Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

PHUNZILO 5

Kodi Mulungu Ali Nalo Colinga Canji Dziko Lapansi?

Kodi Mulungu Ali Nalo Colinga Canji Dziko Lapansi?

1. N’cifukwa ciani Mulungu analenga dziko lapansi?

Yehova anapeleka dziko lapansi kwa akazi ndi amuna. Dzikoli ndilo malo athu okhalapo. Conco, mwamuna ndi mkazi oyamba, Adamu ndi Hava, sanalengedwe kuti akakhale kumwamba ndi kukabeleka ana kumeneko.​—Mulungu anali atalenga kale angelo kuti azikhala kumwamba. (Yobu 38:4, 7) Mwa ici, Mulungu anaika mwamuna woyamba m’paladaiso wokongola wochedwa munda wa Edeni. (Genesis 2:15-17) Yehova anapatsa Adamu ndi mbadwa zake zamtsogolo mwai wokhala ndi moyo wosatha padziko lapansi.​—Ŵelengani Salimo 37:29; 115:16.

Paciyambi, paladaiso anali pa munda wa Edeni cabe. Mwamuna woyamba ndi mkazi woyamba anafunikila kubeleka ana kuti adzaze dziko lapansi. M’kupita kwa nthawi, anafunikila kuti ayang’anile dziko lonse ndi kulipanga kukhala paladaiso. (Genesis 1:28) Dziko lapansi silidzaonongedwa. Nthawi zonse lidzakhala malo okhalapo anthu.​—Ŵelengani Salimo 104:5.

Tambani vidiyo N’cifukwa Ciani Mulungu Analenga Dziko Lapansi?

2. N’cifukwa ciani dziko lapansi panthawi ino silili paladaiso?

Adamu ndi Hava sanamvele Mulungu, conco Yehova anawacotsa m’munda umenewo. Paladaiso anataika, ndipo palibe munthu amene wakwanitsa kubwezeletsa paladaiso. Baibo imati: “Dziko lapansi lapelekedwa m’manja mwa woipa.”​—Yobu 9:24.​—Ŵelengani Genesis 3:23, 24.

Kodi Yehova walephela kukwanilitsa colinga cake coyambilila kwa anthu? Iyai! Iye ndi wamphamvuyonse. Sangalephele. (Yesaya 45:18) Adzakonza zinthu zonse kuti mtundu wa anthu ukhale ngati mmene anali kufunila poyamba.​—Ŵelengani Salimo 37:11, 34.

3. Kodi Paladaiso adzabwezeletsedwa bwanji?

Dziko lapansi lidzakhalanso paladaiso pamene Yesu monga Mfumu ya Mulungu adzacitapo kanthu mu ulamulilo wake. Pankhondo ya Aramagedo, Yesu adzatsogolela angelo a Mulungu ndi kuononga onse amene amatsutsa Mulungu. Ndiyeno Yesu adzaponya Satana m’ndende kwa zaka 1,000. Anthu a Mulungu adzapulumuka cionongeko cifukwa Yesu adzawatsogolela ndi kuwachinjiliza. Iwo adzasangalala ndi moyo wosatha m’Paladaiso padziko lapansi.​—Ŵelengani Chivumbulutso 20:1-3; 21:3, 4.

4. Kodi mavuto adzatha liti?

Kodi ndi liti pamene Mulungu adzacotsapo mavuto padziko lapansi? Yesu anapeleka “cizindikilo” coonetsa pamene mapeto adzayandikila. Mmene zinthu zilili masiku ano zionetsa kuti tili mnthawi ya mapeto a dongosolo la zinthu, ndipo ngati zingapitilize conco, mtundu wonse wa anthu ungaonongekeletu.​—Ŵelengani Mateyu 24:3, 7-14, 21, 22.

Yesu adzacotsapo mavuto onse padziko lapansi mu ulamulilo wake wa zaka cikwi. (Yesaya 9:6, 7; 11:9) Iye sadzakhala cabe Mfumu, koma adzakhalanso Mkulu wa Ansembe ndipo adzafafaniza macimo a anthu okonda Mulungu. Conco, kupitila mwa Yesu, Mulungu adzacotsapo matenda, ukalamba, ndi imfa.​—Ŵelengani Yesaya 25:8; 33:24.

5. Kodi ndani adzakhala m’Paladaiso?

Pa Nyumba ya Ufumu, mudzapeza anthu amene amakonda Mulungu ndipo amaphunzila kumulemekeza

Anthu amene amamvela Mulungu ndi amene adzakhala m’Paladaiso. (1 Yohane 2:17) Yesu anatuma otsatila ake kukafuna-funa anthu ofatsa ndi kuwaphunzitsa mmene angakhalile olandilika kwa Mulungu. Masiku ano, Yehova akukonzekeletsa anthu mamiliyoni kuti akakhale ndi moyo m’Paladaiso padziko lapansi. (Zefaniya 2:3) Pa Nyumba ya Ufumu iliyonse ya Mboni za Yehova, anthu amaphunzila mmene angakhalile amuna abwino ndi atate abwino, ndi mmenenso angakhalile akazi abwino ndi amai abwino. Ana ndi makolo amalambila capamodzi, ndipo amaphunzila mmene uthenga wabwino ungawathandizile.​—Ŵelengani Mika 4:1-4.