Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 5

Mfumu Imveketsa Bwino Mfundo Zokhudza Ufumu wa Mulungu

Mfumu Imveketsa Bwino Mfundo Zokhudza Ufumu wa Mulungu

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Anthu a Mulungu anamvetsetsa mfundo zofunika zokhudza Ufumu wa Mulungu, olamulila ake, nzika zake, ndi kufunika kokhala wokhulupilika

1, 2. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ndi mtsogoleli wanzelu wa anthu?

YELEKEZELANI kuti munthu wodziŵa bwino nchito yotsogolela alendo akukusonyezani mzinda wina wokongola kwambili. Inuyo ndi anthu amene muli nao ndi nthawi yoyamba kuona mzinda umenewo, ndipo mukufunitsitsa kumvetsetsa zonse zimene wokusonyezani maloyo akunena. Pamene mukuyenda mumzindawo, inu ndi anthu ena oona malo mukucita cidwi ndi zinthu zina zimene zili mumzindawo zimene mukalibe kuonapo. Pamene mukufunsa munthu amene akukusonyezani malo ponena za zinthu zina zimene mukuona, iye sakukuyankhani mpaka pa nthawi imene akuona kuti ndi yoyenela. M’kupita kwa nthawi, mukucita cidwi kwambili ndi nzelu za munthuyo cifukwa akukuuzani zinthu zimene mufuna kudziŵa panthawi yoyenela.

2 Akristu oona ali ngati anthu opita kukaona malo. Iwo akuphunzila mwacidwi za mzinda wokongola pa mizinda yonse. Mzinda umenewo ndi Ufumu wa Mulungu umene ndi “mzinda wokhala ndi maziko enieni.” (Aheb. 11:10) Pamene Yesu anali padziko lapansi, iye anathandiza otsatila ake kuti adziŵe bwino Ufumu wa Mulungu. Kodi Yesu anayankha panthawi imodzi mafunso onse a otsatila ake onena za Ufumuwo? Iyai. Iye anati: “Ndili ndi zambili zakuti ndikuuzeni, koma padakali pano simungathe kuzimvetsa zonsezo.” (Yoh. 16:12) Pokhala wotsogolela anthu wanzelu koposa, Yesu sanaphunzitse ophunzila ake zinthu zimene sanali okonzeka kuzimvetsetsa panthawiyo.

3, 4. (a) Kodi Yesu wakhala akuphunzitsa bwanji anthu okhulupilika za Ufumu wa Mulungu? (b) Kodi tiphunzila ciani m’nkhani ino?

3 Yesu anakamba mau a pa Yohane 16:12 pausiku wake womaliza padziko lapansi. Kodi zikanatheka bwanji kuti Yesu apitilize kuphunzitsa anthu okhulupilika za Ufumu wa Mulungu pambuyo pa imfa yake? Iye anatsimikizila atumwi ake kuti: “Mzimu wa coonadi, adzakutsogolelani m’coonadi conse.” * (Yoh. 16:13) Mzimu woyela uli ngati munthu wotsogolela amene ndi woleza mtima. Yesu amagwilitsila nchito mzimu kuphunzitsa otsatila ake zinthu zilizonse zimene afunika kudziŵa ponena za Ufumu wa Mulungu panthawi yoyenela.

4 Tiyeni tione mmene mzimu woyela wa Yehova wakhala ukutsogolela Akristu okhulupilika kumvetsetsa mfundo zokhudza Ufumu wa Mulungu. Coyamba, tidzaphunzila mmene tinadziŵila nthawi imene Ufumu wa Mulungu unayamba kulamulila. Ndiyeno tidzaphunzila za anthu amene adzalamulila mu Ufumuwo ndi nzika zake. Tidzaphunzila kuti io ndani, ndi kuti ali ndi ziyembekezo zotani. Pomalizila pake, tidzaona mmene otsatila a Kristu anafikila pakumvetsetsa tanthauzo la kukhala okhulupilika ku Ufumuwo.

Kudziŵa Bwino Caka Capadela

5, 6. (a) Kodi Ophunzila Baibulo anali ndi maganizo olakwika ati ponena za kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu ndi za nyengo yokolola? (b) N’cifukwa ciani zimenezi siziyenela kutipangitsa kukaikila kuti Yesu anali kutsogolela otsatila ake?

5 Monga mmene tinaonela m’Nkhani 2 m’buku lino, kwa zaka zambili, Ophunzila Baibulo anali kunena kuti caka ca 1914 cidzakhala capadela pakukwanilitsidwa kwa maulosi a m’Baibulo. Komabe, panthawiyo io anali kukhulupilila kuti kukhalapo kwa Kristu kunayamba mu 1874, ndi kuti iye anayamba kulamulila kumwamba mu 1878. Anali kukhulupililanso kuti Ufumu wa Mulungu udzakhazikitsidwa kothelatu mu October 1914, ndi kuti nchito yokolola idzacitika kuyambila mu 1874, ndi kutha mu 1914 pamene odzozedwa adzasonkhanitsidwa kumwamba. Kodi maganizo olakwika amenewa ayenela kutipangitsa kukaikila kuti Yesu anali kutsogolela anthu okhulupilika amenewo ndi mzimu woyela?

6 Ayi sitiyenela kutelo. Taganizilaninso citsanzo cija ca munthu woonetsa malo cimene cili kumayambililo kwa nkhani ino. Kodi kusayankha mafunso amene anthu okaona malo akufunsa panthawi yosayenela kungaonetse kuti munthu woonetsa maloyo ndi wosadalilika? Ayi ndithu. Mofananamo, anthu a Mulungu nthawi zina amafuna kumvetsetsa mfundo zina zokhudza colinga ca Yehova nthawi isanakwane yakuti mzimu woyela uwatsogolele kudziŵa zinthuzo. Ngakhale n’conco, n’zoonekelatu kuti Yesu akuwatsogolela. Ndiye cifukwa cake anthu okhulupilika amalolela kuwongoleledwa, ndipo modzicepetsa amasintha maganizo ao.—Yak. 4:6.

7. Ndi mfundo za coonadi ziti zimene anthu a Mulungu anali ndi mwai wozimvetsetsa?

7 Pambuyo pa caka ca 1919, anthu a Mulungu anali ndi mwai waukulu womvetsetsa mfundo zoonjezeleka za coonadi. (Ŵelengani Salimo 97:11.) M’magazini ya The Watch Tower ya mu 1925, munatuluka nkhani yapadela ya mutu wakuti “Kubadwa kwa Mtundu.” Nkhaniyo inafotokoza bwino umboni wa m’Malemba woonetsa kuti Ufumu wa Mesiya unabadwa m’caka ca 1914. Kubadwa kwa Ufumuwo kunakwanilitsa ulosi wopezeka pa Chivumbulutso caputala 12 pamene pamafotokoza za mkazi wa Mulungu wakumwamba amene anabeleka mwana. * Nkhaniyo inafotokozanso kuti cizunzo ndi mavuto amene anthu a Yehova anakumana nao m’zaka za nkhondozo, zinali cizindikilo cakuti Satana anaponyedwa padziko lapansi, ndipo “ali ndi mkwiyo waukulu podziŵa kuti wangotsala ndi kanthawi kocepa.”—Chiv. 12:12.

8, 9. (a) N’cifukwa ciani Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambili? (b) Kodi tidzakambilana mafunso otani?

8 Kodi Ufumu wa Mulungu ndi wofunika motani? Mu 1928, magazini ya The Watch Tower inayamba kugogomeza mfundo yakuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambili kuposa cipulumutso cathu kupyolela mu dipo. Ndithudi, Yehova adzayeletsa dzina lake, kukweza ulamulilo wake, ndi kukwanilitsa colinga cake kwa anthu kudzela mu Ufumu wa Mesiya.

9 Kodi ndani adzalamulila ndi Kristu mu Ufumu umenewo? Nanga ndani adzakhala nzika za padziko lapansi za Ufumuwo? Kodi otsatila a Kristu ayenela kukhala otangwanika ndi nchito yotani?

Nchito Yosonkhanitsa Odzozedwa

10. N’ciani cimene anthu a Mulungu akhala akukhulupilila ponena za a 144,000?

10 Zaka zambili caka ca 1914 cisanafike, Akristu oona anali atadziŵa kale kuti otsatila a Kristu okwana 144,000 adzalamulila naye kumwamba. * Ophunzila Baibulo anali kukhulupilila kuti ciŵelengelo cimeneci ndi ceniceni, ndi kuti anthu a m’gulu limeneli anayamba kusonkhanitsidwa m’nthawi za atumwi.

11. Kodi anthu amene adzakhala m’gulu la mkwatibwi wa Kristu anadziŵa bwanji nchito imene anafunika kugwila pano padziko lapansi?

11 Koma kodi anthu oyembekezela kukhala m’gulu la mkwatibwi wa Kristu anapatsidwa nchito yotani akali padziko lapansi? Iwo anaona kuti Yesu anali kugogomezela kwambili za nchito yolalikila, ndipo anasonyeza kuti nchitoyo idzacitika m’nyengo yokolola. (Mat. 9:37; Yoh. 4:35) Monga mmene tinaonela m’Nkhani 2, kwa kanthawi ndithu Ophunzila Baibulo anali kuona kuti nyengo yokolola idzatenga zaka 40 ndipo idzatha pamene odzodzedwa adzapita kumwamba. Komabe, popeza kuti nchitoyo inapitilizabe ngakhale pamene zaka 40 zinatha, Ophunzila Baibulo anafunika kumvetsetsa bwino nkhaniyo. Masiku ano timadziŵa kuti nyengo yokolola inayamba m’caka ca 1914. Imeneyo inali nyengo yosiyanitsa tiligu ndi namsongole, kutanthauza Akristu odzozedwa ndi Akristu onama. Nthawi inafika yosonkhanitsa otsalila a odzozedwa amene adzapita kumwamba.

Nyengo yokolola inayamba mu 1914 (Onani ndime 11)

12, 13. Kodi fanizo la Yesu la anamwali 10 ndi la matalente akukwanilitsidwa bwanji masiku otsiliza ano?

12 Kuyambila mu 1919, Kristu wakhala akutsogolela kapolo wokhulupilika ndi wanzelu kuti azigogomezela kufunika kwa nchito yolalikila. Iye anapatsa otsatila ake nchitoyi m’nthawi ya atumwi. (Mat. 28:19, 20) Yesu anasonyezanso makhalidwe amene otsatila ake anafunika kukhala nao kuti akwanilitse nchito yolalikilayo. Kodi anacita bwanji zimenezo? M’fanizo lake la anamwali khumi, Yesu anasonyeza kuti odzozedwa ayenela kukhalabe maso mwakuuzimu kuti akwanilitse colinga cao cokacita nao phwando lalikulu la cikwati kumwamba. Imeneyi ndi nthawi imene Kristu adzagwilizana ndi “mkwatibwi” wake amene ndi a 144,000. (Chiv. 21:2) Kenako, m’fanizo lake la matalente, Yesu ananena kuti atumiki ake odzozedwa adzagwila nchito yolalikila mwakhama imene iye anawapatsa.—Mat. 25:1-30.

13 M’zaka 100 zapitazi, Akristu odzozedwa aonetsa kuti ndi achelu ndiponso akhama. Mosakaikila, adzafupidwa cifukwa cokhala maso. Koma kodi colinga ca nchito yokololayi cinali cosonkhanitsa otsalila a Kristu a 144,000 cabe?

Ufumu wa Mulungu Usonkhanitsa Nzika Zapadziko Lapansi

14, 15. Kodi buku la The Finished Mystery linafotokoza kuti pali magulu anai ati a anthu?

14 Kwa nthawi yaitali, amuna ndi akazi okhulupilika akhala akufunitsitsa kudziŵa “khamu lalikulu” lochulidwa pa Chivumbulutso 7:9-14. Kristu asanavumbule kuti khamu lalikulu limeneli ndani, zinthu zambili zimene anthu anali kunena pankhaniyi n’zosiyana kwambili ndi coonadi comveka bwino cimene timadziŵa ndi kukonda masiku ano.

15 M’caka ca 1917, buku lakuti The Finished Mystery linafotokoza kuti pali “magulu aŵili a anthu amene adzapita Kumwamba, ndiponso magulu aŵili a anthu amene adzakhala ndi moyo padziko lapansi.” Kodi ndani amene anali m’magulu anai amenewo? Ophunzila Baibulo anali kukhulupilila kuti gulu loyamba ndi a 144,000 amene adzalamulila ndi Kristu kumwamba, ndipo laciŵili ndi a khamu lalikulu. Panthawiyo, ophunzila Baibulo anali kuona kuti khamu lalikulu ndi Akristu amene anali m’Machalichi Acikristu. Iwo anali kukhulupilila kuti Akristu amenewo anali ndi cikhulupililo koma cinali cocepa cakuti sakanalimba pa ziyeso. Conco anali kuona kuti anthu amenewo adzapatsidwa malo otsika kumwamba. Ophunzila Baibulo anali kukhulupililanso kuti anthu a m’gulu lacitatu ndi lacinai adzakhala padziko lapansi. Iwo anali kuona kuti gulu lacitatu ndi anthu akale okhulupilika monga Abulahamu, Mose ndi ena otelo amene adzalamulila anthu a m’gulu lacinai. Ophunzila Baibulo anali kuona kuti anthu a m’gulu lacinai ndi anthu onse padziko lapansi.

16. Ndi mfundo za coonadi ziti zimene zinamveketsedwa bwino mu 1923 ndi mu 1932?

16 Kodi mzimu woyela unathandiza bwanji otsatila a Kristu kuti amvetsetse bwino mfundo za coonadi zimene timadziŵa masiku ano? Zimenezi zinacitika pang’onopang’ono. Mu 1923, magazini ya The Watch Tower inanena kuti pali gulu lina limene silidzapita kumwamba koma lidzakhala padziko lapansi ndipo lidzalamulidwa ndi Kristu. Mu 1932, Nsanja ya Mlonda yacingelezi inafotokoza za Yehonadabu amene anagwilizana ndi Yehu, Mfumu ya Aisiraeli yodzozedwa ndi Mulungu. Anagwilizana ndi Yehu kuti am’cilikize pamene anali kumenya nkhondo n’colinga cakuti athetse kulambila konyenga. (2 Maf. 10:15-17) Nkhaniyo inakamba kuti pali gulu lina la anthu masiku ano amene ali ngati Yehonadabu. Magaziniyo inaonjezela kuti gulu limeneli ndi limene Yehova “adzapulumutsa pa nkhondo ya Aramagedo” ndi kukhala padziko lapansi.

17. (a) Ndi mfundo yocititsa cidwi iti ya coonadi imene inadziŵika bwino mu 1935? (b) Kodi Akristu okhulupilika anamva bwanji ataphunzila mfundo yatsopano yokhudza khamu lalikulu? (Onani bokosi lakuti “ Mtima Unakhala M’malo.”)

17 Mu 1935 panakhalanso kuwala kwakukulu kwa coonadi. Pa msonkhano umene unacitikila ku Washington, D.C., khamu lalikulu linadziŵika kuti ndi anthu amene adzakhala padziko lapansi, ndipo amachedwanso nkhosa zina za m’fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi. (Mat. 25:33-40) Magaziniyo inafotokoza kuti khamu lalikulu ndi a “nkhosa zina,” ndipo Yesu anati: “Zimenezonso ndiyenela kuzibweletsa.” (Yoh. 10:16) Pa msonkhanopo, M’bale J.  F. Rutherford anakamba kuti: “Inu nonse amene muli ndi ciyembekezo cokhala ndi moyo kosatha padziko lapansi imililani!” Atakamba conco, anthu oposa hafu ya amene anapezeka pa msonkhonowo anaimilila. Kenako iye analengeza kuti: “Taonani! Khamu lalikulu!” Panthawiyo ambili anasangalala cifukwa cakuti anadziŵa bwino ciyembekezo cao ca mtsogolo.

18. N’ciani cathandiza otsatila a Kristu kucita khama pa nchito yolalikila? Nanga zotsatila zake zakhala zotani?

18 Kuyambila nthawi imeneyo, Kristu wakhala akutsogolela anthu ake kuti acite khama pa nchito yosonkhanitsa anthu a khamu lalikulu amene adzapulumuka pa cisautso cacikulu. Poyamba, nchito yosonkhanitsa khamu lalikulu inaoneka kukhala yovuta cakuti panthawi ina, M’bale Rutherford anati: “Zikuoneka kuti ‘khamu lalikulu’ silidzakula kwambili.” Komabe, masiku ano tikuona kuti Yehova wadalitsa kwambili nchito yokolola kuyambila nthawi imeneyo. Akristu odzozedwa pamodzi ndi anzao a “nkhosa zina” akhala mu “gulu limodzi,” ndipo akutumikila motsogoleledwa ndi “m’busa mmodzi” monga mmene Yesu ananenela. Izi zatheka cifukwa cothandizidwa ndi Yesu ndiponso mzimu woyela.

M’bale Rutherford sanadziŵe kuti a khamu lalikulu adzaculuka (Kuyambila kulamanzele kupita kulamanja: Nathan H. Knorr, Joseph F. Rutherford, ndi Hayden C. Covington)

19. N’ciani cimene tiyenela kucita kuti ciŵelengelo ca khamu lalikulu cipitilizebe kukula?

19 Anthu ambili okhulupilika adzakhala ndi moyo m’paladaiso padziko lapansi kosatha, ndipo adzalamulidwa ndi Kristu ndi olamulila anzake okwanila 144,000. Kodi sizosangalatsa kuona mmene Kristu wakhala akutsogolela anthu a Mulungu kuti adziŵe bwino ciyembekezo cao ca m’Malemba? Timasangalala kwambili kuuzako anthu amene timapeza muutumiki wa kumunda za ciyembekezo cathu cimeneci. Tiyeni tigwile nchitoyi mwakhama mogwilizana ndi mmene zinthu zilili pa moyo wathu kuti ciŵelengelo ca khamu lalikulu cipitilizebe kukula, ndipo zimenezi zidzapeleka citamando ku dzina la Yehova.—Ŵelengani Luka 10:2.

Khamu lalikulu likuculukila-culukila

Kodi Kukhala Wokhulupilika ku Ufumu wa Mulungu Kumatanthauzanji?

20. Ndi magulu ati amene amapanga boma la Satana? Nanga n’cifukwa ciani Akristu sayenela kugwilizana ndi magulu amenewa?

20 Pamene atumiki a Mulungu anapitilizabe kuphunzila za Ufumu wa Mulungu, io anafunika kumvetsetsanso tanthauzo la kukhala okhulupilika ku boma lakumwamba limenelo. Ndiyeno, mu 1922, magazini ya The Watch Tower inafotokoza kuti pali maboma aŵili amene akugwila nchito. Pali boma la Yehova ndiponso boma la Satana. Boma la Satana ndi magulu amalonda, zipembedzo ndi magulu a ndale. Anthu onse okhulupilika ku Ufumu wa Mulungu motsogoleledwa ndi Kristu sayenela kugwilizana ndi boma la Satana ngati afuna kukhalabe okhulupilika. (2 Akor. 6:17) Kodi zimenezi zikutanthauzanji?

21. (a) Ndi macenjezo ati amene kapolo wokhulupilika amapeleka kuti anthu a Mulungu apewe mzimu wokondetsa cuma umene uli m’magulu a zamalonda? (b) Kodi Nsanja ya Mlonda inavumbula ciani za “Babulo Wamkulu” mu 1963?

21 Kapolo wokhulupilika wakhala akuvumbula cinyengo cimene cimacitika m’magulu a malonda ndi kucenjeza atumiki a Mulungu kuti asatengeke ndi mzimu wokondetsa cuma wa magulu amenewa. (Mat. 6:24) Masiku ano, zofalitsa zathu zatithandizanso kudziŵa magulu a zipembezo za Satana. Mu 1963, Nsanja ya Mlonda inafotokoza kuti “Babulo Wamkulu” samaimila cabe Machalichi Acikristu, koma amaimila ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conama. Ndipo monga mmene tidzaonela m’Nkhani 10 m’buku lino, atumiki a Mulungu ocokela m’dziko lililonse ndi a zikhalidwe zosiyanasiyana akhala akulangizidwa kuti ayenela ‘kutuluka mwa iye’ ndi kudziyeletsa mwa kusiya kucita miyambo ya cipembedzo conyenga.—Chiv. 18:2, 4.

22. Panthawi ya Nkhondo Yoyamba Yapadziko Lonse, kodi anthu ambili a Mulungu anali kukhulupilila kuti malangizo a pa Aroma 13:1 amatanthauzanji?

22 Nanga bwanji ponena za gulu la ndale la m’dziko la Satana? Kodi Akristu oona ayenela kutenga nao mbali pa nkhondo ndi mikangano ya maiko? Panthawi ya nkhondo yoyamba yapadziko lonse, Ophunzila Baibulo anali kudziŵa kuti otsatila a Kristu sayenela kupha anthu anzao. (Mat. 26:52) Komabe, ambili anali kukhulupilila kuti malangizo opezeka pa Aroma 13:1 onena kuti tiyenela kumvela “olamulila akuluakulu” anali kutanthauza kuti munthu angathe kukhala m’gulu la asilikali, kuvala yunifomu ya asilikali, ndi kunyamula mfuti, koma sanali kufunika kupha mdani. M’malo mwake anayenela kuombela mfuti m’mwamba.

23, 24. Panthawi ya Nkhondo Yaciŵili ya Padziko Lonse, kodi otsatila a Kristu anali kukhulupilila kuti lemba la Aroma 13:1 limatanthauzanji? Nanga ndi mfundo iti ya coonadi imene io anathandizidwa kumvetsetsa?

23 Pamene nkhondo yaciŵili yapadziko lonse inali kuyamba m’caka ca 1939, mu Nsanja ya Mlonda yacingelezi munatuluka nkhani imene inafotokoza kwambili cifukwa cake sitiyenela kutenga mbali m’zandale. Nkhaniyo inafotokoza kuti Akristu sayenela kutengako mbali m’nkhondo kapena m’mikangano ya maiko a m’dziko la Satana. Malangizowa analidi a panthawi yake. Mwa kutsatila malangizo amenewa, otsatila a Kristu anapewa kukhala ndi mlandu wa magazi umene anthu ambili amene anamenya nao nkhondo anali nao. Komabe, kuyambila mu 1929, zofalitsa zathu zinayamba kufotokoza kuti olamulila akuluakulu ochulidwa pa Aroma 13:1 ndi Yehova ndi Yesu osati olamulila andale. Motelo panafunika mafotokozedwe ena omveka bwino kwambili pankhaniyo.

24 Mu 1962, mzimu woyela unatsogolela otsatila a Kristu kuti amvetse bwino mfundo ya pa Aroma 13:1-7. Mu Nsanja ya Olonda ya November 15 ndi ya December 1 m’cakaco, munatuluka nkhani zapadela zofotokoza lembali. Pomalizila pake, anthu a Mulungu anamvetsetsa tanthauzo la mfundo ya kugonjela imene imapezeka m’mau ochuka a Yesu akuti “pelekani zinthu za Kaisala kwa Kaisala, koma za Mulungu kwa Mulungu.” (Luka 20:25) Masiku ano, Akristu oona amadziŵa kuti olamulila akuluakulu amatanthauza olamulila a maboma a dziko, ndipo Akristu ayenela kuwagonjela. Koma kugonjela kumeneku kuli ndi polekezela. Olamulila a dziko akatiuza kuti tisamvele Yehova Mulungu, timayankha mmene atumwi akale anayankhila kuti: “Tiyenela kumvela Mulungu monga wolamulila, osati anthu.” (Mac. 5:29) M’Nkhani 13 ndi 14 m’buku lino, tidzaphunzila zambili za mmene anthu a Mulungu agwilitsilila nchito mfundo yakuti Akristu sayenela kutenga mbali m’zandale.

Ndi mwai waukulu kwambili kuuzako ena za ciyembekezo cathu ca moyo wosatha

25. N’cifukwa ciani mumayamikila kuti mzimu woyela umatithandiza kumvetsetsa coonadi cokhudza Ufumu wa Mulungu?

25 Ganizilani zinthu zimene otsatila a Kristu aphunzitsidwa ponena za Ufumu wa Mulungu pa zaka 100 zapitazi. Taphunzila za nthawi pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba ndiponso kufunika kwake. Masiku ano tikudziŵa bwino kuti anthu okhulupilika ali ndi ziyembekezo ziŵili zosiyana. Ena ali ndi ciyembekezo copita kumwamba pamene ena ali ndi ciyembekezo codzakhala padziko lapansi. Taphunzilanso mmene tingaonetsele kuti ndife okhulupilika ku Ufumu wa Mulungu, ndipo panthawi imodzimodzi kukhala ogonjela kwa olamulila a dziko pamlingo woyenela. Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndikanadziŵa coonadi ca mtengo wapatali cimeneci zikanakhala kuti Yesu Kristu sanali kutsogolela kapolo wake wokhulupilika padziko lapansi kuti amvetsetse coonadi cimeneci ndi kutiphunzitsa?’ Ndife oyamikila kwambili kuti Kristu ndi mzimu woyela akhala akutitsogolela.

^ par. 3 Buku lina limanena kuti liu Lacigiriki limene analimasulila kuti ‘kutsogolela’ pa vesili limatanthauza “kusonyeza njila.”

^ par. 7 Caka ca 1925 cisanafike, atumiki a Mulungu anali kukhulupilila kuti masomphenya amenewa anali kucitila cithunzi nkhondo ya pakati pa cipembedzo cacikunja ca ufumu wa Roma ndi Chalichi ca Roma Katolika.

^ par. 10 Mu June caka ca 1880, magazini ya Zion’s Watch Tower inanena kuti anthu a 144,000 ndi Ayuda amene adzakhala Akristu pofika caka ca 1914. Koma cakumapeto kwa caka ca 1880, nkhani ina inafalitsidwa imene inafotokoza bwino za anthu amenewa, ndipo mfundo zake sizinasinthe mpaka panthawi ino.