Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Tipita Nanu Limodzi”

“Tipita Nanu Limodzi”

“Anthu inu tipita nanu limodzi, cifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”ZEKARIYA 8:23.

NYIMBO: 65, 122

1, 2. (a) Kodi Yehova anakamba kuti n’ciani cidzacitika masiku ano? (b) Ndi mafunso ati amene adzayankhidwa m’nkhani ino? (Onani cithunzi pamwambapa.)

YEHOVA anakamba kuti masiku ano, “amuna 10 ocokela m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina adzagwila covala ca munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, cifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’” (Zekariya 8:23) “Myuda” akuimila anthu amene Mulungu wawadzoza ndi mzimu woyela. Iwo amachedwanso “Isiraeli wa Mulungu.” (Agalatiya 6:16) “Amuna 10” akuimila anthu amene ali ndi ciyembekezo codzakhala padziko lapansi kwamuyaya. Iwo amadziŵa kuti Yehova wadalitsa odzozedwa, ndipo amaona kuti ndi mwai kutumikila Mulungu pamodzi nao.

2 Mofanana ndi mneneli Zekariya, Yesu anakamba kuti anthu a Mulungu adzakhala ogwilizana. Iye anakamba kuti anthu amene ali ndi ciyembekezo cokakhala kumwamba ndi “kagulu ka nkhosa,” ndipo amene ali ndi ciyembekezo codzakhala padziko lapansi ndi “nkhosa zina.” Komabe, Yesu anakambanso kuti onse adzakhala “gulu limodzi” ndi kuti adzatsatila iye monga ‘m’busa wao mmodzi.’ (Luka 12:32; Yohane 10:16) Popeza pali magulu aŵili, ena angadzifunse kuti: (1) Kodi a nkhosa zina ayenela kudziŵa maina a odzozedwa onse masiku ano? (2) Kodi odzozedwa ayenela kudziona bwanji? (3) Kodi Mkristu wina mumpingo akayamba kudya mkate ndi kumwa vinyo pa Cikumbutso, tiyenela kumuona bwanji? (4) Kodi tiyenela kuda nkhawa tikaona kuti ciŵelengelo ca amene amadya mkate ndi kumwa vinyo pa Cikumbutso cikukwela? Nkhani ino iyankha mafunso amenewa.

KODI TIYENELA KUDZIŴA MAINA A ODZOZEDWA ONSE MASIKU ANO?

3. N’cifukwa ciani n’zosatheka kwa ife kudziŵa amene adzakhaladi mbali ya a 144,000?

3 Kodi a nkhosa zina ayenela kudziŵa maina a odzozedwa onse amene akali padziko lapansi masiku ano? Iyai. Tikutelo cifukwa cakuti palibe munthu amene akhoza kudziŵa Akristu amene adzalandiladi mphoto yao. [1] (Onani mau akumapeto.) Ngakhale kuti Mulungu wawaitana kuti adzapite kumwamba, io adzalandila mphoto yao kokha ngati akhalabe okhulupilika. Satana amadziŵa zimenezi, ndipo amagwilitsila nchito “aneneli onyenga” kuti ‘awasoceletse.’ (Mateyu 24:24) Akristu odzozedwa sangadziŵe kuti adzalandiladi mphoto yao. Iwo adzadziŵa zimenezi Yehova akadzawaweluza kuti ndi okhulupilika. Yehova amawadinda cidindo comaliza asanamwalile, ndipo ena adzawadinda cidindo cimeneci “cisautso cacikulu” citatsala pang’ono kuyamba.—Chivumbulutso 2:10; 7:3, 14.

Yesu ndiye Mtsogoleli wathu, ndipo tiyenela kutsatila iye yekha cabe

4. Popeza n’zosatheka kudziŵa maina a odzozedwa onse amene ali padziko lapansi, zingatheke bwanji ‘kupita nao limodzi’?

4 Popeza n’zosatheka kudziŵa maina a odzozedwa onse amene ali padziko lapansi, zingatheke bwanji kuti a nkhosa zina ‘apite nao limodzi’? Baibulo limakamba kuti “amuna 10” “adzagwila covala ca munthu amene ndi Myuda ndi kunena kuti: ‘Anthu inu tipita nanu limodzi, cifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.’” Lembali lakamba kuti Myuda ngati kuti likunena za munthu mmodzi. Koma mau akuti “inu” ndi akuti “anthu inu,” akusonyeza kuti likukamba za anthu ambili osati munthu mmodzi. Zimenezi zitanthauza kuti Myuda ameneyu si munthu mmodzi koma akuimila gulu lonse la odzozedwa. A nkhosa zina amadziŵa zimenezi, ndipo amatumikila Yehova pamodzi ndi gulu limeneli. Iwo safunika kudziŵa maina a odzozedwa onse kuti ayambe kuwatsatila. Yesu ndiye Mtsogoleli wathu, ndipo Baibulo limatilangiza kuti tiyenela kutsatila iye yekha cabe.—Mateyu 23:10.

KODI ODZOZEDWA AYENELA KUDZIONA BWANJI?

5. Ndi cenjezo liti limene odzozedwa ayenela kukumbukila? Nanga n’cifukwa ciani?

5 Odzozedwa ayenela kukumbukila cenjezo limene lili pa 1 Akorinto 11:27-29. (Ŵelengani.) Kodi wodzozedwa angadye bwanji mkate ndi kumwa vinyo “mosayenelela” pa Cikumbutso? Ngati iye sali paubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo ndi wosakhulupilika, koma wadya mkate ndi kumwa vinyo, ndiye kuti wacita zinthu mopanda ulemu. (Aheberi 6:4-6; 10:26-29) Cenjezo lamphamvu limeneli limakumbutsa odzozedwa kuti ayenela kukhalabe okhulupilika kuti akalandile “mphoto ya ciitano ca Mulungu copita kumwamba, codzela mwa Kristu Yesu.”—Afilipi 3:13-16.

6. Kodi odzozedwa ayenela kudziona bwanji?

6 Paulo anauza Akristu odzozedwa kuti: “Ine, amene ndili m’ndende cifukwa ca Ambuye, ndikukucondelelani kuti muziyenda moyenela kuitana kumene munaitanidwa nako.” Kodi akanacita bwanji zimenezi? Paulo anafotokoza kuti: “Muziyenda modzicepetsa nthawi zonse, mofatsa, moleza mtima, ndiponso mololelana m’cikondi. Muziyesetsa ndi mtima wonse kusunga umodzi wathu mwa mzimuwo, ndi mwamtendele monga comangila cotigwilizanitsa.” (Aefeso 4:1-3) Mzimu woyela wa Yehova umathandiza atumiki ake kukhala odzicepetsa ndi kupewa kudzikuza. (Akolose 3:12) Conco, odzozedwa sadziona kuti ndi apamwamba kuposa anthu ena. Amadziŵa kuti Yehova sapatsa odzozedwa mzimu woyela wambili kuposa a nkhosa zina. Ndipo sadziona kuti ndi amene angamvetse kwambili coonadi ca m’Baibulo kuposa anthu ena. Iwo sayenela kuuza munthu wina kuti wadzozedwa ndiponso kuti azidya mkate ndi kumwa vinyo pa Cikumbutso. M’malomwake, amakhala odzicepetsa ndipo amadziŵa kuti Yehova yekha ndiye amaitana anthu kuti akapite kumwamba.

7, 8. Kodi Akristu odzozedwa sayembekezela ciani? Nanga n’cifukwa ciani?

7 N’zoona kuti odzozedwa amaona kuti ndi mwai wamtengo wapatali kuitanidwa kupita kumwamba, koma sayembekezela kuti anthu aziwaona kukhala apadela. (Aefeso 1:18, 19; ŵelengani Afilipi 2:2, 3.) Iwo amadziŵa kuti pamene Yehova anawadzoza sanadziŵitse munthu wina aliyense. Conco, wodzozedwa sayenela kudabwa ngati anthu sakhulupilila mwamsanga kuti iye wadzozedwa. Amadziŵa kuti Baibulo limatilangiza kuti sitiyenela kukhulupilila mwamsanga ngati munthu wakamba kuti Mulungu anam’patsa udindo winawake wapadela. (Chivumbulutso 2:2) Popeza kuti odzozedwa sayembekezela kupatsidwa ulemu mopambanitsa, io sauza munthu aliyense amene akumana naye koyamba kuti ndi odzozedwa. Ndipo angacite bwino kusakambakamba kuti ndi odzozedwa. Iwo sayenela kudzitama mwa kunena zinthu zabwino zimene adzacita kumwamba.—1 Akorinto 1:28, 29; ŵelengani 1 Akorinto 4:6-8.

8 Akristu odzozedwa sayenela kupanga tumagulu n’kumaceza okhaokha. Iwo safufuza odzozedwa anzao kuti azikambilana nkhani zokhudza odzozedwa, ndipo sakumana m’tumagulu kuti aziphunzila Baibulo. (Agalatiya 1:15-17) Ngati odzozedwa angacite zimenezi, mpingo sungakhale wogwilizana. Ndipo kucita zimenezi kungakhale ngati kulimbana ndi mzimu woyela umene umathandiza anthu a Mulungu kukhala mwamtendele ndiponso mogwilizana.—Ŵelengani Aroma 16:17, 18.

KODI ODZOZEDWA MUYENELA KUWAONA BWANJI?

9. N’cifukwa ciani tiyenela kusamala ndi mmene timaonela Akristu amene amadya mkate ndi kumwa vinyo pa Cikumbutso? (Onani bokosi lakuti “Cikondi ‘Sicicita Zosayenela.’”)

9 Kodi abale ndi alongo odzozedwa muyenela kuwaona bwanji? Yesu anauza ophunzila ake kuti: “Nonsenu ndinu abale.” Kenako anakambanso kuti: “Aliyense wodzikweza adzatsitsidwa, koma aliyense wodzicepetsa adzakwezedwa.” (Mateyu 23:8-12) Conco, si bwino kulemekeza munthu mopambanitsa, ngakhale atakhala m’Kristu wodzozedwa. Ponena za akulu mumpingo, Baibulo limatilangiza kuti tiyenela kutsanzila cikhulupililo cao. Koma silitilangiza kuti tiyenela kuona munthu wina aliyense monga mtsogoleli wathu. (Aheberi 13:7) N’zoona kuti Baibulo limanena kuti akulu amafunika ‘kupatsidwa ulemu waukulu.’ Koma cifukwa cake n’cakuti ‘amatsogolela bwino’ ndiponso “amacita khama kulankhula ndi kuphunzitsa,” osati cifukwa cakuti ndi odzozedwa. (1 Timoteyo 5:17) Sitiyenela kulemekeza odzozedwa mopambanitsa cifukwa kucita zimenezi kungawacititse manyazi. Ndipo vuto lalikulu n’lakuti tingapangitse kuti ayambe kudzikweza. (Aroma 12:3) Tonsefe sitifuna kupangitsa abale a Kristu odzozedwa kucita colakwa cacikulu ngati cimeneci.—Luka 17:2.

Kodi munthu amene amadya mkate ndi kumwa vinyo pa Cikumbutso muyenela kumuona bwanji? (Onani ndime 9-11)

10. Mungaonetse bwanji kuti mumalemekeza Akristu odzozedwa?

10 Tingaonetse bwanji kuti timalemekeza odzozedwa a Yehova? Sitiyenela kuwafunsa mmene anadzozedwela cifukwa iyi ndi nkhani yaumwini, ndipo sitifunika kudziŵa. (1 Atesalonika 4:11; 2 Atesalonika 3:11) Sitiyenela kuganiza kuti mwamuna kapena mkazi wa wodzozedwa, makolo ake, kapena acibale ake naonso ndi odzozedwa. Munthu salandila ciyembekezo cimeneci monga colowa ca banja lake. (1 Atesalonika 2:12) Tiyenelanso kupewa kufunsa mafunso amene angakhumudwitse ena. Mwacitsanzo, sitiyenela kufunsa mkazi wa wodzozedwa kuti; ‘Kodi mumamva bwanji mukaganizila kuti m’dziko latsopano simudzakhala ndi amuna anu? Tisaiŵale kuti m’dziko latsopano, Yehova ‘adzakhutilitsa zokhumba za camoyo ciliconse.’—Salimo 145:16.

11. Kodi timadziteteza bwanji ngati tipewa ‘kutamanda anthu ena’?

11 Ngati tipewa kuona odzozedwa kukhala apamwamba kuposa ena, timadziteteza. Kodi timadziteteza motani? Baibulo limakamba kuti mumpingo mukhoza kukhala “abale onyenga” amene angakambe kuti ndi odzozedwa. (Agalatiya 2:4, 5; 1 Yohane 2:19) Ndiponso odzozedwa ena angakhale osakhulupilika m’kupita kwa nthawi. (Mateyu 25:10-12; 2 Petulo 2:20, 21) Conco, ngati tipewa ‘kutamanda anthu ena,’ sitidzatsatila munthu aliyense, ngakhale atakhala wodzozedwa, m’bale wodziŵika, kapena amene watumikila Yehova kwa nthawi yaitali. Ndipo munthuyo atasintha n’kukhala wosakhulupilika kapena atacotsedwa mumpingo, sitidzaleka kukhulupilila Yehova ndi kumutumikila.—Yuda 16.

KODI TIYENELA KUDA NKHAWA NDI CIŴELENGELO CAO?

12, 13. N’cifukwa ciani sitiyenela kuda nkhawa ndi ciŵelengelo ca amene amadya mkate ndi kumwa vinyo pa Cikumbutso?

12 Kwa zaka zambili, ciŵelengelo ca amene amadya mkate ndi kumwa vinyo pa Cikumbutso cinali kutsika. Koma posacedwapa, ciŵelengeloci cakhala cikukwela caka ciliconse. Kodi zimenezi ziyenela kutidetsa nkhawa? Iyai. Tiyeni tikambilane cifukwa cake.

13 “Yehova amadziŵa anthu ake.” (2 Timoteyo 2:19) Mosiyana ndi Yehova, abale oŵelenga anthu amene amadya mkate ndi kumwa vinyo pa Cikumbutso sadziŵa kuti odzozedwa enieni ndi ati. Motelo, ciŵelengelo cimeneco cimaphatikizapo aja amene si odzozedwa enieni. Mwacitsanzo, anthu ena anali kudya mkate ndi kumwa vinyo pa Cikumbutso, koma patapita nthawi analeka. Ena amayamba kukhulupilila kuti adzalamulila ndi Kristu kumwamba cifukwa ca matenda a maganizo kapena misala. Cotelo, sitidziŵa ciŵelengelo ceniceni ca odzozedwa amene akali padziko lapansi.

14. Kodi Baibulo limakamba ciani za ciŵelengelo ca odzozedwa amene adzakhala padziko lapansi pamene cisautso cacikulu cidzayamba?

14 M’madela ambili padziko lapansi, mudzakhala odzozedwa pamene Yesu adzabwela kudzawatenga kuti apite kumwamba. Baibulo limakamba kuti Yesu “adzatumiza angelo ake ndi kulila kwamphamvu kwa lipenga, ndipo adzasonkhanitsa osankhidwa ake kucokela kumphepo zinayi, kucokela kumalekezelo a m’mlengalenga mpaka kumalekezelo ena.” (Mateyu 24:31) Baibulo limaonetsanso kuti m’masiku otsiliza, padziko lapansi padzakhala odzozedwa ocepa. (Chivumbulutso 12:17) Koma silikamba kuti ndi angati amene adzakhalapo cisautso cacikulu cikadzayamba.

15, 16. N’ciani cimene tiyenela kudziŵa pa nkhani ya a 144,000 osankhidwa ndi Yehova?

15 Yehova ndiye amasankha nthawi yodzoza anthu. (Aroma 8:28-30) Yehova anayamba kusankha odzozedwa Yesu ataukitsidwa. Zikuoneka kuti m’nthawi ya atumwi, Akristu onse oona anali odzozedwa. Zaka zambili pambuyo pake, anthu ambili amene anali kukamba kuti ndi Akristu sanali Akristu oona. Ngakhale n’conco, Yehova anali kudzoza Akristu oona ocepa amene analipo. Iwo anali ngati tiligu amene Yesu anakamba kuti adzamela pakati pa namsongole. (Mateyu 13:24-30) M’masiku otsiliza ano, Yehova akusankhabe anthu amene adzakhala m’gulu la a 144,000. [2] (Onani mau akumapeto.) Cotelo, ngati Mulungu akusankha anthu ena mapeto atatsala pang’ono kufika, sitiyenela kuona ngati akulakwitsa. (Yesaya 45:9; Danieli 4:35; ŵelengani Aroma 9:11, 16.) [3] (Onani mau akumapeto.) Tiyenela kusamala kuti tisayambe kudandaula monga anchito a m’fanizo la Yesu. Iwo anadandaula cifukwa ca malipilo amene mbuye wao anapatsa anthu ena amene anayamba kugwila nchito mu ola lomaliza.—Ŵelengani Mateyu 20:8-15.

16 Si odzozedwa onse amene ndi mbali ya “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” (Mateyu 24:45-47) Mofanana ndi m’nthawi ya atumwi, Yehova ndi Yesu masiku ano akudyetsa kapena kuti kuphunzitsa anthu ambili pogwilitsila nchito anthu ocepa. M’nthawi ya atumwi, Mulungu anagwilitsila nchito Akristu odzozedwa ocepa kuti alembe Malemba Acigiliki Acikristu. Masiku anonso, ndi Akristu odzozedwa ocepa cabe amene ali ndi udindo wopatsa anthu a Mulungu “cakudya pa nthawi yoyenela.”

17. Mwaphunzila ciani m’nkhani ino?

17 N’ciani cimene taphunzila m’nkhani ino? Yehova adzapatsa anthu ambili mwai wokhala ndi moyo wosatha padziko lapansi, ndipo ena adzakhala ndi moyo kumwamba kuti adzalamulile ndi Yesu. Yehova adzapatsa atumiki ake onse mphoto, amene akuimilidwa ndi “Myuda” ndiponso amene akuimilidwa ndi “amuna 10.” Iye amafuna kuti tonse tizimvela malamulo ake ndi kukhalabe okhulupilika. Tonse tifunika kukhalabe odzicepetsa. Tonse tiyenela kum’tumikila pamodzi mogwilizana. Ndipo tonse tiyenela kucitapo kanthu kuti mpingo ukhalebe wogwilizana. Pamene mapeto akuyandikila, tiyeni tonse tipitilize kutumikila Yehova ndi kutsatila Kristu monga gulu limodzi la nkhosa.

^ [1] (ndime 3) Malinga ndi lemba la Salimo 87:5, 6, n’kutheka kuti m’dziko latsopano, Mulungu adzaulula maina a anthu onse amene adzakhala akulamulila ndi Yesu kumwamba.—Aroma 8:19.

^ [2] (ndime 15) Ngakhale kuti lemba la Machitidwe 2:33 limaonetsa kuti Yesu amakhala ndi mbali pamene munthu akudzozedwa, Yehova ndiye amaitana munthuyo.

^ [3] (ndime 15) Kuti mudziŵe zambili, ŵelengani nkhani yakuti “Mafunso Ocokela kwa Oŵelenga” mu Nsanja ya Olonda ya May 1, 2007, tsa 30-31.