Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kumanzele: Katundu wa cithandizo wotumizidwa ndi abale a ku Switzerland wopita kwa abale ku Germany, mu 1946; kulamanja: Nyumba ya Ufumu ikumangidwanso ku Japan pambuyo pa cigumula ca madzi cocedwa tsunami, mu 2011

CIGAWO 6

Kucilikiza Ufumu—Kumanga Malo Olambilila ndi Kupeleka Thandizo Pakacitika Ngozi

Kucilikiza Ufumu—Kumanga Malo Olambilila ndi Kupeleka Thandizo Pakacitika Ngozi

TAYELEKEZELANI kuti mwaloŵa m’Nyumba ya Ufumu, ndipo mukuona kuti m’katimo mwasithilatu. Nyumba ya Ufumu imeneyi mumainyadila. Mumakumbukila nthawi imene munagwila nao nchito yomanga Nyumba ya Ufumu imeneyi mokondwa zaka zingapo zapitazo. Koma tsopano mwapeza cifukwa cina cokhalila wonyadila kwambili ndi Nyumba ya Ufumu imeneyi. Zili conco cifukwa nyumbayo aisandutsa malo ogaŵilapo thandizo la anthu amene akhudzidwa ndi ngozi yacilengedwe. Posacedwapa, kudela kwanuko kunagwa cimvula camkuntho. Madzi anasefukila, ndipo zinthu zambili zinaonongeka. Zitatelo, Komiti ya Nthambi inapanga makonzedwe akuti apezele okhudzidwawo cakudya, zovala, madzi abwino, ndi zina zofunikila. Ndipo katunduyo walongedwa mwadongosolo kwambili mu holomo. Abale ndi amene anapeleka copeleka ca katunduyo. Abale ndi alongo aima pa mzela, ndipo akulandila zinthu zimene akufunikila. Ambili mwa io akugwetsa misozi ya cimwemwe.

Yesu anakamba kuti cizindikilo cacikulu codziŵila anthu ake cidzakhala cikondi cao pa wina ndi mnzake. (Yoh. 13:34, 35) M’cigawo cino, tidzaona mmene Mboni za Yehova zimaonetselana cikondi pa nthawi yomanga malo olambilila kapena pakacitika ngozi. Cikondi cimeneci ndi umboni wakuti tikutsogoleledwa ndi Yesu yemwe ndi mfumu.

M'CIGAWO CINO

NKHANI 18

Mmene Timapezela Ndalama Zoyendetsela Nchito Za Ufumu

Kodi ndalama zimacokela kuti? Nanga zimagwila nchito yanji?

NKHANI 19

Nchito Yomanga Imene Imalemekeza Yehova

Malo olambilila amalemekeza Mulungu. Koma pali cinthu cina cimene iye amaona kuti n’cofunika kwambili.

NKHANI 20

Utumiki Wopeleka Thandizo Pakacitika Ngozi

Timadziŵa bwanji kuti nchito yopeleka thandizo pakacitika ngozi ndi mbali ya utumiki wathu wopatulika kwa Yehova?