Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 6

Anthu Amene Amalalikila—Atumiki Akudzipeleka Mofunitsitsa

Anthu Amene Amalalikila—Atumiki Akudzipeleka Mofunitsitsa

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Mfumu ikhazikitsa gulu la alaliki

1, 2. Ndi nchito yaikulu iti imene Yesu ananenelatu kuti idzacitika? Ndipo pakubuka funso lofunika liti?

NTHAWI zambili atsogoleli a ndale samakwanilitsa malonjezo ao. Ngakhale atsogoleli amene ali ndi zolinga zabwino kaŵilikaŵili amalephela kukwanilitsa malonjezo ao. Koma n’zosangalatsa kuti Yesu Kristu, amene ndi Mfumu Mesiya, nthawi zonse amakwanilitsa malonjezo ake.

2 Atakhala Mfumu mu 1914, Yesu anali wokonzeka kukwanilitsa ulosi umene anakamba zaka pafupifupi 1,900 m’mbuyomo. Atatsala pang’ono kuphedwa, iye ananenelatu kuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu.” (Mat. 24:14) Kukwanilitsidwa kwa mau amenewa ndi mbali ya cizindikilo cakuti Yesu akulamulila monga Mfumu. Komabe pakubuka funso lofunika ili: Kodi Mfumuyo yakwanitsa bwanji kukhazikitsa gulu la alaliki odzipeleka mwa kufuna kwao popeza kuti m’masiku otsiliza ano anthu ambili ndi odzikonda, opanda cikondi ndi osakonda kulambila? (Mat. 24:12; 2 Tim. 3:1-5) Tifunika kudziŵa yankho la funso limeneli cifukwa funsoli limakhudza Akristu onse oona.

3. Kodi mau a Yesu anasonyeza kuti iye anali ndi cidalilo cotani? Nanga n’cifukwa ciani anali ndi cidalilo cimeneco?

3 Ganizilaninso mau a ulosi amene Yesu anakamba. Iye anakamba kuti uthenga wabwino “udzalalikidwa.” Mau amenewa akusonyeza kuti iye sanali kukaikila kuti zimenezi zidzacitikadi. Yesu anali kukhulupilila kuti m’masiku otsiliza iye adzakhala ndi atumiki odzipeleka. N’cifukwa ciani anali ndi cidalilo cotelo? Cifukwa cakuti anatengela Atate wake. (Yoh. 12:45; 14:9) Yesu asanabwele padziko lapansi monga munthu, iye anali kuona kuti Yehova amakhulupilila kuti atumiki Ake ali ndi mtima wodzipeleka. Tiyeni tione mmene Yehova anasonyezela kuti amakhulupilila atumiki ake.

“Anthu Ako Adzadzipeleka Mofunitsitsa”

4. Ndi nchito iti imene Yehova anapempha Aisiraeli kucita? Nanga io anacita ciani?

4 Kumbukilani zimene zinacitika pamene Yehova analamula Mose kuti amange cihema, kapena kuti tenti. Cihemaco cinali kudzakhala malo olambililako a Aisiraeli. Kudzela mwa Mose, Yehova anauza anthu onse kucilikiza nchitoyo. Mose anawauza kuti: “Aliyense amene ali ndi mtima wofunitsitsa apeleke kwa Yehova zinthu.” Kodi zotsatilapo zake zinali zotani? Baibulo limati anthu “anapitilizabe kubweletsa . . . nsembe zao zaufulu tsiku lililonse.” Iwo anabweletsa zinthu zambili cakuti anacita “kuwaletsa kubweletsa zinthuzo.” (Eks. 35:5; 36:3, 6) Aisiraeli anacitadi zinthu mokhulupilika monga mmene Yehova anali kuwadziŵila kuti adzatelo.

5, 6. Malinga ndi Salimo 110:1-3, ndi mzimu wotani umene Yehova ndiponso Yesu anali kuyembekezela kudzapeza pakati pa olambila oona m’masiku otsiliza?

5 Kodi Yehova anali ndi cidalilo cakuti atumiki ake adzakhalanso odzipeleka m’masiku otsiliza? Inde. Zaka zoposa 1,000 Yesu asanabadwe padziko lapansi, Yehova anauzila Davide kulemba za mmene zinthu zidzakhalila panthawi imene Mesiya adzayamba kulamulila. (Ŵelengani Salimo 110:1-3.) Malinga ndi ulosiwo, Yesu, Mfumu yatsopanoyo inali kudzakhala ndi adani. Komabe ulosiwo unasonyezanso kuti iye adzakhala ndi gulu la anthu amene adzamucilikiza. Iwo adzatumikila Mfumuyo mwa kufuna kwao. Ngakhale ana aang’ono adzadzipeleka mwa kufuna kwao, ndipo anthu odzipelekawo adzaculuka kwambili mofanana ndi mmene mame amaculukila pa maudzu m’mawa. *

Anthu amene amacilikiza Ufumu modzipeleka ndi oculuka ngati mame (Onani ndime 5)

6 Yesu anadziŵa kuti ulosi wolembedwa pa Salimo 110 umanena za iye. (Mat. 22:42-45) Conco, iye anali kukhulupilila kuti adzakhala ndi atumiki okhulupilika amene adzadzipeleka mwa kufuna kwao kugwila nchito yolalikila uthenga wabwino padziko lonse. Kodi mbili yakale ikusonyeza ciani pankhaniyi? Kodi Mfumu yakwanitsa kukhazikitsa gulu la alaliki odzipeleka masiku otsiliza ano?

“Kulengeza Uthenga Umenewu Ndi Mwai Ndiponso Udindo Wanga”

7. Atangoikidwa kukhala Mfumu, ndi nchito iti imene Yesu anayamba kukonzekeletsa otsatila ake kugwila?

7 Atangoikidwa kukhala Mfumu, Yesu anayamba kukonzekeletsa otsatila ake kaamba ka nchito yaikulu imene inafunika kugwilidwa. Monga mmene tinaonela m’Nkhani 2, iye anayendela ndi kuyeletsa anthu a Mulungu kuyambila mu 1914 mpaka kuciyambi kwa 1919. (Mal. 3:1-4) Ndiponso mu 1919 mmenemo, iye anaika kapolo wokhulupilika kuti azitsogolela otsatila ake. (Mat. 24:45) Kuyambila nthawi imeneyi, kapoloyu wakhala akugaŵila cakudya cakuuzimu. Iye amagaŵila cakudyaci kupyolela m’nkhani za pa misonkhano yacigawo ndi m’zofalitsa zathu. Zinthu zimenezi zakhala zikulimbikitsa Akristu onse kugwila nao nchito yolalikila.

8-10. Kodi misonkhano yacigawo inalimbikitsa bwanji abale kugwila nchito yolalikila? Pelekani citsanzo. (Onaninso bokosi lakuti “ Misonkhano Yacigawo ya m’Nthawi Yakale Imene Inalimbikitsa Abale Kugwila Nchito Yolalikila.”)

8 Nkhani za pamisonkhano yacigawo. Nkhondo Yoyamba ya Padziko Lonse itatha, Ophunzila Baibulo anasonkhana ku Cedar Point, Ohio, U.S.A., kuyambila pa September 1 mpaka pa September 8 caka ca 1919 kuti alandile malangizo othandiza. Pa tsiku laciŵili la msonkhanowo, M’bale Rutherford anakamba nkhani, ndipo m’nkhaniyo anafotokozela osonkhanawo mosapita m’mbali kuti: “Nchito yaikulu ya Mkristu padziko lapansi . . . ndi kulengeza uthenga wa ufumu wa Ambuye.”

9 Msonkhanowo unafika pacimake patapita masiku atatu pamene M’bale Rutherford anakamba nkhani ya mutu wakuti “Mau kwa Anchito Anzathu.” Pambuyo pake, nkhani imeneyi inafalitsidwa m’magazini ya The Watch Tower, pa mutu wakuti “Kulengeza Ufumu wa Mulungu.” M’nkhaniyo, iye anakamba kuti: “Mkristu akamaganizila za moyo wake, amadzifunsa kuti, N’cifukwa ciani ndili ndi moyo? Yankho lake liyenela kukhala lakuti, Ambuye anandikomela mtima ndi kundipanga kukhala kazembe wake kuti ndilengeze uthenga woyanjanitsa anthu ndi Mulungu pa dziko lapansi, ndipo kulengeza uthenga umenewu ndi mwai ndiponso udindo wanga.”

10 M’nkhani yosaiwalika imeneyo, M’bale Rutherford analengeza kuti kudzayamba kutuluka magazini atsopano ochedwa The Golden Age (imene tsopano timati Galamukani!). Iye ananena kuti colinga ca magaziniwo ndi kuthandiza anthu kukhulupilila kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetsa mavuto a anthu. Kenako iye anafunsa kuti ndi anthu angati pa msonkhanowo amene anali kufuna kudzagwila nao nchito yogaŵila magaziniyo. Lipoti la msonkhanowo linati: “Zimene zinacitika zinali zocititsa cidwi. Anthu onse okwanila 6,000 amene anali pamsonkhanowo anaimilila posonyeza kuti anali kufunitsitsa kudzagwila nao nchitoyo.” * Motelo n’zoonekelatu kuti Mfumu inali ndi atumiki odzipeleka amene anali kufunitsitsa kulengeza za Ufumu wake.

11, 12. Kodi magazini ina ya The Watch Tower ya mu 1920 inafotokoza kuti nchito imene Yesu analosela idzacitika liti?

11 Zofalitsa. Kudzela m’magazini ya The Watch Tower, anthu a Mulungu anadziŵa kuti nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu imene Yesu analosela ndi yofunika kwambili. Onani zitsanzo za m’magazini amene anafalitsidwa kumayambililo kwa zaka za m’ma 1920.

12 Kodi ndi uthenga wotani umene unafunika kulengezedwa kuti lemba la Mateyu 24:14 likwanilitsidwe? Nanga nchitoyo inayenela kucitika liti? Nkhani ya m’magazini ya The Watch Tower ya July 1, 1920 ya mutu wakuti “Uthenga Wabwino wa Ufumu,” inafotokoza uthenga umene ufunika kulengezedwa. Nkhaniyo inati: “Uthenga wabwino umenewu ndi wokhudza kutha kwa dongosolo lakale la zinthu ndi kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mesiya.” Pofotokoza nthawi imene uthengawo ufunika kulalikidwa, nkhaniyo inati: “Uthenga umenewu ufunika kulalikidwa pakati pa nthawi ya nkhondo yaikulu [Nkhondo Yoyamba ya Padziko Lonse] ndi nthawi ya ‘cisautso cacikulu.’” Conco, nkhaniyo inati: “Ino ndiyo nthawi . . . yolalikila uthenga wabwino kwa anthu onse a m’Machalichi Acikristu.”

13. Kodi magazini ya The Watch Tower ya March 15, 1921 inalimbikitsa bwanji Akristu odzozedwa kukhala ndi mtima wodzipeleka?

13 Kodi anthu a Mulungu anafunika kucita kukakamizidwa kuti agwile nchito imene Yesu analosela? Iyai. Nkhani yakuti “Khalani Olimba Mtima,” imene inalembedwa m’magazini ya The Watch Tower ya March 15, 1921, inalimbikitsa Akristu odzozedwa amene anali ndi mtima wofunitsitsa kugwila nchitoyi. Aliyense analimbikitsidwa kuti adzifunse kuti: “Kodi ndimaona kuti kugwila nao nchitoyi ndi mwai wamtengo wapatali ndiponso udindo wanga?” Nkhaniyo inapitiliza kuti: “Tikukhulupilila kuti ngati inuyo mukuona kuti kucita zimenezi [kulalikila] ndi mwai waukulu, mudzakhala ngati Yeremiya, amene mau a Ambuye anali ‘ngati moto woyaka umene autsekela m’mafupa ake,’ ndipo anamulimbikitsa kulankhula.” (Yer. 20:9) Mau olimbikitsa amenewo anasonyeza kuti Yehova ndi Yesu amakhulupilila anthu okhulupilika amene amacilikiza Ufumu wa Mulungu.

14, 15. Kodi magazini ya The Watch Tower ya August 15 1922 inalimbikitsa Akristu odzozedwa kuti azilalikila m’njila zotani?

14 Kodi Akristu oona ayenela kulalikila bwanji uthenga wa Ufumu kwa anthu? Nkhani yaifupi koma yamphamvu ya mutu wakuti “Utumiki Ndi Wofunika,” imene inatuluka m’magazini ya The Watch Tower ya August 15, 1922, inalimbikitsa Akristu odzozedwa kuti afunika “kucita khama kupeleka zofalitsa za uthenga wabwino kwa anthu ndi kulankhula nao ku nyumba zao ndi kucitila umboni kuti ufumu wa kumwamba wayandikila.”

15 N’zoonekelatu kuti kuyambila mu 1919, Kristu wakhala akugwilitsila nchito kapolo wake wokhulupilika ndi wanzelu kugogomezela mfundo yakuti kulalikila uthenga wa Ufumu ndi mwai ndiponso udindo wa Mkristu. Kodi Ophunzila Baibulo oyambilila anacita ciani atalimbikitsidwa kugwila nao nchito yolengeza uthenga wa Ufumu?

“Anthu Okhulupilika Adzadzipeleka mwa Kufuna Kwao”

16. N’ciani cimene akulu ena amene anali kusankhidwa mwa voti anacita atamva mfundo yakuti Akristu onse ayenela kulalikila?

16 M’zaka za m’ma 1920 ndi m’ma 1930, abale ena anali kutsutsa mfundo yakuti Akristu onse odzozedwa afunika kugwila nchito yolalikila. Magazini ya The Watch Tower ya November 1, 1927, inafotokoza zimene zinali kucitika. Iyo inati: “Pali akulu ena m’chalichi [mumpingo] . . . amene safuna kulimbikitsa abale kugwila nchito yolalikila, ndipo ionso amakana kugwila nchitoyi. . . . Iwo amasuliza lamulo lakuti tizipita ku nyumba ndi nyumba kukalalikila za uthenga wa Mulungu, Mfumu yake ndi ufumu wake kwa anthu.” Nkhaniyo inafotokoza mosapita m’mbali kuti: “Nthawi tsopano yakwana yakuti anthu okhulupilika adziŵe anthu amenewa, kuwapewa ndi kuwauza kuti sadzawapatsanso mwai wokhala akulu.” *

17, 18. N’ciani cimene abale ndi alongo m’mipingo anacita atapatsidwa malangizo ocokela kwa kapolo wokhulupilika? Nanga ambili alabadila bwanji malangizowo pa zaka 100 zapitazo?

17 Zinali zosangalatsa kuti abale ndi alongo ambili m’mipingo anamvela ndi mtima wonse malangizo amenewa ocokela kwa kapolo wokhulupilika. Iwo anaona kuti kugwila nchito yolalikila uthenga wa Ufumu unali mwai wao. Magazini ya The Watch Tower ya March 15, 1926, inati: “Anthu okhulupilika adzadzipeleka, . . . kulengeza uthenga umenewu kwa anthu.” Mwa kucilikiza Mfumu Mesiya ndi mtima wonse, anthu okhulupilikawo anakwanilitsa ulosi wolembedwa pa Salimo 110:3.

18 Pa zaka 100 zapitazi, anthu mamiliyoni ambili adzipeleka mofunitsitsa kugwila nchito yolalikila za Ufumu wa Mulungu. M’nkhani zingapo zotsatila, tidzakambilana mmene io amagwilila nchitoyi, njila ndi zida zimene amagwilitsila nchito ndiponso zotsatilapo zabwino za nchitoyi. Koma coyamba tiyeni tikambilane cifukwa cake anthu mamiliyoni ambili amadzipeleka kugwila nchito yolalikila za Ufumu ngakhale kuti tikukhala m’dziko limene anthu ake ndi odzikonda. Pamene tikukambilana zimenezi, tingacite bwino kumadzifunsa kuti, ‘N’cifukwa ciani ndimalalikila uthenga wabwino kwa ena?’

“Pitilizani Kufunafuna Ufumu Coyamba”

19. N’cifukwa ciani timamvela malangizo a Yesu akuti “pitilizani kufunafuna Ufumu coyamba”?

19 Yesu analangiza otsatila ake kuti “pitilizani kufunafuna Ufumu coyamba.” (Mat. 6:33) N’cifukwa ciani timamvela lamulo limeneli? Kunena mwacidule, n’cifukwa cakuti timadziŵa kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambili pokwanilitsa colinga ca Mulungu. Monga mmene tinaphunzilila m’nkhani yapita, mzimu woyela wakhala ukuulula pang’onopang’ono mfundo zocititsa cidwi za coonadi zokhudza Ufumu wa Mulungu. Mfundo za coonadi za Ufumu zikatifika pamtima, timalimbikitsidwa kufunafuna Ufumuwo coyamba pa umoyo wathu.

Monga mmene munthu amasangalalila kwambili akapeza cuma cobisika, Akristu naonso amasangalala kuti anaphunzila coonadi ca Ufumu (Onani ndime 20)

20. Kodi fanizo la Yesu la cuma cobisika linasonyeza bwanji kuti otsatila ake adzamvela malangizo akuti afunika kufunafuna Ufumu coyamba?

20 Yesu anadziŵa kuti otsatila ake adzamvela malangizo akuti apitilizebe kufunafuna Ufumu coyamba. Taganizilani fanizo lake la cuma cobisika. (Ŵelengani Mateyu 13:44.) Pamene anali kugwila nchito yake ya m’munda, mlimi wa m’fanizoli anapeza cuma cobisika, ndipo anadziŵa kuti cinali camtengo wapatali. Kodi mlimiyo anacita ciani atapeza cumaco? Baibulo limanena kuti: “Cifukwa ca cimwemwe cimene anali naco, anapita kukagulitsa zinthu zonse zimene anali nazo n’kukagula mundawo.” Kodi tikuphunzilapo ciani pamenepa? Tikaphunzila coonadi ca Ufumu ndi kudziŵa phindu lake, timasangalala kudzimana zinthu zina n’colinga cakuti tiike zinthu za Ufumu patsogolo pa moyo wathu. *

21, 22. Ndi motani mmene anthu ocilikiza Ufumu mokhulupilika amasonyezela kuti amaika Ufumu patsogolo pa moyo wao? Pelekani citsanzo.

21 Anthu amene amacilikiza Ufumu mokhulupilika amasonyeza kuti akuika Ufumuwo patsogolo mwa zocita zao osati mwa mau cabe. Iwo amagwilitsila nchito moyo wao, luso lao, ndi cuma cao pocilikiza nchito yolalikila za Ufumu. Ndipo ambili adzimana zinthu zambili n’colinga cakuti acite utumiki wa nthawi zonse. Alaliki odzipeleka amenewa adzionela okha kuti Yehova amadalitsa anthu amene amaika Ufumu wake patsogolo. Onani citsanzo ici ca Ophunzila Baibulo oyambilila.

22 Avery Bristow ndi mkazi wake Lovenia, anali kutumikila pamodzi monga makopotala (apainiya) kumwela kwa dziko la United States kuyambila cakumapeto kwa zaka za m’ma 1920. Patapita zaka, Lovenia anati: “Ine ndi mwamuna wanga Avery tasangalala ndi nchito ya upainiya kwa zaka zambili. Nthawi zambili tinali kusoŵelatu ndalama zogulila mafuta a galimoto, cakudya ndi zinthu zina. Koma Yehova anali kutipatsa zosoŵa zathu m’njila zosiyanasiyana. Conco tinapitilizabe kucita upainiya. Nthawi zonse sitinali kusoŵa zinthu zofunika kwambili pa umoyo.” Lovenia anafotokoza zimene zinacitika nthawi ina pamene anali kutumikila mu mzinda wa Pensacola ku Florida, ndipo analibe ndalama, cakudya ndi zinthu zina zofunika. Iwo atafika ku kanyumba kao, anapeza mapulasiki bagi aŵili a zakudya ndi zinthu zina ndiponso kapepala kamene kanali ndi mau akuti: “Zacokela ku Mpingo wa Pensacola.” Pokumbukila zaka zambili zimene anatumikila monga mpainiya, Lovenia anafotokoza kuti: “Yehova sanatitaye ngakhale pang’ono. Iye sangatigwilitse mwala.”

23. Kodi kuphunzila coonadi ca Ufumu kumakupangitsani kumva bwanji? Nanga inuyo muli ndi colinga cotani?

23 Tonse sitingacite zofanana panchito yolalikila cifukwa zocitika pa umoyo wathu n’zosiyanasiyana. Komabe tonsefe tiyenela kuona kuti kugwila nchito yolengeza uthenga wabwino ndi mtima wonse ndi mwai wathu. (Akol. 3:23) Popeza kuti timaona kuti coonadi ca Ufumu cimene tinaphunzila ndi camtengo wapatali, ndife okonzeka ndiponso ofunitsitsa kudzimana zinthu zina n’colinga cakuti titumikile Mulungu mmene tingathele. Kodi cimeneci ndico colinga canu?

24. Ndi cinthu cacikulu koposa citi cimene Ufumu wa Mulungu wacita m’masiku otsiliza ano?

24 Kwa zaka 100 zapitazi, Mfumu Mesiya yakhala ikukwanilitsa mau ake opezeka pa Mateyu 24:14. Ndipo iyo sinacite kuumiliza anthu kuti agwile nchito yolalikila. Komabe anthu amene amacoka m’dziko lodzikondali ndi kukhala otsatila ake, amadzipeleka mofunitsitsa kuti agwile nchitoyi. Nchito yao yolalikila uthenga wabwino padziko lonse ndi mbali ya cizindikilo cakuti Yesu ndi Mfumu. Nchito imeneyi ndi cinthu cimodzi cacikulu koposa cimene Ufumu wa Mulungu wacita m’masiku otsiliza ano.

^ par. 5 M’Baibulo, mau akuti mame angatanthauze zinthu zoculuka. —Gen. 27:28; Mika 5:7.

^ par. 10 Kabuku kakuti To Whom the Work Is Entrusted [Kwa Amene Apatsidwa Nchito] kananena kuti: “Kugaŵila magazini a The Golden Age idzakhala nchito yapadela yolengeza uthenga wa ufumu kunyumba ndi nyumba.  . . Pambuyo polengeza uthengawu, mufunika kusiya magazini ya The Golden Age pa nyumba ya munthu kaya munthuyo anapelekelatu ndalama ya magazini kapena ai.” Nchito yapadela itatha, kwa zaka zingapo abale analimbikitsidwa kuti azipempha anthu kulembetsa kuti azilandila magazini a The Golden Age ndi a The Watch Tower. Kuyambila pa February 1, 1940, atumiki a Yehova analimbikitsidwa kuti azigaŵila magaziniwa ndi kulemba ciŵelengelo ca magazini amene agaŵila.

^ par. 16 Panthawiyo, abale mumpingo anali kuvota kuti asankhe akulu. Motelo abale akanasankha kusavotela anthu mumpingo amene sanali kufuna kugwila nchito yolalikila. M’Nkhani 12, tidzakambilana mmene zinthu zinasinthila kuti akulu ayambe kuikidwa mwa kukwanilitsa ziyeneletso za m’Malemba.

^ par. 20 Yesu anafotokoza mfundo yofanana ndi imeneyi pamene anakamba fanizo la munthu wamalonda woyendayenda amene anapita kukafunafuna ngale ya mtengo wapatali. Wamalondayo atapeza ngaleyo, anagulitsa zonse zimene anali nazo ndi kukagula ngaleyo. (Mat. 13:45, 46) Mafanizo aŵiliwa amatiphunzitsanso kuti tingaphunzile coonadi ca Ufumu m’njila zosiyanasiyana. Anthu ena amaphunzila coonadi pambuyo polalikilidwa koma ena amacita kufunafuna coonadi. Komabe, mosasamala kanthu kuti tinaphunzila bwanji coonadi, timakhala ofunitsitsa kudzimana zinthu zina kuti tiike Ufumu patsogolo pa moyo wathu.