Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 16

Kusonkhana Pamodzi Kuti Tilambile Mulungu

Kusonkhana Pamodzi Kuti Tilambile Mulungu

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Kuphunzila mmene misonkhano yathu inayambila ndiponso kufunika kwake

1. Kodi ophunzila a Yesu analandila thandizo lotani pamene anasonkhana pamodzi? Nanga n’cifukwa ciani anafunika thandizo limenelo?

YESU atangoukitsidwa, ophunzila ake anasonkhana kuti alimbikitsane. Iwo anakhoma zitseko zonse za nyumba imene analimo cifukwa coopa adani ao. Mantha ao anatha pamene Yesu anaonekela pakati pao ndi kunena kuti: “Landilani mzimu woyela.” (Welengani Yohane 20:19-20.) Patapita nthawi, ophunzilawo anasonkhananso pamodzi, ndipo Yehova anawatsanulila mzimu woyela. Zimenezi zinawapatsa mphamvu zogwila nchito yolalikila.—Mac. 2:1-7.

2. (a) Kodi Yehova amatilimbikitsa m’njila yotani? N’cifukwa ciani timafunikila cilimbikitso cimeneco? (b) N’cifukwa ciani makonzedwe a Kulambila kwa Pabanja ndi ofunika kwambili? (Onani mau amunsi ndi kamutu kakuti “ Kulambila kwa Pabanja,” patsamba 175.)

2 Ifenso timakumana ndi mavuto ofanana ndi amene abale athu anakumana nao m’nthawi ya atumwi. (1 Pet. 5:9) Nthawi zina, ena a ife timaopa anthu. Timafunikila mphamvu zimene Yehova amapeleka kuti tipilile mavuto amene timakumana nao pogwila nchito yolalikila. (Aef. 6:10) Yehova amatipatsa mphamvu zimenezi kupyolela m’misonkhano yathu. Masiku ano, tili ndi mwai wopezeka pa misonkhano iŵili mlungu uliwonse. Misonkhano imeneyi ndi Nkhani ya Anthu Onse ndi Phunzilo la Nsanja ya Mlonda, komanso msonkhano wa mkati mwa wiki wochedwa Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu. * Timakhalanso ndi misonkhano ikuluikulu inai pacaka. Misonkhano imeneyi ndi msonkhano wacigawo, misonkhano iŵili yadela, ndi Cikumbutso ca imfa ya Kristu. N’cifukwa ciani tifunika kupezeka pa misonkhano yonse imeneyi? Kodi misonkhano imene timacita masiku ano inayamba bwanji? Nanga mmene timaonela misonkhanoyi zimasonyeza ciani za ifeyo?

N’cifukwa Ciani Tiyenela Kusonkhana Pamodzi?

3, 4. Kodi Yehova amafuna kuti anthu ake azicita ciani? Pelekani zitsanzo.

3 Kuyambila kale, Yehova wakhala akufuna kuti anthu ake azisonkhana pamodzi kuti amulambile. Mwacitsanzo, mu 1513 B.C.E.,Yehova anapatsa mtundu wa Isiraeli Cilamulo. Lamulo limodzi m’Cilamuloco linali lakuti Aisiraeli azisunga Sabata n’colinga cakuti banja lililonse laciisiraeli lizilambila Yehova ndi kuphunzila Cilamulo. (Deut. 5:12; 6:4-9) Pamene Aisiraeli anali kutsatila lamulo limeneli, mabanja ao anali kulimba kwambili, ndipo mtundu wonsewo unali kukhala woyela ndi wolimba mwakuuzimu. Koma pamene mtunduwo unalephela kutsatila Cilamulo mwa kunyalanyaza zinthu zofunika monga kusonkhana kuti alambile Yehova, Mulungu sanali kuwayanja.—Lev. 10:11; 26:31-35; 2 Mbiri 36:20, 21.

4 Taganizilani citsanzo cimene Yesu anatisiila. Mlungu uliwonse pa Sabata, iye anali kupita ku sunagoge. (Luka 4:16) Pambuyo poti Yesu wafa ndi kuukitsidwa, ophunzila ake anapitilizabe kusonkhana pamodzi nthawi zonse ngakhale kuti sanali kufunikanso kusunga Sabata. (Mac. 1:6, 12-14; 2:1-4; Aroma 14:5; Akol. 2:13, 14) Pa misonkhanoyo, Akristu a m’nthawi ya atumwi anali kulandila malangizo ndi cilimbikitso. Iwo analinso ndi mwai wopeleka nsembe za citamando kwa Mulungu mwa kupemphela, kupeleka ndemanga, ndi kuimba nyimbo.—Akol. 3:16; Aheb. 13:15

Ophunzila a Yesu anali kusonkhana pamodzi kuti alimbikitsane wina ndi mnzake

5. N’cifukwa ciani timapezeka pa misonkhano ya mpingo mlungu uliwonse ndiponso pa misonkhano ikuluikulu imene imacitika caka ciliconse? (Onani bokosi la mutu wakuti “ Misonkhano ya pa Caka Imene Imagwilizanitsa Anthu a Mulungu,” patsamba 176.)

5 Mofananamo, tikamapezeka pa misonkhano ya mpingo mlungu uliwonse ndi pa misonkhano ikuluikulu, timasonyeza kuti tikucilikiza Ufumu wa Mulungu. Pa misonkhanoyi timalimbikitsidwanso ndi mzimu woyela, ndipo ndemanga zathu zimalimbikitsa ena. Koposa zonse, timakhalanso ndi mwai wolambila Yehova mwa kupemphela, kupeleka ndemanga, ndi kuimba nyimbo. Ngakhale kuti mmene timacitila misonkhano masiku ano ndi zosiyana ndi mmene Aisiraeli ndiponso Akristu a m’nthawi ya atumwi anali kucitila, misonkhano yathu ndi yofunikanso. Kodi misonkhano imene timacita masiku ano inayamba bwanji?

Misonkhano ya Mlungu uliwonse Imatilimbikitsa pa “Cikondi ndi Nchito Zabwino”

6, 7. (a) Kodi colinga ca misonkhano yathu n’ciani? (b) Kodi misonkhano imene Ophunzila Baibulo anali kucita inali kusiyana m’njila zotani?

6 Pamene M’bale Charles Taze Russell anayamba kufunafuna coonadi ca Mau a Mulungu, anazindikila kufunika kosonkhana ndi anthu amene anali ndi colinga cofanana ndi cake. Mu 1879, M’bale Russell analemba kuti: “Ine limodzi ndi anthu ena ku Pittsburgh, tinakhazikitsa kalasi yophunzila Baibulo ndi colinga cakuti tizifufuza Malemba, ndipo timasonkhana pa Sondo paliponse.” Anthu amene anali kuŵelenga magazini ya Zion’s Watch Tower analimbikitsidwa kuti azisonkhana pamodzi. Podzafika mu 1881, misonkhano inali kucitika pa Sondo ndi pa Citatu paliponse ku Pittsburgh, m’dela la Pennsylvania. Magazini ya Watch Tower ya November 1895, inakamba kuti colinga ca misonkhanoyo cinali kulimbikitsa “mayanjano acikristu, cikondi ndi mgwilizano,” ndiponso kupatsa anthu onse opezekapo mwai wolimbikitsana wina ndi mnzake.—Ŵelengani Aheberi 10:24, 25.

7 Kwa zaka zambili, magulu a Ophunzila Baibulo anali kucita misonkhano yao m’njila zosiyanasiyana, ndipo magulu ena anali kusonkhana kaŵilikaŵili kuposa ena. Mwacitsanzo, gulu lina la Ophunzila Baibulo ku United States linalemba kalata imene inafalitsidwa mu 1911. Kalatayo inati: “Mlungu uliwonse timacita misonkhano isanu.” Iwo anali kucita misonkhano yao pa Mande, pa Citatu, pa Cisanu, ndipo pa Sondo anali kusonkhana kaŵili. Gulu lina mu Africa linalembanso kalata imene inafalitsidwa mu 1914. Kalatayo inati: “Timacita misonkhano yathu kaŵili pa mwezi. Timayamba pa Cisanu mpaka pa Sondo.” Koma m’kupita kwa nthawi, Ophunzila Baibulo anayamba kucita misonkhano yao mofanana ndi mmene timacitila masiku ano. Onani mmene msonkhano uliwonse unayambila.

8. Kodi mitu ina ya nkhani za anthu onse inali yotani?

8 Nkhani ya Anthu Onse. Mu 1880, patapita caka cimodzi kucokela pamene M’bale Russell anayamba kufalitsa magazini a Zion’s Watch Tower, iye anayamba kupanga maulendo okalalikila potsatila citsanzo ca Yesu. (Luka 4:43) Pa maulendowo, M’bale Russell anakhazikitsa njila yocitila msonkhano umene masiku ano timaucha Nkhani ya Anthu Onse. Polengeza za ulendo wa M’bale Russell, magazini ya Watch Tower inakamba kuti M’bale Russell “adzakamba nkhani ya anthu onse pa ‘Zinthu zokhudza Ufumu wa Mulungu.’’’ Mu 1911, pambuyo poti mipingo yakhazikitsidwa m’maiko ambili, mpingo uliwonse unalimbikitsidwa kutumiza alankhuli oyenelela ku madela apafupi ndi kwao kuti azikakamba nkhani zosiyanasiyana zokwana 6. Ina mwa mitu ya nkhanizo inali yokhudza ciweluzo ndi dipo. Pambuyo pankhani iliyonse, mutu wa nkhani ya mlungu wotsatila ndi dzina la mkambi zinali kulengezedwa.

9. Kodi Msonkhano wa Anthu Onse wasintha motani m’kupita kwa zaka? N’ciani cimene muyenela kucita kuti muzicilikiza msonkhano umenewu?

9 Mu 1945, Nsanja ya Mlonda yacingelezi inalengeza za nchito yapadela ya padziko lonse yoitanila anthu ku Nkhani za Anthu Onse. Nkhani za m’Baibulo zimenezo zinalipo 8, ndipo zinali zokhudza “mavuto ofunika kuthetsedwa mwamsanga.” Kwa zaka zambili, akambi a nkhani anali kugwilitsila nchito nkhani zimene kapolo wokhulupilika anali kukonza, ndipo nkhani zina mkambi anali kukonza yekha. Komabe mu 1981, akambi onse a nkhani za anthu onse analangizidwa kuti ayenela kugwilitsila nchito maautilaini amene mipingo imapatsidwa. * Maautilaini a nkhani zina anali kukhala ndi mbali zofuna kukambilana ndi omvela ndi kucita zitsanzo. Koma podzafika mu 1990, malangizo amenewo anasintha, ndipo kuyambila m’cakaco mkambi amafotokoza yekha nkhani. Kusintha kwina kunacitika mu January 2008 pamene nkhani za anthu onse zinayamba kukhala za mphindi 30 m’malo mwa mphindi 45. Ngakhale kuti nkhani za anthu onse zakhala zikusintha, nkhani zokonzekeledwa bwino zimatithandiza kukhulupilila kwambili Mau a Mulungu, ndi kutiphunzitsa mbali zosiyanasiyana zokhudza Ufumu wa Mulungu. (1 Tim. 4:13, 16) Kodi anthu amene timacitako maulendo obweleza ndi anthu ena amene si Mboni mumawaitana kuti adzamvetsele nkhani zozikidwa pa Baibulo zimenezi?

10-12. (a) Ndi kusintha kotani kumene kwacitika pa phunzilo la Nsanja ya Mlonda? (b) Ndi mafunso ati amene muyenela kudzifunsa?

10 Phunzilo la Nsanja ya Mlonda. Mu 1922, abale omwe anali kutumizidwa ndi bungwe la Watch Tower Society kuti akakambe nkhani ku mipingo ndi kukatsogolela pa nchito yolalikila, anapeleka lingalilo lakuti ndi bwino kuti nthawi zina abale azisonkhana n’colinga cakuti aziphunzila magazini ya The Watch Tower. Abale anayambadi kucita zimenezi, ndipo poyamba, phunzilo la Watch Tower linali kucitika mkati mwa mlungu kapena pa Sondo.

Pa phunzilo la Nsanja ku Ghana mu 1931

11 Nsanja ya Mlonda yacingelezi ya June 15, 1932, inapeleka malangizo oonjezeleka a mmene msonkhanowo unayenela kucitikila. Mwa kugwilitsila nchito citsanzo ca mmene banja la Beteli limacitila phunzilo la Nsanja ya Mlonda, nkhani ya m’magaziniyo inanena kuti m’bale mmodzi ayenela kutsogolela msonkhanowo. Abale atatu anali kukhala kutsogolo kwa pulatifomu n’colinga cakuti azilandizana poŵelenga ndime za m’magaziniyo. Panthawiyo, nkhani zophunzila sizinali kukhala ndi mafunso. Conco wotsogoza phunzilo la Nsanja ya Mlonda anauzidwa kuti azipempha gulu kufunsa mafunso pa nkhani imene ikuphunzilidwa. Kenako anali kupeleka mwai kwa osonkhanawo kuti ayankhe mufunsowo. Ngati mfundo ina sinamveketsedwe bwino, wotsogoza analangizidwa kufotokozapo “mwacidule ndi momveka bwino.”

12 Paciyambi, mpingo uliwonse unali kuloledwa kuphunzila nkhani ya m’magazini imene anthu ambili a mpingowo anasankha kuti aphunzile. Komabe, Nsanja ya Mlonda yacingelezi ya April 15, 1933, inapeleka malangizo akuti mpingo uliwonse uyenela kuphunzila magazini yatsopano. Malangizo akuti phunzilo la Nsanja ya Mlonda liyenela kucitika pa Sondo anapelekedwa mu 1937. Ndiyeno mu Nsanja ya Mlonda yacingelezi ya October 1, 1942, munali malangizo ena a mmene phunzilo la Nsanja ya Mlonda liyenela kucitikila, ndipo malangizowo ndi amene timatsatila mpaka masiku ano. Coyamba, magaziniyo inanena kuti mafunso ofunika kugwilitsila nchito pa phunzilo la Nsanja ya Mlonda azipezeka munsi mwa ndime za nkhaniyo. Ndiyeno inanenanso kuti msonkhano wa Nsanja ya Mlonda uyenela kucitika kwa ola limodzi. Inalimbikitsanso anthu amene anali kupeleka mayankho pa phunzilolo kuti “ayenela kuyankha m’mau ao-ao” m’malo moŵelenga yankho mu ndime. Phunzilo la Nsanja ya Mlonda ndi msonkhano wofunika umene kapolo wokhulupilika akugwilitsilabe nchito potipatsa cakudya cakuuzimu ca panthawi yake. (Mat. 24:45) Aliyense wa ife ayenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimakonzekela phunzilo la Nsanja ya Mlonda mlungu uliwonse? Kodi ndimayetsetsa kuyankhapo pa phunziloli?’

13, 14. Kodi Phunzilo la Baibulo la Mpingo linayamba bwanji? N’ciani cimene inuyo mumasangalala naco kwambili pa msonkhanowu?

13 Phunzilo la Baibulo la Mpingo. Ca m’ma 1890, mavoliyamu a buku la Millennial Dawn atafalitsidwa, M’bale H. N. Rahn, mmodzi wa Ophunzila Baibulo amene anali kukhala ku Baltimore, m’dela la Maryland ku United States, anapeleka malingalilo akuti abale aziphunzila Baibulo mu “Magulu a Dawn.” Poyamba anayesa kucitila misonkhanoyo m’nyumba za anthu. Koma podzafika mu September 1895, misonkhano ya Magulu a Dawn imeneyi inali kucitika m’madela ambili m’dziko la United States. Mpake kuti magazini ya Watch Tower ya September 1895, inanena kuti onse amene anali kuphunzila coonadi anayenela kupezeka pa misonkhanoyi. Magaziniyo inanenanso kuti m’bale wocititsa msonkhanowo anafunika kukhala muŵelengi wabwino. Iye anali kuŵelenga ciganizo cimodzi ndi kuyembekezela kuti osonkhanawo athililepo ndemanga. Pambuyo poŵelenga ndi kukambilana ziganizo zonse m’ndime, wotsogozayo anali kuŵelenga malemba onse amene anali m’ndimemo. Pambuyo pokambilana mutu umodzi, opezeka pamsonkhanowo anali kupelekapo ndemanga zacidule pa zimene aphunzilazo.

14 Dzina la msonkhano umenewu linasintha kangapo. Potengela citsanzo ca zimene anthu a ku Bereya anali kucita pophunzila Malemba mosamalitsa m’nthawi za atumwi, msonkhanowu unayamba kuchedwa Magulu a Abereya Ophunzila Baibulo. (Mac. 17:11) M’kupita kwa nthawi msonkhanowu unayamba kuchedwa Phunzilo la Buku la Mpingo. Masiku ano, umachedwa Phunzilo la Baibulo la Mpingo, ndipo umacitikila ku Nyumba ya Ufumu osati m’nyumba za abale. Mpingo wonse umasonkhana pamodzi panthawi yaphunzilo limeneli. Kwa zaka zonsezi, pa msonkhanowu takhala tikugwilitsila nchito mabuku osiyanasiyana, mabrosha, ndiponso nkhani za mu Nsanja ya Mlonda. Kuyambila kale, anthu onse opezeka pa msonkhanowu akhala akulimbikitsidwa kutengamo mbali. Msonkhano umenewu wakhala ukutithandiza kukulitsa cidziwitso cathu ca Baibulo. Kodi mumakonzekela msonkhanowu nthawi zonse ndiponso kuyankhapo mmene mungathele?

15. Kodi colinga ca Sukulu ya Ulaliki cinali ciani?

15 Sukulu ya Ulaliki. M’bale Carey Barber, amene panthawiyo anali kutumikila ku likulu ku Brooklyn, mumzinda wa New York, anati: “Pa Mande usiku, pa February 16, 1942, abale onse a m’banja la Beteli ku Brooklyn anapemphedwa kulembetsa m’sukulu imene masiku ano timaicha Sukulu ya Ulaliki.” M’bale Barber, amene m’kupita kwa nthawi anadzakhala membala wa m’Bungwe Lolamulila, anakamba kuti sukuluyi “ndi imodzi mwa zinthu zazikulu zimene Yehova wacitila anthu ake masiku ano.” Maphunzilo a sukuluyi anathandiza kwambili abale kunola maluso ao pophunzitsa ndi polalikila. Pa cifukwa cimeneci, kuyambila mu 1943, kabuku ka mutu wakuti Course in Theocratic Ministry (Kosi ya Utumiki wa Mulungu) kanayamba kutumizidwa ku mipingo yonse padziko lapansi. Nsanja ya Mlonda yacingelezi ya June 1, 1943, inakamba kuti colinga ca Sukulu ya Ulaliki ndi kuthandiza anthu a Mulungu “kuphunzila kucitila bwino umboni ponena za Ufumu.”—2 Tim. 2:15.

16, 17. Kodi Sukulu ya Ulaliki inali kungophunzitsa munthu kukhala ndi luso lophunzitsa? Fotokozani.

16 Poyamba abale ambili anali kuvutika kulankhula ku gulu lalikulu la anthu. M’bale Clayton Woodworth, Jr., amene atate wake anaikidwa m’ndende popanda cifukwa pamodzi ndi M’bale Rutherford ndiponso abale ena mu 1918, anafotokoza mmene anamvelela pamene anangolembetsa m’sukuluyi mu 1943. M’bale Woodworth anati: “Ndinali kuvutika kukamba nkhani. Lilime langa linali kudzala mkamwa ndipo munali kuuma gwaa, komanso mau anga anali kunjenjemela.” Sukuluyi inanola maluso a m’baleyu, ndipo m’kupita kwa nthawi anakambanso nkhani zina zambili pagulu. Iye anaphunzilanso zinthu zina m’sukuluyi kuonjezela pa luso lophunzitsa. M’bale Woodworth anaphunzilanso kufunika kokhala wodzicepetsa ndi kudalila Yehova. Iye anati: “Ndinazindikila kuti luso la mkambi palokha silingathandize. Koma akakonzekela bwino kwambili nkhani yake ndi kuika cidalilo cake conse pa Yehova, anthu angasangalale kumvetsela nkhani yake, ndipo angaphunzilepo kanthu kena.”

17 Mu 1959, alongo naonso anauzidwa kuti akhoza kulembetsa m’sukulu imeneyi. Mlongo wina dzina lake Edna Bauer anafotokoza mmene zinthu zinalili pamene cilengezoco cinapelekedwa pa msonkhano wina waukulu. Iye anati: “Ndikukumbukila kuti alongo tonse tinasangalala pamene tinamva cilengezoco. Tinazindikila kuti ifenso alongo tapatsidwa mwai wina waukulu.” Kwa zaka zambili, abale ndi alongo ambili anali kulembetsa m’Sukulu ya Ulaliki kuti aphunzitsidwe ndi Yehova. Masiku ano, Mulungu akupitiliza kutiphunzitsa kupitila mu msonkhano wa mkati mwa wiki.—Ŵelengani Yesaya 54:13.

18, 19. (a) Kodi masiku ano timalandila bwanji malangizo otithandiza pa nchito yolalikila? (b) N’cifukwa ciani timaimba nyimbo pa misonkhano yathu? (Onani bokosi la mutu wakuti “ Kuimba Nyimbo za Coonadi.”)

18 Msonkhano wa Nchito. Kuyambila mu 1919, panali kukhala misonkhano yokonzekela utumiki wa kumunda. Panthawiyo, anthu amene anali kuloledwa kupezeka pa msonkhano umenewu ndi aja okha amene anali kutenga nao mbali pa nchito yogaŵila mabuku. Koma mu 1923, Msonkhano wa Nchito unali kucitika kamodzi pa mwezi, ndipo anthu onse mumpingo anali kufunika kupezeka pamsonkhanowo. Podzafika mu 1928, mipingo inalimbikitsidwa kuti izicita Msonkhano wa Nchito kamodzi mlungu uliwonse. Ndiyeno mu 1935, magazini ya Nsanja ya Mlonda inanena kuti pa Msonkhano wa Nchito mipingo yonse izigwilitsila nchito nkhani zopezeka mu Director (imene m’kupita kwa nthawi inayamba kuchedwa Informant ndipo pambuyo pake inayamba kuchedwa Utumiki Wathu wa Ufumu). Posapita nthawi yaitali, msonkhanowu unayamba kucitika mlungu uliwonse m’mipingo yonse.

19 Masiku ano, timalandila malangizo pa msonkhano wathu wa mkati mwa wiki othandiza pa nchito yolalikila. (Mat. 10:5-13) Ngati mumalandila kabuku ka misonkhano, kodi mumakaŵelenga ndi kugwilitsila nchito mfundo zake pamene muli muutumiki wa kumunda?

Msonkhano Wofunika Kwambili pa Caka

Kuyambila m’nthawi ya atumwi, Akristu akhala akusonkhana kamodzi pa caka n’colinga cakuti acite Cikumbutso ca imfa ya Kristu (Onani ndime 20)

20-22. (a) N’cifukwa ciani timacita mwambo wokumbukila imfa ya Yesu? (b) Kodi kupezeka pa Cikumbutso caka ciliconse kumakupindulitsani bwanji?

20 Yesu analamula otsatila ake kuti azikumbukila imfa yake mpaka iye atabwela. Monga mmene mwambo wa Pasika unali kucitikila, Cikumbutso ca imfa ya Kristu ciyenela kucitika kamodzi pa caka. (1 Akor.11:23-26) Anthu mamiliyoni ambili amapezeka pa msonkhano umenewu. Mwambowu umakumbutsa odzozedwa za mwai umene ali nao wokhala olamulila mu Ufumu. (Aroma 8:17) Mwambo umenewu umapangitsa a nkhosa zina kukhala okhulupilika kwa Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndi kuilemekeza.—Yoh. 10:16.

21 M’bale Russell ndi anzake anazindikila kufunika kocita Mgonelo wa Ambuye, ndipo anadziŵa kuti ayenela kucita mwambo umenewu kamodzi pa caka. Magazini ya Watch Tower ya April 1880 inati: “Kwa zaka zambili, ambili a ife kuno ku Pittsburgh  . . . takhala tikucita Pasika [Mgonelo] ndiponso kudya ziphiphilitso za thupi ndi magazi a Ambuye.” Posapita nthawi, anayamba kucita Misonkhano Yacigawo panthawi ya Cikumbutso. Nthawi yoyamba imene ciŵelengelo ca ofika pa mwambo umenewo cinasungidwa ndi mu 1889. Pa mwambowo panali anthu 225, ndipo anthu 22 anabatizidwa.

22 Masiku ano, siticita Cikumbutso panthawi imodzi ndi Msonkhano wa Cigawo. Ngakhale ndi conco, timaitanilabe anthu amene timakhala nao pafupi ku mwambowo umene timacitila pa Nyumba ya Ufumu kapena pa malo ena. Anthu oposa 19 miliyoni anapezeka pa mwambo wokumbukila imfa ya Yesu mu 2013. Ndi mwai waukulu kwambili kupezeka pa Cikumbutso ndiponso kuitanila anthu ena ku mwambo wapadela umenewu. Kodi mumacita khama kuitanila anthu ambili monga mmene mungathele ku Cikumbutso caka ciliconse?

Kodi Kupezeka pa Misonkhano Kumasonyeza Ciani?

23. Kodi misonkhano yathu muyenela kuiona bwanji?

23 Atumiki okhulupilika a Yehova amasangalala kumvela lamulo lakuti azisonkhana pamodzi. (Aheb. 10:24, 25; 1 Yoh. 5:3) Mwacitsanzo, Mfumu Davide anali kukonda kukalambila ku nyumba ya Yehova. (Sal. 27:4) Iye anali kukonda kulambila pamodzi ndi anthu ena amene anali kukondanso Mulungu. (Sal. 35:18) Ganizilaninso citsanzo ca Yesu. Iye anali kukonda kukhala m’nyumba ya Atate wake yolambililamo kuyambila ali mwana.—Luka 2:41-49.

Ngati timakonda kusonkhana, timaonetsa kuti timaona Ufumu wa Mulungu kukhala weniweni

24. Ndi mwai wotani umene timakhala nao tikapezeka pa misonkhano?

24 Kupezeka kwathu pa misonkhano, kumasonyeza kuti timakonda Yehova ndi kuti tikufunitsitsa kulimbikitsa Akristu anzathu. Timasonyezanso kuti tikufuna kuphunzila mmene nzika za Ufumu wa Mulungu ziyenela kukhalila, cifukwa cakuti pa misonkhano ya mpingo ndiponso pamisonkhano ikuluikulu m’pamene timaphunzila zinthu za conco. Kuonjezela pamenepo, misonkhano yathu imatithandiza kukhala ndi luso komanso mphamvu zimene zingatithandize kupilila pogwila nchito yofunika kwambili imene ikucilikizidwa ndi Ufumu wa Mulungu. Nchito imeneyi ndi yopanga ophunzila a Mfumu Yesu Kristu ndi kuwaphunzitsa. (Ŵelengani Mateyu 28:19, 20.) Mosakaikila, ngati timakonda kusonkhana, timaonetsa kuti timaona Ufumu wa Mulungu kukhala weniweni. Tiyeni tiziona misonkhano kukhala yofunika kwambili.

^ par. 2 Kuonjezela pa misonkhano ya mpingo imene timakhala nayo mlungu uliwonse, banja lililonse ndiponso munthu aliyense payekha amalimbikitsidwa kupatula nthawi yocita phunzilo laumwini kapena kulambila kwa pabanja.

^ par. 9 Podzafika mu 2013, panali maautilaini oposa 180 a nkhani za anthu onse.