Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 20

Utumiki Wopeleka Thandizo Pakacitika Ngozi

Utumiki Wopeleka Thandizo Pakacitika Ngozi

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Mmene Akristu oona amasonyezelana cikondi pakacitika ngozi

1, 2. (a) Ndi vuto lotani limene Akristu a ku Yudeya anakumana nalo? (b) Kodi Akristuwo anasonyezedwa cikondi m’njila yotani?

CA M’ma 46 C.E, ku Yudeya kunagwa njala yoopsa. Cakudya cinali cocepa ndiponso cokwela mtengo kwambili moti ophunzila a Kristu aciyuda a kumeneko anali kulephela kugula cakudyaco. Iwo anali kuvutika kwambili ndi njala. Koma Yehova anathandiza ophunzila a Kristu amenewo m’njila yapadela kwambili. Kodi anawathandiza bwanji?

2 Akristu aciyuda ndi a mitundu ina ku Antiokeya wa ku Siriya anakhudzidwa kwambili ndi mavuto amene Akristu aciyuda ku Yerusalemu ndi ku Yudeya anali kukumana nao. Iwo anasonkhanitsa ndalama zokathandizila abale ao. Kenako anasankha amuna aŵili oyenelela pakati pao, Baranaba ndi Saulo, kuti akapeleke thandizolo kwa akulu a mpingo ku Yerusalemu. (Ŵelengani Machitidwe 11:27-30; 12:25.) Taganizilani cisangalalo cimene abale osoŵa ku Yudeya anali naco ataona cikondi cimene abale ao ku Antiokeya anawasonyeza mwa kuwatumizila thandizo.

3. (a) Kodi anthu a Mulungu masiku ano amatsatilabe bwanji citsanzo ca Akristu a ku Antiokeya? Pelekani citsanzo. (Onani bokosi lakuti “ Nchito Yathu Yaikulu Yoyamba Yopeleka Thandizo Masiku Ano.”) (b) Ndi mafunso ati amene tikambilane m’nkhani ino?

3 Zimenezi zinacitika m’nthawi ya atumwi, ndipo iyi ndi nthawi yoyamba imene Baibulo limafotokoza za Akristu amene anatumiza thandizo kwa Akristu anzao okhala m’dela lina. Masiku ano, timatsatila citsanzo ca abale athu a ku Antiokeya. Tikamva kuti ngozi yacitikila abale athu m’dela lina kapena akuzunzidwa, timawathandiza. * Kuti tidziŵe mmene nchito yopeleka thandizo imakhudzila utumiki wathu, tiyeni tikambilane mafunso atatu awa okhudza utumikiwu: N’cifukwa ciani timaona kuti nchito yopeleka thandizo ndi utumiki? Kodi colinga ca nchito yopeleka thandizo n’ciani? Nanga timapindula bwanji ndi utumiki wopeleka thandizo umenewu?

Nchito Yopeleka Thandizo Ndi “Utumiki Wopatulika”

4. N’ciani cimene Paulo anauza Akorinto ponena za utumiki wacikristu?

4 M’kalata yake yaciŵili yopita kwa Akorinto, Paulo ananena kuti utumiki wacikristu uli ndi mbali ziŵili zofunika. Ngakhale kuti kalatayi analembela Akristu odzozedwa, mau ake amakhudzanso “nkhosa zina” za Kristu. (Yoh. 10:16) Mbali yoyamba ya utumiki wathu ndi “utumiki wokhazikitsanso mtendele,” kapena kuti nchito yolalikila ndi kuphunzitsa. (2 Akor. 5:18-20; 1 Tim. 2:3-6) Mbali ina ndi utumiki umene timacita pothandiza okhulupilila anzathu. Paulo anakamba momveka bwino kuti umenewu ndi “utumiki wothandiza” ena. (2 Akor. 8:4) M’Baibulo muli mau akuti “utumiki wokhazikitsanso mtendele” ndi akuti “utumiki wothandiza” oyelawo. M’mau onsewa, liu lakuti “utumiki” linamasulidwa kucokela ku liu limodzi lacigiriki lakuti di·a·ko·niʹa. N’cifukwa ciani zimenezi n’zocititsa cidwi?

5. N’cifukwa ciani n’zocititsa cidwi kuti Paulo anakamba kuti nchito yopeleka thandizo ndi utumiki?

5 Mwa kugwilitsila nchito liu lacigiriki lofanana ponena za mautumiki aŵiliwo, Paulo anaonetsa kuti nchito yopeleka thandizo ndi yofanana ndi mautumiki ena amene anali kucitika mumpingo wacikristu. Asanakambe za mautumiki amenewa, iye anati: “Pali mautumiki osiyanasiyana, koma Ambuye ndi mmodzi. Palinso nchito zosiyanasiyana, . . . Koma nchito zonsezi, mzimu umodzimodziwo ndiwo umazicita.” (1 Akor. 12:4-6, 11) Paulo anasonyeza kuti mautumiki osiyanasiyana amene amacitika pampingo ndi “utumiki wopatulika.” * (Aroma 12:1, 6-8) Ndiye cifukwa cake iye anagwilitsila nchito nthawi yake ‘kutumikila oyela.’—Aroma 15:25, 26.

6. (a) Malinga ndi mau a Paulo, n’cifukwa ciani nchito yopeleka thandizo ndi mbali ya kulambila kwathu? (b) Fotokozani mmene nchito yathu yopeleka thandizo imacitikila padziko lonse masiku ano. (Onani chati cakuti “ Pakacitika Ngozi,” patsamba 214.)

6 Paulo anathandiza Akristu a ku Korinto kuzindikila kuti nchito yopeleka thandizo ndi mbali ya kulambila Yehova, ndiponso kuti ndi mbali ya utumiki wao kwa Iye. Onani kuti iye anakamba kuti Akristu amene amapeleka thandizo amacita zimenezo cifukwa ‘cogonjela uthenga wabwino wonena za Kristu.” (2 Akor. 9:13) Conco, cimene cimalimbikitsa Akristu kuthandiza anzao ndi mtima wao wofuna kutsatila zimene Kristu anaphunzitsa. Paulo ananena kuti zinthu zabwino zimene Akristu amacitila abale ao zimaonetsa “kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.” (2 Akor. 9:14; 1 Pet. 4:10) Conco, ponena za nchito yothandiza abale athu amene akuvutika, magazini ya Nsanja ya Olonda ya December 1, 1975 inati: “Tisakaikile kuti Yehova Mulungu ndi Mwana wake Yesu Kristu amaona utumikiwu kukhala wofunika kwambili.” Zoonadi, nchito yopeleka thandizo ndi mbali yofunika kwambili ya utumiki wopatulika.—Aroma 12:1, 7; 2 Akor. 8:7; Aheb. 13:16.

Zolinga za Nchitoyi N’zodziŵikilatu

7, 8. Kodi colinga coyamba ca utumiki wathu wopeleka thandizo n’ciani? Fotokozani.

7 Kodi colinga ca utumiki wathu wopeleka thandizo pa nthawi yamavuto n’ciani? Paulo anayankha funso limenelo m’kalata yake yaciŵili yopita kwa Akorinto. (Ŵelengani 2 Akorinto 9:11-15.) Palembali, Paulo anafotokoza zolinga zitatu zimene timakwanilitsa tikamacita “utumiki wothandiza anthu” panthawi ya mavuto. Tiyeni tikambilane zolinga zimenezi.

8 Coyamba, utumiki umenewu umalemekeza Yehova. Onani kuti pa mavesi asanu a pa 2 Akorinto 9:11-15, Paulo anagwilitsila nchito mau angapo othandiza abale kuona mmene utumiki wopeleka thandizo umakhudzila Yehova Mulungu. Iye anawakumbutsa kuti utumikiwu umacititsa “anthu kuyamika Mulunguyo” ndiponso “kupeleka mapemphelo oculuka oyamika Mulungu.” (vesi 11 ndi 12) Anafotokozanso kuti nchito yopeleka thandizo imalimbikitsa Akristu ‘kulemekeza Mulungu’ ndi kuyamikila ‘kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu.’ (vesi 13 ndi 14) Ndiyeno Paulo anamaliza nkhani yake yonena za kupeleka thandizo ndi mau akuti: “Tikuyamika Mulungu.”—Vesi 15; 1 Pet. 4:11.

9. Kodi nchito yopeleka thandizo ingathandize anthu kukhala ndi maganizo otani? Pelekani citsanzo.

9 Mofanana ndi Paulo, atumiki a Mulungu lelolino amaona nchito yopeleka thandizo kukhala mwai wao wolemekeza Yehova ndi kukometsela ciphunzitso cake. (1 Akor. 10:31; Tito 2:10) Ndipo nchitoyi imathandiza kwambili kucotsa maganizo olakwika amene anthu ena ali nao ponena za Yehova ndi Mboni zake. Mwacitsanzo, m’dela lina limene linakhudzidwa ndi cimphepo camkuntho, munali kukhala mai wina amene anali ataika cikwangwani pa citseko ca nyumba yake colembedwa kuti: “Pano Sitifuna a Mboni za Yehova.” Tsiku lina, maiyo anaona anthu opeleka thandizo pakacitika ngozi zacilengedwe akukonza nyumba ina pafupi ndi nyumba yake. Kwa masiku angapo, iye anali kuona anthuwo akugwila nchito limodzi mogwilizana. Kenako anapita pamalowo kukafunsa kuti anthuwo anali ndani. Atadziŵa kuti anali a Mboni za Yehova, anacita cidwi kwambili ndipo anati: “Sindinali kudziŵa kuti anthu inu ndinu otele.” Kodi maiyo anacita ciani pambuyo pake? Anacotsa cikwangwani cija pa citseko ca nyumba yake.

10, 11. (a) Ndi zitsanzo ziti zimene zikuonetsa kuti timakwanilitsa colinga caciŵili ca nchito yathu yopeleka thandizo? (b) Ndi kabuku kati kamene kamathandiza ogwila nchito yopeleka thandizo? (Onani kabokosi kakuti “ Cida Cina Cothandiza Ogwila Nchito Yopeleka Thandizo.”)

10 Caciŵili, timapatsa okhulupilila anzathu “zinthu zoculuka zimene akufunikila.” (2 Akor. 9:12a) Ndife okonzeka kupatsa abale ndi alongo athu zosoŵa zao ndi kucepetsa mavuto ao. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti anthu onse mumpingo amapanga ‘thupi limodzi,’ ndipo “ciwalo cimodzi cikavutika, ziwalo zina zonse zimavutikila naco limodzi.” (1 Akor. 12:20, 26) Cifukwa cokonda abale ndi alongo athu ndi kuwamvela cifundo, timacitapo kanthu mwamsanga tikamva kuti io akumana ndi vuto. Mofulumila, timatenga zida zofunika ndi kuthamangila kumene kwacitika ngozi kuti tikathandize Akristu anzathu. (Yak. 2:15, 16) Mwacitsanzo, mu 2011 pamene ku Japan kunacitika tsunami, ofesi ya nthambi ku United States inalembela kalata Makomiti Omanga Nyumba za Ufumu m’dzikolo. M’kalatayo, ofesiyo inapempha makomitiwo kuti apeze “abale ocepa oyenelela” amene angakonde kukathandiza pa nchito yomanganso Nyumba za Ufumu ku Japan. Kodi n’ciani cinacitika? Pa milungu yoŵelengeka cabe, abale ndi alongo odzipeleka pafupifupi 600 anapempha kuti akathandize, ndipo analipila okha ndalama zoyendela ku Japan pa ndeke. Ofesi ya nthambi ku United States inati: “Tasangalala kwambili ndi zimene abalewa acita.” M’bale wina ku Japan anafunsa mmodzi mwa ogwila nchito yopeleka thandizo amene anacokela ku dziko lina cifukwa cake anabwela kudzathandiza m’dzikolo. Iye anayankha kuti: “Abale athu kuno ku Japan ndi mbali ya ‘thupi lathu.’ Iwo akamavutika, ifenso timavutika.” Cifukwa ca cikondi codzimana, abale ndi alongo ogwila nchito yopeleka thandizo nthawi zina amaika moyo wao pangozi kuti athandize abale ao. *1 Yoh. 3:16.

11 Naonso anthu amene si Mboni amayamikila nchito yathu yopeleka thandizo. Mwacitsanzo, pamene m’dela la Arkansas, ku United States kunacitika ngozi mu 2013, nyuzipepala ina inafotokoza mmene Mboni za Yehova zodzipeleka zinathandizila pangoziyo. Nyuzipepalayo inati: “Mboni za Yehova zimacita zinthu mwadongosolo kwambili ndiponso mofulumila.” Ndithudi, monga mmene mtumwi Paulo ananenela, timapeleka “zinthu zoculuka” kwa abale athu amene akuvutika.

12-14. (a) N’cifukwa ciani kukwanilitsa colinga cacitatu ca nchito yopeleka thandizo n’kofunika? (b) Ndi mau ati amene anthu ena anakamba oonetsa kufunika kopitilizabe kucita zinthu za kuuzimu?

12 Cacitatu, timathandiza ovutika kuyambanso kucita zinthu za kuuzimu. N’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika? Paulo anakamba kuti anthu amene alandila thandizo ngozi ikacitika amasonkhezeledwa “kupeleka mapemphelo oculuka oyamika Mulungu.” (2 Akor. 9:12b) Kunena zoona, cinthu cabwino kwambili cimene okhudzidwawo angacite kuti ayamikile Yehova ndi kuyambanso kucita zinthu za kuuzimu mwamsanga. (Afil. 1:10) Mu 1945, Nsanja ya Mlonda ina yacingelezi inati: “Paulo anavomeleza . . . kuti abale azipeleka zopeleka cifukwa cakuti zinali kuthandiza . . . Akristu osauka kupeza zinthu zofunikila. Zimenezi zinathandiza Akristu osaukawo kugwila nchito ya Yehova yocitila umboni mwakhama ndi momasuka.” Colinga cathu n’cofanana ndi cimeneci. Abale athu akayambanso kugwila nchito yolalikila, amalimbikitsa anansi ao ovutika maganizo ndiponso amadzilimbitsa io eni.—Ŵelengani 2 Akorinto 1:3, 4.

13 Abale ndi alongo ena amene analandila thandizo ngozi itacitika, anayambanso nchito yolalikila, ndipo zimenezi zinalimbitsa cikhulupililo cao. Tamvani zimene io anakamba. M’bale wina anati: “Tinaona kuti unali mwai kuyenda mu ulaliki monga banja. Kutonthoza anthu mu ulaliki kunali kutithandiza kuiwalako za mavuto athu.” Mlongo wina anati: “Kucita zinthu za kuuzimu kunandithandiza kuiwalako za ngozi imene inaticitikila. Zinandithandizanso kukhala ndi mtendele wa m’maganizo.” Mlongo winanso anakamba kuti: “Ngakhale kuti zinali zovuta kukonza zinthu zina, kulalikila kunathandiza banja lathu kukhala ndi ciyembekezo. Kuuza ena za ciyembekezo cathu ca dziko latsopano, kunalimbitsa cikhulupililo cathu cakuti zinthu zonse zidzakhala zatsopano.”

14 Kupezeka pa misonkhano ndi cinthu cina cimene Akristu ayenela kuyambilanso mwamsanga ngozi ikawacitikila. Ganizilani zimene zinacitikila mlongo wina amene anali ndi zaka pafupifupi 60, dzina lake Kiyoko. Iye anasowa mtengo wogwila pamene zinthu zonse zimene anali nazo zinaonongeka cifukwa ca tsunami, ndipo anangotsala ndi zovala zimene zinali m’thupi. Kenako mkulu wina amamuuza kuti msonkhano wina umene anali kukhala nao mlungu uliwonse adzacitila m’galimoyo yake. Mlongo Kiyoko anati: “Ine, mkuluyo ndi mkazi wake ndiponso mlongo wina tinakhala m’galimoyo. Msonkhanowo unali wacidule, koma zodabwitsa zinali zakuti pamsonkhanopo ndinaiwalako za tsunami, ndipo maganizo anga anakhala m’malo. Msonkhanowo unandithandiza kuona kuti kusonkhana pamodzi n’kofunika kwambili. Pofotokoza za msonkhano umene anacita pambuyo pa ngozi imene inacitika m’dela lao, mlongo wina anati: “Misonkhano inandithandiza kuti cikhulupililo canga cisafooke.”—Aroma 1:11, 12; 12:12.

Utumiki Wopeleka Thandizo Umabweletsa Madalitso Okhalitsa

15, 16. (a) Ndi mapindu otani amene Akristu a ku Korinto ndi kumadela ena anapeza cifukwa copeleka thandizo kwa abale ao? (b) Kodi ifenso timapindula bwanji ndi nchito yopeleka thandizo masiku ano?

15 Pofotokoza za utumiki wopeleka thandizo, Paulo anauzanso Akristu a ku Korinto za mapindu amene io ndi Akristu ena adzakhala nao cifukwa cocita utumikiwu. Iye anati: “Iwo amakupelekelani mapembedzelo kwa Mulungu ndiponso [Akristu aciyuda okhala ku Yerusalemu amene analandila thandizo] amakukondani kwambili cifukwa ca kukoma mtima kwakukulu kumene Mulungu wakusonyezani.” (2 Akor. 9:14) Akristu aciyuda anali kupemphelela abale ao a ku Korinto, kuphatikizapo anthu a mitundu ina cifukwa ca kuolowa manja kwa Akristu a ku Korintowo. Ndipo zimenezi zinapangitsanso kuti Akristu aciyuda azikonda kwambili abale ao a ku Korinto.

16 Nsanja ya Mlonda yacingelezi ya December 1, 1945, inafotokoza mau a Paulo okhudza mapindu amene amabwela cifukwa ca nchito yopeleka thandizo masiku ano. Magaziniyo inati: “Anthu odzipeleka a Mulungu m’dela lina akathandiza abale ao osoŵa, onsewo amakhala ogwilizana.” Izi n’zimene zimacitikila amene amagwila nchito yopeleka thandizo pakacitika ngozi. Mwacitsanzo, mkulu wina amene anagwilako nchito yopeleka thandizo m’dela lina limene linasefukila madzi anati: “Kugwila nchito yopeleka thandizo kwa abale kunapangitsa kuti ubwenzi wanga ndi abalewo ulimbe kuposa ndi kale lonse.” Mlongo wina anayamikila kwambili atalandila thandizo pambuyo pa ngozi, ndipo anafokoza kuti: “Kukhala pakati pa abale n’cinthu camtengo wapatali cimene tili naco pamene tikuyembekezela Paladaiso.”—Ŵelengani Miyambo 17:17.

17. (a) Kodi nchito yopeleka thandizo imakwanilitsa bwanji mau a pa Yesaya 41:13? (b) Pelekani zitsanzo zoonetsa mmene nchito yopeleka thandizo imalemekezela Yehova ndi kulimbitsa mgwilizano. (Onani mutu wakuti “ Anchito Odzipeleka Padziko Lonse Amathandiza Kwambili.”)

17 Opeleka thandizo akafika m’dela limene mwacitika ngozi, abale athu okhudzidwawo amaona kukwanilitsidwa kwapadela kwa lonjezo la Mulungu lakuti: “Ine, Yehova Mulungu wako, ndagwila dzanja lako lamanja. Ine amene ndikukuuza kuti, ‘Usacite mantha. Ineyo ndikuthandiza.’” (Yes. 41:13) Mlongo wina atapulumuka ngozi imene inacitika m’dela lao anati: “Ndinataya mtima nditaona mmene zinthu zinaonongekela. Koma Yehova anandithandiza. Abalenso anandithandiza kwambili moti sindingathe kufotokoza zonse zimene anandicitila.” Akulu aŵili okhala m’dela lina limene munacitika civomezi analemba kalata moimilako mipingo ya m’delalo. Iwo anati: “Civomezici cinabweletsa mavuto aakulu, koma Yehova anatithandiza kupyolela mwa abale athu. Tinali kungoŵelenga za nchito yopeleka thandizo, koma tsopano tadzionela tokha mmene zimakhalila.”

Kodi Mungagwile Nao Nchitoyi?

18. Mungacite ciani ngati mufuna kugwila nao nchito yopeleka thandizo? (Onani bokosi lakuti “ Nchito Imene Inasintha Moyo Wake.”)

18 Kodi mukufuna kupeza cimwemwe cimene anthu amakhala naco cifukwa cogwila nchito yothandiza ena? Ngati n’conco, dziŵani kuti ogwila nchito yopeleka thandizo amasankhidwa pakati pa abale ndi alongo amene amagwila nchito yomanga Nyumba za Ufumu. Conco, uzani akulu mumpingo wanu kuti mukufuna fomu yofunsila utumikiwu. Mkulu wina amene wagwila nchito yothandiza anthu kwa nthawi yaitali anapeleka malangizo akuti: “Muyenela kupita ku dela limene kwacitika ngozi kokha ngati mwauzidwa kutelo ndi Komiti Yoyang’anila za Cithandizo.” Kutsatila malangizo amenewa kumathandiza kuti nchitoyo iziyenda mwadongosolo.

19. Kodi nchito yopeleka thandizo imaonetsa bwanji kuti ndife ophunzila oona a Kristu?

19 Kugwila nchito yopeleka thandizo pakacitika ngozi ndi njila yabwino kwambili yoonetsela kuti timamvela lamulo la Kristu lakuti ‘tizikondana.’ Kukhala ndi cikondi cotelo kumaonetsa kuti ndife ophunzila oona a Kristu. (Yoh. 13:34, 35) Ndi mwai waukulu kukhala ndi abale ambili odzipeleka amene amalemekeza Yehova mwa kugwila nchito yopeleka thandizo kwa anthu ocilikiza Ufumu wa Mulungu mokhulupilika.

^ par. 3 Nkhani ino ikamba za nchito yopeleka thandizo kwa Akristu anzathu. Koma nthawi zambili nchitoyi imapindulitsanso anthu amene si Mboni.—Agal. 6:10.

^ par. 5 Paulo anagwilitsila nchito liu loculukitsa locokela ku liu lakuti di·aʹko·nos (mtumiki) pokamba za “atumiki othandiza.”—1 Tim. 3:12.

^ par. 10 Onani nkhani yakuti “Kuthandiza Banja Lathu la Cikhulupililo mu Bosnia,” mu Nsanja ya Olonda ya November 1, 1994, tsamba 23 mpaka 27.