuti poyamba anthu sanacidziŵe. Ngakhale angelo anafuna kudziŵa zambili pa cisinsi cimeneci. Kodi ungafune kudziŵa cisinsi cimeneci?—

Kodi apa uganiza kuti angelo afuna kudziŵa ciani?

Kale-kale Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi woyamba. Maina ao anali Adamu ndi Hava. Mulungu anawapatsa malo okhala okongola kwambili ochedwa munda wa Edeni. Adamu ndi Hava akanamvela Mulungu, io ndi ana ao akanapanga dziko lonse kukhala paladaiso monga munda wa Edeni. Iwo akanakhala ndi moyo wosatha m’Paladaiso. Koma, kodi udziŵa cimene Adamu ndi Hava anacita?—

Adamu ndi Hava sanamvele Mulungu, ndiye cifukwa cake masiku ano sitili mu paladaiso. Koma Mulungu anakamba kuti adzapanga dziko lonse kukhala lokongola, ndipo aliyense adzasangalala ndi moyo wosatha. Kodi iye adzacita bwanji zimenezi? Kwa nthawi yaitali anthu sanadziŵe, cifukwa cinali cisinsi.

Pamene Yesu anali padziko lapansi, anaphunzitsa anthu zinthu zambili zonena cisinsi cimeneci. Iye anakamba kuti cisinsi cimeneci cinali kunena za Ufumu wa Mulungu. Yesu anauza anthu kupemphela kuti Ufumu umenewu ubwele. Ufumu umenewo udzapangitsa dziko kukhala paladaiso wokongola.

Kodi wakondwela kudziŵa cisinsi cimeneci?— Kumbukila kuti anthu amene amamvela Yehova ndiwo amene adzakhala m’Paladaiso. Mu Baibulo muli nkhani zambili za amuna ndi akazi amene anamvela Yehova. Kodi ungakonde kuwadziŵa?— Tiye tiphunzile ena a io ndi mmene tingakhalile ngati io.

ŴELENGA M’BAIBULO LAKO

^ par. 3 M’nkhani zonse, mafunso ena ali ndi cizindikilo ici (—). Mukaciona ndiye kuti mufunikila kuima pang’ono ndi kupatsa mpata mwana wanu kuti ayankhe.