Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 9

Zotsatilapo za Nchito Yolalikila—“M’Mindamo, Mwayela Kale ndipo m’Mofunika Kukolola”

Zotsatilapo za Nchito Yolalikila—“M’Mindamo, Mwayela Kale ndipo m’Mofunika Kukolola”

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Yehova wakulitsa mbeu za coonadi ca Ufumu

1, 2. (a) Ncifukwa ciani ophunzila a Yesu anadabwa? (b) Nanga ndi kukolola kotani kumene Yesu anali kunena?

OPHUNZILA a Yesu anadabwa kwambili pamene iye anawauza kuti: “Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayela kale ndipo m’mofunika kukolola.” Iwo anadabwa conco cifukwa cakuti pamene anayang’ana minda imene Yesu anali kuloza, mindayo sinali yoyela koma yobiliŵila cifukwa balele anali atangomela kumene. Mosakaikila io anayamba kuganizila kuti, ‘Kodi tiyenela kukolola ciani, cifukwa pakali miyezi yambili kuti nchito yokolola iyambe?’—Yoh. 4:35.

2 Komabe Yesu sanali kutanthauza kukolola mbeu zenizeni. Panthawiyi, iye anali kuphunzitsa ophunzila ake mfundo ziŵili zofunika kwambili zokhudza kukolola kwa kuuzimu, ndipo zinthu zimene anafunika kukolola ndi anthu. Kodi ndi mfundo ziŵili ziti zimenezo? Kuti tidziŵe bwino mfundozo, tiyeni tipende nkhaniyi mwatsatanetsatane.

Analimbikitsidwa Kugwila Nchito Mwakhama, Ndipo Analonjezedwa Kuti Adzakhala ndi Cimwemwe

3. (a) N’ciani cimene ciyenela kuti cinapangitsa Yesu kunena mau akuti: “M’mindamo, mwayela kale ndipo m’mofunika kukolola”? (Onani mau amunsi.) (b) Kodi Yesu anamveketsa motani mfundo ya zimene ananena?

3 Yesu anauza otsatila ake mau a pa Yohane 4:35 mu 30 C.E., pafupi ndi mzinda wa Sukari ku Samariya. Pamene otsatila a Yesu analoŵa mumzinda umenewu, Yesu anatsala pacitsime. Ali pacitsimepo, iye anayamba kuuza mai winawake coonadi cakuuzimu, ndipo maiyo anazindikila kufunika kwa zimene Yesu anali kumuphunzitsa. Pamene otsatila a Yesu anabwelela kwa iye, mzimai uja anathamanga kupita ku Sukari kuti akauze anansi ake za zinthu zodabwitsa zimene iye anaphunzila. Atamva zimene mzimai ameneyu anakamba, anthu a ku Sukari anadabwa, ndipo ambili a io anathamanga kupita ku citsime kumene kunali Yesu. N’kutheka kuti Yesu ataona gulu la anthu a ku Samariya akubwela capatali m’minda, m’pamene iye anati: ‘Onani m’mindamo, mwayela kale, ndipo m’mofunika kukolola.’ * Koma kuti amveketse bwino kuti anali kutanthauza kukolola kwa kuuzimu osati kukolola kwenikweni, Yesu anakambanso kuti: “Wokolola . . . akusonkhanitsa zipatso ku moyo wosatha.”—Yoh. 4:5-30, 36.

4. (a) Ndi mfundo ziŵili ziti zokhudza nchito yokolola zimene Yesu anaphunzitsa? (b) Ndi mafunso otani amene tidzakambilana?

4 Kodi pamenepa Yesu anali kuphunzitsa zinthu zofunika ziŵili ziti zokhuza kukolola kwa kuuzimu? Coyamba, iye anasonyeza kuti nchitoyo ifunika kugwilidwa mwamsanga. Yesu anasonyeza zimenezi pamene anakamba kuti, “m’mindamo mwayela kale ndipo m’mofunika kukolola.” Mau amenewa analimbikitsa otsatila ake kulalikila. Pofuna kuonetsa ophunzila ake kuti nchitoyi ifunika kugwilidwa mwacangu, Yesu anaonjezela kuti, “wokolola akulandila kale malipilo.” Inde, nchitoyo inali itayamba kale, ndipo panalibe cifukwa cocedwela. Caciŵili n’cakuti anchito ndi osangalala. Yesu anakamba kuti wofesa mbeu ndiponso wokolola ‘adzasangalalila pamodzi.’ (Yoh. 4:35b, 36) Pamene Yesu anaona ‘Asamariya ambili . . . akukhulupilila mwa iye,’ iye ayenela kuti anasangalala kwambili. Naonso ophunzila ake anafunika kusangalala kwambili pogwila nchito yokolola ndi moyo wao wonse. (Yoh. 4:39-42) Tikuphunzilapo mfundo yofunika kwambili pa zimene zinacitika m’nthawi ya atumwi cifukwa cakuti zinali kucitila cithunzi kukolola kwa kuuzimu kumene kukucitika masiku ano. Kodi kukolola kwa kuuzimu kumeneku kunayamba liti? Kodi ndani amene akucita nchito imeneyi? Nanga zotulukapo zake zakhala zotani?

Mfumu Yathu Ikutsogolela Panchito Yokolola Imene Ikugwilidwa Kwambili Masiku Ano

5. Ndani amene akutsogolela panchito yokolola padziko lapansi? Nanga masomphenya amene mtumwi Yohane anaona amaonetsa bwanji kuti nchitoyi iyenela kucitika mwamsanga?

5 Masomphenya amene mtumwi Yohane anaona, amasonyeza kuti Yehova anapatsa Yesu udindo wotsogolela panchito yokolola anthu padziko lonse lapansi. (Ŵelengani Chivumbulutso 14:14-16.) Masomphenya amenewa, akusonyeza Yesu atavala cisoti cacifumu, ndipo wanyamula cikwakwa m’dzanja lake. “Cisoti cacifumu cagolide” cimene Yesu wavala kumutu kwake, cimatsimikizila mfundo yakuti Yesu akulamulila monga Mfumu. “Cikwakwa cakuthwa cili m’dzanja lake” cikuonetsa udindo umene iye ali nawo monga Wokolola. Yehova kupyolela mwa mngelo anagogomezela mfundo yakuti nchito imeneyi iyenela kugwilidwa mwamsanga pamene anati: “Zokolola za padziko lapansi zapsa bwino.” Ndithudi, “ola la kumweta lafika,” ndipo sitifunikila kucedwa. Momvela lamulo la Mulungu lakuti “tsitsa cikwakwa cako,” Yesu anatsitsila cikwakwa cake kudziko lapansi mwamphamvu, ndipo akumweta dziko lapansi, kutanthauza kumweta anthu a padziko lapansi. Masomphenya ocititsa cidwi amenewa akutikumbutsanso kuti “m’mindamo, mwayela kale ndipo m’mofunika kukolola.” Kodi masomphenyawa akutithandiza kudziŵa nthawi pamene nchito yokolola anthu padziko lapansi inayamba? Inde akutelo.

6. (a) Kodi ‘nyengo yokolola’ inayamba liti? (b) Nanga nchito ‘yokolola za padziko lapansi’ inayamba liti? Fotokozani.

6 Popeza kuti masomphenya a pa Chivumbulutso caputala 14 amene Yohane anaona, amaonetsa Yesu, amene ndi Wokolola, atavala cisoti cacifumu (vesi 14), iye anali atakhala kale Mfumu mu 1914 pamene anali kugwila nchito yokolola. (Dan. 7:13, 14) Pambuyo poikidwa kukhala Mfumu, Yesu analamulidwa kuyamba nchito yokolola (vesi 15). Zocitikazi, zinafotokozedwanso m’fanizo la Yesu lokhudza kukolola tiligu, ndipo iye anati: “Nthawi yokolola ikuimila mapeto a nthawi ino.” Motelo, nyengo yokolola ndiponso mapeto a nthawi ino, zonse ziŵili zinayamba m’caka ca 1914. Koma nchito yeniyeni yokolola tiligu inayamba mkati mwa ‘nyengo yokolola.’ (Mat. 13:30, 39) Tikakumbukila bwino zinthu zimene zinacitika m’mbuyomu, timadziŵa kuti nchito yokolola inayamba pambuyo pa zaka zingapo Yesu atayamba kulamulila monga Mfumu. Coyamba, Yesu anayamba nchito yoyeletsa pakati pa otsatila ake odzozedwa kucokela mu 1914 mpaka kuciyambi kwa 1919. (Mal. 3:1-3; 1 Pet. 4:17) Ndiyeno mu 1919, nchito ‘yokolola za padziko lapansi’ inayamba. Mosataya nthawi, Yesu anagwilitsila nchito kapolo wokhulupilika amene anali ataikidwa kumene kuti athandize abale athu kuona kuti nchito yolalikila iyenela kucitika mofulumila kwambili. Taonani zimene zinacitika.

7. (a) Kodi abale athu anaphunzila mfundo iti imene inawathandiza kuona kufunika kogwila nchito yolalikila mwacangu? (b) Kodi abale athu analimbikitsidwa kucita ciani?

7 Magazini ina ya The Watch Tower ya mu 1920 inati: “Pambuyo pophunzila Malemba, n’zoonekelatu kuti chalichi capatsidwa mwai wofalitsa uthenga wokhudza ufumu.” Mwacitsanzo, ulosi wa Yesaya unathandiza abale kudziŵa kuti uthenga wa Ufumu uyenela kulengezedwa padziko lonse lapansi. (Yes. 49:6; 52:7; 61:1-3) Iwo sanadziŵe kuti adzakwanitsa bwanji kucita nchito imeneyo, koma anali ndi cikhulupililo cakuti Yehova adzawathandiza. (Ŵelengani Yesaya 59:1.) Pamene mfundo yakuti nchito yolalikila iyenela kucitika mwamsanga inamveketsedwa bwino, abale analimbikitsidwa kuti azigwila nchito yolalikila mwakhama. Kodi io analabadila bwanji cilimbikitso cimene anapatsidwa?

8. Ndi mfundo ziŵili ziti zimene abale athu anamvetsetsa mu 1921 zokhudza nchito yolallikila?

8 Mu December 1921, magazini ya The Watch Tower inalengeza kuti: “Caka cino ca 1921 cakhala caka cabwino kwambili kuposa zaka zonse. Ciŵelengelo ca anthu amene amvetsela uthenga wa coonadi, cakwela kwambili kuposa zaka zina m’mbuyomu.” Magaziniyo inaonjezela kuti: “Koma pali nchito yoculuka imene tiyenela kucita. . . . Tiyeni tigwile nchitoyi ndi mtima wacimwemwe.” Onani kuti pamenepa abale anazindikila mfundo ziŵili zofunika zokhudza nchito yolalikila zimene Yesu anauza atumwi ake. Mfundozo n’zakuti, nchitoyi ifunika kugwilidwa mwamsanga, ndi yakuti anchitowo ndi osangalala.

9. (a) Kodi Nsanja ya Olonda ina ya mu 1954 inafotokoza mfundo yotani yokhudza nchito yokolola? Nanga n’cifukwa ciani? (b) Kodi ciŵelengelo ca ofalitsa caculuka motani pa zaka 50 zapitazo? (Onani chati ca mutu wakuti “Ciŵelengelo ca Ofalitsa Padziko Lonse Cikuculukilaculukila.”)

9 Mkati mwa zaka za m’ma 1930, pamene abale anadziŵa kuti khamu lalikulu la nkhosa zina lidzalabadila uthenga wa Ufumu, nchito yolalikila inakula kwambili. (Yes. 55:5; Yoh. 10:16; Chiv. 7:9) Kodi zotulukapo zake zinakhala zotani? Ciŵelengelo ca anthu olalikila uthenga wa Ufumu cinakwela kucoka pa 41,000 mu 1934 kufika pa 500,000 mu 1953. Nsanja ya Olonda ya December 1, 1954 inafotokoza bwino kuti: “Nchito yaikulu yokolola ya padziko lonse yatheka cifukwa ca mzimu wa Yehova ndiponso mphamvu ya Mau ake.” *Zek. 4:6.

CIŴELENGELO CA OFALITSA PADZIKO LONSE CIKUCULUKILACULUKILA

Dziko

1962

1987

2013

Australia

15,927

46,170

66,023

Brazil

26,390

216,216

756,455

France

18,452

96,954

124,029

Italy

6,929

149,870

247,251

Japan

2,491

120,722

217,154

Mexico

27,054

222,168

772,628

Nigeria

33,956

133,899

344,342

Philippines

36,829

101,735

181,236

U.S. of America

289,135

780,676

1,203,642

Zambia

30,129

67,144

162,370

 

CIŴELENGELO CA MAPHUNZILO A BAIBULO CIKUCULUKA

1950

234,952

1960

646,108

1970

1,146,378

1980

1,371,584

1990

3,624,091

2000

4,766,631

2010

8,058,359

Zotsatilapo za Nchito Yokolola Zinanenedwelatu m’Mafanizo Omveka Bwino

10, 11. M’fanizo la kanjele kampilu, ndi mbali ziti zokhudza kukula kwa kanjeleko zimene zikuonetsedwa bwino kwambili?

10 M’mafanizo ake onena za Ufumu, Yesu ananenelatu momveka bwino zotsatilapo za nchito yokolola. Tiyeni tikambilane fanizo la kanjele kampilu ndi fanizo la zofufumitsa. Tidzakambilana makamaka mmene maulosi aŵiliwa akukwanilitsidwila m’nthawi ino yamapeto.

11 Fanizo la kanjele kampilu. Fanizoli limanena za munthu amene anabyala kanjele kampilu. Kanjeleko kanakula n’kukhala mtengo waukulu cakuti mbalame zinali kupeza malo okhalamo. (Ŵelengani Mateyu 13:31, 32.) Ndi mbali ziti za m’fanizoli zimene zikuonetsedwa bwino kwambili? (1) Kukula kocititsa cidwi. “Kanjele . . . kakang’ono kwambili mwa njele zonse” kanakula ndi kukhala mtengo wa “nthambi zikuluzikulu.” (Maliko 4:31, 32) (2) Kukula kotsimikizika. Yesu anakamba kuti kanjele kampilu “akakafesa kamamela ndi kukula.” Iye sanakambe kuti “kangakule.” M’malo mwake anakamba kuti ‘kamakula.’ Ndithudi, palibe amene angaimitse kukula kwake. (3) Zinthu zina za moyo zimapeza malo okhala mumtengo waukuluwo. “Mbalame zam’mlengalenga zimatha kupeza malo okhala mumthunzi wake.” Kodi mbali zitatu zimenezi zikugwilizana bwanji ndi kukolola kwa kuuzimu kumene kukucitika masiku ano?

12. Kodi fanizo la kanjele kampilu limakhudza bwanji nchito yokolola masiku ano? (Onani chati ca mutu wakuti “ Ciŵelengelo ca Maphunzilo a Baibulo Cikuculuka.”)

12 (1) Kukula kocititsa cidwi: Fanizoli limasonyeza kukula kocititsa cidwi kwa uthenga wa Ufumu ndi mpingo wacikristu. Kuyambila mu 1919, anchito acangu akhala akusonkhanitsidwa mumpingo wacikristu wokonzedwanso. Panthawiyo, ciŵelengelo ca anchito cinali cocepa kwambili, koma pambuyo pake cinayamba kukula mofulumila. Ndipo kukula kwake kwakhaladi kodabwitsa kucokela kuciyambi kwa zaka za m’ma 1900 mpaka masiku ano. (Yes. 60:22) (2) Kukula kwake ndi kotsimikizilika: Palibe munthu amene angaimitse kukula kwa mpingo wacikristu. Mosasamala kanthu za zitsutso zambili zimene adani a Mulungu amabweletsa, mpingo wacikristu umene uli ngati kanjele ukupitilizabe kukula. (Yes. 54:17) (3) Malo okhala: “Mbalame zam’mlengalenga” zimene zapeza malo okhala mumtengowo, zikuimila anthu mamiliyoni ambili amene alabadila uthenga wa Ufumu ndi kukhala mbali ya mpingo wacikristu. Anthu amenewo ndi ocokela m’maiko pafupifupi 240. (Ezek. 17:23) Anthuwa amalandila cakudya cakuuzimu, citsitsimulo, ndi citetezo mumpingo umenewu.—Yes. 32:1, 2; 54:13.

Fanizo la kanjele kampilu limasonyeza kuti anthu amene ali mumpingo wacikristu amakhala m’malo abwino ndi otetezeka. (Onani ndime 11 ndi 12)

13. Ndi mbali ziti zokhudza kukula zimene zikusonyezedwa bwino m’fanizo la zofufumitsa?

13 Fanizo la zofufumitsa. Mkazi wa m’fanizo limeneli anasakaniza zofufumitsa ku ufa wake, ndipo pambuyo pake zofufumitsazo zinafufumitsa mtanda wonse. (Ŵelengani Mateyu 13:33.) Ndi mbali ziti za m’fanizoli zimene zikuonetsedwa bwino kwambili? Tiyeni tikambilane mbali ziŵili. (1) Kufufuma kunacititsa kuti mtanda wa ufa usinthe. Zofufumitsa zinafalikila, “ndipo mtanda wonsewo unafufuma.” (2)  Kufufuma kunafalikila paliponse. Zofufumitsa zimenezo zinafufumitsa mtanda wonsewo, “wokwana mbale zitatu zazikulu zoyezela.” Kodi mbali ziŵili zimenezi zikugwilizana bwanji ndi kukolola kwa kuuzimu kumene kukucitika masiku ano?

14. Kodi fanizo la zofufumitsa limagwilizana bwanji ndi nchito yokolola imene ikucitika masiku ano?

14 (1) Kusintha: Zofufumitsa zimaimila uthenga wa Ufumu, ndipo mtanda wa ufa umaimila mtundu wa anthu. Pamene mkazi wa m’fanizo anasakaniza zofufumitsa ndi ufa, zofufumitsazo zinasintha muyezo wa ufa uja. Naonso uthenga wa Ufumu umasintha kapena kuti kusanduliza mitima ya anthu akaulandila. (Aroma 12:2) (2) Kunafalikila paliponse: Kufalikila kwa zofufumitsa kumaimila kufalikila kwa uthenga wa Ufumu. Zofufumitsa zimaloŵelela mkati mwa mtanda wa ufa mpaka zitafalikila konse. Mofananamo, uthenga wa Ufumu wafalikila “mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Mbali ya fanizo imeneyi ikusonyezanso kuti uthenga wa Ufumu udzafalikila kumaiko kumene nchito yathu ndi yoletsedwa, ngakhale kuti nthawi zambili kumaikowa anthu samazindikila kuti tikulalikila uthenga wa Ufumu.

15. Kodi lemba la Yesaya 60:5, 22, lakwanilitsidwa bwanji masiku ano? (Muonenso bokosi la mutu wakuti “ Zinatheka Cifukwa ca Yehova,” patsamba 93 ndi lakuti “ Kodi ‘Wamng’ono’ Wasanduka ‘Mtundu Wamphamvu’ Motani?” patsamba 96-97.)

15 Zaka pafupifupi 800 Yesu asanakambe mafanizo amenewa, Yehova ananenelatu momveka bwino kupyolela mwa Yesaya za nchito yokolola mwa kuuzimu imeneyi ndiponso za cisangalalo cimene cidzakhalapo cifukwa ca nchitoyi. * Yehova anafotokoza mmene anthu ‘ocokela kutali’ adzabwelela ku gulu lake. Pamene anali kulankhula ndi “mkazi” amene masiku ano amaimila otsalila odzozedwa, iye anati: “Nkhope yako idzasangalala ukadzaona zimenezi. Mtima wako udzanthunthumila ndi kufutukuka, cifukwa cuma ca m’nyanja cidzabwela kwa iwe. Katundu wa mitundu ya anthu adzabwela kwa iwe.” (Yes. 60:1, 4, 5, 9) Mau amenewo akhaladi oona. Masiku ano anthu amene atumikila Yehova kwa nthawi yaitali, amakhala ndi cimwemwe cacikulu akaona mmene ciŵelengelo ca ofalitsa Ufumu m’maiko amene akukhala cikukulila. Poyamba panali ofalitsa ocepa koma panopa pali masauzande ambili.

Cifukwa Cake Atumiki a Yehova Ayenela Kukhala Osangalala

16, 17. Ndi cifukwa cimodzi citi cimene cimapangitsa kuti “wofesa mbewu ndi wokolola asangalalile pamodzi”? (Onani bokosi la mutu wakuti “ Mmene Tumapepala twa Uthenga Tuŵili Tunakhudzila Anthu Aŵili ku Amazon.”)

16 Yesu anauza atumwi ake mau akuti: “Wokolola . . . akusonkhanitsa zipatso ku moyo wosatha, kuti wofesa mbewu ndi wokolola asangalalile pamodzi.” (Yoh. 4:36) Kodi ‘timasangalalila pamodzi’ m’njila yotani pogwila nchito yokolola padziko lapansi? Timasangalala pa zifukwa zingapo. Koma tiyeni tikambilane zitatu zokha.

17 Coyamba, timasangalala tikaona mmene Yehova amatithandizila pa nchitoyi. Timabyala mbeu za coonadi tikamalalikila uthenga wa Ufumu. (Mat. 13:18, 19) Tikathandiza munthu wina kukhala wophunzila wa Kristu, ndiye kuti takolola cipatso. Koma ife tonse timakhala ndi cimwemwe tikaona mmene Yehova wapangitsila mbeu za Ufumu ‘kumela ndi kukula.’ (Maliko 4:27, 28) Mbeu zina zimene timamwaza zimamela pakapita nthawi, ndipo anthu ena ndi amene amazikolola. Mlongo wina wa ku Britain wochedwa Joan amene anabatizidwa zaka 60 zapitazo, anamwazapo mbeu mwa njila imeneyi, ndipo mwina inunso zimenezi zinakucitikilaponi. Iye anati: “Ndakumanapo ndi anthu ena amene andiuzapo kuti pamene ndinawalalikila zaka zambili zapitazo, ndinabyala mbeu m’mitima yao. Ndipo m’kupita kwa nthawi a Mboni ena anaphunzila nao Baibulo ndi kuwathandiza kukhala atumiki a Yehova. Ndimasangalala ndikaona kuti mbeu imene ndinabyala inakula ndi kukololedwa.”—Ŵelengani 1 Akorinto 3:6, 7.

18. Kodi lemba la 1 Akorinto 3:8, limachula cifukwa citi cokhalila wacimwemwe?

18 Caciŵili, timakhalanso anchito acimwemwe tikamakumbukila zimene Paulo anakamba. Iye anati: “Aliyense payekha adzalandila mphoto yake mogwilizana ndi nchito yake.” (1 Akor. 3:8) Mphoto imapelekedwa cifukwa ca nchito imene timagwila, osati cifukwa ca zotulukapo za nchitoyo. Mfundo imeneyi ndi yolimbikitsa kwambili makamaka kwa amene amalalikila m’magawo ouma. Mulungu amaona kuti Mboni iliyonse imene imatengako mbali pogwila nchito yobyala mbeu za coonadi, ‘imabala zipatso zambili.’ Pa cifukwa cimeneci Mboni iliyonse iyenela kukhala yosangalala.—Yoh. 15:8; Mat. 13:23.

19. (a) Kodi ulosi wa Yesu wopezeka pa Mateyu 24:14 umatithandiza bwanji kukhala acimwemwe? (b) N’ciani cimene tiyenela kukumbukila ngakhale tilephele kupanga ophunzila?

19 Cacitatu, timasangalalanso cifukwa nchito yathu imakwanilitsa ulosi. Taganizilani yankho limene Yesu anapeleka kwa atumwi ake pamene anam’funsa kuti: “Kodi . . . cizindikilo ca kukhalapo kwanu ndi ca mapeto a nthawi ino cidzakhala ciani?” Iye anawayankha kuti mbali imodzi ya cizindikilo cimeneco idzakhala nchito yolalikila padziko lonse lapansi. Kodi Yesu anali kutanthauza nchito yopanga ophunzila? Iyai. Iye anati: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.” (Mat. 24:3, 14) Motelo, nchito yolalikila za Ufumu kapena kuti yobyala mbeu, ndi mbali ya cizindikilo cimeneci. Conco, ngakhale tilephele kupanga wophunzila polalikila uthenga wabwino wa Ufumu, timadziŵa kuti takwanitsa kupeleka “umboni.” * Kunena zoona, kaya anthu amve kapena asamve uthenga umenewu, timakhala kuti tatenga nao mbali pokwanilitsa ulosi wa Yesu, ndiponso timakhala ndi mwai wotumikila monga “anchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:9) Cimeneci n’cifukwa cabwino cokhalila osangalala.

“Kucokela Kotulukila Dzuŵa Kukafika Kumene Limaloŵela”

20, 21. (a) Kodi lemba la Malaki 1:11 likukwanilitsidwa bwanji? (b) N’ciani cimene mwatsimikiza mtima kucita cokhudza nchito yokolola? Nanga n’cifukwa ciani?

20 M’nthawi za atumwi, Yesu anathandiza atumwi ake kuona kuti nchito yokolola iyenela kucitika mwamsanga. Kuyambila mu 1919, Yesu wakhalanso akuthandiza ophunzila ake a masiku ano kuzindikila mfundoyo. Kaamba ka cimeneci, anthu a Mulungu akhala akugwila nchito zao mwakhama. Kunena zoona, palibe amene akwanitsa kuimitsa nchito yokolola. Mogwilizana ndi ulosi wa Malaki, masiku ano nchito yolalikila ikugwilidwa “kucokela kotulukila dzuŵa kukafika kumene limaloŵela.” (Mal. 1:11) Inde, kuyambila m’maŵa mpaka madzulo, kucokela kum’maŵa mpaka kumadzulo, kulikonse kumene kuli atumiki a Mulungu padziko lapansi, okolola ndi obyala akusangalalila pamodzi. Kuyambila pamene dzuŵa likutuluka mpaka pamene likuloŵa, m’mamaŵa mpaka madzulo, tsiku lonse lathunthu, timagwila nchito mwacangu.

21 Tikayang’ana m’mbuyo zaka 100 zapitazo, ndikuona mmene kagulu kakang’ono ka atumiki a Mulungu kakhalila “mtundu wamphamvu,” mitima yathu ‘imanthunthumila ndi kufutukuka’ ndi cimwemwe. (Yes. 60:5, 22) Motelo, tiyeni tilole cimwemwe cimeneco ndi cikondi cathu pa Yehova, amene ndi “Mwini zokololazo,” kulimbikitsa aliyense wa ife kugwila nao nchito yokolola imene ikugwilidwa kwambili masiku ano. Nchitoyi yatsala pang’ono kutha.—Luka 10:2.

^ par. 3 Yesu ananena mau akuti ‘minda yayela kale,’ mwina ataona mikanjo yoyela imene gulu la a Samariya anavala. Gulu limenelo linali kubwela kwa iye.

^ par. 9 Kuti mudziŵe zambili ponena za zimene zinacitika pa zakazo ndiponso zaka zina zambili pambuyo pake, tikukulimbikitsani kuŵelenga buku lacingelezi lakuti Jehovah’s WitnessesProclaimers of God’s Kingdom, patsamba 425 mpaka 520. Bukuli limalongosola zimene nchito yokolola inakwanilitsa kuyambila mu 1919 mpaka mu 1992.

^ par. 15 Kuti mudziŵe zambili za ulosi wosangalatsa kwambili umenewu, onani buku lakuti, Ulosi wa Yesaya—Muuni wa anthu onse. Gawo 2 patsamba 303 mpaka 320.

^ par. 19 Ophunzila Baibulo anali kudziŵa kale coonadi cofunika kwambili cimeneci. Magazini ya Zion’s Watch Tower ya November 15, 1895, inati: “Ngakhale kuti tingasonkhanitse tiligu wocepa, umboni woculuka ndi wamphamvu umakhala kuti wapelekedwa. . . . Anthu onse angalalikile uthenga wabwino.”