Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila

Kalata Yocokela ku Bungwe Lolamulila

Wokondedwa Wolengeza Ufumu Mnzathu:

YELEKEZELANI kuti ndi patsiku la Cisanu m’mawa pa October 2, 1914, ndipo ndinu membala wa banja la Beteli ku Brooklyn. Mwakhala pa mpando wanu pathebulo m’cipinda codyela kuyembekezela M’bale C. T. Russell kuti mudye cakudya ca mmaŵa. Posapita nthawi yaitali, M’bale Russell akuloŵa m’cipindaco. Mwacizoloŵezi cake, iye akuima pang’ono ndi kupeleka moni mosangalala ku banja la Beteli. Iye akuti: “Mwauka bwanji nonse?” Koma m’malo mwakuti akhale pansi pampando wake, iye akuomba m’manja ndi kupeleka cilengezo cosangalatsa cakuti: “Nthawi za Akunja zatha. Nthawi yoti mafumu ao alamulile yatha.” Mutamva zimenezi, mukukondwela kwambili cifukwa cakuti mwakhala mukuyembekezela nthawi imeneyi kwa zaka zambili. Ndiyeno, inu pamodzi ndi onse a m’banja la Beteli, mukuomba m’manja kwa nthawi yaitali cifukwa ca cilengezo cosangalatsa cimeneci.

Papita zaka zambili kucokela pamene M’bale Russell anakamba mfundo yosangalatsa imeneyi. Kodi Ufumu wa Mulungu wacita ciani kucokela panthawiyo? Wacita zambili ndithu. Kupyolela mu Ufumuwu, Yehova wakhala akuyenga ndi kuphunzitsa anthu ake pang’onopang’ono kuyambila pamene anali masauzande oŵelengeka mu 1914 mpaka masiku ano pamene afika pafupifupi 8 miliyoni. Kodi maphunzilo amenewa akupindulitsani m’njila ziti?

Masiku ano, abale amakonda kunena kuti, “galeta la kumwamba la Yehova likuyenda mofulumila.” Zimenezi n’zoona. Komabe, galeta la kumwamba limeneli, kutanthauza mbali yosaoneka ya gulu la Yehova, lakhala likuthamanga kwambili makamaka kuyambila mu 1914. Mukaŵelenga buku lino, mudzaona umboni wa zimenezi. Alengezi a Ufumu akhala akugwilitsila nchito njila zosiyanasiyana zothandiza kufalitsa uthenga wabwino padziko lonse. Zina mwa njila zimenezi ndi kugwilitsila nchito manyuzipepala, makanema, makadi aulaliki, magalamafoni, mawailesi, ndi Intaneti. Nthawi zina anali kulalikila akuyenda gulu atanyamula zikwangwani za uthenga.

Cifukwa cakuti Yehova akudalitsa nchitoyi, tsopano timasindikiza zofalitsa zophunzilila Baibulo zokongola m’zinenelo zoposa 670 ndi kuzigaŵila kwa anthu popanda kuwalipilitsa. Abale ndi alongo amadzipeleka kumanga Nyumba za Ufumu, Malo a Misonkhano, ndi maofesi a nthambi m’maiko olemela ndi osauka omwe. Ndipo m’dela lina mukacitika ngozi, cifukwa ca cikondi abale ndi alongo amathamangilako mwamsanga kukathandiza anthu okhudzidwa ndi ngoziyo. Mwa kucita zimenezi, io amaonetsa kuti abale ‘anabadwila kuti athandize pakagwa mavuto.’Miy. 17:17.

Nthawi zina, atsogoleli a zipembedzo ndi anthu ena otsutsa ‘amayambitsa mavuto mwa kupanga malamulo.’ Koma n’zolimbitsa cikhulupililo kudziŵa kuti kaŵilikaŵili zocita zaozo zimathandiza “kupititsa patsogolo uthenga wabwino m’malo moulepheletsa.”Sal. 94:20; Afil. 1:12.

Ndi mwai kutumikila limodzi ndi inu ‘anchito anzathu apakhomo.’ Dziŵani kuti timakukondani kwambili nonsenu. Pemphelo lathu n’lakuti buku lino likuthandizeni kuyamikila kwambili coloŵa canu cocokela kwa Mulungu kuposa kale.Mat. 24:45.

Tikufunilani zabwino zonse,

Ndife abale anu,

Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova