Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi mumalakalaka kuona malonjezo a Ufumu akukwanilitsidwa?

CIGAWO 7

Malonjezo a Ufumu—Kupanga Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano

Malonjezo a Ufumu—Kupanga Zinthu Zonse Kukhala Zatsopano

TAYELEKEZELANI kuti mwathyola apulo lalikulu lakupsa mu mtengo. Musanaliike m’basiketi mmene muli kale ma apulo ena ambili, mukuinunkhiza ndi kumva kafungo kake kokoma. Mwakhala mukugwila nchitoyi kwa maola ambili, koma simukutopa ndipo mukufuna kupitilizabe kugwila nchito imeneyi. Mukuona amai anu amene ali pamtengo wina umene uli capafupi. Iwo akugwila nchito yokolola mosangalala ndipo akuceza ndi anthu ena a m’banja lanu ndi anzanu amene akuwathandiza nchitoyo. Amai anu akuoneka acitsikana monga mmene anali kuonekela zaka zambili zapitazo pamene inu munali mwana. Zinali zomvetsa cisoni kuwaona akukalamba m’dziko lakale limene linapita tsopano. Munawaona akufooka cifukwa ca matenda. Mukukumbukila kuti munawagwila dzanja pamene anali kumwalila, ndipo munalila kwambili ku manda. Tsopano ndinu osangalala kuwaona kuti ali ndi moyo pamodzi ndi anthu ena ambili, ndipo ali ndi thanzi labwino.

Tili ndi cikhulupililo cakuti zotelezi zidzacitikadi. Zili conco cifukwa cakuti nthawi zonse malonjezo a Mulungu amakwanilitsidwa. M’cigawo cino, tikambilana za maulosi ena okhudza Ufumu amene adzakwanilitsidwa posacedwapa. Zimenezo ndi zimene zidzatsogolela ku nkhondo ya Aramagedo. Tidzakambilananso malonjezo ocititsa cidwi okhudza Ufumu amene adzakwanilitsidwa pambuyo pa Aramagedo. Tidzasangalala kwambili Ufumu wa Mulungu ukadzayamba kulamulila dziko lonse lapansi ndi kupanga zinthu zonse kukhala zatsopano.

M'CIGAWO CINO

NKHANI 21

Ufumu wa Mulungu Udzaononga Adani Ake

Muyenela kukonzekela tsopano kaamba ka nkhondo ya Aramagedo.

NKHANI 22

Ufumu Ukwanilitsa Cifunilo ca Mulungu Padziko Lapansi

Kodi mungatsimikize bwanji kuti zimene Yehova analonjeza zidzakwanilitsidwa?