Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 2

Ufumu Wabadwa Kumwamba

Ufumu Wabadwa Kumwamba

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Mmene Mulungu anathandizila anthu ake kukonzekela kubadwa kwa Ufumu

1, 2. Kodi ndi cocitika capadela koposa citi cimene cinacitikapo m’mbili yonse ya anthu? Ndipo n’cifukwa ciani n’zosadabwitsa kuti anthu sanathe kuona cocitikaci?

KODI mumalakalaka mukanakhalapo panthawi imene zinthu zinasintha kwambili padziko? Ambili akanafuna kutelo. Mukanakhalapo panthawi ya zocitika zapadela, kodi mukanazindikila zimene zinapangitsa kuti zinthuzo zicitike? Mwina simukanazindikila. Nthawi zambili, zocitika zazikulu zimene zimasintha zinthu m’mbili ya anthu, zimacitika anthu ambili asakudziŵa. Komabe zocitikazo zimakhudza anthu ambili.

2 Koma bwanji ponena za cocitika capadela koposa cimene cinacitikapo m’mbili yonse ya anthu? Cocitika cimeneco cinakhudza anthu ambili. Komabe, anthu ambili sanadziŵe zimene zinacitikazo. Cocitika cimeneco ndi kubadwa kwa Ufumu wa Mulungu kumwamba. Ufumu umenewu ndi boma la Mesiya limene Mulungu analonjeza kale-kale. Posacedwapa, bomali lidzaononga dziko loipali. (Ŵelengani Danieli 2:34, 35, 44, 45.) Popeza kuti anthu sanaone kubadwa kwa Ufumuwo, kodi tinganene kuti Yehova sanafune kuti anthu adziŵe za cocitika capedela cimeneci? Kapena kodi iye anakonzekeletsa anthu ake okhulupilika kaamba ka kubadwa kwa Ufumuwo? Tiyeni tikambilane zimenezi.

“Mthenga Wanga . . . Adzandikonzela Njila”

3-5. (a) Ndani anali “mthenga wa pangano” wochulidwa pa Malaki 3:1? (b)  N’ciani cinayenela kucitika “mthenga wa pangano” asanabwele ku kacisi?

3 Kale-kale, Yehova ananenelatu za colinga cake cofuna kuthandiza anthu ake kuti akonzekele kubadwa kwa Ufumu wa Mesiya. Mwacitsanzo, ganizilani ulosi wa pa Malaki 3:1. Ulosiwo umati: “Taonani! Ine nditumiza mthenga wanga ndipo iye adzandikonzela njila. Mwadzidzidzi, Ambuye woona, amene anthu inu mukumufunafuna, adzabwela kukacisi Wake. Adzabwela ndi mthenga wa pangano amene mukumuyembekezela mosangalala. Iye adzabwela ndithu.”

4 Pa kukwanilitsidwa kwa masiku ano kwa ulosi umenewu, kodi Yehova, “Ambuye woona,” anabwela liti kudzayendela anthu amene anali kutumikila m’bwalo la padziko lapansi la kacisi wauzimu? Ulosiwu unanena kuti Yehova adzabwela ndi “mthenga wa pangano.” Kodi mthenga ameneyo ndani? Iye ndi Yesu Kristu, Mfumu Mesiya. (Luka 1:68-73) Monga Mfumu yoikidwa kumene, iye anayendela ndi kuyenga anthu a Mulungu padziko lapansi.—1 Pet. 4:17.

5 Nanga “mthenga” woyamba amene akuchulidwa pa Malaki 3:1 ndani? Mthenga ameneyu anaonekela zaka zambili Mesiya asanakhale Mfumu. Zaka zambili caka ca 1914 cisanafike, kodi ndani amene anakonzela njila Mfumu Mesiya?

6. Ndani anali “mthenga” woyamba amene ananenedwelatu kuti adzakonzekeletsa anthu okhulupilika kaamba ka zocitika za mtsogolo?

6 M’buku lino, tidzapeza mayankho a mafunso monga amenewa mwa kupenda mbili yocititsa cidwi ya anthu a Yehova masiku ano. Mbili imeneyi imaonetsa kuti cakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, kagulu kocepa ka anthu okhulupilika kanaonekela monga Akristu oona pakati pa Akristu onama. Kaguluko kanayamba kuchedwa Ophunzila Baibulo. Amene anali kutsogolela kagulu kameneka anali M’bale Charles. T. Russell ndi anzake. Iwo anali ngati “mthenga” amene analoseledwayo, ndipo anali kutsogolela anthu a Mulungu pa zinthu zauzimu ndi kuwakonzekeletsa kaamba ka zimene zinali kudzacitika mtsogolo. Tiyeni tikambilane zinthu zinai zimene “mthenga” ameneyo anacita pokonzekeletsa anthu a Mulungu.

Kulambila Mulungu m’Coonadi

7, 8. (a) M’zaka za m’ma 1800, ndani amene anayamba kuvumbula ciphunzitso cabodza cakuti moyo sumafa? (b) Ndi ziphunzitso zabodza zina ziti zimene M’bale Charles T. Russell ndi anzake anavumbula?

7 Pamene anali kuphunzila, Ophunzila Baibulo anali kupempha citsogozo ca Yehova. Ndiyeno anali kufufuza mfundo za coonadi zomveka bwino, kuzisonkhanitsa ndi kuzifalitsa. Kwa zaka zambili, anthu a m’Machalichi Acikristu akhala mumdima wauzimu cifukwa ziphunzitso za m’machalichi ao zinayambila kucikunja. Ciphunzitso cochuka mwa ziphunzitso zimenezi ndi ciphunzitso cakuti moyo sumafa. Koma m’zaka za m’ma 1800, ophunzila Baibulo ena akhama anafufuza ciphunzitso cimeneci ndi kuzindikila kuti si cogwilizana ndi Mau a Mulungu. Henry Grew , George Stetson, ndi George Storrs analemba mabuku ndi kuphunzitsa mopanda mantha, ndipo anavumbula ciphunzitso cabodza cocokela kwa Satana cimeneci. * Nchito ya anthu amenewa inathandiza kwambili M’bale C. T. Russell ndi anzake.

8 Kagulu kocepa ka Ophunzila Baibulo kanazindikila kuti ziphunzitso zina zogwilizana ndi ciphunzitso cakuti moyo sumafa, zinalinso zabodza ndi zosamvetsetseka. Zina mwa ziphunzitso zimenezo zinali zakuti anthu onse abwino amapita kumwamba ndiponso kuti Mulungu amalanga anthu oipa ku moto wosatha wa helo. Russell ndi anzake analemba nkhani zambili m’mabuku, timabuku, tumapepala, ndi kufalitsa nkhani za m’Baibulo povumbula mopanda mantha ziphunzitso zabodza zimenezo.

9. Kodi magazini a Zion’s Watch Tower anavumbulula bwanji kuti ciphunzitso ca Utatu n’cabodza?

9 Mofananamo, ophunzila Baibulo anavumbulanso kuti ciphunzitso cofala ca Utatu ndi cabodza. M’caka ca 1887, magazini ya Zion’s Watch Tower inati: “Malemba amafotokoza mosapita m’mbali kuti Yehova ndi wosiyana kwambili ndi Ambuye wathu Yesu. Amafotokozanso bwino unansi umene ulipo pakati pao.” Nkhaniyo inasonyezanso kuti zinali zodabwitsa kuti “ciphunzitso cakuti Mulungu ndi utatu kapena kuti pali milungu itatu mwa Mulungu umodzi cinakhala cofala kwambili. Kufala kwa ciphunzitso cimeneci kukusonyeza kuti mamembala a m’machalichi anali mtulo tofa nato twa kuuzimu pamene mdani anali kuwasokeletsa ndi ciphunzitso cabodza cimeneci.”

10. Kodi magazini a Zion’s Watch Tower anasonyeza bwanji kuti caka ca 1914 cidzakhala capadela?

10 Magazini a Ophunzila Baibulo anali kuchedwa kuti Zion’s Watch Tower and Herald of Christ’s Presence. Dzinalo linasonyeza kuti mbali yaikulu ya magaziniyi inali kufotokoza ulosi wonena za kukhalapo kwa Kristu. Odzozedwa okhulupilika amene anali kugwila nao nchito yolemba magazini imeneyo anazindikila kuti ulosi wa Danieli wonena za “nthawi zokwanila 7” ndi wogwilizana ndi nthawi pamene cifunilo ca Mulungu cokhudza Ufumu wa Mesiya cidzakwanilitsidwa. Kuyambila m’ma 1870, io anali kunena kuti m’caka ca 1914 nthawi 7 zimenezi zidzatha. (Dan. 4:25; Luka 21:24) Ngakhale kuti abale athu panthawiyo sanamvetsetse kwenikweni zimene zidzacitika m’cakaco, io anali kulalikila zimene anali kudziŵa m’madela ambili, ndipo masiku ano timapindula ndi nchito yolalikila coonadi imene anacita.

11, 12. (a) Ndani amene M’bale Russell anayamikila kaamba ka zinthu zimene iye anali kuphunzitsa? (b) Kodi nchito imene M’bale Russell ndi anzake anagwila caka ca 1914 cisanafike inali yofunika motani?

11 M’bale Russell ndi anzake okhulupilika sanafune kudzikweza cifukwa ca kumvetsetsa coonadi cofunika kwambili cimeneci. M’bale Russell anali kuyamikila kwambili anthu ena amene analipo iye asanayambe utumiki umenewo. Koma koposa onse, iye anayamikila kwambili Yehova Mulungu, amene amaphunzitsa anthu Ake zimene afunika kudziŵa panthawi yoyenela. Mwacionekele, Yehova anadalitsa khama la m’bale Russell ndi anzake cifukwa cofufuza ndi kupeza coonadi. Patapita zaka, m’bale Russell ndi anzake anakhala osiyana ndi Machalichi Acikristu.

M’bale Charles Taze Russell ndi anzake anacilikiza coonadi ca m’Baibulo

12 N’zocititsa cidwi kuona nchito imene amuna okhulupilika amenewa anagwila poteteza coonadi cisanafike caka ca 1914. Pambuyo pa zaka zingapo, magazini ya November 1, 1917 ya The Watch Tower and Herald of Christ’s Presence inati: “Anthu mamiliyoni ambili masiku ano ndi omasuka ku ciphunzitso ca moto wa helo ndi ziphunzitso zina zonyenga. . . . Coonadi cinayamba kufalikila kwambili zaka zoposa 40 zapitazo, ndipo cikufalikilabe mpaka cidzadzaza dziko lonse lapansi monga mmene mafunde amadzazila nyanja. Adani a coonadi adzayesa kuimitsa mafunde a coonadi kuti asafalikile padziko lonse lapansi koma adzalephela.”

13, 14. (a) Kodi “mthenga” anathandiza bwanji kukonza njila ya Mfumu Mesiya? (b) Tikuphunzilapo ciani pa zimene abale athu anacita zaka zoposa zapitazo?

13 Taganizilani izi: Kodi anthu a Mulungu akanakonzekela bwanji kukhalapo kwa Kristu akanakhala kuti sanadziŵe kusiyana pakati pa Yesu ndi Atate wake, Yehova? Kunena zoona zikanakhala zovuta. Ndipo io sakanakhala okonzeka akanakhala kuti anali kukhulupilila kuti anthu onse adzalandila moyo wosakhoza kufa. Koma io anadziŵa kuti moyo umenewu ndi mphatso imene imapatsidwa kwa otsatila Kristu owelengeka cabe. Ndiponso io sakanakhala okonzeka ngati anali kukhulupilila kuti Mulungu amazunza anthu ku moto wa helo kwamuyaya. Mosakaikila, “mthenga” anakonzela njila Mfumu Mesiya.

14 Nanga bwanji za ife masiku ano? Kodi tikuphunzila ciani pa zimene abale athu anacita zaka zoposa 100 zapitazo? Ifenso tiyenela kuŵelenga ndi kuphunzila Mau a Mulungu mwakhama. (Yoh. 17:3) Dzikoli limakonda cuma ndipo likusoŵa cakudya cakuuzimu. Koma ife tiyenela kukhala ndi cilakolako cofuna kudya cakudya cakuuzimu kuposa ndi kale lonse.—Ŵelengani 1 Timoteyo 4:15.

“Tulukani mwa Iye Anthu Anga”

15. Kodi Ophunzila Baibulo anazindikila ciani mwa pang’onopang’ono? (Onani mau amunsi.)

15 Ophunzila Baibulo anali kuphunzitsa kuti anthu ayenela kucoka m’zipembedzo zonyenga. M’caka ca 1879, magazini ya Watch Tower anakambapo za “chalichi ca Babulo.” Kodi mau amenewa anali kunena za apapa kapena za Chalichi ca Roma Katolika? Apulotesitanti anali kukamba kuti Babulo wochulidwa mu ulosi wa m’Baibulo ndi Chalichi ca Katolika. Komabe, m’kupita kwa nthawi Ophunzila Baibulo anazindikila kuti “Babulo” wa makono amaphatikizapo machalichi onse acikristu. N’cifukwa ciani anakhulupilila zimenezo? Cifukwa zipembedzo zonse zacikristu zinali kuphunzitsa mabodza amene tachula poyamba paja. * M’kupita kwa nthawi, mabuku athu anayamba kufotokoza mosapita m’mbali zimene anthu onse a m’machalichi a Babulo anayenela kucita.

16, 17. (a) Kodi buku la Millennial Dawn, Voliyamu yacitatu, ndi magazini ya Watch Tower analimbikitsa bwanji anthu kutuluka m’cipembedzo conama? (b) N’ciani cinapangitsa Ophunzila Baibulo kupeputsa macenjezo amenewa? (Onani mau amunsi.)

16 Mwacitsanzo, m’caka ca 1891 buku lakuti Millennial Dawn, Voliyamu yacitatu, linafotokoza kuti Babulo wa makono wakanidwa ndi Mulungu, ndipo linapitiliza kuti: “Machalichi onse Acikristu akanidwa.” Buku limenelo linaonjezela kuti “anthu onse amene sagwilizana ndi ziphunzitso zabodza ndi zocita za Babulo ayenela kutulukamo.”

17 Mu January caka ca 1900, magazini ya Watch Tower anapeleka uphungu kwa anthu amene maina ao anali olembedwabe ku Machalichi Acikristu ndi kupeleka zifukwa zozikhululikila mwakunena kuti “Ndimakonda kwambili coonadi, ndipo ku machalichi ena sindimapitako kaŵilikaŵili.” Koma magaziniyo inafunsa kuti: “Kodi n’zoyenela kuti munthu akhale mbali ya Babulo panthawi imodzimodziyo m’coonadi? Kodi tingati kumeneku ndi kumvela? . . . Kapena kodi Mulungu amakondwela ndi kuvomeleza zimenezi? Ayi ndithu. Munthuyo [membala wa chalichi] anacita pangano ndi chalichi cake, ndipo ayenela kucita zonse zimene anapangana mpaka pamene . . . adzafafanizitsa dzina lake ku chalichi cimeneco poyela.” M’kupita kwa zaka, nkhani imeneyi anaigogomezela kwambili. * Atumiki a Yehova ayenela kuthetselatu mgwilizano uliwonse ndi cipembedzo conyenga.

18. N’cifukwa ciani kunali kofunika kuti anthu atuluke mu “Babulo Wamkulu”?

18 Zikanakhala kuti macenjezo akuti anthu atuluke mu Babulo Wamkulu sanali kupelekedwa nthawi zonse, kodi Kristu monga Mfumu yatsopano yoikidwa ikanakhala ndi atumiki odzozedwa okonzekeletsedwa bwino padziko lapansi? Zimenezi sizikanatheka cifukwa cakuti Akristu okha amene sagwilizana ndi Babulo ndi amene angalambile Yehova “ndi mzimu ndi coonadi.” (Yoh. 4:24) Kodi nafenso tatsimikiza mtima kupewa kugwilizana ndi cipembedzo conyenga? Tiyeni tipitilizebe kumvela lamulo lakuti: “Tulukani mwa iye anthu anga.”—Ŵelengani Chivumbulutso 18:4.

Kusonkhana kuti alambile Mulungu

19, 20. Kodi magazini ya Watch Tower analimbikitsa bwanji anthu a Mulungu kusonkhana pamodzi kuti alambile Mulungu?

19 Ophunzila Baibulo anali kuphunzitsa Akristu anzao kuti ngati n’zotheka, ayenela kusonkhana pamodzi kuti alambile Mulungu. Kwa Akristu oona, kungotuluka m’cipembedzo conyenga sikokwanila. Iwo afunikanso kutenga mbali m’kulambila koona. Kuyambila kalekale, magazini ya Watch Tower akhala akulimbikitsa anthu kuti azisonkhana pamodzi kuti alambile Mulungu. Mwacitsanzo, mu July caka ca 1880, M’bale Russell anafotokoza mmene zinthu zinayendela paulendo wokakamba nkhani m’madela osiyana-siyana. Iye ananena kuti misonkhano yambili imene anapitako inali yolimbikitsa kwambili. Ndiyeno m’bale Russell analimbikitsa anthu onse kuti azitumiza makadi ofotokoza mmene zinthu zinali kuyendela, ndipo zina mwa nkhanizo zinali kulembedwa m’magazini. Kodi panali zotsatilapo zotani? Iye anati: “Tonse tiyenela kudziŵa. . . mmene Ambuye akukudalitsilani pamene mukupitiliza kusonkhana ndi okhulupilila anzanu.”

M’bale Charles Russell pamodzi ndi gulu la Ophunzila Baibulo oyambilila ku Copenhagen, Denmark, mu 1909

20 M’caka ca 1882, m’magazini ya Watch Tower munatuluka nkhani yakuti “Kusonkhana Pamodzi.” Nkhani imeneyo inalimbikitsa Akristu kuti ayenela kumasonkhana kuti “aziphunzitsana ndi kulimbikitsana.” Inafotokozanso kuti: “Zilibe kanthu kaya pamsonkhanopo pali munthu wina wake wophunzila kwambili ndi waluso kapena ai. Aliyense ayenela kubwela ndi Baibulo lake, pepala, ndi pensulo, ndipo ayenela kugwilitsila nchito namlozela mau wa Baibulo . . . mmene angathele kuti apindule. Sankhani nkhani ndi kupempha citsogozo ca Mzimu kuti muimvetsetse. Ndiyeno iŵelengeni, isinkhesinkheni, yelekezelani malemba, ndipo mosakaikila mudzapeza coonadi.”

21. Ndi citsanzo cabwino citi cimene mpingo wa mumzinda wa Allegheny, ku Pennsylvania unapeleka pankhani yosonkhana ndi kucita maulendo aubusa?

21 Likulu la Ophunzila Baibulo linali mu mzinda wa Allegheny, ku Pennsylvania, m’dziko la United States. Akristu kumeneko anali kukonda kusonkhana pamodzi momvela malangizo ouzilidwa a pa Aheberi 10:24, 25. (Ŵelengani.) Patapita nthawi, m’bale wina wacikulile dzina lake Charles Capen anakumbukila mmene zinthu zinali kukhalila akapita ku misonkhano imeneyi pamene anali wacinyamata. Iye analemba kuti: “Ndikukumbukilabe lemba linalake limene linalembedwa pakhoma la Nyumba ya Msonkhano. Lembalo linali lakuti, ‘Mphunzitsi wanu ndi mmodzi yekha, Kristu, ndipo nonsenu ndinu abale.’ Lembali sindinaliiwale mpaka lelo. Pakati pa anthu a Yehova palibe kusiyana pakati pa abusa ndi anthu wamba.” (Mat. 23:8) M’bale Capen sanaiwale misonkhano yopindulitsa, ndi mayanjano abwino amene anali kukhala nao, ndiponso khama la M’bale Russell poweta munthu aliyense mumpingo.

22. Kodi anthu okhulupilika analabadila motani cilimbikitso cakuti azipezeka pa misonkhano yacikristu? Nanga ife tikuphunzilapo ciani?

22 Anthu okhulupilika anatsatila citsanzo ca m’bale Russell ndi Akristu ena ndi kulabadila malangizo amene anali kupelekedwa. Mipingo inakhazikitsidwa m’mizinda ina monga Ohio ndi Michigan. Pambuyo pake mipingo inakhazikitsidwa ku madela ambili a ku North America ndi kumaiko ena. Kodi anthu okhulupilika akanakonzekela kukhalapo kwa Kristu ngati sanaphunzile kumvela malangizo ouzilidwa akuti azisonkhana pamodzi kuti alambile Mulungu? Iyai. Nanga bwanji ife masiku ano? Tiyenela kumapezeka ku misonkhano yacikristu nthawi zonse kuti tilambile Mulungu pamodzi ndi anzathu ndi kulimbikitsana mwakuuzimu.

Kulalikila mwacangu

23. Kodi magazini ya Watch Tower anagogomeza bwanji kuti odzozedwa onse ayenela kukhala alaliki a coonadi?

23 Ophunzila Baibulo anali kuphunzitsa kuti odzozedwa onse ayenela kukhala alaliki a coonadi. M’caka ca 1885, magazini ya Watch Tower inafotokoza kuti: “Tisaiwale kuti membala aliyense wodzozedwa anadzozedwa kuti azilalikila, (Yes. 61:1) kapena kucita utumiki.” Magazini ina ya mu 1888 inali ndi malangizo akuti: Nchito yathu ndi yodziŵikilatu . . . Tikainyalanyaza kapena kulephela kutengako mbali tidzakhala akapolo aulesi. Zimenezi zidzaonetsa kuti ndife osayenela kukhala odzozedwa.”

24, 25. (a) Kodi M’bale Rus­sell ndi anzake anacita ciani kuonjezela pa kulimbikitsa anthu kuti azilalikila? (b) Kodi kopotala wina ananena ciani zokhudza nchito yake?

24 M’bale Russell ndi anzake sanali kulimbikitsa cabe anthu kuti azilalikila. Iwo anayamba kusindikiza tumapepala tochedwa Bible Students’ Tracts (Tumathilakiti twa Ophunzila Baibulo) tumene m’kupita kwanthawi tunayamba kuchedwa Old Theology Quarterly (Ziphunzitso Zakale za Mulungu). Anthu onse amene anali kuŵelenga magazini ya Watch Tower anapatsidwa tumapepala tumenetu kuti azigaŵila anthu ena kwaulele.

Ndi kwanzelu kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndimaona nchito yolalikila kukhala yofunika kwambili paumoyo wanga?

25 Anthu amene anadzipeleka kucita utumiki wakumunda nthawi zonse anali kucedwa Akopotala. M’bale Charles Capen amene tinamuchula poyamba paja anali mmodzi wa Akopotala. Nthawi ina, iye anati: “Ndinali kugwilitsila nchito mapu opangidwa ndi bungwe lofufuza za nthaka ndi miyala la ku United States lochedwa Geological Survey. Mapu amenewa anali kundithandiza kufola bwino gawo langa ku Pennsylvania. Mapuwa anali kusonyeza bwino miseu yonse, ndipo zimenezi zinandithandiza kukwanitsa kuyenda ulendo wapansi kumadela onse m’gawo langa. Pambuyo pozungulila dziko la United States kwa masiku atatu, kutolela maoda a mabuku ochedwa Studies in the Scriptures, ndinali kubweleka hosi [hachi] ndi ngolo kuti ndikapeleke mabukuwa kwa anthu amene anaitanitsa. Kaŵilikaŵili ndinali kugona m’nyumba za alimi a kumeneko. Nthawi imeneyo magalimoto anali asanafale.”

Kopotala. Mphepete mwa ngoloyo muli “Chati ca Zaka”

26. (a) N’cifukwa ciani anthu a Mulungu anafunika kugwila nchito yolalikila kuti akonzekele ulamulilo wa Kristu? (b) Kodi tiyenela kudzifunsa mafunso ati?

26 M’zaka zimenezo, munthu anali kufunika kukhala wolimba mtima ndi wakhama kuti alalikile. Kodi Akristu oona akanakonzekela bwanji kubwela kwa ulamulilo wa Kristu ngati sakanaphunzitsidwa kufunika kwa nchito yolalikila? Zikanakhala zovuta. Ndipo kunena zoona, nchito yolalikila inafunika kukhala cizindikilo cacikulu cosonyeza kukhalapo kwa Kristu. (Mat. 24:14) Atumiki a Mulungu anafunika kuthandizidwa kuti aziona nchito yopulumutsa moyo imeneyo kukhala yofunika kwambili paumoyo wao. Ifenso tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimaona nchito yolalikila kukhala yofunika kwambili paumoyo wanga? Kodi ndimadzimana zinthu zina kuti ndicite zambili pa nchitoyi?’

Ufumu wa Mulungu Wabadwa

27, 28. Kodi mtumwi Yohane anaona ciani m’masomphenya? Nanga Satana ndi ziŵanda zake anamva bwanji pamene Ufumu wa Mulungu unabadwa?

27 Patapita nthawi yaitali, caka capadela ca 1914 cinafika. Monga mmene takambila kuciyambi kwa nkhani ino, palibe munthu amene anaona zinthu zocititsa cidwi zimene zinali kucitika kumwamba. Komabe, mtumwi Yohane anaona masomphenya osonyeza zimene zinali kucitika kumwamba. Iye anaona “cizindikilo cacikulu” kumwamba. “Mkazi” wa Mulungu, kapena kuti gulu la zolengedwa zauzimu zakumwamba, anali woyembekezela ndipo anabeleka mwana wamwamuna. Malemba amanena kuti posacedwapa mwana wophiphilitsa ameneyu “adzakusa mitundu yonse ndi ndodo yacitsulo.” Mwanayo atangobadwa, “anatengedwa msangamsanga n’kupititsidwa kwa Mulungu ndi kumpando wake wacifumu.” Ndipo kumwamba kunamveka mau ofuula akuti: “Tsopano cipulumutso, mphamvu, ufumu wa Mulungu wathu, ndi ulamulilo wa Khristu wake zafika.”—Chiv. 12:1, 5, 10.

28 Mwacionekele, Yohane anaona masomphenya osonyeza kubadwa kwa Ufumu wa Mesiya. Cocitika cimeneco cinali cosangalatsa kwambili, koma osati kwa aliyense. Satana ndi ziwanda zake anamenyana ndi angelo okhulupilika amene anali kutsogoleledwa ndi Mikayeli kapena kuti Kristu. Kodi zotsatilapo zake zinali zotani? Baibulo limati: “Cinjokaco cinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wochedwa Mdyelekezi ndi Satana, amene akusoceletsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.”—Chiv. 12:7, 9.

M’caka ca 1914, Ophunzila Baibulo anayamba kuona cizindikilo ca kukhalapo kwa Kristu

29, 30. Pamene Ufumu wa Mesiya unabadwa, kodi zinthu zinasintha bwanji (a) padziko lapansi? (b) kumwamba?

29 Zaka zambili caka ca 1914 cisanafike, Ophunzila Baibulo anali kunena kuti caka capadela cimeneci cidzakhala ciyambi ca nthawi ya masautso. Koma io sanadziŵe bwino zimene zidzacitika panthawiyo. Malinga ndi masomphenya amene Yohane anaona, zocita za Satana zinayamba kukhudza kwambili anthu panthawiyo. Baibulo limati: “Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, cifukwa Mdyelekezi watsikila kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziŵa kuti wangotsala ndi kanthawi kocepa.” (Chiv. 12:12) Mu 1914, nkhondo yoyamba ya padziko lonse inayamba, ndipo cizindikilo ca kukhalapo kwa Kristu monga Mfumu cinayamba kukwanilitsidwa padziko lonse. “Masiku otsiliza” a dongosolo lino la zinthu anayambanso m’caka cimeneci.—2 Tim. 3:1.

30 Komabe kumwamba kunali cisangalalo panthawiyo. Satana ndi ziwanda zake anathamangitsidwa kumwamba, ndipo sadzabwelelakonso. Buku la Chivumbulutso limati: “Pa cifukwa cimeneci, kondwelani kumwamba inu ndi inu okhala kumeneko.” (Chiv. 12:12) Popeza kuti kumwamba kunali kutayeletsedwa, ndipo Yesu anali ataikidwa kukhala Mfumu, Ufumu wa Mesiya unali wokonzeka kucitapo kanthu kaamba ka anthu a Mulungu padziko lapansi. Kodi Ufumuwo unacitapo ciani? Monga mmene tinaonela kumayambililo kwa nkhani ino, Kristu monga “mthenga wa pangano” coyamba anayenga atumiki a Mulungu padziko lapansi. Kodi iye anacita bwanji zimenezi?

Nthawi ya Kuyesedwa

31. Kodi Malaki analosela ciani ponena za nthawi yoyenga? Nanga ulosi umenewu unakwanilitsidwa bwanji? (Onani mau amunsi.)

31 Malaki analosela kuti zinthu zidzakhala zovuta panthawi ya kuyenga anthu a Mulungu. Iye analemba kuti: “Ndani adzapilile pa tsiku limene adzabwele? Ndipo ndani adzaime cilili iye akadzaonekela? Iye adzakhala ngati moto wa woyenga zitsulo komanso ngati sopo wa ocapa zovala.” (Mal. 3:2) Mau amenewo anakwanilitsidwadi. Kuyambila m’caka ca 1914, anthu a Mulungu padziko lapansi anakumana ndi ziyeso zazikulu ndi mavuto oopsa motsatizanatsatizana. Pamene nkhondo yoyamba yapadziko lonse inali mkati, Ophunzila Baibulo ambili anazunzidwa mwakhanza ndi kuikidwa m’ndende. *

32. Ndi mavuto otani a mkati mwa gulu amene anavutitsa anthu a Mulungu pambuyo pa 1916?

32 Mkati mwa gulu munalinso mavuto ena. M’bale Russell anamwalila ali ndi zaka 64 mu 1916, ndipo anthu ambili a Mulungu anakhumudwa. Pamene m’baleyu anamwalila, zinaonekelatu kuti anthu ena anali kuika cikhulupililo cao conse mwa m’baleyo. Ngakhale kuti M’bale Russell sanali kufuna kupatsidwa ulemu wopambanitsa, anthu ambili anali kuonetsa kuti anali kumulambila. Pamene M’bale Russell anamwalila, anthu ambili anaganiza kuti panalibenso munthu wina amene akanawaululila mfundo zatsopano za coonadi, ndipo anthu ena anali kutsutsa zimene abale ena anali kucita kuti gulu lipite patsogolo. Zimenezi zinapangitsa kuti pakhale ampatuko amene anagawanitsa gulu.

33. Kodi anthu a Mulungu anayesedwa bwanji pamene zinthu zimene anali kuyembekezela sizinakwanilitsidwe?

33 Ciyeso cina cimene abale anakumana naco cinali cakuti zimene anali kuyembekezela sizinakwanilitsike. Ngakhale kuti magazini ya Watch Tower inali itanenelatu kuti m’caka ca 1914, Nthawi za Anthu Amitundu Ina zidzatha, abale sanali kudziŵa bwino zimene zidzacitika m’caka cimeneco. (Luka 21:24) Iwo anali kuganiza kuti m’caka ca 1914, Kristu adzatenga gulu la Akristu odzozedwa kupita nao kumwamba kuti akalamulile naye. Koma zimenezo sizinacitike. Cakumapeto kwa 1917, magazini ya Watch Tower inafotokoza kuti nchito yokolola ya zaka 40 idzatha cakumayambililo kwa 1918. Koma nchito yolalikila sinathe m’caka cimeneco. Nchitoyi inapitabe patsogolo pambuyo pa cakaco. Magazini ya Watch Tower inanena kuti nchito yokolola inathadi koma nchito yosonkhanitsa inali kupitilizabe. Ngakhale kuti magaziniyo inafotokoza conco, anthu ambili anasiya kutumikila Yehova cifukwa cokhumudwa.

34. Ndi ciyeso coopsa citi cimene cinayamba mu 1918? Nanga n’cifukwa ciani anthu azipembedzo zacikristu anaona monga kuti anthu a Mulungu ndi “akufa”?

34 M’caka ca 1918, panalinso ciyeso cina coopsa. M’bale J. F. Rutherford, amene analowa m’malo mwa M’bale C. T. Russell kuti azitsogolela anthu a Mulungu, anamangidwa limodzi ndi abale ena 7 audindo. Abale ameneŵa anaweluzidwa mopanda cilungamo kuti akhale m’ndende kwa nthaŵi yaitali ndipo anatumizidwa kundende ya mu mzinda wa Atlanta, ku Georgia, m’dziko la United States. Kwa kanthawi, nchito ya anthu a Mulungu inaoneka ngati yaima. Atsogoleli ambili a Machalichi Acikristu anasangalala. Iwo anaganiza kuti Ophunzila Baibulo ovuta aja anali monga anthu “akufa” cifukwa cakuti “atsogoleli” a Ophunzila Baibulo anali m’ndende, likulu lao ku Brooklyn linatsekedwa ndipo nchito yolalikila inali itasokonezedwa ku America ndi ku Ulaya. (Chiv. 11:3, 7-10) Kumeneko kunali kudzinamiza.

Ayambanso Kulalikila Mwacangu

35. N’cifukwa ciani Yesu analola kuti otsatila ake akumane ndi mavuto? Koma kodi iye anacita ciani kuti awathandize?

35 Adani a coonadi sanadziŵe kuti Yesu analola kuti anthu a Mulungu akumane ndi mavuto amenewa cifukwa cakuti panthawiyo Yehova anali ngati “woyenga zitsulo ndiponso ngati woyeletsa siliva.” (Mal. 3:3) Yehova ndi Mwana wake anadziŵa kuti anthu okhulupilika adzapilila ziyeso zoopsa zimenezo, ndipo pambuyo pake adzayeletsedwa, kuyengedwa ndi kukhala okonzekela kutumikila Mfumu. Kuciyambi kwa caka ca 1919, zinali zoonekelatu kuti mzimu wa Mulungu unatheketsa zinthu zimene adani a Mulungu anali kuganiza kuti zinali zosatheka. Anthu okhulupilikawo anapatsidwanso mphamvu. (Chiv. 11:11) Panthawiyo, Kristu anakwanilitsa mbali yofunika kwambili ya cizindikilo ca masiku otsiliza. Iye anasankha “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu,” amene ndi kagulu ka amuna odzozedwa amene amatsogolela anthu ake mwa kuwapatsa cakudya cakuuzimu panthawi yoyenela.—Mat. 24:45-47.

36. N’ciani cinaonetsa kuti anthu a Mulungu ayambanso kulimba kuuzimu?

36 M’bale Rutherford ndi anzake anatulutsidwa m’ndende pa March 26, 1919. Atangotulutsidwa m’ndende, anakonza zakuti mu September caka cimeneco kukhale msonkhano wacigawo. Anapanga makonzedwe akuti ayambe kusindikiza magazini ina yochedwa The Golden Age. Magaziniyi inali kusindikizidwa n’colinga cakuti izigwilitsidwa nchito muutumiki wakumunda. * M’caka cimeneco ca 1919, anayamba kusindikiza cofalitsa cina catsopano cochedwa Bulletin cimene panthawi ino timati kabuku ka misonkhano ya Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhiristu. Kungoyambila panthawiyo, Utumiki Wathu wa Ufumu wakhala ukulimbikitsa anthu kugwila mwakhama nchito yolalikila. Kuyambila m’caka cimeneco, abale anayamba kuona nchito yolaliki ku nyumba ndi nyumba kukhala yofunika kwambili.

37. Kodi anthu ena anaonetsa bwanji kusakhulupilika pambuyo pa 1919?

37 Nchito yolalikila nayonso inayenga atumiki a Kristu cifukwa cakuti anthu onyada ndi odzikweza sanali kufuna kugwila nchito yooneka ngati yonyozeka imeneyi. Anthu amene sanali kufuna kugwila nchitoyi analeka kugwilizana ndi anthu okhulupilika. Caka ca 1919 citapita, anthu ena osakhulupilika anakhumudwa, ndipo anayamba kuneneza ndi kuipitsa dzina la atumiki a Yehova. Iwo anayamba ngakhale kugwilizana ndi anthu amene anali kuzunza atumiki okhulupilika a Yehova.

38. Kodi kupita patsogolo kwa otsatila a Kristu ndi zipambano zao ndi umboni wa ciani?

38 Otsatila a Kristu padziko lapansi anapitilizabe kupita patsogolo ndi kulimba mwakuuzimu mosasamala kanthu za mavutowo. Kupita kwao patsogolo ndiponso zipambano zimene apeza mpaka lelo, ndi umboni wamphamvu wakuti Ufumu wa Mulungu ukulamulila. Anthu opanda ungwilo apambana ziyeso zosiyanasiyana zocokela kwa Satana ndi dziko lake loipali. Izi zakhala conco kokha cifukwa Yehova wakhala akuwacilikiza ndi kuwadalitsa kudzela mwa Mwana wake ndi Ufumu wa Mesiya.—Ŵelengani Yesaya 54:17.

M’bale J. F. Rutherford akukamba nkhani yogwila mtima pa msonkhano wacigawo patangopita miyezi yoŵelengeka atatuluka m’ndende

39, 40. (a) Kodi m’buku lino muli zotani? (b) Kodi kuphunzila buku lino kudzakuthandizani bwanji?

39 M’nkhani zotsatila, tidzakambilana zimene Ufumu wa Mulungu wacita padziko lapansi kuyambila pamene unabadwa kumwamba mu 1914. Cigawo ciliconse m’buku lino cidzafotokoza nchito inayake imene Ufumuwu wacita padziko lapansi. M’nkhani iliyonse muli kabokosi ka mafunso obwelelamo ndipo kadzathandiza aliyense wa ife kuona kuti Ufumu wa Mulungu ndi weni-weni. M’nkhani zomalizila, tidzakambilana zimene Ufumuwo udzaticitila ukadzaononga anthu oipa posacedwapa ndi kubweletsa dziko la paladaiso. Kodi inu mudzapindula bwanji mwa kuphunzila bukuli?

40 Satana amafuna kufooketsa cikhulupililo canu mu Ufumu wa Mulungu. Koma Yehova amafuna kulimbitsa cikhulupililo canu kuti cizikutetezani ndi kukuthandizani kuti mukhale olimba. (Aef. 6:16) Motelo tikukulimbikitsani kuti muphunzile buku limeneli mwakhama. Pophunzila bukuli muzidzifunsa kuti, ‘Kodi ndimaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni?’ Ngati mumaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi weni-weni, ndiye kuti mudzakhala ndi moyo panthawi imene wina aliyense adzaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi weniweni ndi kuti ukulamulila. Ndipo mudzacilikiza Ufumuwu mokhulupilika ndi mwacangu.

^ par. 7 Kuti mudziŵe zambili zokhudza Grew, Stetson, ndi Storrs, onani buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom, tsamba 45 ndi 46.

^ par. 15 Ophunzila Baibulo anali kudziŵa kuti sayenela kugwilizana ndi zipembedzo zimene zinali paubwenzi ndi dzikoli. Komabe, kwa zaka zambili io anapitiliza kuona anthu amene sanali Ophunzila Baibulo kukhala abale ao akuuzimu cabe cifukwa cakuti anali kunena kuti amakhulupilila dipo, ndipo ndi odzipeleka kwa Mulungu.

^ par. 17 Cinthu cina cimene cinapangitsa kuti Ophunzila Baibulo ena aone macenjezowo mopepuka cinali cakuti macenjezowo anali kupelekedwa makamaka kwa a 144,000, amene ndi kagulu ka nkhosa ka Kristu. M’Nkhani 5 tidzaona kuti caka ca 1935 cisanafike, Ophunzila Baibulo anali kukhulupilila kuti “khamu lalikulu,” monga mmene lafotokozedwela pa Chivumbulutso 7:9, 10, lidzaphatikizapo mamembala ambilimbili a machalichi acikristu. Anali kukhulupililanso kuti anthu amenewa adzakhala m’gulu laciŵili la anthu amene adzapita kumwamba cifukwa cocilikiza Kristu m’nthawi yamapeto.

^ par. 31 Mu September caka ca 1920, magazini ya The Golden Age (imene tsopano ndi Galamukani!) inafotokoza zizunzo zambili zimene abale anakumana nazo panthawi ya nkhondo ku England, Germany ndi ku United States ndipo zina zinali zankhanza kwambili. Komabe, kwa zaka zambili nkhondo ya padziko lonse isanacitike, zinzunzo sizinali kucitika kaŵilikaŵili.

^ par. 36 Kwa zaka zambili, colinga ca magazini ya Watch Tower cinali kuphunzitsa anthu a m’kagulu ka nkhosa.