Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 19

Nchito Yomanga Imene Imalemekeza Yehova

Nchito Yomanga Imene Imalemekeza Yehova

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Nchito yomanga padziko lonse imapititsa patsogolo zinthu za Ufumu

1, 2. (a) N’ciani cimene anthu a Yehova akhala akucita kwa nthawi yaitali? (b) N’ciani cimene Yehova amayamikila kwambili?

KWA nthawi yaitali, atumiki a Yehova okhulupilika akhala akumanga malo olambilila amene amalemekeza dzina la Mulungu. Mwacitsanzo, Aisiraeli anagwila nchito yomanga cihema mwakhama ndi kupeleka moolowa manja zinthu zothandiza pa nchitoyo.—Eks. 35:30-35; 36:1, 4-7.

2 Yehova saona zipangizo zomangila nyumba zolambililamo kukhala zinthu zofunika kwambili zimene zingam’patse ulemelelo. (Mat. 23:16, 17) Mphatso imene Yehova amaiyamikila kwambili yocokela kwa atumiki ake, imene imam’patsa ulemelelo kuposa zonse, ndiyo kum’lambila kwenikweniko, kuphatikizapo mzimu wodzipeleka pa utumiki wao. (Eks. 35:21; Maliko 12:41-44; 1 Tim. 6:17-19) Mfundo imeneyi ndi yomveka. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti nyumba zimatha. Mwacitsanzo, cihema ndi kacisi kulibenso. Ngakhale kuti zinthu zimenezo zinatha, Yehova sanaiwale kuwolowa manja kwa atumiki ake okhulupilika ndi khama lao pocilikiza nchito yomanga imeneyo.—Ŵelengani 1 Akorinto 15:58; Aheberi 6:10.

3. Tikambilana ciani m’nkhani ino?

3 Atumiki a Yehova amakono naonso akhala akucita khama panchito yomanga malo olambilila. Ndipo zimene tacita motsogoleledwa ndi Mfumu Yesu Kristu n’zocititsa cidwi kwambili. N’zoonekelatu kuti Yehova wakhala akudalitsa khama lathu. (Sal. 127:1) M’nkhani ino, tikambilana za nchito zina zimene zakhala zikucitika ndiponso mmene zathandizila kulemekeza Yehova. Timvanso zimene anthu ena amene akhala akugwila nchitoyi anakamba.

Kumanga Nyumba za Ufumu

4. (a) N’cifukwa ciani tikufunikila malo ambili olambilila? (b) N’cifukwa ciani maofesi ena a nthambi anaphatikizidwa? (Onani bokosi lakuti “ Kumanga Maofesi a Nthambi Mogwilizana ndi Zimene Zikufunika.”)

4 Monga tinaphunzilila m’Nkhani 16, Yehova amafuna tizisonkhana pamodzi kuti timulambile. (Aheb. 10:25) Misonkhano yathu imalimbitsa cikhulupililo cathu ndi kutilimbikitsa kugwila nchito yolalikila mwacangu. Pamene mapeto akuyandikila, Yehova akupitilizabe kufulumizitsa nchito imeneyi. Pa cifukwa cimeneci, anthu masauzande ambilimbili akukhamukila ku gulu la Mulungu caka ciliconse. (Yes. 60:22) Pamene ciŵelengelo ca nzika za Ufumu cikukwela, pakufunikanso nyumba zambili zosindikizila mabuku ophunzitsa Baibulo. Tikufunikanso malo ambili olambilila.

5. N’cifukwa ciani dzina lakuti Nyumba ya Ufumu n’loyenelela? (Onani bokosi lakuti “ Chalichi ca Kuwala Kwatsopano.”)

5 Kuciyambi kwa mbili yamakono ya anthu a Yehova, Ophunzila Baibulo anayamba kuona kufunika kokhala ndi malo ao-ao osonkhanilako. Zikuoneka kuti nyumba yao yoyamba yolambilila inamangidwa mu 1890, ku West Virginia, m’dziko la United States. Podzafika m’ma 1930, anthu a Yehova anali atamanga kapena kukonzanso maholo angapo. Koma panthawiyo, maholowo analibe dzina lenileni. Mu 1935, M’bale Rutherford anapita ku Hawaii, kumene nyumba yolambilila inali kumangidwa panthawi imodzi ndi ofesi ya nthambi yatsopano. M’bale Rutherford atafunsidwa kuti nyumbayo tiziichula kuti bwanji, iye anayankha kuti: “Bwanji tiziichula kuti ‘Nyumba ya Ufumu,’ popeza timalalikila uthenga wabwino wa Ufumu?” (Mat. 24:14) Dzinali n’loyeneleladi. Kucokela pa holo imeneyi, malo ambili olambilila a anthu a Yehova padziko lonse amachedwa Nyumba ya Ufumu.

6, 7. Kodi nchito yomanga Nyumba za Ufumu mofulumila yathandiza bwanji?

6 Pofika m’ma 1970, panali kufunika Nyumba za Ufumu zambili. Mwa ici, abale ku United States anatulukila njila yofulumila yomangila Nyumba za Ufumu zokongola koma zosalila zambili. Anali kutsiliza Nyumba ya Ufumu m’masiku oŵelengeka cabe. Podzafika mu 1983, Nyumba za Ufumu pafupifupi 200 zinamangidwa ku United States ndi ku Canada. Kuti nchitoyi iyende bwino, abale anayambitsa makomiti oyang’anila nchito yomanga Nyumba za Ufumu. Makonzedwe amenewa anayenda bwino kwambili cakuti mu 1986, Bungwe Lolamulila linavomeleza makomiti amenewa. Podzafika mu 1987, ku United States kunali makomiti otelo okwana 60. * Pofika caka ca 1992, makomiti ena otelo anakhazikitsidwanso ku Argentina, Australia, France, Germany, Japan, Mexico, South Africa, ndi ku Spain. Kunena zoona, abale akhama omanga Nyumba za Ufumu ndi Mabwalo a Misonkhano tifunika kuwacilikiza cifukwa cakuti nchito imene amagwila ndi yopatulika.

7 Nyumba za Ufumu zomangidwa mofulumilazo zinapeleka umboni wabwino m’madela amene zinamangidwa. Mwacitsanzo, m’nyuzipepala ina ku Spain munali nkhani ya mutu wakuti “Cikhulupililo Casuntha Mapili.” Pothilila ndemanga pa nchito yomanga Nyumba ya Ufumu m’tauni ya Martos, nyuzipepalayo inafunsa kuti: “Kodi zinatheka bwanji kuti m’dziko lapansi ladyela lino, anthu ocokela kumadela osiyanasiyana [mu Spain] adzipeleke kupita ku Martos kukamanga chalichi? Chalichico anacimanga mofulumila kwambili ndi mwadongosolo kuposa cimango cina ciliconse.” Poyankha funso limeneli, nkhaniyo inagwila mau m’bale wina wodzipeleka pa nchitoyo amene anati: “Cifukwa cake n’cakuti ndife anthu ophunzitsidwa ndi Yehova.”

Kugwila Nchito Yomanga M’maiko Osauka

8. Ndi pulogalamu iti imene Bungwe Lolamulila linavomeleza mu 1999? N’cifukwa ciani linatelo?

8 Ca kumapeto kwa zaka za m’ma 1900, anthu ambili m’maiko osauka anakhamukila ku gulu la Yehova. Abale ndi alongo m’maiko amenewo anacita zimene akanakwanitsa kuti amange nyumba zolambilila. Koma m’maiko ena, abale athu anali kunyozedwa ndi kusalidwa cifukwa cakuti Nyumba za Ufumu zao zinali zosaoneka bwino poyelekeza ndi za machalichi ena. Komabe kuyambila mu 1999, Bungwe Lolamulila linavomeleza pulogalamu yothandiza kumanga Nyumba za Ufumu mofulumila m’maiko osauka. Ndalama zocokela kwa abale a m’maiko olemela zinasonkhanitsidwa ndi kutumizidwa ku maiko osauka kuti zikathandize panchitoyi n’colinga cakuti pakhale “kufanana.” (Ŵelengani 2 Akorinto 8:13-15.) Kuonjezela pamenepo, abale ndi alongo ocokela m’maiko ena anadzipeleka kuthandiza panchitoyi.

9. Ndi nchito iti imene inaoneka ngati yosatheka? Koma n’ciani cinacitika?

9 Poyamba nchitoyo inaoneka ngati yosatheka. Malinga ndi lipoti la mu 2001, Nyumba za Ufumu zokwana 18,300 zinali kufunika m’maiko osauka okwana 88. Koma ndi thandizo la mzimu woyela wa Mulungu ndiponso thandizo la Mfumu yathu Yesu Kristu, palibe nchito yosatheka. (Mat. 19:26) Cifukwa ca pulogalamu yomanga Nyumba za Ufumu m’maiko osauka, anthu a Mulungu anamanga Nyumba za Ufumu zokwana 26,849 pa zaka pafupifupi 15 kucokela mu 1999 mpaka mu 2013. * Yehova akupitilizabe kudalitsa nchito yolalikila moti pofika mu 2013, Nyumba za Ufumu pafupifupi 6,500 zinali kufunikabe m’maiko amenewa. Caka ciliconse, Nyumba za Ufumu zatsopano zokwana mahandiledi ambili zimafunika.

Kumanga Nyumba ya Ufumu m’maiko osauka kulinso ndi zopinga zake

10-12. Kodi nchito yomanga Nyumba za Ufumu yalemekeza bwanji dzina la Yehova?

10 Kodi nchito yomanga Nyumba za Ufumu zatsopano imalemekeza bwanji dzina la Yehova? Ofesi ya nthambi ku Zimbabwe inalemba kuti: “Nthawi zambili, pa mwezi umodzi cabe tikamanga Nyumba ya Ufumu, ciŵelengelo ca osonkhana cimaŵilikiza kaŵili.” M’maiko ambili, anthu oculuka amayamba kusonkhana ndi Mboni za Yehova ngati pamangidwa malo abwino olambilila. Nyumba ya Ufumu ikangomangidwa, ciŵelengelo ca anthu osonkhana cimakwela kwambili, ndipo pamafunikanso Nyumba ina ya Ufumu. Koma si maonekedwe a Nyumba za Ufumu cabe amene amapangitsa anthu kubwela kwa Yehova. Cikondi ceniceni cimene abale ndi alongo omanga maholo amaonetsana cimakopanso anthu kuti abwele ku gulu la Mulungu. Onani zitsanzo izi.

11 Ku Indonesia. Mwamuna wina anali kuona anthu akumanga Nyumba ya Ufumu. Iye atazindikila kuti omangawo anali anchito odzifunila, anati: “Anthu inu ndinu ocititsa cidwi kwambili. Ndakhala ndikuona mmene aliyense wa inu amagwilila nchito mwakhama ndi mosangalala, ngakhale kuti simulandila malipilo. Ndikuganiza kuti palibe chalichi cina cofanana ndi canuci.”

12 Ku Ukraine. Tsiku lililonse, mai wina anali kupita m’njila pafupi ndi pamene abale anali kumanga Nyumba ya Ufumu. Iye sanakaikile kuti omangawo ndi Mboni za Yehova ndi kuti anali kumanga Nyumba ya Ufumu. Maiyo anati: “Ndinamvako za Mboni za Yehova kwa mng’ono wanga amene ndi wa Mboni. Pamene ndinaona nchito yomangayi, ndinaona kuti inenso ndiyenela kukhala m’banja la kuuzimu limeneli. Ndazindikila kuti anthu inu mumakondanadi.” Maiyo anavomela kuphunzila Baibulo, ndipo anabatizidwa mu 2010.

13, 14. (a) N’ciani cimene mwaphunzila pa zimene banja lina linacita litaona abale akumanga Nyumba ya Ufumu? (b) Mungacite ciani kuti malo anu olambilila azilemekeza dzina la Yehova?

13 Ku Argentina. Mwamuna wina ndi mkazi wake anafikila m’bale amene anali kuyang’anila nchito pamalo ena amene anali kumangapo Nyumba ya Ufumu. Mwamunayo anati: “Takhala tikukuonani mukumanga Nyumba ya Ufumu, ndipo . . . tingakonde kuphunzila za Mulungu pa malo ano.” Kenako anafunsa kuti, “Kodi tingacite ciani kuti tizisonkhana nanu pano?” Mwamunayo ndi mkazi wake anakamba kuti adzavomela kuphunzila Baibulo pokhapo abalewo atalola kuti banja lonse lizikhalapo paphunzilolo. Abale anavomela ndi mtima wonse kuphunzila ndi banja lonselo.

14 Mwina munalibe mwai womanga nao Nyumba ya Ufumu imene mumasonkhanamo. Koma pali zambili zimene mungacite kuti malo anu olambilila azilemekeza dzina la Yehova. Mwacitsanzo, mungapemphe ophunzila Baibulo anu, anthu amene mumacitako maulendo obwelelako, ndi anthu ena kuti mukasonkhane nao ku Nyumba ya Ufumu. Mulinso ndi mwai wogwila nchito yoyeletsa ndi kusamalila malo anu olambilila. Mungakonzenso zakuti muzipeleka ndalama zothandizila kusamalila Nyumba yanu ya Ufumu kapena zothandizila kumanga malo olambilila m’madela ena padziko lapansi. (Ŵelengani 1 Akorinto 16:2.) Kucita zimenezi kumathandiza kuti dzina la Yehova litamandidwe.

Anchito Amene ‘Amadzipeleka Mofunitsitsa’

15-17. (a) Ndani amagwila nchito yambili pa nthawi yomanga malo olambilila? (b) Kodi mwaphunzila ciani pa zimene mabanja ena amene amagwila nchito yomanga malo olambilila m’maiko ena anakamba?

15 Mbali yaikulu ya nchito yomanga Nyumba za Ufumu, Mabwalo a Misonkhano, ndi maofesi a nthambi imagwilidwa ndi abale ndi alongo a m’delalo. Komabe, nthawi zambili, io amathandizidwa ndi abale ndi alongo ocokela m’maiko ena omwe amadziŵa bwino nchitoyi. Ena mwa abale ndi alongo amenewa amadzipeleka kuti akagwile nchito yomanga m’maiko ena kwa milungu ingapo pamene ena adzipeleka kuti akagwile nchito yomangayi kwa zaka zambili m’maiko osiyanasiyana.

Timo ndi Lina Lappalainen (Onani ndime 16)

16 Nchito yomanga malo olambilila m’maiko osiyanasiyana ili ndi mavuto ake, koma imabweletsanso madalitso ambili. Mwacitsanzo, Timo ndi mkazi wake Lina, akhala akuyenda m’maiko osiyanasiyana ku Asia, Europe, ndi ku South America kukagwila nchito yomanga Nyumba za Ufumu, Mabwalo a Misonkhano, ndi maofesi a nthambi. Timo anati: “Pa zaka 30 zapitazi, ndakhala ndikusamukila ku maiko osiyanasiyana kukagwila nchito yomanga pa zaka ziŵili zilizonse.” Lina amene wakhala m’banja ndi Timo zaka 25, anati: “Kucokela pamene tinakwatilana, tatumikila limodzi m’maiko 10 osiyanasiyana. Pamafunika khama ndiponso nthawi yaitali kuti munthu azolowele cakudya catsopano, nyengo yatsopano, cinenelo catsopano, ndi gawo latsopano ndiponso kuti apeze mabwenzi atsopano.” * Kodi khama lao lawapindulitsa bwanji? Lina anati: “Mosasamala kanthu za mavutowa, talandila madalitso osaneneka. Abale akhala akutisonyeza cikondi ndi kuticeleza. Ndipo taona kuti Yehova amatikonda ndi kutisamalila. Taonanso kukwanilitsidwa kwa zimene Yesu analonjeza atumwi ake, zolembedwa pa Maliko 10:29, 30. Tapeza abale, alongo ndi amai akuuzimu oculuka kuŵilikiza maulendo 100.” M’bale Timo anati: “Timakondwela kwambili kugwilitsila nchito luso lathu pa nchito yofunika kwambili yopititsa patsogolo zinthu za Mfumu.”

17 Darren ndi Sarah, amene athandiza pa nchito yomanga ku Africa, Asia, Central America, Europe, South America, ndi ku South Pacific, amaona kuti adalitsidwa kwambili cifukwa ca nchito imene amagwila. Ngakhale kuti amakumana ndi mavuto ena, Darren anati: “Ndakhala ndi mwai waukulu wogwila nchito pamodzi ndi abale a m’maiko osiyanasiyana. Ndaona kuti kukonda kwathu Yehova n’kumene kwathandiza kuti tikhale ogwilizana.” Sarah anati: “Ndaphunzila zambili kwa abale ndi alongo a zikhalidwe zosiyanasiyana. Ndikaona kudzipeleka kwao potumikila Yehova, ndimalimbikitsidwa kupitilizabe kum’tumikila ndi mtima wanga wonse.”

18. Kodi ulosi wa pa Salimo 110:1-3 ukukwanilitsidwa bwanji?

18 Mfumu Davide inalosela kuti ngakhale kuti nzika za Ufumu wa Mulungu zidzakumana ndi mavuto osiyanasiyana, izo ‘zidzadzipeleka mofunitsitsa’ popititsa patsogolo zinthu za Ufumu. (Ŵelengani Salimo 110:1-3.) Anthu onse amene akugwila nchito yocilikiza Ufumu akukwanilitsa nao ulosi umenewu. (1 Akor. 3:9) Kumangidwa kwa maofesi a nthambi, Mabwalo a Misonkhano ambili, ndi Nyumba za Ufumu masauzande ambili, ndi umboni woonekelatu wakuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni ndi kuti ukulamulila. Ndi mwai waukulu kwambili kutumikila Mfumu Yesu Kristu mwa kugwila nchito imene imalemekeza kwambili Yehova. Iye ndi woyeneladi kulandila ulemelelo.

^ par. 6 Mu 2013, anchito odzipeleka oposa 230,000 a ku United States analoledwa kugwila nchito yomanga limodzi ndi Makomiti a Nchito Yomanga Nyumba za Ufumu okwana 132 a m’dzikolo. M’dzikolo, makomiti amenewo amayang’anila nchito yomanga Nyumba za Ufumu pafupifupi 75 ndi kukonza zina pafupifupi 900 caka ciliconse.

^ par. 9 Ciŵelengeloci sicikuphatikizapo Nyumba za Ufumu zimene zinamangidwa m’maiko olemela.

^ par. 16 Atumiki a m’mayiko ena ndiponso anchito odzipeleka a m’mayiko ena amathela nthawi yao yoculuka pa nchito yomanga. Koma amagwilanso nchito yolalikila pamodzi ndi mipingo ya m’delalo kumapeto kwa mlungu kapena madzulo.