NKHANI 21
Ufumu wa Mulungu Udzaononga Adani Ake
1, 2. (a) N’ciani cikuonetsa kuti Mfumu yathu yakhala ikulamulila kuyambila mu 1914? (b) Kodi tidzaphunzila ciani m’nkhani ino?
CIKHULUPILILO cathu calimba kwambili pambuyo pophunzila zimene Ufumu wa Mulungu wacita pakati pa adani ake. (Sal. 110:2) Mfumu yathu yakhazikitsa gulu la alaliki odzipeleka mwa kufuna kwao. Iyo yayeletsa ndi kuyenga otsatila ake mwa kuuzimu ndi mwamakhalidwe. Ndipo tikusangalala ndi mgwilizano wathu padziko lonse lapansi mosasamala kanthu kuti adani a Ufumu akhala akuyesetsa kutigawanitsa. Zinthu zimenezi ndiponso zina zambili zimene Ufumu wacita zomwe taphunzila m’buku lino, ndi umboni wosatsutsika wakuti Mfumu yathu yakhala ikulamulila pakati pa adani a Ufumu kuyambila mu 1914.
2 Ufumu wa Mulungu udzacita zinthu zina zambili zocititsa cidwi mtsogolomu. Ufumuwo ‘udzabwela’ ‘kudzaphwanya ndi kutha’ adani ake onse. (Mat. 6:10; Dan. 2:44) Koma nthawiyo isanafike, zinthu zina zapadela zidzacitika. Kodi zinthu zimenezo n’ziti? Pali maulosi ambili a m’Baibulo amene amayankha funso limeneli. Tiyeni tikambilane ena mwa maulosi amenewo kuti tidziŵe zinthu zimene zidzacitika mtsogolomu.
Zimene Zidzacitika “Ciwonongeko Codzidzimutsa” Cikadzatsala Pang’ono Kuyamba
3. N’ciani cidzayambilila kucitika pa zinthu zimene tikuyembekezela?
3 Kulengeza mtendele. Pamene mtumwi Paulo anali kulembela kalata abale a ku Tesolonika, iye anafotokoza za cocitika coyamba cimene tikuyembekezela. (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:2, 3) M’kalatayo, Paulo anachulamo za “tsiku la Yehova,” limene lidzayamba ndi kuukilidwa kwa “Babulo Wamkulu.” (Chiv. 17:5) Komabe, “tsiku la Yehova” likadzatsala pang’ono, mitundu idzayamba kulengeza kuti “Bata ndi mtendele!” Cilengezo cimeneco mwina cidzapelekedwa kamodzi kapena kangapo. Kodi atsogoleli azipembedzo adzatenga nao mbali polengeza zimenezi? Popeza kuti io ali mbali ya dziko, mosakaikila adzagwilizana ndi mitundu mwa kunena kuti, “Kuli mtendele!” (Yer. 6:14; 23:16, 17; Chiv. 17:1, 2) Cilengezo ca bata ndi mtendele cikadzapelekedwa, ndiye kuti tsiku la Yehova lili pafupi kuyamba. Adani a Ufumu wa Mulungu “sadzapulumuka.”
4. Kodi kudziŵa tanthauzo la ulosi wa Paulo wonena za bata ndi mtendele kuli ndi phindu lanji?
1 Ates. 5:3, 4) Mosiyana ndi anthu ambili, ife tikudziŵa tanthauzo la zimene zikucitika tsopano. Kodi ulosi wa bata ndi mtendele udzakwanilitsidwa bwanji? Panopa sitikudziŵa. Tiyenela kungoyembekezela kuti tidzaone zimene zidzacitika. Motelo, tiyeni “tikhalebe maso ndipo tikhalebe oganiza bwino.”—1 Ates. 5:6; Zef. 3:8.
4 Kodi kudziŵa tanthauzo la ulosi umenewu kuli ndi phindu lanji? Paulo anati: “Simuli mu mdima ayi, kuti tsiku limenelo lidzakudzidzimutseni ngati mmene lingacitile kwa mbala.” (Kuyamba kwa Cisautso Cacikulu
5. Kodi cisautso cacikulu cidzayamba bwanji?
5 Kuonongedwa kwa cipembedzo. Kumbukilani kuti Paulo anati: “Pamene azidzati: “Bata ndi mtendele!” ciwonongeko codzidzimutsa cidzafika pa iwo nthawi yomweyo.” Monga mmene zimakhalila ngati mphezi yang’anima, mwamsanga timamva kugunda kwa mvula. Ndi mmene zidzakhalila panthawi imene azidzati “Bata ndi mtendele!” nthawi yomweyo “ciwonongeko codzidzimutsa cidzafika.” N’ciani cimene cidzaonongedwa? Coyamba, ndi “Babulo Wamkulu,” amene ndi ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conama, ndipo amachedwanso “hule.” (Chiv. 17:5, 6, 15) Kuonongedwa kwa Machalichi Acikristu ndi magulu ena onse a zipembedzo zonama kudzakhala ciyambi ca “cisautso cacikulu.” (Mat. 24:21; 2 Ates. 2:8). Cocitika cimeneci cidzadzidzimutsa anthu ambili. N’cifukwa ciani tikutelo? Zidzakhala conco cifukwa cakuti kufikila nthawi imeneyo, huleli lidzapitilizabe kudziona kuti ndi “mfumukazi” ndi kuti ‘silingalile ngakhale pang’ono.’ Koma hulelo lidzazindikila kuti linali kudzinamiza. Ilo lidzaonongedwa “m’tsiku limodzi.”—Chiv. 18:7, 8.
6. Ndani amene adzaononga “Babulo Wamkulu”?
6 Kodi ndani amene adzaononga “Babulo Wamkulu”? “Cilombo” cokhala ndi “nyanga 10” n’cimene cidzaononga “Babulo Wamkulu.” Buku la Chivumbulutso limaonetsa kuti cilombo cimeneci cimaimila bungwe la United Nations (UN). Nyanga 10 zimaimila maiko onse amene amacilikiza “cilombo cofiila kwambili” cimeneci. (Chiv. 17:3, 5, 11, 12) Kodi cionongeko cimeneco cidzakhala cacikulu bwanji? Maiko amene amacilikiza bungwe la United Nations adzaononga cuma conse ca huleli, kulisakaza ndi “kulinyeketsa ndi moto.”—Ŵelengani Chivumbulutso 17:16. *
7. Kodi mau a Yesu a pa Mateyu 24:21, 22 anakwanilitsidwa bwanji m’nthawi ya atumwi? Nanga adzakwanilitsidwa bwanji mtsogolo?
7 Kufupikitsa masikuwo. Mfumu yathu inafotokoza zimene zidzacitika pa nthawi imene Babulo Wamkulu azidzaonongedwa. Yesu anati: “Cifukwa ca osankhidwawo, masikuwo adzafupikitsidwa.” (Ŵelengani Mateyu 24:21, 22.) Mau a Yesu amenewo anakwanilitsidwa pa mlingo wocepa mu 66 C.E. Panthawi imeneyo, Yehova ‘anafupikitsa masiku’ amene asilikali a Roma anaukila Yerusalemu. (Maliko 13:20) Zitatelo, Akristu a ku Yerusalemu ndi Yudeya anakhala ndi mwai wopulumuka. Nanga n’ciani cimene cidzacitika pa dziko lonse pa cisautso cacikulu? Pamene bungwe la United Nations lidzaukila cipembedzo, Yehova kupyolela mwa Mfumu yathu, ‘adzafupikitsa’ kuukilako n’colinga cakuti cipembedzo coona cisadzaonongedwe panthawi imene cipembedzo conyenga cidzaonongedwa. Conco, zipembedzo zonse zonyenga zidzaonongedwa, ndipo cipembedzo coona cokha ndi cimene cidzapulumuka. (Sal. 96:5) Tsopano tiyeni tione zimene zidzacitika pambuyo pakuti mbali imeneyi ya cisautso cacikulu yapita.
Zimene Zidzacitika Aramagedo Ikadzatsala Pang’ono Kuyamba
8, 9. Kodi Yesu ayenela kuti anali kunena za zocitika ziti? Nanga anthu adzacita ciani akadzaona zimenezo?
8 Ulosi wa Yesu wokhudza masiku otsiliza umaonetsa kuti padzacitika zinthu zingapo zapadela Aramagedo ikadzatsala pang’ono kuyamba. Tiyeni tsopano tikambilane zinthu ziŵili zoyambilila zimene zidzacitika. Zinthuzo zinachulidwa ndi olemba Mauthenga Abwino Mateyu, Maliko, ndi Luka.—Ŵelengani Mateyu 24:29-31; Maliko 13:23-27; Luka 21:25-28.
9 Kumwamba kudzacitika zinthu zodabwitsa. Yesu ananenelatu kuti: “Dzuŵa lidzacita mdima ndipo mwezi sudzapeleka kuwala kwake. Nyenyezi zidzagwa kucokela kumwamba.” Zoonadi, anthu adzaona kuti atsogoleli azipembedzo sangawauunikile ngakhale pang’ono. Kodi Yesu anali kutanthauzanso kuti kumwamba kudzacitika zinthu zina zodabwitsa? Mwina anali kutelo. (Yes. 13:9-11; Yow. 2:1, 30, 31) Kodi anthu adzacita ciani akadzaona zimenezo? Iwo adzazunzika, cifukwa ‘cothedwa nzelu.’ (Luka 21:25; Zef. 1:17) Indedi, adani a Ufumu wa Mulungu, kaya mafumu kapena akapolo, “adzakomoka cifukwa ca mantha ndi kuyembekezela zimene zicitikile dziko lapansi,” ndipo adzayesa kubisala. Koma sadzapeza malo obisalamo oti angawateteze ku mkwiyo wa Mfumu yathu.—Luka 21:26; 23:30; Chiv. 6:15-17.
10. N’ciani cimene Yesu adzacita? Kodi anthu amene amacilikiza Ufumu wa Mulungu ndiponso amene amakana kuucilikiza adzacita ciani?
10 Kulekanitsa nkhosa ndi Mbuzi. Adani a Ufumu wa Mulungu adzaona cocitika cina cimene cidzaonjezela mantha ao. Yesu anati: “Adzaona mwana wa munthu akubwela m’mitambo ndi mphamvu yaikulu ndiponso ulemenelo.” (Maliko 13:26) Zimenezi zidzaonetsa kuti Yesu wabwela kudzalekanitsa nkhosa ndi mbuzi. Mu ulosi wina wonena za masiku otsiliza, Yesu anafotokoza mwatsanetsane zimene zidzacitika panthawiyo. Mfundo zimenezo timazipeza m’fanizo la nkhosa ndi mbuzi. (Ŵelengani Mateyu 25:31-33, 46.) Anthu amene amacilikiza Ufumu mokhulupilika adzaweluzidwa monga “nkhosa” ndipo ‘adzatukula mitu yao’ pozindikila kuti ‘cipulumutso cao cayandikila.’ (Luka 21:28) Koma aja amene amatsutsa Ufumu wa Mulungu, adzaweluzidwa monga “mbuzi” ndipo “adzadziguguda pacifuwa cifukwa ca cisoni” podziŵa kuti ‘adzaonongedwa kothelatu.’—Mat. 24:30; Chiv. 1:7.
11. N’ciani cimene sitiyenela kuiwala tikaganizila zimene zidzacitika mtsogolo?
Mat. 25:32) Zinthu ziŵili zimene zidzacitika ndi kuukila kwa Gogi ndi kusonkhanitsa odzozedwa. Tsopano tiyeni tikambilane zinthu zimenezi, ndipo pamene tikukambilana, tisaiwale kuti Mau a Mulungu safotokoza nthawi yeniyeni pamene zinthuzo zidzacitika. Ndipo zikuoneka kuti cinthu cina cili mkati mocitika, cinanso cidzayamba.
11 Yesu akadzalekanitsa “mitundu yonse ya anthu,” padziko lapansi padzacitikanso zinthu zina zapadela nkhondo ya Aramagedo isanayambe. (12. Kodi Satana adzaukila bwanji Ufumu wa Mulungu?
12 Kuukila koopsa. Gogi wa ku dziko la Magogi adzaukila otsalila odzozedwa ndi anzao a nkhosa zina. (Ŵelengani Ezekieli 38:2, 11.) Mwa kucita izi, Satana adzakhala akuukila Ufumu wa Mulungu wokhazikitsidwa. Kuukila kumeneku, kudzakhala kuukila komaliza kumene Satana adzacita pa nkhondo yake yolimbana ndi otsalila odzozedwa kucokela pamene iye anathamangitsidwa kumwamba. (Chiv. 12:7-9, 17) Satana wakhala akulimbana ndi odzozedwa amenewa makamaka pamene io anayamba kusonkhanitsidwa mumpingo wacikristu wokonzedwanso. Colinga cake ndi kuononga unansi wao ndi Yehova, koma iye sangapambane. (Mat. 13:30) Panthawi yakuti zipembezo zonse zonyenga zaonongedwa, anthu a Mulungu adzaoneka ngati akukhala “m’midzi yopanda mipanda, ndipo alibe zotsekela ndiponso zitseko.” Satana adzaona kuti wapeza mpata wabwino woukila anthu a Mulungu. Iye adzasonkhezela mafumu onse a padziko lapansi kuti aukile moopsa anthu amene amacilikiza Ufumu wa Mulungu.
13. N’ciani cimene Yehova adzacita kuti ateteze anthu ake?
13 Ezekieli analosela zimene Gogi adzacita. Mu ulosiwo, iye anati: “Udzabwela kucokela kumalo ako, kumadela akutali a kumpoto. Udzabwela ndi mitundu yambili ya anthu. Anthuwo adzakhala khamu lalikulu, adzakhala cigulu cacikulu cankhondo. Onsewo adzabwela atakwela pamahachi. Ndithu iwe udzabwela ngati mitambo kudzaphimba dzikolo ndi kudzaukila anthu anga.” (Ezek. 38:15, 16) Kodi Yehova adzacita ciani ndi kuukila koopsa kumeneko? Yehova anati: “Mkwiyo wanga udzatulukila m’mphuno mwanga.” Ndipo anapitiliza ndi mau akuti: “Ndidzamubweletsela lupanga.” (Ezek. 38:18, 21; ŵelengani Zekariya 2:8.) Zoonadi, Yehova adzacitapo kanthu kuti apulumutse atumiki ake padziko lapansi. Kumeneko kudzakhala kuyamba kwa nkhondo ya Aramagedo.
14, 15. Ndi cocitika cina citi cimene cidzacitika Satana atayamba kale kuukila anthu a Mulungu?
14 Tisanakambilane mmene Yehova adzatetezela anthu ake pa nkhondo ya Aramagedo, coyamba tiyeni tikambilane za cocitika cina capadela. Cocitika cimeneco cidzacitika Satana atayamba kale kuukila atumiki a Mulungu, koma Yehova asanalowelelepo ndi nkhondo ya Aramagedo. Monga mmene taonela kale m’ndime 11, cocitika caciŵilici ndi kusonkhanitsa otsalila odzozedwa.
15 Kusonkhanitsa odzozedwa. Onse aŵili, Mateyu ndi Maliko, analemba mau a Yesu okhudza “osankhidwa” amene ndi Maliko 13:27; Mat. 24:31) Kodi Yesu anali kutanthauza kusonkhanitsa kotani? Iye sanali kutanthauza kudinda cidindo comaliza pa Akristu otsalila a odzozedwa kumene kudzacitika cisautso cacikulu cikadzatsala pang’ono kuyamba. (Chiv. 7:1-3) M’malomwake, iye anali kutanthauza zimene zidzacitika mkati mwa cisautso cacikulu. Mwacionekele, panthawi ina Satana atayamba kale kuukila atumiki a Mulungu, odzozedwa amene adzakhala akali padziko lapansi adzasonkhanitsidwila kumwamba.
Akristu odzozedwa. Iye anaonetsa kuti kusonkhanitsa odzozedwa kudzakhala mbali ina ya zimene zidzacitika Aramagedo ikadzatsala pang’ono kuyamba. (Onani ndime 7.) Pofotokoza za iye mwini monga Mfumu, Yesu anati: “Ndiyeno adzatumiza angelo ndipo adzasonkhanitsa pamodzi osankhidwa ake kucokela kumphepo zinayi, kucokela kumalekezelo ake a dziko lapansi kukafika kumalekezelo a m’mlengalenga.” (16. Kodi odzozedwa oukitsidwa adzacita ciani pa nkhondo ya Aramagedo?
16 Kodi kusonkhanitsa odzozedwa kudzatha Aramagedo isanayambe? Nthawi imene odzozedwa amenewa akusonkhanitsidwa, ikuonetsa kuti odzozedwawo adzakhala ali kumwamba nkhondo ya Aramagedo isanayambe. Akadzakhala kumwamba, olamulila anzake a Kristu a 144,000, adzapatsidwa ulamulilo wothandiza Yesu pa nchito yokusa anthu “ndi ndodo yacisulo” n’colinga cakuti aononge adani a Ufumu wa Mulungu. (Chiv. 2:26, 27) Kenako, otsalila odzozedwa oukitsidwa pamodzi ndi angelo amphamvu, adzatsatila Kristu, Mfumu ya Nkhondo, pamene adzapita kukakumana ndi “cigulu cacikulu cankhondo” ca adani amene adzakhala akuŵendelela anthu a Mulungu. (Ezek. 38:15) Zimenezo zikadzacitika, ndiye kuti nkhondo ya Aramagedo yayamba.—Chiv. 16:16.
Mapeto a Cisautso Cacikulu
17. N’ciani cidzacitikila anthu amene ali monga “mbuzi” pa Aramagedo?
17 Kupeleka ciweluzo. Nkhondo ya Aramagedo idzakhala mapeto a cisautso cacikulu. Panthawiyo, Yesu adzayambanso nchito ina. Kuonjezela pa kukhala woweluza “mitundu yonse,” iye adzakhalanso Wakupha mitundu, kutanthauza anthu amene adzawaweluza monga “mbuzi.” (Mat. 25:32, 33) Mfumu yathu ‘idzapha mitundu ya anthu’ ndi “lupanga lalitali lakuthwa.” Ndithudi, onse amene ali monga mbuzi, kaya ndi “mafumu” kapena “akapolo”, “adzapita ku cionongeko cothelatu.”—Chiv. 19:15, 18; Mat. 25:46.
18. (a) Kodi zinthu zidzawayendela bwanji anthu amene ali monga “nkhosa”? (b) N’ciani cimene Yesu adzacita kuti amalize nkhondo yake?
18 Anthu amene Yesu adzawaweluza monga “nkhosa,” zinthu zidzawayendela bwino. M’malo mofafanizidwa ndi magulu a nkhondo a Satana, amene ndi anthu okhala monga “mbuzi,” khamu lalikulu la “nkhosa” limene lidzaoneka monga losatetezeka, lidzapulumuka kuukila kwa adani, ndipo ‘lidzatuluka m’cisautso cacikulu.’ (Chiv. 7:9, 14) Ndiyeno, pambuyo pakuti Yesu wagonjetsa ndi kucotsa anthu onse amene ndi adani a Ufumu wa Mulungu, iye adzaponya Satana ndi ziŵanda zake kuphompho. Satana ndi ziŵanda zake adzakhala kumeneko kwa zaka 1,000, ndipo adzakhala wopanda mphamvu.—Ŵelengani Chivumbulutso 6:2; 20:1-3.
Kodi Tingakonzekele Bwanji Zocitikazi?
19, 20. Kodi mfundo ya pa Yesaya 26:20 ndi pa Yesaya 30:21 tingaigwilitsile nchito bwanji?
19 N’ciani cimene tiyenela kucita kuti tikonzekele zocitika zogwedeza dziko zimenezi? Zaka zambili zapitazo, magazini ina yacingelezi ya Nsanja ya Mlonda inati: “Kuti munthu adzapulumuke adzafunika kukhala womvela.” N’cifukwa ciani tiyenela kumvela? Yankho lake likupezeka m’malangizo amene Yehova anapeleka kwa Ayuda amene anali ku ukapolo ku Babulo wakale. Yehova anali atalosela kuti Babulo adzagonjetsedwa. Koma kodi anthu a Mulungu anayenela kucita ciani kuti akonzekele zimenezo? Yehova anati: “Inu anthu anga, pitani mukalowe m’zipinda zanu zamkati ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) Onani kuti mu vesi limeneli muli mau akuti “pitani,” “mukalowe,” “mukatseke,” ndi akuti “mukabisale.” Mau amenewa ndi malangizo opelekedwa monga malamulo. Ayuda amene anamvela malangizo amenewo anakhala m’nyumba zao, kubisala asilikali amene anabwela kudzaukila, ndipo anali kuyendayenda m’miseu. Motelo, io anafunikila kumvela malangizo a Yehova kuti apulumuke. *
20 Kodi tikuphunzilapo ciani pamenepa? Mofanana ndi atumiki a Mulungu a m’nthawi zakale, kuti tidzapulumuke tiyenela kumvela malangizo a Yehova. (Yes. 30:21) Malangizo amenewo timawalandila kupyolela mumpingo. Conco, tiyenela kumvela ndi mtima wonse malangizo onse amene timapatsidwa. (1 Yoh. 5:3) Ngati panopa timamvela, ndiye kuti kutsogoloku sitidzavutika kumvela. Mwakutelo, Atate wathu, Yehova, ndi Mfumu yathu Yesu, adzatiteteza. (Zef. 2:3) Ndipo Mulungu akadzatiteteza, tidzakhala ndi mwai wodzionela tokha mmene Ufumu wa Mulungu udzacotsela adani ake. Kunena zoona, zocitikazo zidzakhala zosaiwalika.
^ par. 6 N’kwanzelu kunena kuti cionongeko ca “Babulo Wamkulu” cikuimila cionongeko ca magulu onse a zipembedzo osati kuphedwa kwa anthu onse a m’zipembedzo zimenezo. Motelo, anthu ambili a m’zipembedzo zimenezi, sadzaphedwa pamene Babulo adzaonongedwa. Zikadzatelo, io adzayesa kupewa kugwilizana ndi cipembedzo poyela, mogwilizana ndi mau a pa Zekariya 13:4-6.
^ par. 19 Kuti mumve zambili, onani buku la Ulosi wa Yesaya—Muuni wa Anthu Onse, Gawo 1, patsamba 282 mpaka 283.