Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 4

Yehova Akweza Dzina Lake

Yehova Akweza Dzina Lake

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Mmene Anthu a Mulungu anayambila kulemekeza kwambili dzina la Mulungu

1, 2. Kodi Baibulo la Dziko Latsopano limakweza bwanji dzina la Mulungu?

KAGULU kocepa ka abale odzozedwa a pa Beteli ya ku Brooklyn, mu mzinda wa New York, kanayamba nchito yaikulu yotembenuza Baibulo latsopano pa Ciŵili pa December 2, 1947. Tsikulo, dzuŵa linali kuwala ndipo kunja kunali kozizila pang’ono. Ngakhale kuti nchitoyo inali yaikulu kwambili ndi yovuta, io anapitiliza kuigwila kwa zaka 12. Iwo anamaliza nchitoyo pa Sondo pa March 13, 1960. Pambuyo pa miyezi itatu, pa June 18, 1960, M’bale Nathan Knorr analengeza za kutuluka kwa Baibulo la Dziko Latsopano lathunthu pa msonkhano wacigawo wosangalatsa umene unacitikila ku Manchester, m’dziko la England. Mau amene iye anakamba anafotokoza bwino mmene anthu pa msonkhanowo anamvelela. Iye analengeza kuti: ‘Lelo ndi tsiku lacisangalalo kwa Mboni za Yehova padziko lonse lapansi!’ Baibulo latsopano limeneli ndi lapadela cifukwa cakuti linabwezeletsa dzina la Mulungu pa malo onse amene linali kupezeka m’mipukutu yoyamba ya Baibulo. Zimenezi n’zimene zinapangitsa kuti anthuwo asangalale kwambili.

Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Acigiriki Acikristu linatulutsidwa m’Cingelezi mu 1950, pa msonkhano wadela wa mutu wakuti Kuwonjezeka kwa Teokalase (Kulamanzele: Yankee Stadium, mu mzinda wa New York City; Ku Ghana)

2 M’ma Baibulo ambili anacotsamo dzina la Mulungu. Koma atumiki odzozedwa a Yehova analimbana ndi macenjela a Satana ofuna kupangitsa anthu kuiwalilatu dzina la Mulungu. Mau oyamba a mu Baibulo la Dziko Latsopano limene linatulutsidwa panthawiyo anati: “Cinthu capadela kwambili m’Baibulo lino n’cakuti tabwezeletsa dzina la Mulungu m’malo ake oyenelela.” Ndithudi, Baibulo la Dziko Latsopano limagwilitsila nchito dzina la Mulungu lakuti Yehova nthawi zoposa 7,000. Kunena zoona, Baibulo limeneli lakweza kwambili dzina la Atate wathu wakumwamba, Yehova.

3. (a) Kodi abale athu anazindikila kuti dzina la Mulungu limatanthauzanji? (b) Kodi lemba la Ekisodo 3:13, 14 limatanthauzanji? (Onani bokosi lakuti “Tanthauzo la Dzina la Mulungu.”)

3 Poyamba, Ophunzila Baibulo anali kukhulupilila kuti dzina la Mulungu limatanthauza kuti “Ine ndine yemwe ndili ine.” (Eks. 3:14, Buku lopatulika) Conco, magazini ya Watch Tower ya 1926 inati: “Dzina lakuti Yehova limatanthauza kuti iye anakhalako yekha, . . . alibe ciyambi ndi mapeto.” Koma pamene abale anayamba kutembenuza Baibulo la Dziko Latsopano, Yehova anawathandiza kuzindikila kuti dzina lake silimangotanthauza kuti iye anakhalako yekha, koma makamaka kuti Mulungu amacita zinthu kuti akwanilitse colinga cake. Iwo anadziŵa kuti dzina lakuti Yehova limatanthauza kuti “Iye Amacititsa Kukhala.” Iye analenga cilengedwe conse kuphatikizapo zolengedwa za nzelu, ndipo akupitilizabe kukwanilitsa colinga cake. N’cifukwa ciani n’zofunika kwambili kuti dzina la Mulungu likwezedwe, nanga tingathandize bwanji kukweza dzinalo?

Kuyeletsedwa kwa Dzina la Mulungu

4, 5. (a) Tikamapemphela kuti: “Dzina lanu liyeletsedwe,” n’ciani cimene timakhala tikupempha? (b) Kodi Mulungu adzayeletsa bwanji dzina lake? Nanga adzacita liti zimenezo?

4 Yehova amafuna kuti dzina lake likwezedwe. Ndipo colinga cake cacikulu ndi kuyeletsa dzina lakelo. Cinthu coyamba cimene Yesu anapempha m’pemphelo lake lacitsanzo, cimaonetsa colinga ca Mulungu cacikulu cimeneci. Iye anati: “Dzina lanu liyeletsedwe.” (Mat. 6:9) Kodi tikamanena mau amenewa timakhala tikupempha ciani?

5 Monga mmene tinaphunzilila m’Nkhani 1 ya buku lino, pempho lakuti “Dzina lanu liyeletsedwe” ndi limodzi mwa mapempho atatu a m’pemphelo lacitsanzo la Yesu amene amakhudza colinga ca Yehova. Mapempho ena aŵili ndi akuti: “Ufumu wanu ubwele” ndi kuti “Cifunilo canu cicitike.” (Mat. 6:10) Conco, tikamapempha Yehova kuti Ufumu wake ubwele ndi kuti cifunilo cake cicitike, timakhala tikupempha Yehova kuti acitepo kanthu kuti ayeletse dzina lake. M’mau ena, timapempha Yehova kuti acite zinthu zimene zingayeletse dzina lake cifukwa cakuti lakhala likutonzedwa kucokela pamene anthu anam’pandukila mu Edeni. Kodi Yehova adzayankha bwanji pemphelo limeneli? Iye anati: “Ndidzayeletsa dzina langa lalikulu limene linali kudetsedwa pakati pa mitundu ina ya anthu.” (Ezek. 36:23; 38:23) Pa Aramagedo, Yehova adzayeletsa dzina lake mwa kucotsa kuipa konse.

6. Kodi tingathandize bwanji kuyeletsa dzina la Mulungu?

6 Kuyambila kale, Yehova wakhala akupatsa anthu mwai wothandiza kuyeletsa dzina lake. Koma ife sitingapangitse dzina la Mulungu kukhala lapadela kuposa mmene lilili. Dzinalo ndi lapadela kwambili, ndipo ndi lopatulika kale. Nanga tingaliyeletse bwanji? Yesaya anati: “Yehova wa makamu ndi amene muyenela kumuona kuti ndi woyela.” Pokamba za anthu ake, Yehova anati: “Iwo adzayeletsa dzina langa . . . , ndipo adzalemekeza kwambili Mulungu wa Isiraeli.” (Yes. 8:13; 29:23) Motelo timayeletsa dzina la Mulungu mwa kuliona kukhala lopatulika ndi lokwezeka kuposa maina onse. Timayeletsanso dzina la Mulungu mwa kulemekeza mwini wa dzinalo ndi kuthandiza ena kuti aziliona kukhala loyela. Njila yaikulu yolemekezela dzina la Mulungu ndi kuvomeleza kuti Yehova ndi Wolamulila wathu ndi kumumvela ndi mtima wonse.—Miy. 3:1; Chiv. 4:11.

Mulungu anakonzekeletsa anthu ake kuti azidziŵika ndi dzina lake ndi kulikweza

7, 8. (a) N’cifukwa ciani panatenga nthawi yaitali kuti anthu a Mulungu ayambe kudziŵika ndi dzina lake? (b) Nanga tsopano tikambilana ciani?

7 Atumiki a Mulungu amakono akhala akugwilitsila nchito dzina la Mulungu m’zofalitsa zao kuyambila m’zaka za m’ma 1870. Mwacitsanzo, m’magazini ya Watch Tower ya August 1879, ndiponso m’buku la nyimbo limene linafalitsidwa m’cakaco, (Songs of the Bride), munali dzina lakuti Yehova. Komabe, panthawiyo Yehova anali asanavomeleze kuti anthu ake azidziŵika ndi dzina lake loyela. Iye anafuna kuwakonzekeletsa coyamba kuti akhale oyenelela kulandila mwai wodziŵika ndi dzinalo. Kodi Yehova anakonzekeletsa bwanji Ophunzila Baibulo oyambililawo kuti azidziŵika ndi dzina lake?

8 Tikaganizila mmene zinthu zinalili cakumapeto kwa zaka za m’ma 1800 ndi kuciyambi kwa zaka za m’ma 1900, timaona mmene Yehova anathandizila anthu ake kumvetsetsa mfundo za coonadi zokhudza dzina lake. Tiyeni tikambilane mfundo zitatu mwa mfundo za coonadi zimenezi.

9, 10. (a) N’cifukwa ciani nkhani za m’magazini ya Watch Tower oyambilila zinali kukamba kwambili za Yesu? (b) Zinthu zinasintha bwanji mu 1919? Nanga panali zotsatilapo zotani? (Onani bokosi lakuti “ Kodi Nsanja ya Mlonda Yakweza Bwanji Dzina la Mulungu?”)

9 Coyamba, atumiki a Yehova anazindikila kuti dzina la Mulungu ndi lofunika kwambili. Ophunzila Baibulo okhulupilika anali kuona nkhani ya dipo monga ciphunzitso cacikulu ca Baibulo. Ndiye cifukwa cake nthawi zambili magazini ya Watch Tower anali kukamba za Yesu. Mwacitsanzo, m’caka cimene magaziniyi inayamba kufalitsidwa, dzina la Yesu linali kuchulidwa maulendo 10 kuposa dzina la Yehova. Ponena za Ophunzila Baibulo oyambilila, Nsanja ya Olonda ya March 15, 1976 inanena kuti io anali kupatsa Yesu “ulemu wopambanitsa.” Koma m’kupita kwa nthawi, Yehova anawathandiza kuzindikila kuti Baibulo limasonyeza kuti dzina la Mulungu ndi lofunika kwambili. Kodi Ophunzila Baibulo anacita ciani atazindikila zimenezi? Nsanjayo inanenanso kuti, kuyambila m’caka ca 1919, “io anayamba kulemekeza kwambili Yehova, Atate a Mesiya akumwamba.” Ndipo pa zaka 10 kucokela mu 1919, magazini ya The Watch Tower inachula dzina la Mulungu nthawi zoposa 6,500.

10 Pamene abale athu anayamba kulemekeza kwambili dzina lakuti Yehova, io anasonyeza kuti anali kukonda kwambili dzinalo. Mofanana ndi Mose, io anayamba ‘kulengeza dzina la Yehova.” (Deut. 32:3; Sal. 34:3) Conco, mogwilizana ndi zimene Malemba amanena, Yehova anaona kuti io anali kukonda dzina lake, ndipo anawakomela mtima.—Sal. 119:132; Aheb. 6:10.

11, 12. (a) Kodi magazini athu anasintha bwanji kuyambila m’caka ca 1919? (b) N’ciani cimene Yehova anathandiza atumiki ake kuzindikila? Nanga n’cifukwa ciani?

11 Caciŵili, Akristu oona anazindikila nchito imene Mulungu anawapatsa. Caka ca 1919 citatha, abale odzozedwa amene anali kutsogolela gulu anayamba kupenda ulosi wa Yesaya. Pambuyo pake, zofalitsa zathu zinayamba kufotokoza kwambili nkhani zokhudza nchito yolalikila. Kodi kusintha kumeneku kunathandiza bwanji atumiki a Mulungu kulandila “cakudya pa nthawi yoyenela”?—Mat. 24:45.

12 Caka ca 1919 cisanafike, magazini ya The Watch Tower anali asanafotokozepo momveka bwino mau a Yesaya akuti: “‘Inu ndinu mboni zanga,” akutelo Yehova. ‘Ndinu mtumiki wanga amene ndakusankhani.’” (Ŵelengani Yesaya 43:10-12.) Koma caka ca 1919 citatha, zofalitsa zathu zinayamba kufotokoza tanthauzo la mau amenewa momveka bwino ndi kulimbikitsa odzozedwa onse kugwila nao nchito yocitila umboni za Yehova, imene Mulungu anawapatsa. Ndipo kucokela mu 1925 mpaka mu 1931, lemba la Yesaya 43 linafotokozedwa m’magazini osiyanasiyana ya The Watch Tower okwanila 57, ndipo magazini onsewo anafotokoza kuti lembali limanena za Akristu. N’zoonekelatu kuti m’zaka zimenezo, Yehova anali kuthandiza atumiki ake kudziŵa nchito imene anayenela kugwila. N’cifukwa ciani anacita zimenezi? Iye anacita zimenezi kuti ‘awayese kaye ngati anali oyenelela.’ (1 Tim. 3:10) Ophunzila Baibulo asanayambe kudziŵika ndi dzina la Mulungu, io anafunikila kuonetsa mwa nchito zao pamaso pa Yehova kuti analidi mboni zake.—Luka 24:47, 48.

13. Kodi Mau a Mulungu amaonetsa bwanji kuti kuyeletsedwa kwa dzina la Mulungu n’kofunika koposa?

13 Cacitatu, anthu a Yehova anazindikila kufunika kwakuti dzina la Mulungu liyeletsedwe. M’zaka za m’ma 1920, io anazindikila kuti cinthu cofunika koposa ndi kuyeletsedwa kwa dzina la Mulungu. Kodi Mau a Mulungu amavumbula bwanji mfundo yofunika ya coonadi imeneyi? Ganizilani zitsanzo ziŵili izi. Kodi cifukwa cacikulu cimene Mulungu anapulumutsila Aisiraeli ku Iguputo cinali ciani? Yehova anati: “Kuti dzina langa lilengezedwe padziko lonse lapansi.” (Eks. 9:16) Nanga n’cifukwa ciani Yehova anacitila cifundo Aisiraeli pamene anamupandukila? Yehova ananenanso kuti: “Ndinacita zinthu molemekeza dzina langa kuti lisadetsedwe pamaso pa anthu a mitundu ina.” (Ezek. 20:8-10) Kodi Ophunzila Baibulo anaphunzilapo ciani pa nkhani za m’Baibulo zimenezi ndi zina?

14. (a) Kodi anthu a Mulungu anazindikila ciani cakumapeto kwa zaka za m’ma 1920? (b) Kodi mfundo imene Ophunzila Baibulo anamvetsetsa inakhudza bwanji nchito yolalikila? (Onani kabokosi kakuti “ Cifukwa Cacikulu Cogwilila Nchito Yolalikila.”)

14 Cakumapeto kwa zaka za m’ma 1920, anthu a Mulungu anazindikila kufunika kwa mau amene Yesaya ananena zaka 2,700 zapitazo. Ponena za Yehova, Yesaya anati: “Inu munatsogolela anthu anu kuti mudzipangile dzina lokongola.” (Yes. 63:14) Ophunzila Baibulo anazindikila kuti cinthu cofunika kwambili ndi kuyeletsedwa kwa dzina la Mulungu osati kupulumutsidwa kwao. (Yes. 37:20; Ezek. 38:23) Mu 1929, buku lacingelezi lochedwa Prophecy linafotokoza momveka bwino mfundo ya coonadi imeneyi. Ilo linati: “Kuyeletsedwa kwa dzina la Mulungu ndiyo nkhani yofunika kwambili kuposa zonse.” Kumvetsetsa mfundo imeneyi kunalimbikitsa anthu a Mulungu kuti azicitila umboni za Yehova ndi kucotsa citonzo pa dzina lake.

15. (a) Kodi abale athu anazindikila ciani ca m’ma 1930? (b) Kodi nthawi imeneyi inali yakuti Mulungu acite ciani?

15 Pofika kuciyambi kwa zaka za m’ma 1930, abale athu anazindikila kuti dzina la Mulungu ndi lofunika kwambili. Iwo anazindikilanso nchito imene Mulungu anawapatsa ndiponso anamvetsetsa kuti kuyeletsedwa kwa dzina la Mulungu ndi kofunika kwambili kuposa zonse. Tsopano nthawi inakwana yakuti Yehova apatse anthu ake mwai wodziŵika ndi dzina lake. Kuti timvetsetse mmene anthu a Mulungu anayambila kudziŵika ndi dzina lake, tiyeni tikambilane zinthu zina zimene zinacitika m’mbuyomu.

Yehova Atenga “Anthu Odziwika ndi Dzina Lake”

16. (a) Ndi njila yaikulu iti imene Yehova amakwezela dzina lake? (b) Ndani anali woyamba kuimila dzina la Mulungu m’nthawi yakale?

16 Njila yaikulu imene Yehova amakwezela dzina lake ndi kukhala ndi anthu odziŵika ndi dzina lake pano padziko lapansi. Kuyambila m’caka ca 1513 B.C.E, mtundu wa Isiraeli unali kuimila Yehova monga anthu ake. (Yes. 43:12) Koma io analephela kusunga pangano limene anapanga ndi Mulungu, ndipo mu 33 C.E., anataya mwai wao wokhala naye paubwenzi wapadela. Patapita nthawi yocepa, Yehova “anaceukila anthu a mitundu ina . . . kuti mwa io atengemo anthu odziŵika ndi dzina lake.” (Mac. 15:14) Gulu limene linasankhidwalo linayamba kuchedwa “Isiraeli wa Mulungu,” amene ndi otsatila a Kristu odzozedwa ocokela m’mitundu yosiyanasiyana.—Agal. 6:16.

17. Kodi Satana anacita ciani pofuna kuti Akristu oona asadziŵike?

17 Ca m’ma 44 C.E., ophunzila a Kristu “anayamba kuchedwa Akhristu, motsogoleledwa ndi Mulungu.” (Mac. 11:26) Poyamba, Akristu oona okha ndi amene anali kudziŵika ndi dzina limeneli. (1 Pet. 4:16) Komabe, monga mmene fanizo la Yesu la tiligu ndi namsongole limasonyezela, Satana mwamacenjela anapangitsa kuti anthu ena azidziŵika ndi dzina lapadela lakuti Akristu. Conco kwa zaka zambili, Akristu oona sanali kudziŵika pakati pa anthu odzicha Akristu. Koma zimenezi zinayamba kusintha ‘m’nthawi yokolola’ imene inayamba mu 1914. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti angelo anayamba kusiyanitsa Akristu oona ndi onama.—Mat. 13:30, 39-41.

18. N’ciani cinathandiza abale athu kudziŵa kuti afunikila dzina latsopano?

18 Pambuyo poika kapolo wokhulupilika mu 1919, Yehova anathandiza anthu ake kudziŵa nchito imene anayenela kugwila. Patapita nthawi yocepa, anthu a Mulungu anadziŵa kuti nchito yolalikila khomo ndi khomo inali kuwasiyanitsa ndi Akristu onama. Atangozindikila mfundo imeneyi, io anaona kuti dzina lakuti “Ophunzila Baibulo” silinali kuwasiyanitsa mokwanila ndi Akristu onama. Iwo anadziŵa kuti colinga cao cacikulu pa umoyo sicinali kuphunzila Baibulo cabe koma kucitila umboni za Mulungu ndiponso kulemekeza ndi kukweza dzina lake. Conco, kodi ndi dzina liti limene linali loyenelela malinga ndi nchito imene anali kugwila? Funso limenelo linayankhidwa m’caka ca 1931.

Kapulogilamu ka msonkhano wa cigawo, mu 1931

19, 20. (a) Kodi anthu amene anasonkhana pa msonkhano wacigawo mu 1931 anavomeleza ciani? (b) Kodi abale athu anamva bwanji atalandila dzina latsopano?

19 Mu July 1931, Ophunzila Baibulo pafupifupi 15,000 anapezeka pa msonkhano wacigawo umene unacitikila ku Columbus, Ohio, m’dziko la United States. Ataona kapulogalamu ka msonkhano, io anacita cidwi ndi zilembo zazikulu ziŵili za J ndi W zimene zinalembedwa patsamba loyamba la kapulogalamuko. Iwo anadabwa, ndipo anali kudzifunsa kuti ‘Kodi zilembozi zikutanthauzanji?’ Iwo anali ndi maganizo osiyanasiyana ponena za tanthauzo la zilembozo. Ndiyeno pa Sondo, pa July 26, M’bale Joseph Rutherford anaŵelenga cigamulo cofunika kwambili cakuti: “Tikufuna kuchedwa ndi dzina lakuti, Mboni za Yehova.” Panthawiyo, onse amene anapezeka pa msonkhanowo anadziŵa kuti zilembo za J ndi W zinali kuimila dzina lakuti Mboni za Yehova m’Cingelezi. Dzina la m’Malemba limeneli linatengedwa pa Yesaya 43:10.

20 Anthu anavomeleza kuti azidziŵika ndi dzina limeneli pamene anaomba m’manja kwa nthawi yaitali ndi kufuula mokondwela. Kuomba m’manja ndi kufuula mokondwela kumene abale anacita ku msonkhano umene unacitikila ku Columbus, kunamveka madela ambili padziko lapansi kudzela pa wailesi. M’bale Ernest ndi mlongo Naomi Barber a ku Australia ananena kuti: “Pamene abale a ku Melbourne anamva kuomba m’manja kwa abale ku America, io analumphalumpha ndi kuyambanso kuomba m’manja. Sitidzaiwala zimene zinacitikazo.” *

Dzina la Mulungu Likulemekezedwa Padziko Lonse

21. Kodi kukhala ndi dzina latsopano kunalimbikitsa bwanji abale kugwila nchito yolalikila?

21 Atumiki a Mulungu atalandila dzina la m’Malemba lakuti Mboni za Yehova, analimbikitsidwa kwambili kugwila nchito yolalikila. M’bale Edward Grimes ndi mkazi wake Jessie, amene anali apainiya ku United States ndipo anapezekapo pa msonkhano wacigawo wa ku Columbus mu 1931, anati: “Pamene tinali kucoka kunyumba tinali kuchedwa Ophunzila Baibulo, koma pobwelela kunyumba tinayamba kuchedwa Mboni za Yehova. Tinasangalala kuti tsopano tili ndi dzina limene limatipangitsa kulemekeza dzina la Mulungu wathu.” Msonkhanowo utatha, Mboni zina zinayamba kugwilitsila nchito njila ina yatsopano polalikila. Iwo akafika pakhomo la mwininyumba anali kumupatsa kakhadi kolembedwa kuti: “Ndine mmodzi wa mboni za YEHOVA, ndikulalikila za Ufumu wa YEHOVA Mulungu wathu.” Ndithudi, anthu a Mulungu anali kunyadila kudziŵika ndi dzina la Yehova, ndipo anali okonzeka kulengeza za dzinalo pa dziko lonse.—Yes. 12:4.

“Pamene tinali kucoka kunyumba tinali kuchedwa Ophunzila Baibulo, koma pobwelela kunyumba tinayamba kuchedwa Mboni za Yehova”

22. N’ciani cimaonetsa kuti anthu a Yehova ndi apadela?

22 Tsopano papita zaka zambili kucokela pamene Yehova anathandiza abale athu odzozedwa kuti ayambe kudziŵika ndi dzina lapadela limeneli. Dzinali lakhala cizindikilo ca mboni za Mulungu kucokela panthawiyo. Zocita za Satana sizinalepheletse anthu ena kudziŵa anthu a Mulungu. Mosasamala kanthu zoyesayesa zake, anthu amatha kusiyanitsa pakati pa anthu a Mulungu ndi anthu a zipembedzo zina. (Ŵelengani Mika 4:5; Malaki 3:18.) Tsopano timadziŵika kwambili ndi dzina la Mulungu cakuti munthu aliyense amene wagwilitsila nchito dzinali amaonedwa monga Mboni ya Yehova. Atumiki oona a Yehova amadziŵika bwino kwambili pakati pa zipembedzo zonama, ndipo kulambila koona ‘kwakwezedwa pamwamba pa mapili ang’onoang’ono.’ (Yes. 2:2) Kulambila koona ndiponso dzina la Yehova lopatulika zakwezedwa kwambili masiku ano.

23. Mogwilizana ndi Salimo 121:5, ndi mfundo iti yokhudza Yehova imene imatilimbikitsa?

23 N’zolimbikitsa kwambili kudziŵa kuti Yehova amatiteteza kwa Satana masiku ano ndiponso adzatiteteza mtsogolo. (Sal. 121:5) Motelo, tili ndi cifukwa comveka cokhalila osangalala ngati wamasalimo amene anati: “Wodala ndi mtundu umene Mulungu wao ndi Yehova, anthu amene iye wawasankha kukhala colowa cake.”—Sal. 33:12.

^ par. 20 Kuti mumve zambili zokhudza mmene anali kugwilitsila nchito wailesi imeneyi, onani Nkhani 7, patsamba 72 mpaka 74.