PHUNZILO 8
Yosiya Anali ndi Anzake Abwino
Kodi umaona kuti kucita zabwino ndi kovuta?— Ambili amaganiza conco. Baibulo limatiuza kuti mnyamata wina dzina lake Yosiya anali kuvutika kwambili kucita zabwino. Koma iye anali ndi anzake abwino amene anam’thandiza. Tiye tiphunzile zambili za Yosiya ndi anzake.
Atate a Yosiya anali Amoni, ndipo anali mfumu ya Yuda. Amoni anali kucita zinthu zoipa ndipo anali kulambila mafano. Pamene atate a Yosiya anamwalila, iye anakhala mfumu ya Yuda. Nthawi imeneyo iye anali ndi zaka 8 cabe. Kodi uganiza kuti nayenso anali kucita zoipa monga atate wake?— Iyai, iye anali kucita zabwino.
Ngakhale pamene anali wamng’ono kwambili, Yosiya anali kumvela kwambili Yehova. Conco, anthu amene iye anasankha kukhala mabwenzi ake anali cabe aja amene anali kukonda Yehova. Ndipo io anathandiza Yosiya kucita zabwino. Kodi anzake a Yosiya anali ndani?
Mmodzi wa io anali Zefaniya. Zefaniya anali mneneli amene anacenjeza anthu a
ku Yuda kuti, ngati alambila mafano adzakumana ndi mavuto. Yosiya anatsatila zimene Zefaniya anamuuza ndipo anali kulambila Yehova osati mafano.Mnzake wina wa Yosiya anali Yeremiya. Iye anali ndi zaka zofanana ndi Yosiya, ndipo pamene anali kukula anali kukhala moyandikana. Anali mabwenzi apamtima cakuti pamene Yosiya anafa, Yeremiya analemba nyimbo yacisoni yosonyeza mmene anali kumukondela. Yeremiya ndi Yosiya anali kuthandizana pocita zabwino ndi pomvela Yehova.
Yosiya ndi Yeremiya anali kuthandizana kucita zabwino
Kodi uphunzilapo ciani pa citsanzo ca Yosiya?— Ngakhale pamene anali kamnyamata, Yosiya anali wofunitsitsa kucita zabwino. Iye anali kudziŵa kuti ayenela kukhala paubwenzi ndi anthu amene amakonda Yehova. Iwenso uyenela kusankha mabwenzi amene amakonda Yehova ndipo amene angakuthandize kucita zabwino.
ŴELENGA M’BAIBULO LAKO
-
2 Mbiri 33:21-25; 34:1, 2; 35:25