Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 7

Njila Zolalikilila—Kugwilitsila Nchito Njila Zosiyanasiyana Polalikila Anthu

Njila Zolalikilila—Kugwilitsila Nchito Njila Zosiyanasiyana Polalikila Anthu

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Anthu a Mulungu amagwilitsila nchito njila zosiyanasiyana zolalikilila kuti alalikile anthu ambili

1, 2. (a) N’ciani cimene Yesu anacita kuti alankhule momveka bwino ku khamu la anthu? (b) Kodi ophunzila okhulupilika a Kristu atsatila bwanji citsanzo cake? Ndipo n’cifukwa ciani?

PAMENE Yesu anali m’mphepete mwa Nyanja, khamu la anthu linasonkhana kwa iye, koma iye anakwela bwato ndi kuliyendetsa patali pang’ono. N’cifukwa ciani anacita zimenezo? Cifukwa cakuti iye anadziŵa kuti madzi adzathandiza kuti mau ake amveke patali n’colinga cakuti khamu la anthulo limvetsele uthenga wake mosavuta.—Ŵelengani Maliko 4:1, 2.

2 Kwa zaka zambili Ufumu wa Mulungu usanakhazikitsidwe ndiponso utakhazikitsidwa, ophunzila okhulupilika a Kristu anatengela citsanzo cake mwa kugwilitsila nchito njila zatsopano zolalikilila uthenga wabwino wa Ufumu kwa anthu ambili. Motsogoleledwa ndi Mfumu Mesiya, anthu a Mulungu akuzindikila njila zatsopano zolalikilila malinga ndi kusintha kwa zinthu ndiponso kupita patsogolo kwa sayansi ya zopangapanga. Colinga cathu ndi kulalikila anthu ambili mmene tingathele mapeto asanafike. (Mat. 24:14) Tiyeni tione njila zina zimene takhala tikugwilitsila nchito pofuna kulalikila anthu kulikonse kumene angapezeke. Ndiyeno ganizilani mmene mungatsanzilile cikhulupililo ca Akristu amene anali kulalikila uthenga wabwino m’nthawi ya Ophunzila Baibulo.

Kulalikila Anthu Ambili

3. Kodi adani a coonadi anakhumudwa bwanji pamene tinayamba kugwilitsila nchito manyuzipepala polalikila?

3 Manyuzipepala: M’bale Russell ndi anzake anali kufalitsa magazini ya The Watch Tower kuyambila mu 1879 kuti afalitse uthenga wa Ufumu kwa anthu ambili. Koma ca m’ma 1903, Kristu anawathandiza kupeza njila zolalikilila uthenga wabwino kwa anthu ambili. Kuyambila m’caka cimeneco, abale anayamba kugwilitsila nchito njila zatsopano zolalikilila. M’cakaco, Dr. E. L. Eaton, amene anali wolankhulila gulu la Abusa Aciprotestanti ku Pennsylvania, anayamba kutsutsa ziphunzitso za m’Baibulo zimene M’bale Charles Taze Russell anali kuphunzitsa. Eaton analembela kalata M’bale Russell kuti: “Ndikuganiza kuti anthu ambili angasangalale . . . kumvetsela pamene iwe ndi ine tikutsutsana poyela pa nkhani zimene timasiyana maganizo.” M’bale Russell ndi anzake naonso anaganiza kuti anthu ambili adzasangalala kumvetsela nkhani zotsutsanazo. Conco anakonza zakuti nkhanizo zizifalitsidwa m’nyuzipepala yochuka ya The Pittsburgh Gazette. Anthu ambili anayamba kukonda nkhanizo, ndipo anakopeka kwambili ndi mmene M’bale Russell anali kufotokozela mfundo za coonadi momveka bwino. Izi zinapangitsa kuti olemba nyuzipepalayi akonze zakuti azifalitsa nkhani za M’bale Russell mlungu uliwonse. Mwacionekele, zimenezi zinakhumudwitsa kwambili adani a coonadi.

Pofika mu 1914, manyuzipepala oposa 2,000 anali kufalitsa nkhani za M’bale Russell?

4, 5. Ndi khalidwe lotani limene M’bale Russell anaonetsa? Nanga anthu amene ali paudindo angamutsanzile bwanji?

4 Patapita nthawi yocepa, makampani ambili olemba manyuzipepala anayamba kulemba nkhani za M’bale Russell. Podzafika mu 1908, magazini ya The Watch Tower inafotokoza kuti nkhani zimenezo zinali kufalitsidwa “nthawi zonse m’manyuzipepala okwanila 11.” Komabe, abale odziŵa bwino mmene nyuzipepala imakopela anthu ambili anauza M’bale Russell kuti asamutse maofesi a Sosaite kucoka ku Pittsburgh kupita mumzinda wina wochuka. Iwo anati kucita zimenezo kudzathandiza kuti nyuzipepala zambili ziyambe kufalitsa nkhani zake za m’Baibulo. Pambuyo poganizila malangizo amenewa ndi mfundo zina, M’bale Russell anasamutsila maofesi a Sosaite ku Brooklyn, New York, m’caka ca 1909. Kodi zotsatilapo zake zinali zotani? Patangopita miyezi ingapo, manyuzipepala oposa 400 anayamba kufalitsa nkhani za M’bale Russell, ndipo makampani ena ambili olemba manyuzipepala anali kufuna kulembanso nkhanizo. Pamene Ufumu wa Mulungu unali kukhazikitsidwa mu 1914, manyuzipepala oposa 2,000 anali kufalitsa nkhanizo m’zinenelo zinai.

5 Kodi tikuphunzilapo ciani pa zimene zinacitikazo? Abale amene ali ndi udindo m’gulu la Mulungu masiku ano ayenela kutengela citsanzo ca M’bale Russell ca kudzicepetsa. Motani? Pamene akupanga zosankha zofunika kwambili, ayenela kumvela malangizo a anthu ena.—Ŵelengani Miyambo 15:22.

6. Kodi coonadi cofalitsidwa m’nyuzipepala cinakhudza bwanji munthu wina?

6 Mfundo za coonadi ca Ufumu zimene zinali kufalitsidwa m’manyuzipepala amenewo zinathandiza anthu ena kusintha miyoyo yao. (Aheb. 4:12) Mwacitsanzo, Ora Hetzel, amene anabatizidwa mu 1917, anali mmodzi mwa anthu amene anaphunzila coonadi cifukwa ca nkhani zimenezo. Iye anati: “Nditakwatiwa ndinapita kukaona amai ku Rochester, Minnesota. Nditafika ndinawapeza akuduladula tumapepala m’nyuzipepala. Tumapepalato tunali ndi nkhani zosiyanasiyana za M’bale Russell. Amai anandiuza zimene anali kuphunzila m’nkhanizo.” Ora anaphunzila coonadi, ndipo anakhala mlaliki wa Ufumu wa Mulungu wokhulupilika kwa zaka 60.

7. N’cifukwa ciani abale otsogolela gulu la Mulungu anaganiza zosiya kufalitsa uthenga wabwino mwa kugwilitsila nchito manyuzipepala?

7 Mu 1916, munacitika zinthu ziŵili zazikulu zimene zinapangitsa kuti abale amene anali kutsogolela gulu aganize zosiya kufalitsa uthenga wabwino mwa kugwilitsila nchito manyuzipepala. Coyamba, Nkhondo Yaikulu imene inali mkati panthawiyo inapangitsa kuti zikhale zovuta kupeza zipangizo zosindikizila manyuzipepala. Pofotokoza vuto limene linalipo mu 1916, dipatimenti yathu ya manyuzipepala ku Britain inati: “Panthawi ino, pali manyuzipepala oposa 30 cabe amene akufalitsa Nkhani zathu. N’zoonekelatu kuti ciŵelengelo cimeneci cidzacepa kwambili poganizila kuti mapepala akukwela mtengo.” Caciŵili cinali imfa ya M’bale Russell pa October 31, 1916. Magazini ya The Watch Tower yacingelezi ya December 15, 1916 inati: “Tsopano popeza kuti M’bale Russell wafa, tileka kufalitsa nkhani zake [za m’manyuzipepala].” Ngakhale kuti abale analeka kugwilitsila nchito njila imeneyi polalikila, io anayamba kugwilitsila nchito njila zina monga “Seŵelo la Pakanema la Cilengedwe.”

8. Ndi nchito yotani imene abale anagwila kuti apange “Seŵelo la Pakanema la Cilengedwe”?

8 Kugwilitsila nchito mafilimu. M’bale Russell ndi anzake anagwila nchito kwa zaka pafupifupi zitatu kuti apange “Seŵelo la Pakanema la Cilengedwe,” limene linatulutsidwa mu 1914. (Miy. 21:5) Seŵelo limeneli linapangidwa mwaluso pogwilitsila nchito mafilimu okhala ndi mau, zithunzithunzi zoyenda ndi zosayenda. Popanga seŵeloli, anthu mahandiledi ambili anayelekezela zocitika za m’Baibulo, ndipo anawajambula. M’seŵeloli anagwilitsilanso nchito nyama. Lipoti la mu 1913 linati: “Nyama zambili za m’nkhalango ina yaikulu yosungilako nyama zinagwilitsidwa nchito poyelekezela zimene zinacitika m’nthawi ya Nowa.” Akatswili ojambula zithunzithunzi a ku London, New York, Paris, ndi ku Philadelphia, ndi amene anakongoletsa zithunzithunzi mahandiledi ambili zosayenda za m’seŵeloli.

9. N’cifukwa ciani abale anataya nthawi yambili ndi cuma cambili kupanga “Seŵelo” limeneli?

9 N’cifukwa ciani abale anataya nthawi yambili ndi cuma cambili kupanga “Seŵelo” limeneli? Pa misonkhano yacigawo ya 1913 panali cigamulo cakuti: “Anthu olemba manyuzipepala a ku America akopa kwambili maganizo a anthu mwa kuika zithunzithunzi m’manyuzipepala ndi m’magazini ao. Iwo apanganso mafilimu amene anthu osiyanasiyana akuwakonda, ndipo mafilimuwo akhala ochuka kwambili. Zimenezi zikuonetsa kuti kugwilitsila nchito zithunzithunzi ndi njila yabwino yophunzitsila. Pacifukwa cimeneci, taona kuti ndi bwino kuti ife monga alaliki ndi aphunzitsi a Baibulo opita patsogolo, tizigwilitsila nchito kwambili mafilimu ndi zithunzithunzi zina polalikila.”

Pamwamba: Kanyumba kamene munali kukhala makina oonetsela “Seŵelo la Pakanema”; pansi:“Zithunzithunzi za “Seŵelo la Pakanema”

10. Kodi “Seŵelo la Pakanema” linaonetsedwa m’madela oculuka bwanji?

10 Mu 1914, “Seŵelo” limeneli linali kuonetsedwa m’mizinda 80 tsiku lililonse. Anthu pafupifupi 8 miliyoni ku United States ndi ku Canada anapenyelela seŵelo limeneli. M’caka cimodzimodzico, “Seŵelo” limeneli linaonetsedwanso ku Australia, Britain, Denmark, Finland, Germany, New Zealand, Norway, Sweden, ndi Switzerland. Abale anapanganso seŵelo la pakanema lacilengedwe la zithunzithunzi zosayenda lochedwa “Seŵelo la Eureka,” n’colinga cakuti azilionetsa m’matauni ang’onoang’ono. Seŵeloli linali losaonongetsa ndalama zambili polipanga ndi losavuta kutumiza ku madela ena. Pofika m’caka ca 1916, maseŵelo onse aŵili ochedwa “Seŵelo la Pakanema” ndi “Seŵelo la Eureka,” anamasulidwa mu Ciameniya, Cidano-Nowejani, Cifulenchi, Cijeremani, Cigiriki, Ciitaliyana, Cipolishi, Cisipanya, ndi Ciswidishi.

M’caka ca 1914, “Seŵelo la Pakanema” linaonetsedwa m’maholo odzaza ndi anthu

11, 12. N’ciani cimene mnyamata wina anacita atapenyelela “Seŵelo la Pakanema”? Nanga iye anapeleka citsanzo cotani?

11 “Seŵelo la Pakanema” la Cifulenchi linakhudza kwambili Charles Rohner amene anali ndi zaka 18. Iye anati: “Seŵeloli linaonetsedwa m’tauni yathu ya Colmar, m’cigawo ca Alsace, ku France. Nditangoyamba kulimvetsela, ndinacita cidwi ndi mfundo za coonadi za m’Baibulo zomveka bwino za m’seŵeloli.”

12 Zotsatilapo zake zinali zakuti Charles anabatizidwa, ndipo mu 1922 anayamba utumiki wa nthawi zonse. Nchito yoyamba imene iye anapatsidwa inali yoonetsa anthu “Seŵelo la Pakanema” ku France. Ponena za nchitoyi, Charles anati: “Ndinapatsidwa nchito zingapo. Ndinauzidwa kuimba vayolini, kukhala mtumiki wa maakaunti ndiponso wamabuku. Ndinauzidwanso kuthandiza anthu kukhala cete pulogalamu isanayambe. Panthawi yopuma, tinali kugaŵila zofalitsa. Abale ndi alongo ena anali kupatsidwa zigawo m’holo yoonetsela kanema kuti agaŵile zofalitsazo. Aliyense anali ndi zofalitsa zokwanila, ndipo anali kugaŵila munthu aliyense m’cigawo cake. Komanso pa khomo lililonse la holoyo panali matebulo odzaza ndi zofalitsa.” Mu 1925, Charles, anaitanidwa kuti akatumikile ku Beteli ya ku Brooklyn, ku New York. Kumeneko, iye anapatsidwa nchito yotsogolela gulu la oimba a pa wailesi yokhazikitsidwa kumene ya WBBR. Pambuyo pokambilana citsanzo ca M’bale Rohner cimeneci, tingacite bwino kuganizila kuti: ‘Kodi ndine wokonzeka kugwila nchito iliyonse imene ndapatsidwa n’colinga cakuti ndithandize pa nchito yofalitsa uthenga wa Ufumu?’—Ŵelengani Yesaya 6:8.

13, 14. Kodi abale anagwilitsila nchito bwanji mawailesi polalikila uthenga wabwino? (Onaninso kamutu kakuti “ Mapulogalamu a pa Wailesi ya WBBR,” ndi kakuti “ Msonkhano Wacigawo Wosaiwalika.”)

13 Kugwilitsila nchito wailesi. M’zaka za m’ma 1920, nchito yolalikila mwa kugwilitsila nchito “Seŵelo la Pakanema” inayamba kucepa. Komabe, abale anayamba kugwilitsila nchito wailesi monga njila yatsopano yofalitsila uthenga wabwino wa Ufumu kwa anthu ambili. Pa April 16, 1922, M’bale Rutherford anakamba nkhani pawailesi m’nyumba yocitilamo maseŵelo mu mzinda wa Philadelphia ku Pennsylvania kwa nthawi yoyamba. Anthu pafupifupi 50,000 anamvetsela nkhani ya mutu wakuti: “Anthu Mamiliyoni Ambili Amene Ali ndi Moyo Sadzafa.” Ndipo mu 1923, kwa nthawi yoyamba, mbali ina ya msonkhano wacigawo inaulutsidwa pawailesi. Kuonjezela pa kugwilitsila nchito mawailesi a anthu ena, abale otsogolela anaganiza kuti ndi bwino kuti Sosaite ikhale ndi nyumba ya wailesi. Nyumbayo inapangidwa pa cilumba ca Staten ku New York, ndipo inali kuchedwa WBBR. Wailesi imeneyi anayamba kuigwilitsila nchito pa February 24, 1924.

Mu 1922, anthu pafupifupi 50,000 anamvetsela nkhani pa wailesi imene inali ndi mutu wakuti “Anthu Mamiliyoni Ambili Amene Ali ndi Moyo Sadzafa”

14 Pofotokoza colinga ca wailesi ya WBBR, magazini ya The Watch Tower ya December 1, 1924, inati: “Tikukhulupilila kuti wailesi ndi njila yotsika mtengo kwambili ndiponso yothandiza kwambili polengeza uthenga wa coonadi kuposa njila zina zonse zimene tagwilitsilapo nchito m’mbuyomu.” Kenako inaonjezela kuti: “Ngati Ambuye akuona kuti ndi bwino kuti tikhazikitse mawailesi ena olengeza coonadi, adzatithandizanso kupeza ndalama m’njila imene akuona kuti ndi yoyenela.” (Sal. 127:1) Pofika caka ca 1926, atumiki a Yehova anali ndi nyumba za wailesi zokwanila 6. Aŵili mwa mawailesi amenewa anali ku United States m’mizinda ya New York ndi Chicago. Wailesi ya ku New York inali kuchedwa WBBR, ndipo ya ku Chicago inali kuchedwa WORD. Mawailesi ena anai anali ku Canada, m’mizinda ya Alberta, British Columbia, Ontario, ndi Saskatchewan.

15, 16. (a) N’ciani cimene atsogoleli acipembedzo ku Canada anacita cifukwa ca nchito yathu yolalikila pa wailesi? (b) Kodi kuulutsa nkhani pa wailesi kunathandiza bwanji kuti nchito yolalikila ku nyumba ndi nyumba iyende bwino?

15 Atsogoleli a Machalichi Acikristu anakhumudwa ndi nchito yofalitsa coonadi ca m’Baibulo imeneyi. M’bale Albert Hoffman, amene anali kudziŵa bwino nchito imene inali kucitika pa nyumba ya wailesi ya ku Saskatchewan, m’dziko la Canada, anati: “Ophunzila Baibulo [dzina la Mboni za Yehova panthawiyo] anayamba kudziŵika kwa anthu ambili. Nchito yofalitsa uthenga wabwino inali kuyenda bwino mpaka mu 1928, pamene atsogoleli a cipembedzo anakakamiza akuluakulu a boma kuti aletse nchitoyi, ndipo mawailesi onse a Ophunzila Baibulo ku Canada anatsekedwa.”

16 Ngakhale kuti mawailesi athu anatsekedwa ku Canada, abale anapitilizabe kuulutsa nkhani za m’Baibulo pa mawailesi a anthu ena. (Mat. 10:23) Kuti nchito yofalitsa uthenga wabwino ithandize anthu ambili, m’magazini ya The Watch Tower ndi The Golden Age [imene tsopano imachedwa Galamukani!] munali kupezeka m’ndandanda wa maina a mawailesi amene anali kuulutsa nkhani za m’Baibulo. Zimenezi zinathandiza kuti ofalitsa amene akulalikila azitha kulimbikitsa anthu kumvetsela nkhanizi pa mawailesi m’madela ao. Kodi panali zotsatilapo zotani? Bulletin ya January 1931 inati: “Kufalitsa nkhani pa wailesi kwalimbikitsa kwambili abale kugwila nchito yolalikila ku nyumba ndi nyumba. Ku ofesi kwafika malipoti ambili onena kuti anthu akumvetsela nkhani za M’bale Rutherford, ndipo pambuyo pomvetsela, io akulandila mabuku amene akupatsidwa.”Bulletin imeneyo inanena kuti kugwilitsila nchito mawailesi ndiponso kulalikila ku nyumba ndi nyumba zinali “njila ziŵili zazikulu zolalikilila zimene gulu la Ambuye likugwilitsila nchito.”

17, 18. Ndi motani mmene mawailesi anathandizila pa nchito yolalikila ngakhale pamene zinthu zinayamba kuvuta?

17 M’zaka za m’ma 1930, anthu anayamba kutsutsanso nchito yathu yolalikila pa mawailesi a anthu ena. Conco, kumapeto kwa 1937, atumiki a Yehova anasintha njila zao zolalikilila. Iwo analeka kulalikila pa mawailesi, ndipo analimbikila kulalikila ku nyumba ndi nyumba. * Ngakhale zinali conco, mawailesi ena anathandiza kwambili pa nchito yofalitsa uthenga wa Ufumu m’madela akutali kapena madela ovuta kufikako cifukwa ca mavuto a zandale. Mwacitsanzo, kuyambila m’caka ca 1951 mpaka mu 1991, wailesi ina ku West Berlin, m’dziko la Germany, inali kuulutsa nkhani za m’Baibulo n’colinga cakuti anthu okhala ku East Germany amvetsele uthenga wa Ufumu. Kwa zaka zoposa 30 kuyambila m’caka ca 1961, wailesi ya boma m’dziko la Suriname, ku South America, inali kuulutsa pulogalamu ya mphindi 15 yolengeza coonadi ca m’Baibulo mlungu uliwonse. Kuyambila mu 1969 mpaka mu 1977, gulu la Mulungu linajambula nkhani zopitilila 350 za mutu wakuti “Malemba Onse Ndi Opindulitsa.” M’madela 48 a ku United States, mawailesi okwanila 291 anali kuulutsa nkhani zimenezo. Mu 1996, wailesi ina ku Apia, likulu la dziko la Samoa kum’mwela kwa nyanja ya Pacific, inali kuulutsa pulogalamu yakuti “Mayankho a Mafunso Anu a m’Baibulo” mlungu uliwonse.

18 Pofika cakumapeto kwa zaka za m’ma 1900, mawailesi sanali kugwilitsidwanso nchito kwambili pofalitsa uthenga wabwino. Koma pofuna kulalikila anthu ambili, gulu la Mulungu linayamba kugwilitsila nchito njila ina yamakono.

19, 20. N’cifukwa ciani atumiki a Yehova anakhazikitsa Webusaiti ya jw.org? Ndipo Webusaiti imeneyi yakhala yothandiza bwanji? (Kuti mudziŵe mfundo zina zokhudza “ JW.ORG,” onani pa tsamba 75.)

19 Kugwilitsila nchito Intaneti. Pofika m’caka ca 2013, anthu oposa 2.7 biliyoni anali kugwilitsila nchito Intaneti. Izi zikusonyeza kuti anthu pafupifupi 40 pa anthu 100 aliwonse pa dziko lapansi amagwilitsila nchito Intaneti. Malinga ndi kafukufuku wina, anthu pafupifupi 2 biliyoni amatsegula Intaneti mwa kugwilitsila nchito zipangizo monga mafoni ndi matabuleti. Ciŵelengeloci cikukulilakulila, ndipo cikukula mofulumila kwambili mu Africa, mmene anthu oposa 90 miliyoni amagwilitsila nchito Intaneti. Cotelo, Intaneti yakhala njila yaikulu imene anthu akulandilila uthenga.

20 Atumiki a Yehova anayamba kugwilitsila nchito Intaneti mu 1997. Mu 2013, Webu saiti ya jw.org inayamba kupezeka m’zinenelo pafupifupi 300, ndipo nkhani zina za m’Baibulo zimene munthu angatenge zinayamba kupezeka m’zinenelo zoposa 520. Tsiku lililonse, anthu pafupifupi 750,000 amagwilitsila nchito webusaiti imeneyi. Kuonjezela pa kupenyelela mavidiyo, mwezi uliwonse anthu amatenga mabuku 3 miliyoni, magazini 4 miliyoni, ndi 22 miliyoni nyimbo ndi zinthu zina zomvetsela pa webusaiti imeneyi.

21. N’ciani cimene mwaphunzila pa zimene zinacitikila Sina?

21 Webu saiti imeneyi yakhala njila yothandiza kwambili pofalitsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ngakhale m’madela amene nchito yathu ndi yoletsedwa. Mwacitsanzo, kuciyambi kwa 2013, munthu wina wochedwa Sina atagwilitsila nchito webusaiti ya jw.org, anatuma foni ku likulu lathu ku United States kuti adziŵe zambili za m’Baibulo. Zimenezi zinali zocititsa cidwi kwambili cifukwa cakuti Sina anabadwila m’banja la Cisilamu, ndipo amakhala m’mudzi wina wakutali m’dziko limene nchito ya Mboni za Yehova ndi yoletsedwa kwambili. Abale atalandila foniyo, anapanga makonzedwe akuti m’bale wina wa ku United States aziphunzila Baibulo ndi Sina kaŵili pa mlungu. Phunzilo limenelo linali kucitika mwa kugwilitsila nchito pulogalamu inayake ya pa Intaneti yokhala ndi vidiyo.

Kuphunzitsa anthu ku nyumba ndi nyumba

22, 23. (a) N’cifukwa ciani njila zolalikilila anthu ambili sizinaloŵe m’malo njila yolalikila ku nyumba ndi nyumba? (b) Kodi Mfumu yadalitsa bwanji khama lathu pa nchito yolalikila?

22 Njila zimene atumiki a Mulungu akhala akugwilitsila nchito monga manyuzipepala, “Seŵelo la Pakanema,” mawailesi ndi Intaneti kuti alalikile kwa anthu ambili sizinaloŵe m’malo njila yolalikila ku nyumba ndi nyumba. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti atumiki a Yehova amatengela citsanzo ca Yesu. Iye sanali kungolalikila makamu a anthu, koma nthawi zambili anali kuthandiza munthu aliyense payekhapayekha. (Luka 19:1-5) Yesu anaphunzitsanso ophunzila ake kulalikila kwa munthu aliyense payekhapayekha, ndipo anawauza uthenga umene anafunika kulengeza. (Ŵelengani Luka 10:1, 8-11.) Monga mmene Nkhani 6 inafotokozela, abale otsogolela gulu la Mulungu nthawi zonse akhala akulimbikitsa atumiki a Yehovakulalikila kwa munthu aliyense payekhapayekha.—Mac. 5:42; 20:20.

23 Tsopano patha zaka 100 kucokela pamene Ufumu wa Mulungu unabadwa, ndipo ofalitsa oposa 7.9 miliyoni akuphunzitsa ena zolinga za Mulungu mwakhama. N’zosakaikitsa kuti Mfumu Mesiya yakhala ikudalitsa njila zimene takhala tikugwilitsila nchito polengeza Ufumu wa Mulungu. Monga mmene tidzaonela m’nkhani yotsatila, Mfumuyi yatipatsanso zida zothandiza kuti tifalitse uthenga wabwino kudziko lililonse, fuko lililonse ndi cinenelo ciliconse.—Chiv. 14:6.

^ par. 17 Mu 1957, abale otsogolela gulu la Mulungu anatseka nyumba yathu ya wailesi yomaliza ya WBBR ku New York.