Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 18

Mmene Timapezela Ndalama Zoyendetsela Nchito Za Ufumu

Mmene Timapezela Ndalama Zoyendetsela Nchito Za Ufumu

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Anthu a Yehova amacilikiza nchito za Ufumu

1, 2. (a) Kodi M’bale Russell anamuyankha bwanji m’busa wina atam’funsa za mmene Ophunzila Baibulo anali kupezela ndalama zoyendetsela nchito yao? (b) Tikambilana ciani m’nkhani ino?

NTHAWI ina, m’busa wa cipembedzo ca Reformed Church anafikila M’bale Charles T. Russell. Iye anali kufuna kudziŵa mmene Ophunzila Baibulo anali kupezela ndalama zoyendetsela nchito yao.

M’bale Russell anayankha kuti: “Ife sitisonkhetsa ndalama.”

M’busayo anafunsa kuti: “Nanga ndalama mumazipeza bwanji?”

M’bale Russell anayankha kuti: “Ndidzakuuzani cilungamo, koma mwina simudzakhulupilila. Anthu akabwela ku misonkhano yathu saona mbale iliyonse ya zopeleka. Koma amaona kuti pali zinthu zimene zimafunikila ndalama. Ndipo anthuwo paokha amaganizila kuti, ‘Nyumba ino imafunikila ndalama . . . Nanga ndingacite ciani kuti ndithandize kulipila zimenezi?’”

M’busayo anayang’ana M’bale Russell modabwa.

M’bale Russell anapitiliza kunena kuti: “Ndikukuuzani cilungamo, ndipo ambili amandifunsa kuti,’ Kodi ndingacite bwanji ngati ndifuna kucita copeleka?’ Zinthu zikamuyendela bwino munthu, ndipo wapeza ndalama, amafuna kugwilitsila nchito ndalamayo pa nchito ya Ambuye. Ngati munthuyo alibe ndalama, n’kumukakamizilanji kucita copeleka?” *

2 M’bale Russell anali kukambadi “cilungamo.” Kuyambila kale, anthu a Mulungu akhala akucita zopeleka n’colinga cocilikiza kulambila koona. M’Nkhani ino, tiphunzila zitsanzo za m’Malemba ndiponso zitsanzo zina za m’nthawi yathu za anthu amene akucita zopeleka. Pamene tikuphunzila za mmene nchito ya Ufumu imacilikizidwila masiku ano, aliyense wa ife ayenela kudzifunsa kuti: “Ndingacite ciani kuti ndionetse kuti ndimacilikiza Ufumu wa Mulungu?”

“Aliyense Amene Ali Ndi Mtima Wofunitsitsa Apeleke kwa Yehova”

3, 4. (a) Kodi Yehova ali ndi cikhulupililo cotani mwa atumiki ake? (b) Kodi Aisiraeli anacilikiza bwanji nchito yomanga cihema?

3 Yehova amawakhulupilila kwambili olambila ake oona. Iye amadziŵa kuti atumiki ake akapatsidwa mpata woonetsa kudzipeleka kwao kwa Mulungu, io amapeleka mofunitsitsa zopeleka zao. Taganizilani zitsanzo ziŵili za m’nthawi ya Aisiraeli.

4 Pambuyo potulutsa Aisiraeli mu Iguputo, Yehova anawauza kuti amange cihema colambililamo cimene akanatha kucinyamula. Kuti amange cihemaco ndi kucikongoletsa panafunika ndalama zambili. Conco Yehova anauza Mose kuti apatse anthu mwai wocilikiza nchito yomangayo, ndipo anamuuza kuti: “Aliyense amene ali ndi mtima wofunitsitsa apeleke kwa Yehova.” (Eks. 35:5) Kodi Aisiraeliwo amene anali atacoka mu “ukapolo wa mtundu uliwonse umene anatha kuwagwilitsa nchito mwankhanza,” anacita ciani? (Eks. 1:14) Iwo anacilikiza moolowa manja mwa kupeleka golide, siliva, ndi zinthu zina za mtengo wapatali, ndipo zambili mwa izo anali atapatsidwa ndi Aigupto omwe anali kuwatumikila. (Eks. 12:35, 36) Aisiraeli anapeleka zinthu zambili kuposa zimene zinali kufunikila cakuti anacita ‘kuwaletsa kubweletsa zinthuzo.’—Eks. 36:4-7.

5. Kodi Aisiraeli anatani Davide atawapatsa mwai wopeleka zopeleka pa nchito yomanga kacisi?

5 Patapita zaka pafupifupi 475, Davide nayenso anapeleka copeleka kucokela mu ‘cuma cake capadela’ n’colinga cakuti acilikize nchito yomanga kacisi amene anali nyumba yoyamba yolambililamo Mulungu padziko lapansi. Ndiyeno anapatsanso Aisiraeli onse mwai wopeleka zopeleka mwa kuwafunsa kuti: “Ndani lelo ali wokonzeka kupeleka mphatso kwa Yehova?” Poyankha, anthuwo “anapeleka nsembezo kwa Yehova ndi mtima wathunthu.” (1 Mbiri 29:3-9) Davide anasonyeza kuti anali kuzindikila gwelo la zopelekezo pamene anapemphela kwa Yehova kuti: “Ciliconse n’cocokela kwa inu, ndipo tapeleka kwa inu zocokela m’dzanja lanu.”—1 Mbiri 29:14.

6. N’cifukwa ciani ndalama n’zofunika pa nchito ya Ufumu masiku ano? Nanga pakubuka mafunso otani?

6 Mose ndi Davide sanaumilize anthu a Mulungu kuti apeleke zopeleka. M’malo mwake, anthu anapeleka ndi mtima wofunitsitsa. Nanga bwanji masiku ano? Timadziŵa bwino kuti nchito yokhudza Ufumu wa Mulungu imafuna ndalama. Ndalama n’zofunika kuti ma Baibulo ndiponso mabuku Ophunzitsa Baibulo asindikizidwe ndi kufalitsidwa. Pamafunikanso ndalama kuti amange ndi kusamalila nyumba zolambililamo ndi maofesi a nthambi, ndi kupeleka cithandizo kwa Akristu anzathu pakagwa tsoka. Pa cifukwa cimeneci, pakubuka mafunso ofunika awa: Kodi ndalama zimenezi zimacokela kuti? Kodi otsatila a Mfumu ayenela kukakamizidwa kuti apeleke zopeleka?

“Sitidzapempha Thandizo kwa Anthu Kapena Kuwacondelela Kuti Athandize pa Nchitoyi”

7, 8. N’cifukwa ciani anthu a Yehova samapemphapempha ndalama kwa anthu?

7 M’bale Russell ndi anzake anakana kutsatila njila zopemphela ndalama zimene n’zofala m’machalichi acikristu. M’magazini yaciŵili ya Watch Tower munali nkhani ya mutu wakuti “Kodi mufuna magazini a ‘Zion’s Watch Tower’?” M’bale Russell anati: “Sitikayikila kuti YEHOVA ndi amene akutsogolela nchito yofalitsa magazini ino ya ‘Zion’s Watch Tower,’ motelo sitidzapempha thandizo kwa anthu kapena kuwacondelela kuti athandize pa nchitoyi. Mwiniwakeyo, amene ananena kuti: ‘Siliva ndi golidi yense wa m’mapili ndi wanga,’ akadzalephela kupeleka ndalama zokwanila, tidzadziŵa kuti nthawi yosiya kufalitsa magaziniyi yakwana.” (Hag 2:7-9) Papita zaka zoposa 130 tsopano, koma Nsanja ya Mlonda ndiponso gulu limene limafalitsa magaziniyo zikalipo.

8 Anthu a Yehova sapemphapempha ndalama. Iwo sayendetsamo mbale ya zopeleka kapena kutumiza makalata opempha ndalama kwa anthu. Iwo sacita maphwando, kugulitsa zinthu, ndi kuyenda ndawala n’colinga cofuna kupeza ndalama. Iwo amatsatilabe zimene magazini ya Watch Tower inakamba zaka zambili zapitazo kuti: “Ife timaona kuti n’kulakwa kupemphapempha ndalama za nchito ya Ambuye monga mmene zipembedzo zina zimacitila . . . Tikuona kuti ndalama zimene anthu amapeza pogwilitsila nchito njila zosiyanasiyana zopemphela ndalama m’dzina la Ambuye n’zoipa, n’zosafunika kwa iye, ndipo Ambuye sadalitsa amene amapeleka ndalamazo kapena nchito imene amacita pogwilitsila nchito ndalama zimenezo.” *

“Aliyense Acite Mogwilizana ndi Mmene Watsimikizila Mumtima Mwake”

9, 10. Pali cifukwa cimodzi citi cimene timapelekela zopeleka mwakufuna kwathu?

9 Ifenso monga nzika za Ufumu za masiku ano, siticita kukakamizidwa kupeleka zopeleka. M’malo mwake, timakondwela kugwilitsila nchito ndalama zathu ndi zinthu zina pocilikiza nchito za Ufumu. N’cifukwa ciani timakhala ofunitsitsa kutelo? Timatelo pa zifukwa zitatu.

10 Coyamba, timapeleka mwa kufuna kwathu cifukwa cakuti timakonda Yehova ndipo timafuna “kucita zinthu zomukondweletsa.” (1 Yoh. 3:22) Yehova amasangalala kwambili ndi mtumiki wake amene amapeleka ndi mtima wonse. Tiyeni tikambilane mau a mtumwi Paulo okhudza zopeleka za Akristu. (Ŵelengani 2 Akorinto 9:7) Mkristu woona sacita kukakamizidwa kupeleka zopeleka. M’malo mwake, iye amapeleka cifukwa cakuti “watsimikizila mumtima mwake” kuti atelo. * Izi zikutanthauza kuti iye akaona kuti pafunika thandizo amacitapo kanthu kuti athandize. Munthu wotelo amakondedwa ndi Yehova cifukwa cakuti “Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.” Baibulo lina linamasulila mau a pa lembali kuti: “Mulungu amakonda anthu amene amakonda kupatsa.”

Acicepele athu ku Mozambique naonso amakonda kupeleka zopeleka

11. N’ciani cimatisonkhezela kupatsa Yehova mphatso yabwino koposa?

11 Caciŵili, timapeleka zopeleka kuti tiyamikile Yehova cifukwa ca zinthu zabwino zimene amaticitila. Taganizilani za mfundo yogwila mtima imene inali m’Cilamulo ca Mose. (Ŵelengani Deuteronomo 16:16, 17) Popita ku zikondwelelo za pacaka, mwamuna aliyense waciisiraeli anali kufunikila kupeleka mphatso ‘yolingana ndi madalitso amene Yehova anamupatsa.’ Conco, asanapite ku cikondwelelo, mwamuna aliyense anali kufunikila kuona mmene Mulungu wamudalitsila ndi kufufuza mumtima mwake kuti aone mphatso yabwino yopeleka kwa Mulungu. Mofananamo, tikaganizila mmene Yehova amatidalitsila, timasonkhezeledwa kum’patsa mphatso zabwino koposa. Mphatso zimene timamupatsa ndi mtima wonse, ndi umboni wakuti timayamikila kwambili madalitso ambili amene Yehova amatikhuthulila.—2 Akor. 8:12-15.

12, 13. Kodi zopeleka zathu zimasonyeza bwanji kuti timakonda Mfumu yathu? Nanga munthu aliyense ayenela kupeleka ndalama zingati?

12 Cacitatu, tikamapeleka zopeleka mwakufuna kwathu, timasonyeza kuti timakonda Mfumu Yesu Kristu. Mwa njila yotani? Onani zimene Yesu anauza ophunzila ake pa usiku womaliza wamoyo wake padziko lapansi. (Ŵelengani Yohane 14:23) Iye anati: “Ngati munthu amandikonda, adzasunga mau anga.” “Mau” a Yesu amaphatikizapo lamulo lake lakuti tilalikile uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Timasunga “mau” amenewo mwa kucita zonse zimene tingathe pogwilitsila nchito nthawi yathu, mphamvu ndi ndalama zathu popititsa patsogolo nchito yolalikila za Ufumu. Tikamacita zimenezi, timasonyeza kuti timakonda Mfumu Mesiya.

13 Ndithudi, monga nzika zokhulupilika za Ufumu wa Mulungu, timafuna kucilikiza Ufumu ndi mtima wathu wonse mwa zopeleka zathu za ndalama. Kodi tiyenela kupeleka ndalama zingati? Imeneyo ndi nkhani yaumwini. Aliyense ayenela kupeleka zimene angakwanitse. Ambili a abale athu ndi osauka. (Mat. 19:23, 24; Yak. 2:5) Koma abale athu ameneŵa amakondwela kudziŵa kuti Yehova ndi Mwana wake amayamikila kwambili zopeleka zao zimene amapeleka ndi mtima wonse ngakhale zitakhala zocepa bwanji.—Maliko 12:41-44.

Kodi Ndalama Zimacokela Kuti?

14. Kwa zaka zambili, kodi Mboni za Yehova zinali kuomboletsa bwanji zofalitsa zao?

14 Kwa zaka zambili, Mboni za Yehova zinali kufalitsa mabuku ofotokoza Baibulo pa copeleka ca mtengo woikika. Copeleka cimeneco cinali kukhala cocepa kwambili n’colinga cakuti ngakhale anthu osoŵa azitha kuombolako zofalitsa zimenezo. Koma ngati mwininyumba alibe ndalama yoombolela cofalitsa, ndipo wasonyeza cidwi cacikulu, ofalitsa a Ufumu anali kumusiiyila cofalitsaco. Colinga cacikulu ca ofalitsa cinali kusiya cofalitsa kwa anthu ofunitsitsa kuphunzila Baibulo kuti aŵelenge ndi kupindula ndi cofalitsaco.

15, 16. (a) Kodi Bungwe Lolamulila linasintha bwanji mmene timagaŵila zofalitsa zathu kuyambila mu 1990? (b) Kodi timapeleka bwanji zopeleka za ufulu? (Onani chati ca mutu wakuti “ Kodi Zopeleka Zathu Zimagwila Nchito Yanji?”)

15 Mu 1990, Bungwe Lolamulila linayamba kusintha mmene tinali kufalitsila zofalitsa zathu. Kuyambila m’cakaco, zofalitsa zonse zinayamba kufalitsidwa pa copeleka caufulu cosakhala ndi mtengo woikika ku United States. Kalata imene inalembedwela mipingo yonse m’dzikolo inati: “Magazini ndiponso mabuku adzipatsidwa kwa ofalitsa ndi anthu ena onse acidwi popanda kuwauza kuti apeleke copeleka coikika akafuna kutenga cofalitsa. . . . Aliyense amene afuna kupeleka zopeleka kuti athandize kulipilila zofunika pa nchito yathu yophunzitsa Baibulo angatelo. Koma aliyense ali ndi ufulu wolandila cofalitsa kaya wapeleka copeleka kapena ai.” Makonzedwe amenewa anaonetselatu colinga ca zopeleka zathu ndiponso ca nchito yathu, ndi kuti “mau a Mulungu siticita nao malonda.” (2 Akor. 2:17) M’kupita kwa nthawi, maofesi a nthambi zonse padziko lapansi, anayambanso kugwilitsila nchito mokonzedwe opeleka zopeleka mwakufuna kwa munthu akalandila cofalitsa.

16 Kodi timapeleka bwanji zopeleka za ufulu? Mu Nyumba za Ufumu za Mboni za Yehova, muli mabokosi a zopeleka amene anaikidwa kumbuyo kwa holo. Aliyense amene akufuna angaponyemo ndalama kapena angatumize copeleka cake mwacindunji ku bungwe lililonse lovomelezedwa mwa lamulo la Mboni za Yehova. Caka ciliconse, mu Nsanja ya Mlonda mumakhala nkhani imene imafotokoza zimene anthu ofuna kupeleka copeleka ayenela kucita.

Nanga Ndalamazo Zimagwila Nchito Yanji?

17-19. Fotokozani mmene zopeleka zathu zimagwilila nchito (a) panchito ya padziko lonse, (b) panchito yomanga Nyumba Za Ufumu padziko lonse, ndi (c) zothandiza pa mpingo.

17 Za Nchito ya Padziko Lonse. Ndalamazi zimathandiza kulipilila zinthu zina zokhudza nchito yolalikila padziko lonse. Zinthu zimenezo zimaphatikizapo kusindikiza mabuku kuti afalitsidwe padziko lonse, kumanga ndi kusamalila maofesi a nthambi ndi nyumba za Beteli, ndiponso kucilikiza sukulu zophunzitsa atumiki a Mulungu. Ndalama zina zimagwila nchito posamalila amishonale, woyang’anila woyendela, ndi apainiya apadela. Ndalamazi zimagwilanso nchito popeleka cithandizo kwa Akristu anzathu pakacitika ngozi. *

18 Za nchito yomanga Nyumba Za Ufumu padziko lonse. Mipingo imene ikufuna kumanga kapena kukonzanso Nyumba za Ufumu, imapatsidwa ndalama. Pamene mipingo icita zopeleka, mipingo ina imapatsidwanso ndalama kuti imange kapena kukonzanso Nyumba zao za Ufumu. *

19 Zothandiza pa Mpingo. Ndalamazi zimagwilitsidwa nchito ndi mpingo pogulila ndi kulipila zinthu zofunika pa Nyumba ya Ufumuyo. Akulu angakambilane kuti mpingo wao utumize ndalama zina ku ofesi ya nthambi kuti zithandize kupititsa patsogolo nchito ya padziko lonse. Kenako, akulu amafunsa mpingo za nkhani ya cowindaco. Mpingo ukavomeleza, ndalama ya cowindaco imatumizidwa ku nthambi. Mwezi uliwonse, m’bale amene amasamalila za maakaunti pa mpingo amakonza lipoti la mmene ndalama zagwilila nchito, ndipo lipotilo limaŵelengedwa kumpingo wonse.

20. Kodi mungalemekeze bwanji Yehova ndi ‘zinthu zanu zamtengo wapatali’?

20 Tikaganizila zinthu zonse zimene zimalowetsedwamo pogwila nchito yolalikila za Ufumu ndi kupanga ophunzila padziko lonse lapansi, timasonkhezeledwa ‘kulemekeza Yehova ndi zinthu zathu zamtengo wapatali.’ (Miy. 3:9, 10) Zinthu zathu zamtengo wapatali zimaphatikizapo mphamvu zathu, maganizo athu, ndi cuma cakuuzimu. Timafunitsitsa kugwilitsila nchito zinthu zimenezi panchito ya Ufumu. Koma musaiwale kuti zinthu zathu za mtengo wapatali zimaphatikizaponso cuma cathu cakuthupi. Tiyeni tizipeleka zimene tingathe pa nthawi iliyonse imene tingakwanitse. Zopeleka zathu zaufulu zimalemekeza Yehova, ndipo zimasonyeza kuti tikucilikiza Ufumu wa Mesiya.

^ par. 1 Magazini ya The Watch Tower, ya July 15, 1915, tsamba 218 mpaka 219.

^ par. 8 Magazini ya Watch Tower, ya August 1, 1899, tsamba 201.

^ par. 10 Katswili wina anakamba kuti mau acigiriki amene anawamasulila kuti “watsimikizila” amatanthauza kuti “munthuyo amayamba waganizila coyamba.” Iye ananenanso kuti: “Ngakhale kuti kupatsa kumabweletsa cimwemwe coculuka, tiyenela kuganizila ndi kulinganiza copeleka cathu pasadakhale.”—1 Akor. 16:2.

^ par. 17 Onani Nkhani 20 m’buku lino kuti mumve zambili zokhudza nchito yopeleka cithandizo kwa Akristu anzathu pakagwa tsoka.

^ par. 18 Onani Nkhani 19 kuti mumve zambili zokhudza nchito yomanga Nyumba za Ufumu.