Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 10

Mfumu Iyenga Anthu Ake Mwakuuzimu

Mfumu Iyenga Anthu Ake Mwakuuzimu

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Cifukwa cake Yesu wakhala akuyenga ndi kuyeletsa anthu ake mwakuuzimu, ndi mmene akucitila zimenezi

1-3. N’ciani cimene Yesu anacita pamene anapeza kacisi akudetsedwa?

YESU anali kulemekeza kwambili kacisi wa ku Yerusalemu cifukwa anali kudziŵa zimene kacisiyo anali kuimila. Kwa zaka zambili, kacisi ameneyo anali likulu la kulambila koona padziko lapansi. Koma kulambila Yehova, Mulungu woyela, kuyenela kukhala koyela ndi kosadetsedwa. Ndiyeno taganizilani mmene Yesu anamvelela pa Nisan 10, mu 33 C.E. Iye atafika pa kacisi anapeza kuti kacisiyo wadetsedwa. N’ciani cinacititsa kuti adetsedwe?—Ŵelengani Mateyu 21:12, 13.

2 M’bwalo la anthu akunja, munali amalonda acinyengo ndi osintha ndalama, ndipo anali kudyela masuku pamutu anthu amene anali kubwela ku kacisi kuti apeleke nsembe kwa Yehova. * Mokalipa, Yesu anathamangitsa “onse ogulitsa ndi ogula m’kacisimo, ndipo anagubuduza matebulo a osintha ndalama.” (Yelekezelani ndi Nehemiya 13:7-9.) Iye anadzudzula anthu adyela amenewo amene anasandutsa Nyumba ya Atate ake kukhala “phanga la acifwamba.” Mwakutelo, Yesu anaonetsa kuti amalemekeza kacisi ndi zimene kacisiyo anali kuimila. Kulambila Atate ake kunafunika kukhala koyela.

3 Patapita zaka zambilimbili Yesu ataikidwa kukhala Mfumu Mesiya, iye anayeletsanso kacisi amene masiku ano amaimila anthu onse amene amafuna kulambila Yehova movomelezeka. Kodi kacisi ameneyo ndi uti?

Kuyeletsa “Ana a Levi”

4, 5. (a) Kodi otsatila a Kristu odzozedwa anayengedwa ndi kuyeletsedwa bwanji kuyambila mu 1914 mpaka kuciyambi kwa 1919? (b) Kodi zimenezo zinatanthauza kuti anthu a Mulungu sadzayengedwanso ndi kuyeletsedwanso? Fotokozani.

4 Monga mmene tinaphunzilila mu Nkhani 2 ya buku lino, Yesu atakhala mfumu mu 1914, anabwela ndi Atate wake kudzayendela kacisi wakuuzimu, amene amatanthauza makonzedwe a kulambila koyela. * Atamaliza kuyendelako, Mfumu Mesiya anaona kuti Akristu odzozedwa kapena kuti “ana a Levi,” anali kufunikila kuyengedwa ndi kuyeletsedwa. (Mal. 3:1-3) Kuyambila mu 1914 mpaka kuciyambi kwa 1919, Yehova amene ndi Woyenga, analola kuti anthu ake akumane ndi mayeselo osiyanasiyana ndi zovuta zina n’colinga cakuti awayenge ndi kuwayeletsa. N’zosangalatsa kuti odzozedwa amenewa anapyola bwinobwino m’mayeselo oopsa amenewo, ndipo anakhala oyela, ndi okonzeka kucilikiza Mfumu Mesiya.

5 Kodi zimenezi zinatanthauza kuti anthu a Mulungu sadzayengedwanso ndi kuyeletsedwanso? Iyai. M’masiku otsiliza ano, Yehova kupyolela mwa Mfumu Mesiya akupitilizabe kuthandiza otsatila ake kukhala oyela n’colinga cakuti akhalebe m’kacisi wakuuzimu. M’nkhani ziŵili zotsatila, tidzaphunzila zimene Yesu wakhala akucita kuti ayenge otsatila ake mwa makhalidwe ndiponso kuti awayenge monga gulu. Koma coyamba tiyeni tikambilane za kuyeletsa kwakuuzimu. Cikhulupililo cathu cimalimba kwambili tikaganizila zinthu zooneka ndi zosaoneka zimene Yesu wakhala akucita kuti athandize otsatila ake kukhalabe oyela kuuzimu.

“Khalani Oyela”

6. Kodi malamulo amene Yehova anapatsa Ayuda amene anali mu ukapolo amatithandiza bwanji kudziŵa zimene tiyenela kucita kuti tikhale oyela mwakuuzimu?

6 Kodi kukhala oyela mwakuuzimu kumatanthauza ciani? Kuti tiyankhe funso limeneli, coyamba tiyeni tipende mau amene Yehova anauza Ayuda atatsala pang’ono kutuluka mu ukapolo ku Babulo, mu 537 B.C.E. (Ŵelengani Yesaya 52:11.) Ayudawo anali kubwelela kwao ku Yerusalemu kuti akamangenso kacisi ndi kubwezeletsa kulambila koyela. (Ezara 1:2-4) Yehova anafuna kuti anthu ake asatenge cinthu ciliconse cokhudzana ndi cipembedzo ca ku Babulo. Onani kuti Mulungu anawapatsa malamulo angapo. Iye anati: “Musakhudze cinthu ciliconse codetsedwa,” “cokani pakati pake,” ndi kuti “khalani oyela.” Kulambila koyela kwa Yehova sikuyenela kudetsedwa ndi kulambila konyenga. N’ciani cimene tikuphuzila pamenepa? Kuti tikhale oyela mwakuuzimu, tiyenela kupewa ziphunzitso ndi makhalidwe a zipembedzo zonyenga.

7. Kodi Yesu wakhala akugwilitsila nchito njila iti kuti athandize otsatila ake kukhalabe oyela mwakuuzimu?

7 Atangoikidwa kukhala Mfumu, Yesu anakonza njila imene yathandiza otsatila ake kuti akhale oyela mwakuuzimu. Anacita zimenezi pamene anaika kapolo wokhulupilika ndi wanzelu mu 1919. (Mat. 24:45) Podzafika m’caka cimeneco, Ophunzila Baibulo anali atadziyeletsa kale kuziphunzitso zambili zabodza. Ngakhale zinali conco, io anali kufunika kuyeletsedwa mwakuuzimu. Kupyolela mwa kapolo wake wokhulupilika, Kristu pang’onopang’ono wakhala akuthandiza otsatila ake kupewa miyambo ndi zikondwelelo zoipa. (Miy. 4:18) Tiyeni tikambilane zitsanzo zina.

Kodi Akristu Ayenela Kukondwelela Krisimasi?

8. N’ciani cimene Ophunzila Baibulo anali kudziŵa kuyambila kale cokhudza Krisimasi? Nanga n’ciani cimene io analephela kuona?

8 Kuyambila kale, Ophunzila Baibulo anali kudziŵa kuti Krisimasi inayambila kucikunja ndi kuti Yesu sanabadwe pa December 25. Magazini ya Zion’s Watch Tower ya December 1881 inati: “Anthu ambili amene ali m’chalichi anacokela kucikunja. Koma kusinthako kunali cabe kwa dzina, cifukwa ansembe acikunja anakhala ansembe acikristu, ndiponso maholide acikunja anayamba kuchedwa ndi maina acikristu, mwacitsanzo Krisimasi.” Nkhani ina ya m’magazini ya Watch Tower ya mu 1883 inali ndi mutu wakuti “Kodi Yesu anabadwa liti?” Nkhaniyo inafotokoza kuti Yesu anabadwa kuciyambi kwa October. * Koma panthawiyo, Ophunzila Baibulo sanaone cifukwa colekela kukondwelela Krisimasi. Iwo anapitilizabe kucita cikondwelelo ca Krisimasi, ndipo banja la Beteli la ku Brooklyn linali kucita nao cikondwelelo cimeneci. Koma pambuyo pa caka ca 1926, zinthu zinayamba kusintha. Cifukwa ciani?

9. N’ciani cimene Ophunzila Baibulo anazindikila cokhudza Krisimasi?

9 Pambuyo pakuti ophunzila Baibulo afufuza mosamala kwambili za nkhaniyi, io anazindikila kuti ciyambi ca Krisimasi limodzi ndi zinthu zimene zimacitika panthawiyo sizilemekeza Mulungu. Nkhani imene inatuluka m’magazini ya The Golden Age ya December 14, 1927 yokhala ndi mutu wakuti “Ciyambi ca Krisimasi,” inasonyeza kuti cikondwelelo ca Krisimasi ndi cacikunja, ndipo cimaphatikizapo zisangalalo ndi kulambila mafano. Nkhaniyo inafotokoza bwino kuti Yesu sanatilamule kuti tizicita cikondwelelo cimeneco, ndipo inamaliza ndi mau amphamvu okhudza Krisimasi akuti: “Popeza kuti tadziŵa kuti dziko, anthu ocimwa, ndiponso Mdyelekezi ndi amene akulimbikitsa mwambo umenewu . . . cimeneci ndi cifukwa camphamvu cimene ciyenela kupangitsa anthu onse amene anadzipeleka kucita cifunilo ca Yehova kupewa mwambo umenewo.” Ndiye cifukwa cake banja la Beteli linaleka kucita Krisimasi, ndipo kuyambila mwezi wa December umenewo, silinacitenso cikondwelelo ca Krisimasi.

10. (a) Mu December 1928, ndi malangizo osapita m’mbali ati oonetsa kuipa kwa Krisimasi amene anapelekedwa? (Onani kabokosi ka mutu wakuti “ Ciyambi ca Krisimasi ndi Colinga Cake.”) (b) Kodi anthu a Mulungu anadziŵa bwanji maholide ndi zikondwelelo zimene ayenela kupewa? (Onani bokosi la mutu wakuti “ Kuvumbula Kuipa kwa Maholide Ena ndi Zikondwelelo Zina.”)

10 Caka cotsatila, Ophunzila Baibulo analandilanso malangizo ena ambili oonetsa kuipa kwa Krisimasi. Pa December 12, 1928, M’bale Richard H. Barber, amene anali kugwila nchito kulikulu lathu, anakamba nkhani ya pawailesi imene inaonetselatu poyela kuti ciyambi ca holide imeneyi ndi conyansa. Kodi atumiki a Mulungu analabadila motani malangizo osapita m’mbali ocokela kulikulu amenewo? Pokumbukila nthawi imene M’bale Charles Brandlein ndi banja lake analeka kucita cikondwelelo ca Krisimasi, iye anati: “Ife sitinakhumudwe kuleka kucita zikondwelelo zacikunja zimenezo. . . . Zinali monga tavula covala cakuda ndi kucitaya.” Nayenso M’bale Henry A. Cantwell, amene m’kupita kwa nthawi anadzatumikila monga woyang’anila woyendela ananena kuti: “Tinasangalala kuti tinali okhoza kusiya zinthu zina n’colinga cakuti tionetse kukhulupilika kwathu kwa Yehova.” Otsatila okhulupilika a Kristu anali ofunitsitsa kusintha ndi kuleka kucita cikondwelelo cimene cinayambila ku cipembedzo cabodza. *Yoh. 15:19; 17:14.

11. Tingaonetse bwanji kuti tikucilikiza Mfumu Mesiya?

11 Ophunzila Baibulo amenewa anatisiyila citsanzo cabwino kwambili. Poganizila citsanzo cao cimeneci, tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi malangizo amene ndimalandila kucokela kwa kapolo wokhulupilika ndimawaona bwanji? Kodi ndimawalabadila mopanda kudandaula ndi kugwilitsila nchito zimene ndimaphunzila?’ Ngati timagonjela ndi mtima wonse, timaonetsa kuti timacilikiza Ufumu wa Mesiya amene amagwilitsila nchito kapolo wokhulupilikayo kutipatsa cakudya cakuuzimu ca panthawi yake.—Mac. 16:4, 5.

Kodi Akristu Ayenela Kugwilitsila Nchito Mtanda?

Cizindikilo ca mtanda ndi cisoti cacifumu (Onani ndime 12 ndi 13)

12. Kwa zaka zambili, kodi Ophunzila Baibulo anali kuuona bwanji mtanda?

12 Kwa zaka zambili, Ophunzila Baibulo anali kuona kuti mtanda ndi cizindikilo covomelezeka cacikristu. Koma anali kuona kuti n’kosayenela kulambila mtanda, cifukwa anali kudziŵa kuti kulambila mafano n’kulakwa. (1 Akor. 10:14; 1 Yoh. 5:21) Mu 1883, magazini ya Watch Tower inanena mosapita m’mbali kuti, “Mulungu amanyansidwa ndi kulambila mafano kwa mtundu uliwonse.” Komabe, panthawiyo, Ophunzila Baibulo sanali kuona colakwika ciliconse ndi mmene anali kugwilitsila nchito mtanda. Mwacitsanzo, io monyadila anali kuvala monga baji, cizindikilo ca mtanda ndi cisoti cacifumu cokhala ku kanaphini. Ophunzila Baibulo anali kukhulupilila kuti kuvala cizindikiloco kunali kutanthauza kuti, ngati adzakhala okhulupilika mpaka imfa adzalandila kolona wamoyo. N’cifukwa cake kuyambila mu 1891, cizindikilo ca mtanda ndi cisoti cacifumu cinali kuikidwa pa cikuto ca magazini ya Watch Tower.

13. Ndi malangizo otani amene otsatila a Kristu anapatsidwa okhudza mtanda? (Muonenso bokosi la mutu wakuti “ Kuphunzitsidwa Pango’onopang’ono za Kuipa Kogwilitsila Nchito Mtanda.”)

13 Ophunzila Baibulo anali kukonda kwambili cizindikilo ca mtanda ndi cisoti cacifumu cimeneco. Koma kuyambila ca kumapeto kwa zaka za m’ma 1920, otsatila Kristu pang’onopang’ono anayamba kuphunzitsidwa kuti mtanda ndi wosayenela. M’bale Grant Suiter amene m’kupita kwa nthawi anadzatumikila mu Bungwe Lolamulila anafotokoza za msonkhano umene unacitikila ku Detroit, Michigan, ku United States. Iye anati: “Pamsokhanowo panakambidwa nkhani zimene zinasonyeza kuti cizindikilo ca mtanda ndi cisoti cacifumu n’cosayenela ndiponso n’conyansa.” M’kupita kwa nthawi atumiki a Mulungu anapatsidwanso malangizo ena owonjezeleka okhudza mtanda. Zinali zoonekelatu kuti kugwilitsila nchito mtanda sikunali mbali ya kulambila koyela.

14. Kodi anthu a Mulungu analabadila bwanji malangizo amene anapatsidwa okhudza mtanda?

14 Kodi anthu a Mulungu analabadila bwanji malangizo amene anali kupatsidwa okhudza mtanda? Kodi anapitilizabe kugwilitsila nchito cizindikilo cimeneco cimene anali kukonda kwambili? Mlongo amene watumikila Yehova zaka zambili anati: “Pamene tinadziŵa tanthauzo la cizindikiloco, tinasiya kucigwilitsila nchito. Mlongo wina wokhulupilika wochedwa Ursula Serenco nayenso anati: “Tinadziŵa kuti cizindikilo cimene tinali kuganiza kuti cimaimila imfa ya Ambuye Yesu ndiponso kudzipeleka kwathu monga Mkristu, ndi cacikunja. Tinayamikila kwambili kuti kuwala kunayamba kuunikila panjila yathu mogwilizana ndi lemba la Miyambo 4:18.” Otsatila okhulupilika a Kristu sanali kufuna kutenga nao mbali m’makhalidwe odetsa a zipembedzo zonyenga.

15, 16. Tingaonetse bwanji kuti tikufunitsitsa kuti mabwalo a padziko lapansi a kacisi wakuuzimu a Yehova akhalabe oyela?

15 Masiku ano, ifenso tili ndi maganizo ofanana ndi amenewa. Tikudziŵa kuti Kristu wakhala akugwilitsila nchito kapolo wokhulupilika ndi wanzelu kuthandiza anthu ake kukhala oyela mwakuuzimu. Conco, timagonjela mofulumila tikacenjezedwa kupewa zikondwelelo, miyambo, kapena zocita zina zogwilizana ndi cipembedzo cabodza kudzela m’cakudya cakuuzimu cimene timalandila. Mofanana ndi abale athu amene anali ndi moyo panthawi ya kukhalapo kwa Kristu, ndife ofunitsitsa kuti mabwalo a padziko lapansi a kacisi wakuuzimu a Yehova akhalebe oyela.

16 M’masiku otsiliza ano, Kristu wakhala akucita zinthu zina zosaoneka n’colinga cakuti ateteze mpingo wa anthu a Mulungu kwa anthu amene akufuna kuuononga mwakuuzimu. Kodi wacita bwanji zimenezo? Tiyeni tione.

Kucotsa Anthu “Oipa Pakati pa Olungama”

17, 18. M’fanizo la khoka, kodi zotsatilazi zimatanthauza ciani? (a) kuponya khoka, (b) “kusonkhanitsa nsomba zamitundumitundu,” (c) kusankha nsomba zabwino ndi kuziika m’mitanga, ndi (d) kutaya nsomba zosafunika.

17 Mfumu Yesu Kristu amayang’anila mwachelu mpingo wa anthu a Mulungu padziko lapansi. Yesu ndi angelo akhala akugwila nchito yocotsa anthu oipa pakati pa anthu abwino m’njila zimene ife sitingazindikile. Yesu anafotokoza za nchito imeneyi m’fanizo lake la khoka. (Ŵelengani Mateyu 13:47-50.) Kodi fanizo limeneli limatanthauza ciani?

Khoka limaimila nchito yolalikila Ufumu imene ikucitika m’nyanja ya anthu yophiphilitsila (Onani ndime 18)

18 Kuponya “khoka . . m’nyanja.” Khoka limaimila nchito yolalikila Ufumu imene ikucitika m’nyanja yophiphilitsa ya anthu. ‘Kusonkhanitsa nsomba zamitundumitundu.’ Uthenga wabwino umakopa anthu a mitundu yonse. Ena amasankha kukhala Akristu oona, ndipo ena poyamba amasonyeza cidwi koma amalephela kupanga cosankha cokhala Mkristu. *[26] Kusankha “zabwino ndi kuziika m’mitanga.” Anthu amene afuna kuphunzila coonadi amasonkhanitsidwa ndi kuikidwa m’mipingo imene ili ngati mitanga, ndipo m’mipingomo amalambila Yehova m’njila yoyela. Kutaya nsomba “zosafunika.” M’masiku otsiliza ano, Kristu ndi angelo akhala akucotsa anthu “oipa pakati pa olungama.” * Ndipo cotulukapo n’cakuti anthu a mitima yoipa, kutanthauza anthu amene safuna kusiya zikhulupililo zoipa ndiponso makhalidwe oipa, samaloledwa kudetsa mipingo. *

19. Kodi mumamva bwanji mukaona zimene Kristu wakhala akucita kuti ateteza anthu a Mulungu n’colinga cakuti akhalebe oyela mwakuuzimu?

19 Kodi sizolimbikitsa cikhulupililo kudziŵa kuti Mfumu yathu Yesu Kristu amateteza anthu ake? Ndipo kodi sizolimbikitsa kudziŵa kuti cangu cimene Yesu ali naco pakulambila koona cikali camphamvu kwambili monga mmene cinalili m’nthawi ya atumwi pamene anayeletsa kacisi? Ndife oyamikila kwambili kuti Yesu wakhala akuteteza anthu a Mulungu n’colinga cakuti akhalebe oyela mwakuuzimu. Tikhoza kuonetsa kuti timacilikiza Mfumu ndi Ufumu wake mwa kupewa kugwilizana ndi cipembedzo conama mwa njila iliyonse.

^ par. 2 Ayuda ocokela kutali anali kufunikila kugwilitsila nchito ndalama zovomelezeka kuti apeleke msonkho wapacaka pakacisi, ndipo osintha ndalama anali kulipilitsa anthu ofuna kusinthitsa ndalamawo. Alendowo ayenelanso kuti anali kugula nyama kuti apeleke nsembe. Yesu anacha amalondawo kuti “acifwamba” mwina cifukwa cakuti io anali kubela anthu powalipilitsa ndalama zambili akafuna kusinthitsa ndalama zao kapena kugula nyama.

^ par. 4 Atumiki a Yehova a padziko lapansi amalambila Mulungu m’bwalo lapadziko lapansi la kacisi wake wamkulu wauzimu.

^ par. 8 Nkhani imeneyi inafotokoza kuti deti la m’nyengo yozizila limene anthu ena amati ndi pamene Yesu anabadwa, siligwilizana ndi nkhani ya m’Baibulo imene imafotokoza kuti abusa anali kunja usiku ndi ziweto zao. —Luka 2:8.

^ par. 10 Kalata imene M’bale Frederick W. Franz analemba pa November 14, 1927 inati: “Caka cino sitidzakhala ndi Krisimasi. Banja la Beteli lagamula kuti tisamacite Krisimasi.” Pambuyo pa miyezi ingapo, M’bale Franz analembanso kalata ina. M’kalatayo iye anati: “Ambuye pang’onopang’ono akutiyeletsa kucoka ku zodetsa za Mdyelekezi zimene zili m’machalichi a Babulo.”

^ par. 18 Mwacitsanzo, mu 2013 ciŵelengelo capamwamba ca ofalitsa cinali 7,965,954 ndipo amene anapezeka ku mwambo wapacaka wa Cikumbutso ca imfa ya Kristu anali 19,241,252

^ par. 18 Kucotsa nsomba zabwino pa nsomba zoipa n’kosiyana ndi nchito yolekanitsa nkhosa ndi mbuzi. (Mat. 25:31-46) Kulekanitsa, kapena kuti ciweluzo comaliza ca nkhosa ndi mbuzi, cidzacitika pa cisautso cacikulu. Komabe nthawiyo isanafike, anthu amene ali monga nsomba zoipa angabwelele kwa Yehova ndi kusonkhanitsidwa m’mipingo imene ili ngati mitanga.—Mal. 3:7.

^ par. 18 Pamapeto pake anthu oipa adzaponyedwa m’ng’anjo yamoto yophiphilitsa, imene ikuimila cionongeko ca m’tsogolo.