Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 11

Kuyenga Anthu a Mulungu Mwamakhalidwe—Kuonetsa Ciyelo ca Mulungu

Kuyenga Anthu a Mulungu Mwamakhalidwe—Kuonetsa Ciyelo ca Mulungu

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Mmene Mfumu yaphunzitsila nzika zake kulemekeza mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino

Yelekezelani kuti mukuloŵa pacipata ca bwalo lakunja la kacisi waukulu wauzimu wa Yehova

1. N’ciani cimene Ezekieli anaona cimene cimaticititsa cidwi?

KODI mukanatani mukanaona masomphenya monga amene mneneli Ezekieli anaona zaka 2500 zapitazo? Tayelekezelani kuti mukuyandikila kacisi wamkulu ndi wokongola, ndipo mngelo wamphamvu ali nanu limodzi kuti akusonyezeni kacisi wocititsa cidwi ameneyo. Ndiyeno mukukwela masitepe 7 opita ku cimodzi ca zipata zitatu za kacisiyo. Mutaona zipatazo mukucita cidwi kwambili cifukwa ndi zazitali, pafupifupi mamita 30. Mutangoloŵa pacipataco, mukuona zipinda za alonda zimene zili capafupi. Mukuonanso zithunzi zokongola za mitengo ya kanjedza zozokotedwa kuzipilala za kacisiyo.—Ezek. 40:1-4, 10, 14, 16, 22; 41:20.

2. (a) Kodi masomphenya a kacisi amaimila ciani? (Onaninso mau amunsi.) (b) N’ciani cimene tingaphunzilepo pa zinthu zimene zinali capafupi ndi zipata za kacisiyo?

2 Awa anali masomphenya a kacisi wauzimu. Ezekieli anafotokoza momveka bwino kwambili za kacisi ameneyu moti nkhani yonena za kacisiyu inalembedwa kuyambila caputala 40 mpaka 48 m’buku laulosi lochedwa ndi dzina lake. Kacisiyu amaimila makonzedwe a Yehova a kulambila koyela. Zinthu zonse za m’kacisiyo zili ndi tanthauzo pa kulambila kwathu masiku otsiliza ano. * Kodi zipata zomwe zinali pamwamba m’kacisiyo zimatanthauzanji? Zimatikumbutsa kuti anthu amene afuna kugwilizana ndi makonzedwe a Yehova a kulambila koyela, ayenela kutsatila mfundo zapamwamba ndi zolungama za Mulungu paumoyo wao. Zithunzi za mitengo ya kanjedza zozokota nazonso zimatikumbutsa mfundo yomweyi, cifukwa cakuti m’Baibulo nthawi zina mtengo wa kanjedza umaimila cilungamo. (Sal. 92:12) Nanga zipinda za alonda zimasonyezanji? Zimasonyeza kuti anthu amene salemekeza mfundo za Mulungu samaloledwa kuloŵa m’kacisi wauzimu wokongola ameneyu amene adzathandiza anthu kudzapeza moyo.—Ezek. 44:9.

3. N’cifukwa ciani otsatila a Kristu amafunikabe kuyengedwa?

3 Kodi masomphenya a Ezekieli akwanilitsidwa bwanji masiku ano? Monga mmene tinaonela m’Nkhani 2 m’buku lino, Yehova anagwilitsila nchito Kristu kuyenga anthu ake m’njila yapadela kuyambila mu 1914 mpaka kuciyambi kwa 1919. Kodi kuyengako kunathela pomwepo? Ayi ndithu. Pa zaka 100 zapitazi, Kristu wapitilizabe kucilikiza mfundo zolungama za Yehova za makhalidwe abwino. Conco, otsatila ake akhala akufunikabe kuyengedwa. Tikutelo cifukwa Kristu wakhala akusonkhanitsa otsatila ake kucoka m’dziko la makhalidwe oipa, ndipo Satana sanaleke kuwakopa kuti ayambilenso kucita zoipa. (Ŵelengani 2 Petulo 2:20-22.) Tiyeni tsopano tikambilane mbali zitatu za mmene Akristu oona ayeletsedwela pang’onopang’ono. Coyamba, tikambilana mmene io ayengedwela kuti akhale ndi makhalidwe abwino, kenako tikambilana za njila yofunika imene imathandiza mpingo kukhalabe woyela. Pomaliza, tikambilana mmene anthu a Mulungu athandizidwila kukhala ndi maganizo oyenela okhudza banja.

Anthu a Mulungu Akhala Akuyengedwa kuti Akhale ndi Makhalidwe Abwino

4, 5. Ndi msampha uti umene Satana wakhala akugwilitsila nchito kwa zaka zambili? Nanga zotsatila zake zakhala zotani?

4 Kuyambila kale, anthu a Yehova akhala akuyesetsa kukhala ndi makhalidwe abwino. Iwo akhala akutsatila malangizo osapita m’mbali okhudza makhalidwe abwino amene amapatsidwa. Onani zitsanzo zingapo.

5 Ciwelewele. Yehova amafuna kuti kugonana kuzikhala kwa anthu okwatilana ndiponso kuti kuzicitika moyenela. Satana amasukulutsa mphatso yamtengo wapatali imeneyi yocokela kwa Mulungu, ndipo akuigwilitsila nchito monga nyambo kuti anthu a Yehova aononge ubwenzi wao ndi Mulungu. M’masiku a Balamu, Satana anagwilitsila nchito ciwelewele kukopa anthu a Mulungu, ndipo zotsatila zake zinali zoopsa. M’masiku otsiliza ano, iye akugwilitsilanso nchito kwambili ciwelewele kuti akole anthu a Mulungu.—Num. 25:1-3, 9; Chiv. 2:14.

6. Ndi lumbilo liti limene linafalitsidwa m’magazini ya Watch Tower, ndipo anali kuligwilitsila nchito bwanji? Nanga n’cifukwa ciani pambuyo pake abale analeka kuligwilitsila nchito? (Onani mau amunsi.)

6 Pofuna kugonjetsa zoyesayesa za Satana, m’magazini ya Watch Tower ya June 15, 1908, munali lumbilo lakuti: “Nthawi zonse ndiponso pamalo alionse, ndizicita zinthu mwaulemu ndi munthu amene si mwamuna kapena mkazi wanga. Ndizicita naye zinthu mwaulemu monga mmene ndingacitile ndikakhala naye pagulu.” * Ngakhale kuti lumbilo limeneli silinali lamulo, anthu a Mulungu ambili anayamba kulisunga, ndipo analembetsa maina ao kuti afalitsidwe m’magazini ya Zion’s Watch Tower posonyeza kuvomeleza lumbilo limenelo. Poyamba lumbiloli linali lothandiza, koma m’kupita kwa zaka, abale ambili anayamba kuliona mwamwambo cabe. Motelo anasiya kulumbila, koma io anapitiliza kutsatila mfundo zapamwamba za makhalidwe abwino zimene zinali maziko a lumbiloli.

7. Kodi Nsanja ya Mlonda ya mu 1935 inafotokoza vuto liti? Nanga magaziniyo inagogomezela mfundo yotani?

7 Komabe Satana anapitilizabe kuyesa anthu a Mulungu. Nsanja ya Mlonda yacingelezi ya March 1, 1935, inafotokozanso momveka bwino za vuto limene linayamba kufala pakati pa anthu a Mulungu. Iwo anayamba kuganiza kuti malinga ngati alalikilabe, akhoza kunyalanyaza mfundo za Yehova za makhalidwe abwino pa umoyo wao. Magaziniyo inanena mosapita m’mbali kuti: “Aliyense afunika kukumbukila kuti kulalikila kokha si kokwanila. Mboni za Yehova zimaimila Mulungu, ndipo zili ndi udindo woimila Yehova ndi ufumu wake moyenelela.” Kenako, nkhaniyo inapeleka malangizo omveka bwino okhudza ukwati ndi kugonana. Malangizowo anathandiza anthu a Mulungu ‘kuthawa dama.’—1 Akor. 6:18.

8. N’cifukwa ciani Nsanja ya Mlonda yakhala ikugogomeza tanthauzo lenileni la liu Lacigiriki lakuti por·neiʹa?

8 Pa zaka zaposacedwapa, Nsanja ya Mlonda yakhala ikufotokoza mobwelezabweleza tanthauzo lenileni la liu lacigiriki lakuti por·neiʹa limene limamasulidwa kuti ciwelewele. Liuli silimangotanthauza kugonana kokha. M’malomwake, liu lakuti por·neiʹa limaphatikizapo makhalidwe onse onyansa amene amacitika m’nyumba zamahule. Mfundo zimenezi zathandiza otsatila a Kristu kukhala otetezeka kuti asatengele khalidwe loipa laciwelewele limene lafala kwambili m’dzikoli.—Ŵelengani Aefeso 4:17-19.

9, 10. (a) Kodi Nsanja ya Mlonda ya mu 1935 inafotokoza vuto liti? (b) Kodi Baibulo limati ciani pankhani ya kumwa mowa?

9 Kumwa mwaucidakwa. Nsanja ya Mlonda yacingelezi ya March 1, 1935, inafotokoza vuto lina limene anthu a Mulungu anali nalo. Magaziniyo inati: “Zaoneka kuti ena amalalikila ndi kusamalila maudindo ena m’gulu atamwa [mowa]. Kodi Malemba amalola kumwa mowa pamlingo wotani? Kodi n’zoyenela kuti munthu amwe mowa mpaka kufika posokoneza utumiki wake m’gulu la Ambuye?”

10 Poyankha mafunso amenewa, magaziniyo inafotokoza mfundo za m’Mau a Mulungu zokhudza kamwedwe ka mowa. Baibulo silimaletsa kumwa vinyo ndi zakumwa zina zoledzeletsa pamlingo woyenelela, koma limaletsa mwamphamvu kumwa mwaucidakwa. (Sal. 104:14, 15; 1 Akor. 6:9, 10) Pankhani yakuti munthu sayenela kucita zinthu zokhudza kulambila atamwa mowa, atumiki a Mulungu akhala akukumbutsidwa za nkhani ya ana a Aroni. Iwo anaphedwa ndi Mulungu cifukwa copeleka zofukiza pamoto wosaloledwa pa guwa lansembe la Mulungu. Nkhaniyi imaonetsa cimene cinapangitsa kuti ana a Aroni acite zinthu zosayenela zimenezi cifukwa mwamsanga izi zitacitika, Mulungu anapeleka lamulo loletsa ansembe onse kumwa mowa pogwila nchito pakacisi. (Lev. 10:1, 2, 8-11) Masiku ano, otsatila a Kristu amatsatila mfundo imeneyi, ndipo amaonetsetsa kuti sakucita zinthu zokhudza kulambila atamwa mowa.

11. N’cifukwa ciani n’zothandiza kuti anthu a Mulungu akhala akulandila malangizo oonjezeleka okhudza vuto la ucidakwa?

11 Pa zaka zaposacedwapa, otsatila a Kristu aphunzila zambili zokhudza vuto la ucidakwa. Ucidakwa ndi cizoloŵezi coipa cokonda kumwa mowa mopambanitsa. Cifukwa ca malangizo a panthawi yake amene timalandila, ambili akwanitsa kugonjetsa cizoloŵezi coipaci. Malangizowa athandizanso anthu ambili kupewelatu vutoli. Aliyense ayenela kupewa cizoloŵezi cimeneci kuti asadzicotsele ulemu, asasokoneze banja lake, ndiponso koposa zonse, kuti asataye mwai wake wolambila Yehova.

“N’zosatheka kuganizila Ambuye akumveka fungo la fodya kapena kudya cinthu ciliconse codetsa.”—C. T. Russell

12. Ngakhale masiku otsiliza asanayambe, kodi atumiki a Kristu anali kuciona bwanji cizoloŵezi cogwilitsila nchito fodya?

12 Kugwilitsila nchito fodya. Masiku otsiliza asanayambe, atumiki a Kristu anali kuona kuti kugwilitsila nchito fodya n’kulakwa. Kalekale m’bale wina wacikulile dzina lake Charles Capen, anafotokoza zimene zinacitika pamene anakumana ndi M’bale Charles Taze Russell nthawi yoyamba cakumapeto kwa zaka za m’ma 1800. Panthawiyo M’bale Capen anali ndi zaka 13, ndipo iye pamodzi ndi abale ake atatu, anali pa masitepe ku Beteli yochedwa Nyumba ya Baibulo ku Allegheny, Pennsylvania. Pamene M’bale Russell anali kudutsa anawafunsa kuti: “Kodi anyamatanu mukusuta? Ndikumva fungo la fodya.” Iwo anamutsimikizila kuti sakusuta. Pamenepo, io anadziŵa kuti M’bale Russell anali kuona kuti kusuta n’koipa. M’magazini ya Watch Tower ya August 1, 1895, M’bale Russell anathilila ndemanga pa lemba la 2 Akorinto 7:1. Iye anati: “Ndikuona kuti ngati Mkristu amagwilitsila nchito fodya, Mulungu sangalandile ulemelelo kapena kusangalala nazo.  . . N’zosatheka kuganizila Ambuye akumveka fungo la fodya kapena kudya cinthu ciliconse codetsa.”

13. Ndi mfundo zina ziti zokhudza makhalidwe zimene zinafotokozedwa bwino m’caka ca 1973?

13 Mu 1935, Nsanja ya Mlonda yacingelezi inanena kuti fodya uli monga “udzu woipa wa kaufiti,” ndipo inafotokoza kuti aliyense amene anali kutafuna kapena kusuta fodya sangaloledwe kupitiliza kutumikila pa Beteli kapena kuimila gulu la Mulungu monga mpainiya kapena woyang’anila woyendela. M’caka ca 1973 kunafalitsidwanso mfundo zina zomveka bwino zokhudza nkhaniyi. M’cakaco, Nsanja ya Olonda ya June 1 inafotokoza kuti Mboni iliyonse ya Yehova imene sikufuna kusiya cizoloŵezi covulaza, codetsa, ndi copanda cikondi cimeneci, sidzaloledwa kukhala mumpingo. Anthu amene sanafune kuleka kugwilitsila nchito fodya anayenela kucotsedwa mumpingo. * Mwanjilayi, Kristu anacitanso cinthu cina cofunika kwambili kuti ayeletse otsatila ake.

14. Kodi malangizo a Mulungu pankhani ya kugwilitsila nchito magazi ndi otani? Nanga cizoloŵezi coika anthu magazi cinafala bwanji?

14 Kugwilitsila nchito magazi molakwika. M’nthawi ya Nowa, Mulungu ananena kuti kudya magazi n’kulakwa. Mulungu anafotokozanso mfundo imeneyi m’Cilamulo cimene anapatsa mtundu wa Aisiraeli. Kenako, iye analamulanso Akristu kuti ayenela “kupewa . . . magazi.” (Mac. 15:20, 29; Gen. 9:4; Lev. 7:26) Masiku ano, Satana wapangitsa anthu ambili kuphwanya lamulo la Mulungu limeneli. M’zaka za m’ma 1800, madokotala anayamba kuyesa kuika anthu magazi monga mankhwala. Ndipo pamene anatulukila mitundu yosiyanasiyana ya magazi, cizoloŵezi coika magazi cinafala kwambili. Mu 1937, magazi anayamba kusungidwa kumalo osungila magazi, ndipo Nkhondo Yaciŵili Yapadziko Lonse inapangitsa kuti cizoloŵezi cimeneci cikule. Patangopita nthawi yocepa, cizoloŵezici cinafala kwambili padziko lonse lapansi.

15, 16. (a) Kodi Mboni za Yehova zinalimba mtima bwanji pankhani yokhudza kuika magazi? (b) Ndi thandizo lotani limene otsatila a Kristu amapatsidwa pankhani ya kuika magazi ndi kupeleka thandizo popanda kugwilitsila nchito magazi? Nanga zotsatilapo zake zakhala zotani?

15 Kalekale m’caka ca 1944, Nsanja ya Mlonda yacingelezi inasonyeza kuti kuikidwa magazi ndi cimodzimodzi ndi kudya magazi. M’caka cotsatila, mfundo ya m’Malemba imeneyi anaigogomeza ndi kuimveketsa bwino. Podzafika mu 1951, kunafalitsidwa m’ndandanda wa mafunso ndi mayankho okhudza nkhaniyi n’colinga cothandiza anthu a Mulungu kudziŵa mmene angakambile nkhaniyi ndi madokotala. Otsatila okhulupilika a Kristu padziko lonse lapansi anakhalabe olimba mtima pamene anali kunyozedwa, kutsutsidwa kapena kuzunzidwa cifukwa cokana kuikidwa magazi. Koma Kristu anapitilizabe kutsogolela gulu lake kuti lizipeleka thandizo loyenelela pankhaniyi. Conco, gulu linafalitsa tumabuku ndi nkhani zofufuzidwa bwino ndiponso zosavuta kumva zokhudza nkhaniyi.

16 Mu 1979, akulu ena anayamba kupita ku zipatala kuti athandize madokotala kumvetsetsa cifukwa ca m’Malemba cimene timakanila kuikidwa magazi. Iwo anali kuwafotokozelanso za njila zina zothandizila odwala popanda kuwaika magazi. Mu 1980, akulu ocokela m’mizinda 39 ya ku United States anaphunzitsidwa maphunzilo apadela okhudza nchitoyi. M’kupita kwa nthawi, Bungwe Lolamulila linavomeleza kuti padziko lonse lapansi pakhale Makomiti Olankhulana ndi Acipatala. Kodi zimenezi zakhala zothandiza bwanji? Masiku ano, anthu ogwila nchito zacipatala masauzande ambilimbili, kuphatikizapo madokotala a opaleshoni ndi madokotala a zamankhwala oletsa kupweteka pocita opaleshoni, amalemekeza cosankha ca Mboni za Yehova cofuna kulandila thandizo popanda kuikidwa magazi akadwala. Masiku ano, m’zipatala zambili amapeleka cithandizo kwa odwala popanda kuwaika magazi, ndipo ena amaona kuti cimeneci ndi cithandizo cabwino koposa. Kodi sizocititsa cidwi kuona mmene Yesu wakhala akutetezela otsatila ake kwa Satana amene amafuna kuwaipitsa?—Ŵelengani Aefeso 5:25-27.

Masiku ano, m’zipatala zambili amapeleka cithandizo kwa odwala popanda kuwaika magazi, ndipo ena amaona kuti cimeneci ndi cithandizo cabwino koposa

17. Tingaonetse bwanji kuti timayamikila zimene Kristu wakhala akucita poyenga otsatila ake?

17 Motelo tingacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimayamikila zimene Kristu wacita kuti ayeletse otsatila ake mwa kutiphunzitsa kutsatila mfundo zapamwamba za Yehova za makhalidwe abwino?’ Tisaiwale kuti nthawi zonse Satana amafuna kutipangitsa kuti tizinyalanyaza mfundo za Mulungu za makhalidwe abwino n’colinga cakuti aononge ubwenzi wathu ndi Yehova ndi Yesu. Pofuna kutiteteza, gulu la Yehova mwacikondi limaticenjeza ndi kutikumbutsa za kuipa kwa makhalidwe a m’dzikoli. Tiyeni tipitilizebe kukhala maso, kukhala womvela ndi wogonjela ku malangizo othandiza amenewa.—Miy. 19:20.

Kuteteza Mpingo ku Makhalidwe Oipa

18. Kodi masomphenya a Ezekieli amatikumbutsa mfundo iti pankhani ya anthu amene amasiya mwadala kutsatila mfundo za Mulungu?

18 Mbali yaciŵili imene yathandiza anthu a Mulungu kukhala ndi khalidwe loyela ndi zimene gulu limacita pofuna kuti mpingo ukhalebe woyela. N’zomvetsa cisoni kuti ena amene poyamba anali odzipeleka kwa Mulungu ndiponso anali kutsatila mfundo za Yehova za makhalidwe abwino, aleka kuzitsatila. Ena afika pokhala ndi mtima woipa, ndipo mwadala asiya kutsatila mfundo zimenezo. Kodi anthu otelo afunika kucita nao ciani? Masomphenya amene Ezekieli anaona a kacisi wauzimu amene tinakambilana kuciyambi kwa nkhani ino, amatiphunzitsa mfundo ina pankhaniyi. Kumbukilani kuti zipata za kacisiyo zinali pamalo apamwamba, ndipo pacipata ciliconse panali zipinda za alonda. Alonda anali kuteteza kacisiyo kuti anthu ‘osacita mdulidwe wa mtima’ asalowemo. (Ezek. 44:9) Zimenezi zikutikumbutsa kuti kulambila koyela ndi mwai umene umapelekedwa kwa okhawo amene amayesetsa kutsatila mfundo za Yehova za makhalidwe abwino. Mofananamo, si munthu aliyense amene angaloledwe kukhala mumpingo wacikristu.

19, 20. (a) Kodi Kristu wathandiza bwanji otsatila ake kuongolela mmene amasamalila nkhani zokhudza macimo aakulu? (b) Pali zifukwa zitatu ziti zocotsela anthu osalapa mumpingo?

19 Mu 1892, magazini ya Watch Tower inafotokoza kuti “ndi udindo wathu kucotsa (Akristu) amene amakana kuti Kristu anadzipeleka monga dipo [malipilo ofanana] la anthu onse.” (Ŵelengani 2 Yohane 10.) Mu 1904, buku lakuti The New Creation linanena kuti anthu amene saleka khalidwe loipa amafooketsa mpingo. M’masiku amenewo, mpingo wonse unali kutengako mbali “pofufuza” munthu amene wacita chimo lalikulu. Koma zimenezo sizinali kucitika kaŵilikaŵili. Mu 1944, Nsanja ya Mlonda yacingelezi inasonyeza kuti abale audindo okha ndi amene afunika kusamalila macimo aakulu mumpingo. Mu 1952, ndi pamene Nsanja ya Mlonda inafotokoza njila imene iyenela kutsatilidwa posamalila nkhani zaciweluzo mogwilizana ndi Malemba, ndipo inagogomeza cifukwa cacikulu cocotsela anthu osalapa mumpingo. Cifukwa cimeneco n’cakuti mpingo ukhalebe woyela.

20 Kuyambila nthawi imeneyo, Kristu wathandiza otsatila ake kuongolela zina ndi zina pa kasamalidwe ka nkhani zokhudza macimo aakulu. Akulu mumpingo wacikristu amaphunzitsidwa bwino kuti azisamalila nkhani zaciweluzo mwacilungamo ndi mwacifundo mogwilizana ndi mfundo za Yehova. Masiku ano timadziŵa bwino kuti pali zifukwa zitatu zocotsela munthu wosalapa mumpingo: (1) kuti dzina la Yehova lisanyozedwe, (2) kuteteza mpingo kuti usaipitsidwe, ndi (3) kuthandiza munthu wocimwa kuti mwina alape.

21. Kodi makonzedwe ocotsa anthu osalapa mumpingo ateteza bwanji anthu a Mulungu?

21 Kodi mwaona mmene makonzedwe a kucotsa anthu osalapa mumpingo amatetezela otsatila a Kristu masiku ano? M’nthawi ya Aisiraeli, anthu ocita zoipa anali kuipitsa kwambili mtunduwo, ndipo nthawi zina anthu otelo anali kukhala oculuka kwambili kuposa amene anali kukonda Yehova ndi kuyesetsa kucita zabwino. Pa cifukwa cimeneci, kaŵilikaŵili mtunduwo unali kunyozetsa dzina la Yehova ndi kuononga ubwenzi wao ndi iye. (Yer. 7:23-28) Koma masiku ano, Yehova ali ndi gulu la amuna ndi akazi auzimu. Kucotsa anthu osalapa m’gulu lathu kumathandiza kuti Satana asawagwilitsile nchito kuipitsa mpingo ndi kuufooketsa. Conco, io sakhalanso ndi mphamvu yoipitsa mpingo. Zimenezi zimathandiza kuti Yehova apitilize kutikonda tonse monga gulu. Kumbukilani kuti Yehova analonjeza kuti: “Cida ciliconse cimene cidzapangidwe kuti cikuvulaze sicidzapambana.” (Yes. 54:17) Kodi timacilikiza mokhulupilika akulu mumpingo amene ali ndi udindo waukulu wosamalila nkhani zaciweluzo?

Kulemekeza Amene Amapangitsa Banja Lililonse Kukhala ndi Dzina

22, 23. N’cifukwa ciani tiyenela kuwayamikila Akristu anzathu a m’zaka za kuciyambi kwa 1900? Koma n’ciani cimaonetsa kuti io anafunika kusintha mmene anali kuonela banja?

22 Cifukwa cacitatu cimene otsatila a Kristu akhala akuyengedwela ndi cokhudza mmene amaonela cikwati ndi banja. Kodi atumiki a Mulungu asintha mmene amaonela banja pa zaka zapitazi? Inde. Mwacitsanzo, tikamaŵelenga za atumiki a Mulungu amene anali ndi moyo kumayambililo kwa zaka za m’ma 1900, timacita cidwi kwambili ndi mzimu wao wodzimana. Timayamikila kwambili kuti io anali kuika utumiki wopatulika patsogolo pa zinthu zina zonse. Ngakhale zinali conco, io anali kufunika kucita zinthu mosamala kwambili. N’cifukwa ciani tikutelo?

23 Kaŵilikaŵili abale anali kusiya mabanja ao kwa miyezi yambili ndi kupita kumadela akutali kukagwila nchito yolalikila kapena yoyendela mipingo. Mosiyana ndi zimene Malemba amanena, nthawi zina atumiki a Mulungu anali kuphunzitsidwa kuti cikwati ndi cosafunika kwenikweni. Komanso panali nkhani zocepa cabe zimene zinali kufotokoza mmene Akristu angalimbitsile mabanja ao. Kodi otsatila a Kristu akali ndi maganizo amenewa masiku ano? Kutalitali!

Munthu safunika kunyalanyaza udindo wosamalila banja lake n’colinga cakuti atumikile Mulungu

24. Kodi Kristu anathandiza bwanji anthu ake okhulupilika kuti aziona cikwati ndi banja moyenelela?

24 Masiku ano, munthu safunika kunyalanyaza udindo wosamalila banja lake n’colinga cakuti atumikile Mulungu. (Ŵelengani 1 Timoteyo 5:8.) Ndipo Kristu wakhala akuonetsetsa kuti otsatila ake okhulupilika padziko lapansi nthawi zonse akulandila malangizo a m’Malemba othandiza ndi oyenelela okhudza cikwati ndi banja. (Aef. 3:14, 15) Mu 1978, panatuluka buku lakuti Kupangitsa Moyo Wanu wa Banja Kukhala Wachimwemwe. Patapita zaka 18, panatulukanso buku la Chinsinsi cha Chimwemwe cha Banja. Kuonjezela apo, mu Nsanja ya Mlonda mwakhala mukutuluka nkhani zambilimbili zothandiza anthu amene ali pabanja kutsatila mfundo za m’Malemba.

25-27. Kwa zaka zambili, kodi kapolo wokhulupilika wasonyeza bwanji kuti amaganizila kwambili zosoŵa za ana a misinkhu yosiyanasiyana?

25 Nanga bwanji ponena za ana? Kwa zaka zambili gulu la Yehova lasonyeza kuti limaganizilanso zosoŵa za ana. Gululi lakhala likupeleka zinthu zothandiza ana a misinkhu yosiyanasiyana, ndipo masiku ano zinthuzo zaculuka kwambili kuposa kale. Mwacitsanzo, kuyambila mu 1919 mpaka mu 1921, m’magazini ya The Golden Age munali kutuluka nkhani ya mutu wakuti “Juvenile Bible Study.” Pambuyo pake, mu 1920 panatuluka kabulosha kakuti The Golden Age ABC, ndipo mu 1941 kunatuluka buku lakuti Children. M’zaka za m’ma 1970, panatulukanso mabuku ena. Loyamba linali kuchedwa Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuruyo, ndipo lina linali lacingelezi lakuti Your Youth—Getting the Best out of It, ndiponso Buku Langa La Nkhani Za M’baibo. M’caka ca 1982, m’magazini ya Galamukani! munayamba kutuluka nkhani za mutu wakuti “Zimene Achinyamata Amadzifunsa.” Pambuyo pake mu 1989, kapolo anafalitsa buku lochedwa Mayankho a Zimene Achinyamata Amafunsa.

Pa msonkhano wacigawo uwu ku Germany, anthu anasangalala kwambili kulandila kabulosha kakuti Zimene Ndimaphunzila m’Baibo

26 Masiku ano, tili ndi mabuku aŵili atsopano a Zimene Achinyamata Amafunsa, ndipo nkhani zina zofanana ndi za m’mabukuwa, zimapezekanso pa Webu saiti yathu ya jw.org. Tilinso ndi buku lochedwa Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Pa Webu saiti yathu palinso zinthu zambili za ana aang’ono. Zina mwa zinthu zimenezo ndi maseŵela okhudza anthu a m’Baibulo, zoti mucite pophunzila Baibulo, maseŵela ena ofuna kuganiza, mavidiyo, zithunzi zofotokoza nkhani za m’Baibulo, ndi maphunzilo a m’Baibulo a ana a zaka zitatu kapena kucepelapo. N’zoonekelatu kuti Kristu akali kukonda ana monga mmene anacitila m’nthawi ya atumwi pamene anatenga ana m’manja mwake. (Maliko 10:13-16) Iye amafuna kuti ana amene tili nao m’gululi azidzimva kuti amakondedwa ndiponso kuti akudyetsedwa bwino mwakuuzimu.

27 Yesu amafunanso kuti ana azikhala otetezeka. Pamene makhalidwe a anthu akuipilaipila m’dzikoli, vuto locitila nkhanza ana likufala kwambili. Pacifukwa cimeneci, nkhani zomveka bwino ndi zosapita m’mbali zafalitsidwa n’colinga cakuti zithandize makolo kuteteza ana ao kwa anthu ankhanza amenewo. *

28. (a) Mogwilizana ndi masomphenya a Ezekieli a kacisi, tingacite bwanji kuti titenge nao mbali pa kulambila koyela? (b) Kodi inuyo mwatsimikiza mtima kucita ciani?

28 N’zocititsa cidwi kwambili kuona mmene Kristu wakhala akuyengela otsatila ake ndi kuwaphunzitsa kulemekeza ndi kutsatila mfundo zapamwamba za makhalidwe abwino za Yehova, ndiponso mmene io angapindulile cifukwa cotsatila mfundozo. Ganizilaninso za kacisi amene Ezekieli anaona m’masomphenya. Kumbukilani kuti zipata za kacisiyo zinali pamwamba. N’zoona kuti kacisiyo si malo enieni, koma ndi wauzimu. Komabe, kodi timakhulupilila kuti alikodi? Timaloŵa m’kacisiyu osati cabe mwa kupita ku Nyumba ya Ufumu, kungoŵelenga Baibulo kapena kupita muulaliki. Zimenezo ndi zinthu zoti ngakhale munthu wacinyengo angacite popanda kuloŵa m’kacisi wa Yehova. Koma ngati pamene tikucita zinthu zimenezo timatsatilanso mfundo za Yehova za makhalidwe abwino ndi kulambila Mulungu ndi mtima woyela, ndiye kuti taloŵa m’malo opatulikitsa, ndipo tikum’tumikila m’kacisimo. Malowa akuimila kulambila koyela kwa Yehova Mulungu. Tiyeni nthawi zonse tiziyamikila mwai wamtengo wapatali umenewu. Tiyeni tipitilize kucita zimene tingathe poonetsa ciyelo ca Yehova mwa kutsatila mfundo zake zolungama.

^ par. 2 Mu 1932, buku lakuti Vindication Voliyamu 2, linakamba kuti masiku ano maulosi a m’Baibulo okhudza kubwezeletsa anthu a Mulungu kudziko la kwao akukwanilitsidwa pa Isiraeli wauzimu, osati Isiraeli wakuthupi. Maulosi amenewa amakhudza kubwezeletsedwa kwa kulambila koyela. Nsanja ya Olonda ya March 1, 1999, inanena kuti masomphenya a kacisi amene Ezekieli anaona ndi ulosi wonena za kubwezeletsedwa kwa kulambila koona. Pa cifukwa cimeneci kukwanilitsidwa kwake kwakukulu kukucitika masiku otsiliza ano.

^ par. 6 Lumbiloli linali kuletsa mwamuna ndi mkazi kukhala okha m’cipinda, koma pokhapo ngati citseko n’cotsekula kwambili, kapena ngati anthuwo ndi okwatilana kapena ngati anthuwo ndi pacibale. Kwa zaka zingapo, lumbiloli linali kukambidwa pa Kulambila kwa m’Mawa ku Beteli tsiku lililonse.

^ par. 13 Kugwilitsila nchito fodya n’koipa, ndipo kumaphatikizapo kuusuta, kuutafuna, kuufwenkha, ndi kuulima.

^ par. 27 Mwacitsanzo, onani mutu 32 m’buku la Phunzirani kwa Mphunzitsi Waluso. Onaninso Galamukani! ya October 2007 patsamba 3 mpaka 11.