Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI 1

“Ufumu Wanu Ubwele”

“Ufumu Wanu Ubwele”

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Kuunika zimene Yesu anaphunzitsa ponena za Ufumu wa Mulungu

1, 2. Kodi atumwi atatu a Yesu anamva mau otani a Yehova? Nanga io anacita ciani?

KODI mungatani ngati Yehova Mulungu atakuuzani kuti mucite zina zake? Mosakaikila, mungakonde kucita zilizonse zimene iye angakuuzeni, si conco?

2 Izi n’zimene zinacitikila atumwi atatu a Yesu, Petulo, Yakobo ndi Yohane panthawi inayake pambuyo pa pasika wa mu 32 C.E. (Ŵelengani Mateyu 17:1-5.) Pamene anali pa ‘phiri lalitali’ ndi Mbuye wao, io anaona masomphenya a Yesu ali kumwamba monga Mfumu yaulemelelo. Petulo anaona ngati masomphenyawo ndi zocitika zenizeni cakuti anafuna kutengako mbali m’zocitikazo. Petulo akali kulankhula, panabwela mtambo umene unawaphimba. Ndiyeno, iye ndi anzakewo anamva liu la Yehova, ndipo umenewo unali mwai waukulu kwambili cifukwa ndi anthu ocepa cabe amene anamvapo liu la Yehova. Pambuyo pakuti Yehova wanena kuti Yesu ndi Mwana wake, Iye ananenanso motsindika kuti “muzimumvela.” Atumwi anatsatila malangizo a Mulungu amenewo. Iwo anamvela zimene Yesu anali kuphunzitsa, ndipo analimbikitsanso ena kucita cimodzimodzi.—Mac. 3:19-23; 4:18-20.

Yesu anali kukonda kulankhula za Ufumu wa Mulungu kuposa nkhani ina iliyonse

3. N’cifukwa ciani Yehova amafuna kuti tizimvela Mwana wake? Kodi tikambilana za ciani?

3 Zimene Mulungu anakamba kuti “muzimumvela” zinalembedwa m’Baibulo kuti zitithandize. (Aroma 15:4) N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti Yesu ndi wolankhulila wa Mulungu, ndipo nthawi zonse Yesu anali kuphunzitsa zimene Atate wake anali kufuna kuti anthufe tidziŵe. (Yoh. 1:1, 14) Yesu anali kukonda kuphunzitsa za Ufumu wa Mulungu umene ndi boma la kumwamba la ufumu wa Mesiya, ndipo limaphatikizapo Yesu Kristu ndi olamulila anzake a 144,000. Popeza kuti Yesu anali kukonda kuphunzitsa za Ufumuwo kuposa nkhani ina iliyonse, tiyenela kupenda nkhani yofunika imeneyi mosamala kwambili. (Chiv. 5:9, 10; 14:1-3; 20:6) Koma coyamba, tiyeni tikambilane cifukwa cake Yesu anali kukonda kuphunzitsa za Ufumu wa Mulungu.

“Zosefukila Mumtima”

4. Kodi Yesu anaonetsa bwanji kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambili kwa iye?

4 Yesu amaona Ufumu wa Mulungu kukhala wofunika kwambili. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti zimene timalankhula zimavumbula zimene zili mumtima mwathu kapena kuti zimene timaona kukhala zofunika kwambili. Yesu mwiniyo anati: “Pakamwa pamalankhula zosefukila mumtima.” (Mat. 12:34) Yesu anali kukonda kulankhula za Ufumu wa Mulungu nthawi iliyonse. Anthu amene analemba mabuku a Uthenga Wabwino analemba zokhudza Ufumuwo nthawi zoposa 100, ndipo ambili mwa mau amenewo anakambidwa ndi Yesu. Nkhani yaikulu imene iye anali kulalikila ndi yokhudza Ufumu. Iye anati: “Ndiyenela kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, cifukwa ndi zimene anandituma kudzacita.” (Luka 4:43) Ngakhale pambuyo poukitsidwa, Yesu anapitilizabe kuphunzitsa ophunzila ake za Ufumu wa Mulungu. (Mac. 1:3) Yesu anali kukonda kutelo cifukwa cakuti anali kuona kuti Ufumuwo ndi wofunika kwambili.

5-7. (a) Kodi timadziŵa bwanji kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambili kwa Yehova? Pelekani fanizo. (b) Kodi tingaonetse bwanji kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambili kwa ife?

5 Yehova amaonanso kuti Ufumuwo ndi wofunika kwambili. Kodi timadziwa bwanji zimenezo? Kumbukilani kuti Yehova anatumiza mwana wake wobadwa yekha pa dziko lapansi. Zilizonse zimene Mwana wake anali kukamba ndi kuphunzitsa zinali zocokela kwa Yehova. (John 7:16; 12:49, 50) Ndiponso nkhani zonse zolembedwa m’Mauthenga Abwino zokhudza umoyo ndi utumiki wa Yesu, ndi zocokela kwa Yehova. Kodi zimenezi zikutiphunzitsa ciani?

Aliyense wa ife ayenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambili?’

6 Tayelekezelani kuti mukusankha zithunzithunzi zoika mu aubamu yanu ndipo muli ndi zithunzithunzi zambili, koma aubamu yanu ndi yaing’ono. Kodi mungacite ciani? Mungasankhe zimene muona kuti n’zofunika kwambili kuika mu aubamu yanu. Mofananamo, Mauthenga Abwino ali ngati aubamu imene imatipatsa cithunzi cokwanila ca umoyo wa Yesu. Yehova sanauzile alembi a Mauthenga Abwino kulemba zonse zimene Yesu anakamba ndi kucita pamene anali padziko lapansi. (Yoh. 20:30; 21:25) M’malomwake, mzimu wa Yehova unawatsogolela kulemba mau ndi zocita za Yesu zimene zimatithandiza kudziŵa colinga ca utumiki wa Yesu ndiponso cinthu cofunika kwambili kwa Yehova. (2 Tim. 3:16, 17; 2 Pet. 1:21) Conco, popeza kuti Mauthenga Abwino ndi odzaza ndi zimene Yesu anali kuphunzitsa ponena za Ufumu wa Mulungu, tinganene kuti Ufumuwo ndi cinthu cofunika kwambili kwa Yehova. Zoonadi, Yehova amafuna kuti tidziŵe bwino zinthu zokhudza Ufumuwo.

7 Aliyense wa ife ayenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimaona kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika kwambili?’ Ngati timaona kuti Ufumu ndi wofunika kwambili, tidzakhala ofunitsitsa kumvela zimene Yesu anakamba ndi kuphunzitsa ponena za Ufumuwo. Iye anaphunzitsa za kufunika kwa Ufumuwo, zimene udzacita ukadzabwela, ndi nthawi pamene udzabwela.

Kodi ‘Ufumu wa Mulungu Udzabwela’ Motani?

8. Kodi Yesu anasonyeza bwanji m’mau acidule kuti Ufumu wa Mulungu ndi wofunika?

8 Taganizilani pemphelo lacitsanzo la Yesu. Mwakugwilitsila nchito mau osavuta kumva, Yesu anafotokoza mwacidule kufunika kwa Ufumu wa Mulungu ndi zimene udzakwanilitsa. Pemphelo limeneli lili ndi mapempho 7, ndipo atatu mwa mapempho amenewa akukhudza zolinga za Yehova. Zolinga zimenezo ndi kuyeletsedwa kwa dzina lake, kubwela kwa Ufumu wake, ndi kuti cifunilo cake cicitike padziko lapansi monga kumwamba. (Ŵelengani Mateyu 6:9, 10.) Mapempho atatu amenewa ndi ogwilizana kwambili. Ufumu wa Mesiya ndi njila imene Yehova adzagwilitsila nchito kuti ayeletse dzina lake ndi kukwanilitsa cifunilo cake.

9, 10. (a) Kodi Ufumu wa Mulungu udzacita ciani ukadzabwela? (b) Kodi inuyo mumafunitsitsa kuti mukaone lonjezo liti la m’Baibulo likukwanilitsidwa?

9 Kodi Ufumu wa Mulungu udzacita ciani ukadzabwela? Tikamapemphela kuti “Ufumu wanu ubwele,” timapempha Mulungu kuti Ufumu wake ukonze zinthu padziko lapansi. Ufumuwo ukadzabwela, udzaonetsa kuti uli ndi mphamvu zolamulila dziko lapansi mwa kucotsa dongosolo loipali, kuphatikizapo maboma onse a anthu, ndipo udzabweletsa dziko latsopano lolungama. (Dan. 2:44; 2 Pet. 3:13) Ndiyeno, pamene Ufumuwo udzalamulila, dziko lonse lapansi lidzakhala paladaiso. (Luka 23:43) Anthu onse amene Mulungu akuwakumbukila adzaukitsidwa ndipo adzagwilizananso ndi acibale ao. (Yoh. 5:28, 29) Anthu omvela adzakhala angwilo ndi kusangalala ndi moyo wosatha. (Chiv. 21:3-5) Pomalizila pake, cifunilo ca Yehova Mulungu cidzacitika padziko lapansi monga kumwamba. Kodi mukulakalaka mutaona malonjezo olembedwa m’Baibulo amenewo atakwanilitsidwa? Musaiwale kuti nthawi zonse mukamapemphela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele, mumapempha kuti malonjezo osangalatsa amenewa akwanilitsidwe.

10 Mwacionekele, Ufumu wa Mulungu ‘usanabwele,’ ndipo pemphelo lacitsanzo lisanayankhidwe. Maboma a anthu akali kulamulila, ndipo dziko latsopano lolungama lisanabwele. Koma uthenga wabwino ndi wakuti Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa monga mmene tidzaonela m’nkhani yotsatila. Tsopano tiyeni tipende zimene Yesu anakamba ponena za nthawi imene Ufumuwo udzakhazikitsidwa ndi pamene udzabwela.

Kodi Ufumu wa Mulungu Unakhazikitsidwa Liti?

11. Kodi Yesu anasonyeza ciani ponena za Ufumu wa Mulungu?

11 Yesu anasonyeza kuti Ufumu sunakhazikitsidwe m’nthawi ya atumwi monga mmene ophunzila ake ena anali kuganizila. (Mac. 1:6) Ganizilani za mafanizo aŵili amene iye ananena. Fanizo lina ayenela kuti analifotokoza m’caka ca 31 C.E., ndipo lina mu 33 C.E.

12. Kodi fanizo la tiligu ndi namsongole limaonetsa bwanji kuti Ufumu wa Mulungu sunakhazikitsidwe m’nthawi ya atumwi?

12 Fanizo la tiligu ndi namsongole. (Ŵelengani Mateyu 13:24-30.) Yesu ananena fanizo limeneli mwina cakumayambililo kwa caka ca 31 C.E. Pambuyo pake, iye anafotokozela ophunzila ake tanthauzo la fanizoli. (Mat. 13:36-43) Mfundo yaikulu ndiponso tanthauzo la fanizoli ndi lakuti: Pambuyo pakuti atumwi onse afa, Mdyelekezi anabzala namsongole (Akristu abodza) pakati pa tiligu (“ana a Ufumu,” kapena kuti Akristu odzozedwa). Tiligu ndi namsongoleyo zinaloledwa kuti zikulile pamodzi mpaka panthawi yokolola imene ndi “mapeto a nthawi ino.” Pamene nyengo yokolola inayamba, namsongole anasonkhanitsidwa. Ndiyeno, tiligu nayenso anasokhanitsidwa. Fanizo limeneli likusonyeza kuti Ufumu unayenela kukhazikitsidwa nyengo ya kukula kwa tiligu ndi namsongole itatha osati m’nthawi ya atumwi. Nthawi yokulayo inatha, ndipo nthawi yokolola inayamba mu 1914.

13. Kodi Yesu anapeleka fanizo lotani losonyeza kuti iye sadzaikidwa kukhala Mfumu Mesiya akadzangobwelela Kumwamba?

13 Fanizo la ndalama za mina. (Ŵelengani Luka 19:11-13.) Yesu anakamba fanizo limeneli m’caka ca 33 C.E. pamene anali paulendo wake womaliza wopita ku Yerusalemu. Anthu ena amene anali kumvetsela zimene Yesu anali kukamba anaganiza kuti iye adzakhazikitsa Ufumu wake akadzangofika ku Yerusalemu. Kuti aongolele maganizo ao ndi kusonyeza kuti Ufumuwo udzakhazikitsidwa mtsogolo, Yesu anadziyelekezela ndi “munthu wina wa m’banja lacifumu” amene “anapita kudziko lakutali kuti akalandile ufumu.” * “Dziko lakutali” limene Yesu anapitako ndi kumwamba kumene anapatsidwa mphamvu za Ufumu ndi Atate wake. Koma Yesu anadziwa kuti sadzaikidwa kukhala Mfumu Mesiya akadzangobwelela kumwamba. M’malomwake, iye anayenela kukhala kudzanja lamanja la Mulungu kuyembekezela nthawi yoikika. Ndipo nthawi yoyembekezela imeneyo inatenga zaka zambili.—Sal. 110:1, 2; Mat. 22:43, 44; Aheb. 10:12, 13.

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzabwela Liti?

14. (a) Kodi Yesu anayankha bwanji funso limene atumwi ake anai anamufunsa? (b) Kodi kukwanilitsidwa kwa ulosi wa Yesu kumatiphunzitsa ciani ponena za kukhalapo kwake ndi za Ufumu wa Mulungu?

14 Kutatsala masiku ocepa kuti Yesu aphedwe, atumwi ake anai anam’funsa kuti: “Kodi . . . cizindikilo ca kukhalapo kwanu ndi ca mapeto a nthawi ino cidzakhala ciani?” (Mat. 24:3; Maliko 13:4) Yesu anawayankha mwa kufotokoza ulosi waukulu umene timaŵelenga pa Mateyu caputala 24 ndi 25. Iye anafotokoza zinthu zosiyanasiyana zimene zidzacitika padziko lonse lapansi zimene zidzapanga cizindikilo ca nthawi ya “kukhalapo” kwake. Nthawi ya kukhalapo kwa Yesu inayamba pamene Ufumu unakhazikitsidwa, ndipo idzatha pamene Ufumuwo udzabwela. Tili ndi umboni wokwanila umene umasonyeza kuti ulosi wa Yesu wakhala ukukwanilitsidwa kuyambila mu 1914. * Motelo, m’caka cimeneco nthawi ya kukhalapo kwa Yesu inayamba ndiponso Ufumu unakhazikitsidwa.

15, 16. Kodi mau akuti “m’badwo uwu” amanena za ndani?

15 Koma kodi Ufumu wa Mulungu udzabwela liti? Yesu sanafotokoze nthawi yeniyeni pamene Ufumuwo udzabwela. (Mat. 24:36) Koma iye ananena mfundo inayake imene imatipangitsa kukhulupilila kuti ufumuwo uli pafupi kwambili. Yesu anasonyeza kuti Ufumuwo udzabwela pambuyo pakuti “m’badwo uwu” waona cizindikilo ca kukwanilitsidwa kwa ulosi umenewu. (Ŵelengani Mateyu 24:32-34.) Kodi mau akuti “m’badwo uwu” amanena za ndani? Tiyeni tipende mosamala mau a Yesu amenewa.

16 “M’badwo uwu.” Kodi pamene Yesu anakamba mau amanewa anali kunena za anthu osakhulupilila? Iyai. Kumbukilani kuti Yesu anali kufotokoza ulosi umenewu kwa atumwi ake ocepa amene “anafika kwa iye mwamseli.” (Mat. 24:3) Atumwiwo anali pafupi kudzozedwa ndi mzimu woyela. Ganizilaninso nkhani imene Yesu anali kukamba panthawiyo. Iye asanakambe za “m’badwo uwu,” ananena kuti: “Tsopano phunzilani mfundo imeneyi pa fanizo ili la mkuyu: Nthambi yake yanthete ikaphuka ndi kucita masamba, mumadziŵa kuti dzinja lili pafupi. Inunso cimodzimodzi, mukadzaona zinthu zonsezi, mudzadziwe kuti iye ali pafupi, ali pakhomo penipeni.” Mwacionekele, otsatila odzozedwa a Yesu, osati anthu osakhulupilila, ndi amene akanaona zinthu zimenezi zikukwanilitsidwa ndi kudziŵa kuti Yesu ali “pakhomo penipeni.” Motelo, pamene Yesu anakamba kuti “m’badwo uwu,” iye anali kunena za otsatila ake odzozedwa.

17. Kodi mau akuti “m’badwo” ndiponso akuti “zinthu zonsezi” amatanthauza ciani?

17 “Sudzatha wonse kucoka kufikila zinthu zonsezi zitacitika.” Kodi mau amenewa adzakwanilitsika motani? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyenela kudziŵa tanthauzo la liu lakuti “m’badwo” ndi mau akuti “zinthu zonsezi.” Nthawi zambili liu lakuti “m’badwo” limanena za anthu amisinkhu yosiyanasiyana amene amakhala ndi moyo panyengo inayake. Nthawi imeneyi sicita kukhala yaitali mopambanitsa, ndipo imakhala ndi pothela. (Eks. 1:6) Mau akuti “zinthu zonsezi” amatanthauza zinthu zonse zimene zinanenedwelatu kuti zidzacitika panthawi ya kukhalapo kwa Yesu kuyambila mu 1914 mpaka pa “cisautso cacikulu.”—Mat. 24:21.

18, 19. Kodi mau a Yesu onena za “m’badwo uwu” amatanthauza ciani? Nanga tikuphunzilapo ciani?

18 Motelo, kodi mau a Yesu akuti “m’badwo uwu” amatanthauza ciani? M’badwo uwu uli ndi magulu aŵili a odzozedwa. Gulu loyamba ndi Akristu odzozedwa amene analipo ndi moyo mu 1914, ndipo anaona cizindikilo cakuti Yesu wayamba kulamulila m’cakaco. Gulu laciŵili ndi odzozedwa amene anadzakhalapo panthawi imene odzozedwa ena a m’gulu loyamba analipobe ndi moyo. Koma a m’magulu aŵiliwa anakhala limodzi kwa nthawi yocepa cabe. Odzozedwa ena a m’gulu laciŵili la “m’badwo uwu” adzakhalapobe ndi moyo pamene cisautso cacikulu cidzayamba. Conco, magulu onse aŵili a odzozedwa amenewa amapanga m’badwo umodzi. Tikutelo cifukwa cakuti gulu laciŵili la odzozedwa linayamba kukhalapo pamene gulu loyamba lisanatheletu. *

19 Kodi tingati ciani tsopano pambuyo pophunzila nkhaniyi? Mbali za cizindikilo cakuti Yesu anakhala Mfumu tikuziona padziko lonse lapansi. Ndiponso, odzozedwa amene ali mbali ya “m’badwo uwu” omwe akali ndi moyo tsopano ndi okalamba, koma sadzatha onse cisautso cacikulu cisanayambe. Conco, tinganene kuti Ufumu wa Mulungu udzabwela posacedwapa ndi kulamulila dziko lonse lapansi. Tidzakhala osangalala kwambili poona kuti pemphelo limene Yesu anatiphunzitsa layankhidwa, lakuti: “Ufumu wanu ubwele.”

20. Kodi buku lino lidzafotokoza nkhani yofunika kwambili iti? Kodi m’nkhani yotsatila tidzakambitsilana ciani?

20 Tisaiwale mau amene Yehova anakamba kucokela kumwamba ponena za Mwana wake akuti “Muzimumvela.” Monga Akristu, timamvela lamulo la Mulungu limeneli ndi mtima wonse. Timafunitsitsa kudziŵa zinthu zonse zimene Yesu anakamba ndi kuphunzitsa ponena za Ufumu wa Mulungu. M’buku lino tidzaphunzila nkhani yofunika kwambili yokhudza zinthu zimene Ufumu umenewu wacita kale ndi zimene udzacita mtsogolo. Nkhani yotsatila idzafotokoza zinthu zocititsa cidwi zimene zinacitika Ufumu wa Mulungu usanakhazikitsidwe kumwamba ndi pambuyo pake.

^ par. 13 Fanizo la Yesu limeneli liyenela kuti linakumbutsa omvela ake za Arikelao, mwana wa Herode wamkulu. Herode asanafe, anasankha Arikelao kukhala womulowa m’malo monga mfumu ya ku Yudeya ndi madela ena. Koma Arikelao asanayambe kulamulila, anayenda mtunda wautali kupita ku Roma kuti akalandile civomelezo ca Augusto Kaisala.

^ par. 14 Kuti mumve zambili, onani nkhani 9 m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni.

^ par. 18 Gulu loyamba la odzozedwa amene ali mbali ya “m’badwo uwu” ndi Akristu amene anaona “ciyambi ca masautso” mu 1914. Aliyense amene anadzozedwa pambuyo pakuti odzozedwa onse a m’gulu loyambali afa, sali mbali ya “m’badwo uwu.”—Mat. 24:8.