Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 12

Gulu Lotumikila “Mulungu Wamtendele”

Gulu Lotumikila “Mulungu Wamtendele”

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Mmene Yehova wakonzela gulu lake pang’onopang’ono

1, 2. Kodi magazini a Zion’s Watch Tower anasintha bwanji mu January 1895? Nanga abale anamva bwanji ataona kusinthako?

WOPHUNZILA Baibulo wina wacangu wochedwa John A. Bohnet anasangalala ndi zimene anaona pamene analandila magazini ya Zion’s Watch Tower ya January 1895. Magaziniyo inali ndi cikuto catsopano, ndipo pacikutopo panali cithunzi ca nyumba ya nsanja yokhala ndi nyale yowala kwambili usiku. Nyumba ya nsanjayo inali pakati pa nyanja ya mafunde. M’magaziniyo munali cilengezo cokhudza kusintha kwa cithunzi ca pa magazini. Cilengezoco cinali ndi mutu wakuti “Kaonekedwe Katsopano ka Magazini Athu.”

2 M’bale Bohnet anasangalala kwambili, ndipo analembela kalata M’bale Russell kuti: “Ndasangalala kuona mmene magazini a WATCH TOWER akongolela. Akuoneka bwino kwambili.” Wophunzila Baibulo wina wokhulupilika dzina lake John H. Brown analembanso maganizo ake ponena za cithunzi ca pacikutoco. Iye anati: “Cithunzici cikuoneka mwapadela kwambili. Ngakhale kuti nyumba ya nsanjayi ikuombedwa ndi mafunde ndiponso cimphepo ca mkuntho, maziko ake akuoneka kukhala olimba kwambili.” Cimeneci cinali ciyambi cabe ca kusintha kwa cikuto ca magazini. M’mwezi wa November caka cimeneco, abale athu anaonanso kusintha kwina kwakukulu pa cithunzi ca pacikuto ca magazini. Koma zocititsa cidwi ndi kusinthako zinali zakuti cithunzico cinali kuonetsanso cimphepo ca mkuntho panyanja.

3, 4. Ndi vuto liti limene Nsanja ya Mlonda ya November 1895 inafotokoza? Nanga magaziniyo inalengeza kuti padzakhala kusintha kwakukulu kotani?

3 Nkhani imene inatuluka m’magazini ya Watch Tower ya November 15, 1895, inafotokoza mwatsatanetsatane za vuto limene linalipo. Magaziniyo inanena kuti panali mavuto ena amene anali kusokoneza mtendele pakati pa Ophunzila Baibulo. Mavutowo anali monga cimphepo ca mkuntho. Kaŵilikaŵili abale anali kukangana pankhani yokhudza amene ayenela kutsogolela pampingo. Pofuna kuthandiza abale kuthetsa mzimu wogawanitsa anthu umenewu, nkhaniyo inayelekezela gulu la Mulungu ndi combo. Ndipo inanenanso mosapita m’mbali kuti abale amene anali kutsogolela panthawiyo, anali atalephela kukonzekeletsa gulu la Mulungu kaamba ka mavuto. Kodi io anayenela kucita ciani?

4 Nkhani ya m’magaziniyo inafotokoza kuti woyendetsa combo waluso amaonetsetsa kuti wanyamula zovala zothandiza anthu kuti asamile pakacitika ngozi. Amaonetsetsanso kuti ogwila nchito m’combomo, ndi okonzekela ngozi iliyonse imene angakumane nayo panthawi ya cimphepo camkuntho. Mofananamo, abale amene anali kutsogolela gulu anafunika kukonzekeletsa mipingo yonse kaamba ka mavuto amene anali kubwela mtsogolo. Kuti zimenezo zitheke, nkhaniyo inafotokoza za kusintha kwakukulu kumene kunayenela kucitika. Inakamba kuti kuyambila nthawiyo, “akulu anayenela kusankhidwa mumpingo uliwonse kuti ‘aziyang’anila’ nkhosa.”—Mac. 20:28.

5. (a) N’cifukwa ciani makonzedwe akuti pampingo pazikhala akulu anali a panthawi yake? (b) Kodi tikambilana mafunso ati?

5 Makonzedwe akuti pampingo pazikhala akulu anali a panthawi yake cifukwa anathandiza kuti mipingo ikhale yolimba. Makonzedwewa anathandizanso abale kupilila mavuto amene anakumana nao pa Nkhondo Yoyamba Yapadziko Lonse. M’zaka zotsatilapo, panakhalanso kusintha kwina m’gulu kumene kunathandiza anthu a Mulungu kutumikila Yehova bwino lomwe. Kodi ndi ulosi wa m’Baibulo uti umene unanenelatu za zocitikazi? Ndi kusintha kotani kumene inu mwaona kukucitika m’gulu? Kodi mwapindula bwanji ndi kusintha kumeneko?

“Ndidzaika Mtendele Kuti Ukhale Ngati Wokuyang’anila”

6, 7. (a) Kodi lemba la Yesaya 60:17 limatanthauza ciani? (b) Kodi mau akuti “wokuyang’anila” ndi “wokupatsa nchito” amasonyeza ciani?

6 Monga mmene tinaphunzilila m’Nkhani 9, Yesaya analosela kuti Yehova adzaculukitsa anthu ake. (Yes. 60:22) Kupyolela mwa Yesaya, Yehova analonjezanso kuti adzacita zinthu zina zambili. Mu ulosi womwewo, Iye anati: “M’malo mwa mkuwa, ndidzabweletsa golide. M’malo mwa citsulo, ndidzabweletsa siliva. M’malo mwa mtengo, ndidzabweletsa mkuwa ndipo m’malo mwa miyala, ndidzabweletsa citsulo. Ndidzaika mtendele kuti ukhale ngati wokuyang’anila, ndi cilungamo kuti cikhale ngati wokupatsa nchito.” (Yes. 60:17) Kodi ulosi umenewu umatanthauzanji? Kodi umatikhudza bwanji masiku ano?

Kusinthako ndi kusintha cinthu cabwino kuti cikhale cabwino kwambili

7 Ulosi wa Yesaya unasonyeza kuti cinthu cina cidzalowedwa m’malo ndi cina. Onani kuti kusinthako ndi kusintha cinthu cabwino kale kuti cikhale cabwino kwambili. Ngati golide aloŵa m’malo mwa mkuwa ndiye kuti zinthu zikuyenda bwino, cimodzimodzinso ndi zinthu zina zomwe zachulidwa mu ulosiwu. Ndi mau ophiphilitsa amenewa, Yehova analosela kuti zinthu pakati pa anthu ake zidzakhala bwino kwambili m’kupita kwa nthawi. Kodi ulosiwu ukunena za kusintha kotani? Pochula “wokuyang’anila” ndi “wokupatsa nchito,” Yehova anasonyeza kuti anthu ake adzayamba kusamalidwa ndi kutsogoleledwa bwino kwambili.

8. (a) Ndani amene akucititsa masinthidwe olembedwa mu ulosi wa Yesaya? (b) Kodi timapindula bwanji cifukwa ca masinthidwewo? (Onani bokosi lakuti “ Analandila Uphungu Modzicepetsa.”)

8 Kodi ndani amapangitsa kusinthaku? Mu ulosiwo, Yehova anati: “Ndidzabweletsa golide, . . . ndidzabweletsa siliva, . . . ndidzaika mtendele.” Zoonadi, Yehova ndi amene wacititsa kuti zinthu zisinthe m’gulu lake osati anthu. Ndipo kucokela pamene Yesu anakhala Mfumu, Yehova wakhala akusintha zinthu m’gulu lake kupyolela mwa Mwana wakeyo. Kodi timapindula bwanji ndi kusinthako? Lembalo limasonyeza kuti kusinthako kudzabweletsa “mtendele” ndi “cilungamo.” Tikamagonjela citsogozo ca Mulungu ndi kusintha zinthu zina paumoyo wathu, timakhala ndi mtendele pakati pathu. Ndipo kukonda cilungamo kumatipangitsa kutumikila Yehova amene ndi “Mulungu wamtendele,” mogwilizana ndi mau a mtumwi Paulo.—Afil. 4:9.

9. N’ciani cimathandiza kuti mumpingo mukhale dongosolo ndi mgwilizano? N’cifukwa ciani mwayankha telo?

9 Ponena za Yehova, mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu si Mulungu wacisokonezo, koma wamtendele.” (1 Akor. 14:33) Pa lembali, Mtumwi Paulo sanasiyanitse khalidwe lacisokonezo ndi khalidwe ladongosolo. M’malo mwake, iye anasiyanitsa khalidwe lacisokonezo ndi khalidwe lamtendele. N’cifukwa ciani anatelo? Cifukwa cakuti ngati zinthu zikuyenda mwadongosolo sizitanthauza kuti nthawi zonse pamakhala mtendele. Mwacitsanzo, gulu la asilikali lingayende mwadongosolo kudela la nkhondo. Koma ngakhale ayende mwadongosolo, zotsatilapo zake zimakhala nkhondo osati mtendele. Motelo, monga Akristu, nthawi zonse tiyenela kukumbukila mfundo yofunika iyi: Gulu lililonse la anthu amene pakati pao palibe mtendele, m’kupita kwa nthawi limasokonezeka kapena kutha kumene. Mosiyana ndi zimenezi, mtendele wa Mulungu umalimbikitsa mzimu wa dongosolo umene umakhalitsa. Conco, ndife osangalala kuti tili m’gulu limene limatsogoleledwa ndi kuyengedwa ndi “Mulungu amene amapatsa mtendele.” (Aroma 15:33) Mtendele umene Mulungu amapeleka umapangitsa kuti m’mipingo yathu padziko lonse lapansi mukhale dongosolo ndi mgwilizano wolimba umene timasangalala nao.—Sal. 29:11.

10. (a) Ndi masinthidwe otani amene anacitika m’gulu lathu m’nthawi ya Ophunzila Baibulo? (Onani bokosi lakuti “ Mmene Zinthu Zinasinthila Pankhani ya Kuyang’anila Mpingo.”) (b) Kodi tikambilana mafunso otani tsopano?

10 Bokosi lamutu wakuti, “ Mmene Zinthu Zinasinthila Pankhani ya Kuyang’anila Mpingo” likufotokoza za kusintha kumene kunathandiza kuti zinthu ziziyenda mwadongosolo mumpingo m’nthawi ya Ophunzila Baibulo. Koma kodi Yehova posacedwapa wasintha zinthu ziti m’gulu kupyolela mwa Mfumu yathu? Kodi kusintha makonzedwe okhudza anthu amene ayenela kukhala oyang’anila, kwalimbikitsa motani mtendele ndi mgwilizano m’mipingo padziko lonse lapansi? Nanga kusinthako kumakuthandizani bwanji inuyo panokha potumikila “Mulungu wamtendele”?

Mmene Kristu Amatsogolela Mpingo

11. (a) Ndi masinthidwe otani okhudza kamvedwe kathu amene anakhalapo pambuyo pophunzila Malemba? (b) Kodi abale a m’bungwe lolamulila anali otsimikiza mtima kucita ciani?

11 Kuyambila mu 1964 mpaka mu 1971, bungwe lolamulila linali kuyang’anila nchito yophunzila Baibulo mwakuya n’colinga cakuti amvetsetse zinthu zina zambili. Cimodzi mwa zinthu zimene anali kufuna kudziŵa ndi mmene mpingo wacikristu wa m’nthawi ya atumwi unali kuyendela. * Pakafufuku amene anacita, io anadziŵa kuti m’nthawi ya atumwi, mipingo inali kuyang’anilidwa ndi bungwe la akulu osati mkulu kapena woyang’anila mmodzi. (Ŵelengani Afilipi 1:1; 1 Timoteyo 4:14.) Pamene abale anamvetsetsa mfundoyo, bungwe lolamulila linazindikila kuti Mfumu yao, Yesu, inali kuwatsogolela kuti akonze kayendetsedwe ka gulu la Mulungu. Motelo, abale a m’bungwe lolamulila anali ofunitsitsa kutsatila citsogozo ca Mfumuyo. Mwamsanga io anasintha zinthu zina n’colinga cakuti aziika akulu mogwilizana ndi mmene Malemba amanenela. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zinasintha kuciyambi kwa zaka za m’ma 1970?

12. (a) Kodi ndi masinthidwe otani amene anacitika m’bungwe lolamulila? (b) Fotokozani mmene Bungwe Lolamulila lalinganizidwila masiku ano. (Onani bokosi lakuti “ Mmene Bungwe Lolamulila Limasamalila Zinthu za Ufumu,” patsamba 130.)

12 Kusintha koyamba kunakhudza bungwe lolamulila lomwelo. Caka ca 1971 cisanafike, madailekitala 7 a Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, amene anali abale odzozedwa, ndi amene anali m’bungwe lolamulila. Komabe, mu 1971, ciŵelengelo ca abale a m’bungwe lolamulila cinakwela kucoka pa mamembala 7 kufika pa mamembala 11. Kuyambila nthawiyo, panakhala kusiyana pakati pa gulu la madailekitala amenewo ndi bungwe lolamulila. Koma mamembalawo anali kuona kuti panalibe kusiyana kulikonse pakati pao, ndipo anayamba kusintha cheyamani caka ciliconse motsatila alifabeti.

13. (a) Kodi ndi makonzedwe otani amene anali kugwila nchito kwa zaka 40? (b) N’ciani cimene Bungwe Lolamulila linacita mu 1972?

13 Kusintha kwina kunakhudza mipingo yonse. Motani? Kuyambila mu 1932 mpaka mu 1972, mpingo unali kuyang’anilidwa ndi m’bale mmodzi. M’baleyo anali kuchedwa wotsogolela utumiki mpaka kudzafika mu 1936. Pambuyo pake dzinalo linasintha, ndipo anayamba kuchedwa mtumiki wa mpingo, kenako anayamba kuchedwa woyang’anila mpingo. Abalewa anali kusamalila nkhosa za Mulungu mwacangu. Woyang’anila mpingo, kaŵilikaŵili anali kupanga zosankha za mpingo popanda kufunsila maganizo a atumiki ena mumpingo. Komabe, mu 1972, Bungwe Lolamulila linasintha zinthu zina. Kodi kusintha kumeneko kunali kotani?

14. (a) Kodi ndi makonzedwe otani amene anayamba kugwila nchito pa October 1, 1972? (b) Kodi mgwilizanitsi wa bungwe la akulu amagwilitsila nchito bwanji uphungu wa pa Afilipi 2:3?

14 Abale ena amene anali kukwanilitsa ziyeneletso za m’Malemba, anayamba kuikidwa kukhala akulu m’mipingo, m’malo mokhala ndi m’bale mmodzi woyang’anila mpingo. Abalewo anayamba kutumikila pamodzi monga bungwe la akulu limene linali kuyang’anila mpingo. Makonzedwe atsopano amenewa anayamba kugwila nchito pa October 1, 1972. Masiku ano, mgwilizanitsi wa bungwe la akulu samadziona ngati wofunika kwambili kuposa akulu ena, koma amadziona “ngati wamng’ono.” (Luka 9:48) Ndi dalitso lalikulu kwambili kukhala ndi abale odzicepetsa amenewo.—Afil. 2:3.

N’zosacita kufunsa kuti Mfumu yathu inacita zinthu mwanzelu potipatsa abusa panthawi yake

15. (a) Kodi makonzedwe akuti pampingo pazikhala akulu akhala opindulitsa bwanji? (b) N’ciani cikusonyeza kuti Mfumu yathu inacita zinthu mwanzelu?

15 Makonzedwe akuti akulu azigwila nchito pamodzi monga bungwe la akulu akhala othandiza kwambili. Taonani mapindu atatu amene akhalapo cifukwa ca makonzedwewa. Coyamba ndiponso cacikulu, makonzedwewa amathandiza akulu onse kukumbukila kuti Yesu ndiye Mutu wa mpingo mosasamala kanthu za maudindo amene akuluwo ali nao pampingo. (Aef. 5:23) Caciŵili, lemba la Miyambo 15:22 limati: “Aphungu akaculuka zimakwanilitsidwa.” Conco, akulu amakumana ndi kukambilana nkhani zokhudza mpingo, ndipo pokambilanapo, amamvetsela maganizo a akulu anzao. Zimenezi zimathandiza kuti io apange zosankha mogwilizana ndi mfundo za m’Baibulo. (Miy. 27:17) Yehova amadalitsa zosankha zaozo moti zimathandiza kuti mpingo upite patsogolo. Cacitatu, kukhala ndi abale ambili otumikila monga akulu, kwathandiza kuti pakhale abale okwanila oti aziyang’anila ndi kuweta nkhosa m’mipingo imene ikuculukilaculukila. (Yes. 60:3-5) Tangoganizilani mmene mipingo yaculukila kucokela pa 27,000 mu 1971 kufika pa mipingo yoposa 113,000 mu 2013. Apa n’zosacita kufunsa kuti Mfumu yathu inacita zinthu mwanzelu potipatsa abusa panthawi yake.—Mika 5:5.

“Mukhale Zitsanzo kwa Gulu la Nkhosa”

16. (a) Kodi akulu ali ndi udindo wotani? (b) Kodi Ophunzila Baibulo anali kuwaona bwanji malangizo a Yesu akuti ‘weta nkhosa’?

16 Kale m’nthawi ya Ophunzila Baibulo, akulu anali kudziŵa kuti ali ndi udindo wothandiza okhulupilila anzao kupitilizabe kutumikila Mulungu. (Ŵelengani Agalatiya 6:10.) Mu 1908, nkhani inayake ya mu Nsanja ya Mlonda yacingelezi, inafotokoza malangizo a Yesu akuti: “Weta ana a nkhosa anga.” (Yoh. 21:15-17) Nkhaniyo inalangiza akulu kuti: “N’kofunika kuti tiziona nchito imene Ambuye anatipatsa yosamalila nkhosa kukhala yofunika kwambili pa umoyo wathu, ndi kuona kuti ndi mwai wamtengo wapatali kudyetsa ndi kuweta otsatila a Ambuye.” Magazini ina ya The Watch Tower ya mu 1925, inagogomezelanso kufunika kocita ubusa pamene inakumbutsa akulu kuti: “Chalichi ndi ca Mulungu, . . . ndipo onse amene amatumikila abale adzayenela kuyankha mlandu kwa iye.”

17. Kodi oyang’anila akhala akuthandizidwa bwanji kuti akhale abusa abwino?

17 Kodi gulu la Yehova lathandiza bwanji akulu kunola maluso ao monga abusa? Akuluwo akhala akupatsidwa maphunzilo. Mu 1959, Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ya akulu inayamba. Nkhani inayake imene inaphunzilidwa panthawi ya sukuluyo inali ndi mutu wakuti, “Kuthandiza Munthu Aliyense Payekha.” Akulu analimbikitsidwa “kupanga ndandanda yoyendela abale ndi alongo kunyumba zao.” Nkhaniyo inasonyeza njila zosiyanasiyana za mmene abusa angapangile maulendo ao kukhala olimbikitsa. Mu 1966, Sukulu ya Utumiki wa Ufumu yatsopano inayamba. Sukuluyo inali ndi nkhani yakuti “Kufunika kwa Nchito ya Ubusa.” Kodi mfundo yaikulu ya nkhaniyo inali yotani? Nkhaniyo inafotokoza kuti abale amene akutsogolela “ayenela kutengako mbali pa nchito yosamalila nkhosa za Mulungu, koma sayenela kunyalanyaza mabanja ao ndiponso ulaliki wakumunda.” M’zaka za posachedwapa, pakhalanso masukulu ena a akulu. Kodi pakhala mapindu otani cifukwa ca maphuzilo amene gulu la Yehova lakhala likupeleka? Masiku ano, mumpingo wacikritsu muli abale ambilimbili oyenelela amene akutumikila monga abusa akuuzimu.

Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ku Philippines, mu 1966

18. (a) Ndi udindo waukulu uti umene akulu apatsidwa? (b) N’cifukwa ciani Yehova ndi Yesu amakonda kwambili akulu amene amagwila nchito mwakhama?

18 Yehova kupyolela mwa Mfumu yathu, Yesu, ndi amene anapanga makonzedwe akuti pampingo pazikhala akulu kuti azigwila nchito yofunika. Nchito yotani? Nchito yotsogolela nkhosa za Mulungu m’nthawi yovuta kwambili ino. (Aef. 4:11, 12; 2 Tim. 3:1) Yehova ndi Yesu amakonda kwambili akulu amene amagwila nchito yao mwakhama cifukwa cakuti abalewo amamvela lamulo la m’Malemba lakuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu . . . mofunitsitsa . . . , ndi mtima wonse . . . , mukhale zitsanzo kwa gulu la nkhosa.” (1 Pet. 5:2, 3) Tiyeni tsopano tikambilane njila ziŵili zokha za mmene abusa acikristu alili zitsanzo kwa gulu la nkhosa ndi mmene amathandizila kuti mumpingo mukhale mtendele ndi cimwemwe.

Mmene Akulu Amawetela Nkhosa za Mulungu Masiku Ano

19. Kodi timamva bwanji akulu akamapita nafe mu ulaliki?

19 Coyamba, akulu amalalikila ndi anthu osiyanasiyana mumpingo. Ponena za Yesu, wolemba Uthenga Wabwino Luka anati: “Yesu anayamba ulendo woyenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi. Ulendowu unali wokalalikila ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu. Ndipo atumwi 12 aja anali naye limodzi.” (Luka 8:1) Monga mmene Yesu anali kulalikila limodzi ndi atumwi ake, akulu acitsanzo cabwino naonso amagwila nchito yolalikila limodzi ndi Akristu anzao. Akuluwo amadziŵa kuti kucita zimenezi kumathandiza kuti mpingo ulimbe. Nanga anthu ena mumpingo amawaona bwanji akulu acitsanzo cabwino amenewo? Mlongo wina dzina lake Jeannine, amene ali ndi zaka za m’ma 80, anati: “Kugwila nchito yolalikila limodzi ndi mkulu kumandipatsa mpata woceza naye ndi kum’dziŵa bwino kwambili.” M’bale wina dzina lake Steven, wa zaka za m’ma 30, anati: “Mkulu akagwila nane nchito yolalikila khomo ndi khomo, ndimaona kuti akufuna kundithandiza. Ndikalandila thandizo lake, ndimasangalala kwambili.”

Monga mmene m’busa amapitila kukafunafuna nkhosa yotayika, naonso akulu amacita khama kuti apeze anthu amene anasiya kuyanjana ndi mpingo

20, 21. Ndi citsanzo cotani cimene akulu angatengele kwa m’busa wa m’fanizo la Yesu? Pelekani citsanzo. (Onani bokosi lakuti “ Maulendo Aubusa Aphindu.”)

20 Caciŵili, gulu la Yehova laphunzitsa akulu kuti azithandiza anthu amene anasiya kuyanjana ndi mpingo. (Aheb. 12:12) N’cifukwa ciani akulu ayenela kuthandiza anthu ofooka mwakuuzimu, ndipo ayenela kuwathandiza bwanji? Timapeza yankho la funsoli m’fanizo la Yesu la m’busa ndi nkhosa yotaika. (Ŵelengani Luka 15:4-7.) Pamene m’busa wa m’fanizoli anazindikila kuti nkhosa ina palibe, iye anayamba kuifunafuna monga kuti ndi nkhosa yokhayo imene anali nayo. Kodi akulu acikristu masiku ano angatengele bwanji citsanzo ca m’busa ameneyo? Monga mmene nkhosa yotaika imakhalilabe yofunika kwa m’busa, akulu naonso amaona kuti anthu amene anasiya kuyanjana ndi gulu la Mulungu ndi ofunikabe. Iwo amaona kuti anthu otelo ndi nkhosa zotaika, ndipo ndi ofunikadi kuwathandiza. Ndiponso, monga mmene m’busa amapitila “kukafunafuna [nkhosa] imodzi yotayikayo kufikila ataipeza,” naonso akulu amacita zonse zimene angathe kuti apeze anthu ofooka ndi kuwathandiza.

21 Kodi m’busa wa m’fanizo la Yesu anacita ciani atapeza nkhosa yotaikayo? Iye anainyamula mwacikondi ndi kuiika “paphewa pake,” ndipo anapita nayo kumene kunali nkhosa zina zija. Mofananamo, cikondi cimene mkulu angasonyeze munthu wofooka, cingamulimbikitse kubwelela mumpingo. M’bale wina mu Africa muno dzina lake Victor, anathandizidwapo ndi akulu pamene anasiya kuyanjana ndi mpingo. Iye anati: “Kwa zaka zonse 8 zimene ndinakhala wozilala, akulu sanaleke kundithandiza.” Kodi n’ciani cinam’khudza mtima kwambili mbaleyu? Iye anati: “Tsiku lina, mkulu wina amene ndinaloŵa naye pamodzi Sukulu ya Apainiya, dzina lake John, anandicezela. Iye anandionetsa zithunzi zimene anajambula panthawi imene tinali ku sukulu ya apainiya. Zithunzizo zinandikumbutsa zinthu zambili zabwino cakuti ndinayamba kulakalaka nditakhalanso ndi cimwemwe cimene ndinali naco pamene ndinali kutumikila Yehova.” Victor anayambanso kuyanjana ndi mpingo patangopita nthawi yocepa pambuyo pocezeledwa ndi John. Masiku ano, Victor akutumikilanso monga mpainiya. Ndithudi, akulu amene amadela nkhawa anthu ena amatipangitsa kukhala osangalala.—2 Akor. 1:24. *

Uyang’anilo Wabwino Umalimbikitsa Mgwilizano wa Anthu a Mulungu

22. Kodi cilungamo ndi mtendele zimalimbikitsa bwanji mgwilizano mumpingo wacikristu? (Muonenso bokosi lakuti “ Tinacita Cidwi Kwambili.”)

22 Monga mmene taonela poyamba, Yehova ananenelatu kuti cilungamo ndi mtendele zidzaculuka pakati pa anthu a Mulungu. (Yes. 60:17) Makhalidwe aŵili amenewa amapangitsa kuti mpingo ukhale wogwilizana. Motani? Pa nkhani yokhudza cilungamo, “Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.” (Deut. 6:4) Mipingo yonse padziko lapansi imatsatila mfundo za Mulungu za cilungamo zofanana. Mfundo zake pa cabwino ndi coipa n’zofanana, ndipo sizimasiyana “m’mipingo yonse ya oyelawo.” (1 Akor. 14:33) Motelo, tikamatsatila mfundo za Mulungu, mipingo imapita patsogolo. Ndipo ponena za mtendele, Mfumu yathu imafuna kuti tizisangalala ndi mtendele mumpingo, komanso kuti tikhale “anthu amene amabweletsa mtendele.” (Mat. 5:9) Conco, timatsatila “zinthu zobweletsa mtendele.” Izi zikutanthauza kuti timayamba ndife kuthetsa kusiyana maganizo kumene kungakhalepo pakati pathu nthawi zina. (Aroma 14:19) Mwakutelo, timathandiza kuti mumpingo mukhale mtendele ndi mgwilizano.—Yes. 60:18.

23. N’ciani cimene tikusangalala naco masiku ano monga atumiki a Yehova?

23 Mu November 1895, pamene magazini ya Watch Tower inalengeza kuti pampingo pazikhala akulu, abale audindo naonso anasonyeza mtima wofuna kucilikiza makonzedwe amenewo. Kodi anasonyeza bwanji zimenezo? Iwo anapemphela kuti makonzedwe atsopanowo athandize anthu a Mulungu kuti “agwilizane mofulumila pa cikhulupililo.” Tikakumbukila mmene zinthu zinali kuyendela m’nthawi za kumbuyo, timayamikila mmene Yehova kupyolela mwa Mfumu yathu wakhala akusinthila zinthu. Kusintha kumeneko kwapangitsa kuti tikhale ogwilizana pa kulambila kwathu. (Sal. 99:4) Masiku ano, anthu onse a Yehova padziko lapansi, amasangalala pamene akuyenda “mumzimu umodzi,” kutsatila “m’mapazi amodzimodzi,” ndi kutumikila “Mulungu wamtendele” “mogwilizana.”—2 Akor. 12:18; ŵelengani Zefaniya 3:9.

^ par. 11 Zimene anapeza atacita kafukufuku ameneyo zinafalitsidwa m’buku la Aid to Bible Understanding.

^ par. 21 Onani nkhani yakuti “Akulu Achikhristu ndi Antchito Anzathu Otipatsa Chimwemwe,” imene ili mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2013, tsamba 27-31.