Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kulamanzele: Mlongo ku Alabama, m’dziko la U.S.A., akumvetsela nkhani ya M’bale Rutherford imene inajambulidwa pa tepi ca kumapeto kwa zaka za m’ma 1930; kulamanja: ku Switzerland

CIGAWO 1

Coonadi ca Ufumu—Kugaŵila Cakudya Cakuuzimu

Coonadi ca Ufumu—Kugaŵila Cakudya Cakuuzimu

YELEKEZELANI kuti mukuphunzila Baibulo ndi wophunzila Baibulo wanu. Nkhope yake ikuoneka yacimwemwe cifukwa cakuti wamvetsetsa mfundo ya palemba limene mwaŵelenga naye. Motsitsa mau, wophunzilayo akufunsa kuti, “Kodi mukutanthauza kuti Baibulo limaphunzitsa kuti tingakhale m’Paladaiso kwamuyaya pano padziko lapansi?” Mnzanu amene muli naye muutumiki akumwetulila ndi kuyankha kuti, “Izi n’zimene Baibulo limaphunzitsa.” Kenako wophunzilayo akugwedeza mutu, ndipo modabwa akunena kuti, “Izi n’zocititsa cidwi kwambili, ndipo sindinaphunzilepo zimenezi.” Ndiyeno inu mukukumbukila kuti milungu ingapo yapita, iye anakamba mau ofanana ndi amenewa pamene anadziŵa kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.

Kodi zotelezi zinakucitikilamponi? Atumiki ambili a Mulungu zinawacitikilapo. Zocitika zotele zimatikumbutsa za mphatso ya mtengo wapatali imene tinapatsidwa. Mphatso imeneyi ndi coonadi cimene tinaphunzila. Komabe, kodi zinatheka bwanji kuti inuyo muphunzile coonadi cimeneci? M’cigawo cino tiphunzila yankho la funso limeneli. Njila imene anthu a Mulungu aphunzilila coonadi ndi umboni wakuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni. Kwa zaka zambili, Mfumu ya Ufumuwu, Yesu Kristu, yakhala ikuthandiza anthu a Mulungu kuphunzila coonadi.

M'CIGAWO CINO

NKHANI 3

Yehova Anaulula Colinga Cake

Kodi Ufumu wa Mesiya unali mbali ya colinga ca Yehova kucokela paciyambi? Kodi Yesu anamveketsa bwanji coonadi conena za Ufumu wa Mulungu?

NKHANI 4

Yehova Akweza Dzina Lake

Kodi Ufumu wa Mulungu wacita zotani pofuna kuyeletsa dzina la Mulungu? Kodi inuyo mungathandize bwanji kuyeletsa dzina la Yehova?

NKHANI 5

Mfumu Imveketsa Bwino Mfundo Zokhudza Ufumu wa Mulungu

Phunzilani kuti mudziŵe bwino Ufumu wa Mulungu, olamulila ake, nzika zake ndi zimene mungacite kuti mukhale okhulupilika ku ufumuwo.